Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinkaopa Imfa Koma Tsopano Ndikuyembekezera ‘Moyo Wochuluka’

Ndinkaopa Imfa Koma Tsopano Ndikuyembekezera ‘Moyo Wochuluka’

Ndinkaopa Imfa Koma Tsopano Ndikuyembekezera ‘Moyo Wochuluka’

Yosimbidwa ndi Piero Gatti

M’CHAKA cha 1943 ndi 1944, mumzinda wa Milan ku Italy munali nkhondo. Nthawi ndi nthawi kunali kumveka phokoso limene linkawonjezekawonjezeka. Kenako kunkalira mabelu ochenjeza anthu kupeza malo otetezeka. Ndiyeno kunkachitika phokoso loboola m’makutu la mabomba akuphulika komanso kuwononga zinthu ndipo anthu ankachita mantha.

Ine ndinali msilikali wachinyamata mumzindawu nthawi imeneyo. Nthawi zambiri ndinkauzidwa kuchotsa mitembo m’nyumba zimene anakonza kuti anthu azikabisalamo kukamaphulika mabomba. Nthawi zina nyumbazi zinkaphulitsidwanso. Anthu obisalawo sankatha kutuluka ndipo ankafera momwemo n’kunyenyekanyenyeka moti munthu sangawazindikire. Koma sindinkangoona imfa ya anthu ena okha. Inenso nthawi zina ndinkatsala pang’ono kuphedwa. Pa nthawi zimenezi ndinkapemphera kwa Mulungu n’kumulonjeza kuti ndikapulumuka, ndidzachita chifuniro chake.

Ndinasiya Kuopa Imfa

Ndinakulira m’mudzi umene unali pa mtunda wa makilomita 10 kuchokera kutauni ya Como ku Italy. Tauni imeneyi ili pafupi ndi malire a dzikoli ndi la Switzerland. Ndili wamng’ono ndinakumana ndi zinthu zomvetsa chisoni ndipo ndinkaopa imfa. Achemwali anga awiri anafa ndi chimfine cha ku Spain. Kenako mu 1930 pamene ndinali ndi zaka 6, amayi anga a Luigia anamwalira. Popeza kuti ndinakulira m’chipembedzo cha Katolika, ndinkatsatira malamulo a chipembedzochi ndiponso ndinkapita ku Misa mlungu uliwonse. Koma patapita zaka, ndinasiya kuopa imfa chifukwa cha zimene zinachitika kumalo ometera tsitsi osati kutchalitchi.

M’chaka cha 1944, anthu ankaphedwa kwambiri pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Ine ndinali mmodzi wa asilikali masauzande ambiri a ku Italy amene anathawira ku dziko la Switzerland limene silinkamenya nawo nkhondo. Titafika anatitengera kumisasa ya anthu othawa kwawo. Ine ananditumiza kumsasa wa pafupi ndi mudzi wa Steinach umene uli kumpoto chakum’mawa kwa dzikoli. Kumeneko anatipatsa ufulu ndithu. Ndiyeno munthu wina amene ankameta tsitsi ku Steinach ankafuna thandizo kumalo ake ometera. Ndinakhala naye ndiponso kugwira naye ntchito kwa mwezi umodzi wokha. Koma nthawi imeneyi inali yokwanira kuti ndiyambe kucheza ndi munthu amene anandithandiza kusintha moyo wanga.

Munthu wina amene ankakonda kubwera kudzametetsa anali Adolfo Tellini. Iye anali wa ku Italy koma ankakhala ku Switzerland ndipo anali wa Mboni za Yehova. Ndinali ndisanamvepo za gulu limeneli chifukwa pa nthawiyo ku Italy kunali Mboni zosapitirira 150. Adolfo anandiuza mfundo za choonadi zosangalatsa zochokera m’Baibulo. Mfundo zake zinali zokhudza malonjezo a mtendere ndiponso ‘moyo wochuluka.’ (Yoh. 10:10; Chiv. 21:3, 4) Ndinachita chidwi kwambiri kumva uthenga wakuti nkhondo ndi imfa zidzatha. Nditabwerera kumsasa kuja, ndinauza mnyamata wina wa ku Italy dzina lake Giuseppe Tubini za chiyembekezo chimenechi ndipo nayenso anachita chidwi kwambiri. Adolfo limodzi ndi Mboni zina ankabwera kumsasaku kudzationa.

