Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mpumulo wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Mpumulo wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Mpumulo wa Mulungu N’chiyani?

“Mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.”​—AHEB. 4:9.

1, 2. Kodi tingaphunzire chiyani pa lemba la Genesis 2:3, ndipo tingafunse mafunso ati?

CHAPUTALA choyamba cha Genesis chimatiuza kuti Mulungu anakonza dziko lapansi m’masiku 6 ophiphiritsira kuti anthu akhalemo. Ponena za kumapeto a tsiku lililonse lophiphiritsira, buku la Genesis limanena kuti: “Panali madzulo ndiponso panali m’mawa.” (Gen. 1:5, 8, 13, 19, 23, 31) Koma ponena za tsiku la 7, Baibulo limati: “Mulungu anadalitsa tsiku la 7. Analipatula kuti likhale lopatulika, chifukwa kuyambira pa tsikuli, iye wakhala akupuma pa ntchito yake yonse yolenga.”​—Gen. 2:3.

2 Mawu akuti “wakhala akupuma” akusonyeza kuti tsiku la 7, lomwe ndi la mpumulo wa Mulungu, linali kupitirirabe pamene Mose ankalemba buku la Genesis mu 1513 B.C.E. Nanga masiku ano, kodi tsiku la mpumulo wa Mulungu likupitirirabe? Ngati ndi choncho, kodi tingalowe mu mpumulowo masiku ano? Mayankho a mafunso amenewa ndi ofunika kwambiri kwa ife.

Kodi Yehova ‘Akupumabe’?

3. Kodi mawu a Yesu a pa Yohane 5:16, 17 akusonyeza bwanji kuti tsiku la 7 linali kupitirirabe m’nthawi ya Yesu?

3 Pali mfundo ziwiri zotithandiza kudziwa kuti tsiku la 7 linali kupitirirabe m’nthawi ya Yesu ndiponso ya Akhristu oyambirira. Choyamba, taganizirani zimene Yesu anauza adani ake omwe ankamutsutsa chifukwa chochiritsa munthu pa Sabata. Adaniwo ankaona kuti iye analakwa pogwira ntchito pa Sabata. Yesu anawauza kuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.” (Yoh. 5:16, 17) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Mawu a Yesu akuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito” anayankha mlandu wakuti anagwira ntchito pa Sabata. Ponena zimenezi, Yesu anatanthauza kuti: ‘Ine ndi Atate wanga tikugwira ntchito yofanana. Popeza Atate wanga akhala akugwira ntchito pa Sabata lawo la zaka masauzande ambiri, inenso ndikhoza kugwira ntchito pa Sabata.’ Choncho mawu a Yesu akusonyeza kuti tsiku la 7, limene Mulungu anali kupuma pa ntchito yake yolenga zinthu padziko, linali kupitirirabe m’nthawi ya Yesu. Koma Mulungu anali kugwirabe ntchito kuti akwaniritse cholinga chake chokhudza anthu ndiponso dziko lapansi. *

4. Kodi Paulo anapereka umboni wotani wotsimikizira kuti tsiku la 7 linali kupitirirabe m’nthawi yake?

4 Mtumwi Paulo ananena mfundo yachiwiri. Asanagwire mawu a Genesis 2:2 onena za mpumulo wa Mulungu, iye analemba kuti: “Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mu mpumulowo.” (Aheb. 4:3, 4, 6, 9) Izi zikusonyeza kuti tsiku la 7 linali kupitirirabe m’nthawi ya Paulo. Koma kodi tsiku limeneli likupitirirabe?

5. Kodi cholinga cha tsiku la 7 n’chiyani ndipo chidzakwaniritsidwa liti?

5 Kuti tiyankhe funsoli tiyenera kukumbukira cholinga cha tsiku la 7. Lemba la Genesis 2:3 limafotokoza cholingachi kuti: “Mulungu anadalitsa tsiku la 7. Analipatula kuti likhale lopatulika.” Yehova ‘anapatula’ tsikuli pofuna kuti akwaniritse cholinga chake. Cholinga chimenechi n’chakuti padziko lapansi pakhale anthu omvera amene angalisamalire ndiponso kusamalira zamoyo zonse. (Gen. 1:28) Yehova Mulungu ndiponso Yesu Khristu, yemwe ndi “Mbuye wa sabata,” “akugwirabe ntchito mpaka pano” kuti akwaniritse cholinga chimenechi. (Mat. 12:8) Tsiku la mpumulo wa Mulungu lipitirirabe mpaka pamene cholinga chimenechi chidzakwaniritsidwa pa mapeto pa ulamuliro wa Khristu wa zaka 1,000.

‘Tisatengere Chitsanzo cha Kusamvera’

6. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene sitiyenera kutengera ndipo tikuphunzira chiyani pa zitsanzo zimenezi?