Tsiku lina Adolfo ananditengera kutauni ya Arbon imene inali pa mtunda wa makilomita 10 kuchokera ku Steinach. Kutauni imeneyi kagulu ka Mboni za Yehova kankachita misonkhano m’Chitaliyana. Ndinasangalala kwambiri ndi zimene ndinamva kumeneko moti mlungu wotsatira ndinapitako wapansi. Nthawi ina ndinapita ku msonkhano waukulu wa Mboni za Yehova kuholo ya mumzinda wa Zurich. Ndinakhudzidwa kwambiri nditaona zithunzi za anthu amene anaphedwa kumisasa yophera anthu. Ankaonetsa mitembo ya anthu itaunjikidwa milumilu. Ndinamva kuti Mboni zambiri za ku Germany zinaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Pa msonkhano umenewu ndinakumana ndi Maria Pizzato. Iye analamulidwa ndi boma lopondereza la ku Italy kuti akhale m’ndende zaka 11 chifukwa chakuti anali wa Mboni za Yehova.

Nkhondo itatha, ndinabwerera ku Italy ndipo ndinkasonkhana ndi mpingo waung’ono wa ku Como. Palibe amene ankapanga nane phunziro la Baibulo koma ndinkadziwa bwino mfundo zazikulu za choonadi. Nayenso Maria Pizzato ankasonkhana mu mpingo umenewu. Iye anandiuza kuti ndiyenera kubatizidwa ndipo anandipempha kuti ndikaonane ndi Marcello Martinelli, amene ankakhala ku Castione Andevenno m’chigawo cha Sondrio. Marcello anali m’bale wodzozedwa wokhulupirika. Pa nthawi ya boma lopondereza, iye analamulidwa kuti akhale m’ndende zaka 11. Ndinayenera kuyenda makilomita 80 pa njinga kuti ndikafike kwa Marcello.

Marcello anagwiritsa ntchito Baibulo kuti andiuze zimene ndiyenera kuchita kuti ndibatizidwe ndipo titapemphera tinapita kumtsinje wa Adda kumene ndinakabatizidwa. Izi zinachitika mu September 1946. Limeneli linali tsiku lapadera kwambiri. Ndinali wosangalala kwambiri kuti ndasankha kutumikira Yehova ndiponso kuti ndinali ndi chiyembekezo chabwino moti madzulo ake sizinkadziwikanso kuti ndapalasa njinga mtunda wa makilomita 160.

Mu May 1947, ku Milan kunachitika msonkhano waukulu ndipo unali woyamba kuchitika ku Italy nkhondo itatha. Kunali anthu pafupifupi 700 ndipo ambiri anali amene anazunzidwa nthawi imene boma lopondereza linkalamulira. Ku msonkhano umenewu kunachitika chinthu chochititsa chidwi. Giuseppe Tubini, amene ndinamulalikira kumsasa wa anthu othawa kwawo uja, anakamba nkhani ya ubatizo ndipo kenako iyeyo anabatizidwa.

Ku msonkhano umenewu, ndinali ndi mwayi wokumana ndi M’bale Nathan Knorr wa ku Beteli ya ku Brooklyn. Iye analimbikitsa ine ndi Giuseppe kuti tigwiritse ntchito moyo wathu kutumikira Mulungu. Ndinaganiza zoyamba utumiki wa nthawi zonse pasanathe mwezi umodzi. Nditabwerera kunyumba, ndinauza banja langa zimene ndikufuna kuchita ndipo anayesa kundiletsa. Koma ine sindinalole. Patangotha mwezi umodzi, ndinayamba kutumikira ku Beteli ya ku Milan. Amishonale anayi omwe ankatumikira kumeneko anali Giuseppe (Joseph) Romano ndi mkazi wake Angelina ndiponso Carlo Benanti ndi mkazi wake Costanza. Munthu wachisanu anali Giuseppe Tubini, yemwe anali atangofika kumene, ndipo ine ndinali wa 6.

Nditakhala mwezi umodzi ku Beteli, anandiuza kuti ndikhale woyang’anira dera. Ndinali woyang’anira dera woyamba wobadwira ku Italy komweko. M’bale George Fredianelli anali mmishonale woyamba kubwera ku Italy kuchokera ku United States mu 1946, ndipo pa nthawi imene ndinkayamba n’kuti iye ali kale woyang’anira woyendayenda. Iye anandiphunzitsa milungu yochepa kenako ndinayamba kuchita zonse ndekha. Ndikukumbukira bwino mpingo wa Faenza umene unali woyamba kuuchezera. Tangoganizani, m’mbuyo monsemu ndinali ndisanakambepo nkhani mu mpingo. Ngakhale zinali choncho, ndinalimbikitsa omvera onse, kuphatikizapo achinyamata ambiri, kuti ayambe utumiki wa nthawi zonse. Patapita nthawi, ena a achinyamata amenewa anapatsidwa maudindo akuluakulu ku Italy.