6 Mulungu anafotokoza cholinga chake momveka bwino kwa Adamu ndi Hava koma iwo anachita zosemphana ndi cholingachi. Adamu ndi Hava anali anthu oyambirira kusamvera Mulungu. Kuchokera nthawi imeneyo, anthu mamiliyoni ambiri akhala osamvera. Ngakhale Aisiraeli, omwe anali anthu osankhika a Mulungu, anali ndi chizolowezi chosamvera Mulungu. N’chifukwa chake Paulo anachenjeza Akhristu m’nthawi yake kuti ngakhale iwowo akhoza kuyamba chizolowezi chosamvera cha Aisiraeli akale. Iye analemba kuti: “Chotero, tiyeni tichite chilichonse chotheka kuti tilowe mu mpumulo umenewo, kuopera kuti wina angagwe ndi kutengera chitsanzo cha kusamvera cha makolo athuwo.” (Aheb. 4:11) Paulo anagwirizanitsa kusamvera ndi kulephera kulowa mu mpumulo wa Mulungu. Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Kodi zikutanthauza kuti tikachita zinthu zinazake zosemphana ndi cholinga cha Mulungu, tikhoza kulephera kulowa nawo mu mpumulo wa Mulungu? Tikambirana yankho la funso limeneli m’nkhani ino chifukwa ndi lofunika kwambiri kwa ife. Koma panopa tiyeni tikambirane za chitsanzo choipa cha Aisiraeli kuti tione zinthu zina zokhudza kulowa mu mpumulo wa Mulungu.

“Sadzalowa mu Mpumulo Wanga”

7. Kodi cholinga cha Yehova polanditsa Aisiraeli ku Iguputo chinali chiyani ndipo Aisiraeliwo anayenera kuchita chiyani?

7 M’chaka cha 1513 B.C.E., Yehova anauza mtumiki wake Mose za cholinga chake chokhudza Aisiraeli. Mulungu anati: “Nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo, ndi kuwatulutsa m’dzikolo [Iguputo], n’kuwalowetsa m’dziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.” (Eks. 3:8) Cholinga cha Yehova polanditsa Aisiraeli “m’manja mwa Aiguputo” chinali choti iwo akhale anthu ake. Izi n’zogwirizana ndi zimene iye analonjeza kholo lawo, Abulahamu. (Gen. 22:17) Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulo amene akanawathandiza kukhala naye pa ubwenzi wabwino. (Yes. 48:17, 18) Iye anauza Aisiraeli kuti: “Ngati mudzalabadiradi mawu anga ndi kusunga pangano langa [limene analifotokoza m’Chilamulo], pamenepo mudzakhaladi chuma changa chapadera pakati pa anthu ena onse, chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa.” (Eks. 19:5, 6) Choncho Aisiraeli anayenera kumvera mawu a Mulungu kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi iye.

8. Kodi Aisiraeli akanakhala ndi moyo wotani ngati akanamvera Mulungu?

8 Tangoganizirani za moyo wabwino kwambiri umene Aisiraeli akanakhala nawo ngati akanamvera mawu a Mulungu. Yehova akanadalitsa minda ndiponso ziweto zawo. Mulungu akanawatetezanso kwa adani awo. (Werengani 1 Mafumu 10:23-27.) Ngakhale pa nthawi imene Mesiya anabwera, iye akanapeza Aisiraeli ali pa ufulu osati akuponderezedwa ndi Aroma. Ufumu wa Isiraeli ukanakhala wachitsanzo kwa mitundu yonse yowazungulira. Ukanaperekanso umboni wosatsutsika wakuti kumvera Mulungu woona kumabweretsa madalitso auzimu ndiponso akuthupi.

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Aisiraeli analakwitsa kwambiri ponena kuti akufuna kubwerera ku Iguputo? (b) Kodi kubwerera ku Iguputo kukanasokoneza bwanji kulambira kwa Aisiraeli?

9 Aisiraeli anali ndi mwayi waukulu kwambiri. Yehova akanawagwiritsa ntchito kukwaniritsa cholinga chake ndipo izi zikanabweretsa madalitso kwa iwowo ndiponso kwa mabanja onse padziko lapansi. (Gen. 22:18) Koma pa nthawiyi, Aisiraeli ambiri anasonyeza kuti sakufuna kukhala ufumu wolamuliridwa ndi Mulungu umene ukanapereka chitsanzo chabwino ku mitundu ina. Iwo anafika ngakhale ponena kuti akufuna kubwerera ku Iguputo. (Werengani Numeri 14:2-4.) Kodi kubwerera ku Iguputo kukanawathandiza kukwaniritsa cholinga cha Mulungu choti iwo akhale ufumu wachitsanzo chabwino? Ayi ndithu. Ngati Aisiraeli akanabwerera n’kukakhala akapolo a anthu osalambira Mulungu sakanakhalanso ndi mwayi wotsatira Chilamulo cha Mose. Iwo sakanapindulanso ndi dongosolo la Yehova lokhululukira machimo awo. Apa zikungosonyezeratu kuti sankaganizira za Mulungu ndiponso cholinga chake. M’pake kuti Yehova ananena za anthu opandukawa kuti: “Ndinanyansidwa ndi m’badwo umenewo, ndipo ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera, ndipo sadziwa njira zanga.’ Choncho ndinalumbira mu mkwiyo wanga kuti, ‘Sadzalowa mu mpumulo wanga.’”​—Aheb. 3:10, 11; Sal. 95:10, 11.