Ndinakumana ndi zinthu zambiri potumikira monga woyang’anira dera. Mu ntchitoyi, ndinkakumana ndi zinthu zosayembekezereka, mavuto, zinthu zosangalatsa ndiponso ndinkayenera kuzolowera zinthu zachilendo. Koma abale ndi alongo okondedwa ankandisonyeza chikondi kwambiri.

Mmene Nkhani Zachipembedzo Zinalili ku Italy Nkhondo Itatha

Tsopano ndiloleni ndikufotokozereni mmene zinthu zokhudza chipembedzo zinalili ku Italy pa nthawi imeneyo. Tchalitchi cha Katolika chinali champhamvu kwambiri moti panalibe chopikisana nacho. Ngakhale kuti malamulo atsopano anayamba kugwira ntchito mu 1948, malamulo oletsa Mboni za Yehova kulalikira mwaufulu, amene boma lopondereza linakhazikitsa, anatha mu 1956. Chifukwa cha atsogoleri achipembedzo, nthawi zambiri misonkhano yadera inkasokonezedwa. Koma nthawi zina zofuna za atsogoleriwo zinkalephereka. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika mu 1948 ku katauni kotchedwa Sulmona kamene kali m’chigawo chapakati ku Italy.

Ku Sulmona kunali msonkhano waukulu womwe unkachitikira m’holo inayake. Lamlungu m’mawa ine ndinali tcheyamani ndipo Giuseppe Romano anakamba nkhani ya onse. Pa nthawiyo, m’dziko lonse munali ofalitsa osakwana 500 koma pa msonkhanowu panafika anthu okwana 2,000. Choncho tingati kunabwera anthu ambiri pa msonkhanowu. Nkhani ya onse itatha, munthu wina wachinyamata, amene anatumidwa ndi ansembe awiri, anakwera kupulatifomu. Pofuna kusokoneza msonkhano, anayamba kukuwa kwambiri. Nthawi yomweyo ndinamuuza kuti, “Ngati muli ndi mawu, nanunso muchite lendi holo kuti munene chilichonse chimene mukufuna.” Ndiyeno gulu lonse linayamba kulankhula zinthu zosonyeza kuti silikusangalala moti mawu ake sankamvekanso. Zitatero, munthuyu anathawa.

Pa nthawi imeneyo, pankachitika zambiri m’ntchito yoyendayenda. Nthawi zina pochoka kumpingo wina kupita kumpingo wina ndinkayenda pansi, pa njinga, m’mabasi akalekale omwe ankakhala odzadza kwambiri apo ayi pa sitima. Nthawi zina ndinkagona m’khola kapena m’nyumba yosungiramo zipangizo. Nkhondo inali itangotha kumene ndipo anthu ambiri ku Italy anali pa umphawi. Kunali abale ochepa ndipo nawonso anali osauka. Ngakhale zinali choncho, kutumikira Yehova kunali kosangalatsa.

Maphunziro a ku Giliyadi

Mu 1950, ine ndi Giuseppe Tubini tinaitanidwa kuti tikalowe kalasi ya nambala 16 ya sukulu ya Giliyadi yophunzitsa amishonale. Nditangofika, ndinazindikira kuti zindivuta kuphunzira Chingelezi. Ndinayesetsa kwambiri koma zinali zovuta. Tinkafunika kuwerenga Baibulo lonse m’Chingelezi. Kuti izi zitheke, nthawi zina sindinkapita kukadya chakudya masana n’cholinga choti ndiziyeserera kuwerenga mokweza. Ndiyeno linafika tsiku loti ndikambe nkhani. Ndimakumbukirabe bwinobwino zimene mlangizi ananena. Iye anati, “Mmene umagwiritsira ntchito manja ndiponso mphamvu ya mawu zili bwino kwambiri koma Chingelezi chako ndiye iii! N’chosamveka.” Ngakhale kuti zinkandivuta, ndinamaliza maphunzirowo bwinobwino. Titamaliza, ine ndi Giuseppe tinauzidwa kuti tibwerere ku Italy kukatumikira kumeneko. Maphunziro owonjezereka amene tinalandira anatithandiza kutumikira bwino abale.