10 Ponena kuti akufuna kubwerera ku Iguputo, anthu osamverawa anasonyeza kuti zinthu monga anyezi ndi adyo, zimene zinali ku Iguputo, n’zofunika kwambiri kwa iwo kuposa madalitso auzimu amene analandira. (Num. 11:5) Mofanana ndi Esau, anthu opandukawa akanalolera kutaya madalitso auzimu kuti apeze chakudya chokoma.​—Gen. 25:30-32; Aheb. 12:16.

11. Kodi kusakhulupirika kwa Aisiraeli m’nthawi ya Mose kunalepheretsa Mulungu kukwaniritsa cholinga chake?

11 Ngakhale kuti Aisiraeli amene anachoka ku Iguputo sanali okhulupirika kwa Yehova, iye sanasinthe cholinga chake chokhudza mtunduwo. Mosiyana ndi iwowo, ana awo ankamvera Mulungu. Anawo anamvera lamulo la Yehova loti alowe m’Dziko Lolonjezedwa n’kuyamba kugonjetsa mitundu ya kumeneko. Lemba la Yoswa 24:31 limanena kuti: “Aisiraeli anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akulu amene anapitiriza kukhalabe ndi moyo Yoswa atamwalira, omwe ankadziwa ntchito zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli.”

12. Kodi tikudziwa bwanji kuti n’zotheka kulowa mu mpumulo wa Mulungu masiku ano?

12 Koma Aisiraeli omverawa atakalamba n’kufa, m’badwo wotsatira “sunadziwe Yehova kapena ntchito zimene iye anachitira Isiraeli.” Ndiyeno “ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova, n’kuyamba kutumikira Abaala.” (Ower. 2:10, 11) Choncho Dziko Lolonjezedwa silinakhale ‘malo ampumulo’ kwa iwo. Chifukwa chosamvera, sanakhale pa mtendere ndi Mulungu kosatha. Paulo ananena za Aisiraeli amenewa kuti: “Ngati Yoswa anawalowetsa m’malo ampumulo, Mulungu sakananenanso pambuyo pake za tsiku lina.” Kenako iye anati: “Chotero mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.” (Aheb. 4:8, 9) Ponena kuti “anthu a Mulungu,” Paulo ankanena za Akhristu. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akhristu angalowe mu mpumulo wa Mulungu? Inde, Akhristu achiyuda komanso a mitundu ina akhoza kulowa mu mpumulowu.

Ena Analephera Kulowa Nawo mu Mpumulo wa Mulungu

13, 14. (a) Kodi m’nthawi ya Mose, Aisiraeli anayenera kuchita chiyani kuti alowe mu mpumulo wa Mulungu? (b) Kodi m’nthawi ya Paulo, Akhristu anayenera kuchita chiyani kuti alowe mu mpumulo wa Mulungu?

13 Nthawi imene Paulo ankalembera Akhristu achiheberi, ankadera nkhawa kuti ena a iwo sankachita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. (Werengani Aheberi 4:1.) Kodi iwo ankatani? Iwo anali kutsatirabe zinthu zina za m’Chilamulo cha Mose. Kwa zaka zoposa 1,500, Aisiraeli amene ankafuna kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu anayenera kutsatira Chilamulo. Koma Chilamulocho chinachotsedwa pamene Yesu anafa. Akhristu ena sanazindikire zimenezi ndipo ankatsatirabe zinthu zina za m’Chilamulo. *

14 Paulo anafotokozera Akhristu achiheberi amenewa kuti Yesu anali mkulu wa ansembe wabwino kuposa mkulu wa ansembe aliyense wopanda ungwiro. Iye anasonyeza kuti pangano latsopano linali labwino kuposa pangano limene Mulungu anachita ndi Isiraeli. Anasonyezanso kuti kachisi wauzimu wa Yehova ndi ‘wamkulu ndi wangwiro kwambiri’ kuposa wopangidwa “ndi manja a anthu.” (Aheb. 7:26-28; 8:7-10; 9:11, 12) Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Sabata la m’Chilamulo cha Mose kuti afotokoze mmene Akhristu angalowere mu tsiku la mpumulo wa Yehova. Iye analemba kuti: “Mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu. Munthu amene walowa mu mpumulo wa Mulungu, ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake, monga mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake.” (Aheb. 4:8-10) Akhristu achiheberi amenewa anayenera kusiya kuganiza kuti angapeze mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova chifukwa cha ntchito zawo zotsatira Chilamulo cha Mose. Kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., Mulungu anayamba kupereka mwaulere mwayi umenewu kwa anthu amene amakhulupirira Yesu Khristu.

15. Ngati tikufuna kulowa mu mpumulo wa Mulungu, n’chifukwa chiyani kumvera kuli kofunika?

15 Kodi n’chiyani chinalepheretsa Aisiraeli m’nthawi ya Mose kuti alowe m’Dziko Lolonjezedwa? Kunali kusamvera. Nanga n’chiyani chinalepheretsa Akhristu ena m’nthawi ya Paulo kuti alowe mu mpumulo wa Mulungu? Kunalinso kusamvera komweko. Iwo sanazindikire kuti Chilamulo chinasiya kugwira ntchito ndipo Yehova ankafuna kuti anthu ake azichita zinthu zina pomulambira.

Zimene Tingachite Kuti Tilowe mu Mpumulo wa Mulungu

16, 17. (a) Kodi Akhristu angalowe bwanji mu mpumulo wa Mulungu masiku ano? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

16 Masiku ano, ife sitikhulupirira zoti Akhristu ayenera kutsatira Chilamulo cha Mose kuti apulumutsidwe. Mawu a Paulo kwa Aefeso ndi omveka bwino. Iye anati: “Mwa kukoma mtima kwakukulu kumeneku, ndithudi mwapulumutsidwa kudzera m’chikhulupiriro, osati mwa inu nokha, koma monga mphatso ya Mulungu. Si chifukwanso cha ntchito ayi, kuti munthu asakhale ndi chifukwa chodzitamandira.” (Aef. 2:8, 9) Ndiyeno kodi Akhristu angalowe bwanji mu mpumulo wa Mulungu masiku ano? Yehova anapatula tsiku la 7 monga tsiku lake lopumula kuti akwaniritse cholinga chake chokhudza dziko lapansi. Kudzera m’gulu lake, Yehova amatiuza za cholinga chake ndiponso zimene akufuna kuti tizichita. Tikhoza kulowa mu mpumulo wa Yehova ngati timamumvera ndiponso kugwira ntchito mogwirizana ndi gulu lake.

17 Koma ngati sitimvera malangizo ochokera m’Baibulo amene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsa n’kumafuna kuchita zinthu zathuzathu, ndiye kuti tikusemphana ndi cholinga cha Mulungu. Izi zikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zinthu zina zimene anthu a Mulungu angakumane nazo zomwe zingatipatse mwayi wosonyeza kuti ndife anthu omvera. Zimene timachita tikakumana ndi zinthu zimenezi zimasonyeza ngati talowa mu mpumulo wa Mulungu kapena ayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ansembe ndi Alevi ankagwira ntchito tsiku la Sabata pakachisi koma ‘ankakhalabe osalakwa.’ Popeza Yesu ndi mkulu wa ansembe wa kachisi wamkulu wauzimu wa Mulungu, iye akanatha kugwira ntchito yake yauzimu osaopa kuti akuphwanya lamulo la Sabata.​—Mat. 12:5, 6.

^ ndime 13 Sitikudziwa ngati Akhristu ena achiheberi ankapereka nsembe pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo pambuyo pa Pentekosite mu 33 C.E. Koma ngati ankatero, ndiye kuti sankalemekeza nsembe ya Yesu. Chomwe tikudziwa n’chakuti Akhristu ena achiheberi anali kutsatirabe miyambo ina ya mu Chilamulo cha Mose.​—Agal. 4:9-11.

Mafunso Oyenera Kuwasinkhasinkha

• Kodi cholinga cha tsiku la 7 lomwe ndi la mpumulo wa Mulungu n’chiyani?

• Kodi tikudziwa bwanji kuti tsiku la 7 likupitirirabe masiku ano?

• N’chiyani chinalepheretsa Aisiraeli m’nthawi ya Mose ndiponso Akhristu ena m’nthawi ya Paulo kulowa mu mpumulo wa Mulungu?

• Kodi Akhristu angalowe bwanji mu mpumulo wa Mulungu masiku ano?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Tikhoza kulowa mu mpumulo wa Yehova ngati timamumvera ndiponso kugwira ntchito mogwirizana ndi gulu lake

[Zithunzi pamasamba 26, 27]

Kuyambira kale, kodi chofunika n’chiyani kuti anthu a Mulungu alowe mu mpumulo wake?