Mu 1955 ndinakwatira Lidia, yemwe ndinali nditakamba nkhani ya ubatizo wake zaka 7 m’mbuyomo. Bambo ake a Domenico anali m’bale wabwino kwambiri ndipo anathandiza ana ake onse 7 kukhala m’choonadi. Anachita zimenezi ngakhale kuti anazunzidwa ndi boma lopondereza ndipo analamulidwa kuti akakhale kudera lina mosiyana ndi banja lawo kwa zaka zitatu. Lidia nayenso anali wolimbikira kwambiri m’choonadi. Mboni zisanalandire ufulu wolalikira kunyumba ndi nyumba, iye anasumiridwa mlandu katatu. Titakhala m’banja zaka 6, mwana wathu woyamba dzina lake Beniamino anabadwa. Mu 1972 tinaberekanso mwana wina wamwamuna dzina lake Marco. Ndine wosangalala kwambiri kuti iwo limodzi ndi mabanja awo akutumikira Yehova mwakhama.

Ndikuchitabe Zonse Zimene Ndingathe mu Utumiki wa Yehova

Pa moyo wanga wosangalatsa wotumikira anthu ena, ndakumana ndi zinthu zambiri zosaiwalika. Mwachitsanzo, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1980, apongozi anga analembera kalata Sandro Pertini, yemwe anali pulezidenti wa Italy nthawi imeneyo. Pa nthawi ya boma lopondereza, apongozi anga limodzi ndi pulezidentiyu anatumizidwa kukakhala ku chilumba cha Ventotene, kumene ankasungako anthu onse amene boma linkaona kuti ndi adani. Apongozi anga anapempha zoti akambirane ndi pulezidentiyu n’cholinga choti amulalikire. Ataloledwa, ndinatsagana nawo ndipo tinalandiridwa bwino kwambiri. Zimenezi zinali zachilendo chifukwa sitinkayembekezera kuti angatilandire bwino choncho. Polandira apongozi anga, pulezidentiyo anawakumbatira mwachikondi. Kenako tinakambirana naye za chikhulupiriro chathu n’kumupatsa mabuku ena.

Mu 1991 ndinapuma pambuyo pogwira ntchito yoyang’anira dera kwa zaka 44 ndipo pa nthawiyi ndinali nditayendera mipingo m’dziko lonse la Italy. Kwa zaka zinayi zotsatira ndinkatumikira monga woyang’anira Nyumba ya Msonkhano koma kenako ndinadzasiya chifukwa cha kudwala. Chifukwa cha kukoma mtima kwa Yehova, ndikupitirizabe utumiki wa nthawi zonse. Ndimachita zonse zimene ndingathe polalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino ndipo panopa ndili ndi maphunziro a Baibulo. Abale amanenabe kuti nkhani zanga ndimazikamba “motenthedwa maganizo kwambiri.” Ndikuthokoza Yehova chifukwa ngakhale kuti ndine wokalamba ndikumutumikirabe mwakhama.

Ndili mwana, ndinkaopa kwambiri imfa koma chifukwa chophunzira choonadi cha m’Baibulo, ndili ndi chiyembekezo cha moyo wosatha kapena kuti ‘moyo wochuluka’ malinga ndi mawu a Yesu. (Yoh. 10:10) Panopa ndikuyembekezera moyo wabwino, wamtendere, wotetezeka, wosangalatsa ndiponso madalitso ambiri ochokera kwa Yehova. Ulemerero wonse upite kwa Mlengi wathu wachikondi amene tili ndi mwayi wodziwika ndi dzina lake.​—Sal. 83:18.

[Mapu pamasamba 22, 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

SWITZERLAND

BERN

Zurich

Arbon

Steinach

ITALY

ROME

Como

Milan

Mtsinje wa Adda

Castione Andevenno

Faenza

Sulmona

Ventotene

[Chithunzi patsamba 22]

Tikupita ku Giliyadi

[Chithunzi patsamba 22]

Ndili ndi Giuseppe ku Giliyadi

[Chithunzi patsamba 23]

Tsiku la ukwati wathu

[Chithunzi patsamba 23]

Mkazi wanga wokondedwa watumikira nane limodzi kwa zaka zoposa 55