Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nsanja ya Olonda Yatsopano ya M’Chingelezi Chosavuta

Nsanja ya Olonda Yatsopano ya M’Chingelezi Chosavuta

Nsanja ya Olonda Yatsopano ya M’Chingelezi Chosavuta

NDIFE osangalala kukudziwitsani kuti tayamba kusindikiza Nsanja ya Olonda yatsopano ya m’Chingelezi chosavuta. Tiyesa kuchita zimenezi kwa chaka chimodzi ndipo tikaona kuti ikuthandiza tipitiriza. M’magazini imeneyi muzikhala nkhani zophunzira ndipo ngati malo alipo muzikhalanso nkhani zina. Tikukhulupirira kuti ithandiza Mboni za Yehova zambiri kupindula ndi chakudya chauzimu. N’chifukwa chiyani tikutero?

Chingelezi chimalankhulidwa kwambiri ndi abale a m’mayiko monga Fiji, Ghana, Kenya, Liberia, Nigeria, Papua New Guinea, ndi Solomon Islands. Ngakhale kuti abale athu m’mayiko amenewa amalankhula zinenero zina, nthawi zambiri iwo amagwiritsa ntchito Chingelezi ku misonkhano ya mpingo ndiponso mu utumiki wakumunda. Koma Chingelezi chimene amalankhula n’chosavuta tikayerekeza ndi chimene chimakhala m’mabuku athu. Komanso pali anthu ena a Yehova amene anasamukira m’mayiko ena. Anthu amenewa amafunika kulankhula Chingelezi kuti amvane ndi anthu ena ngakhale kuti iwowo sachidziwa bwino. Vuto lina n’lakuti m’mayiko ngati amenewa misonkhano sichitika m’chilankhulo chawo.

Njira yaikulu imene timalandirira chakudya chauzimu pa nthawi yake ndi kudzera m’nkhani zimene timaphunzira mlungu uliwonse pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Choncho pofuna kuti aliyense azipindula ndi nkhanizi, mu Nsanja ya Olonda yatsopanoyi tikugwiritsa ntchito mawu ndi ziganizo zosavuta. Chikuto cha magazini imeneyi chizikhala chosiyana ndi cha magazini ya nthawi zonse. Koma timitu, ndime, mafunso obwereza ndiponso zithunzi zizigwirizana ndi za m’magazini ya nthawi zonse. Choncho pa Phunziro la Nsanja ya Olonda munthu akhoza kugwiritsa ntchito magazini iliyonse n’kutsatira bwinobwino. Kuti muone kusiyana kwa Chingelezi m’magazini awiriwa, onani mabokosi amene ali m’munsimu. Mabokosiwa akusonyeza ziganizo zochokera m’ndime yachiwiri ya m’nkhani yophunzira yoyamba m’magazini ino. Bokosi lakumanzere lili ndi Chingelezi cha m’magazini ya nthawi zonse ndipo lakumanja lili ndi Chingelezi chosavuta.

Tikukhulupirira kuti magazini ya Chingelezi chosavuta imeneyi iyankha mapemphero a anthu ambiri amene amapempha Yehova kuti: “Ndithandizeni kukhala wozindikira, kuti ndiphunzire malamulo anu.” (Sal. 119:73) Tikukhulupiriranso kuti magazini imeneyi ithandiza anthu amene sadziwa bwino Chingelezi ndiponso ana olankhula Chingelezi kuti azitha kukonzekera bwino Phunziro la Nsanja ya Olonda mlungu uliwonse. Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chakuti akugwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti apereke chakudya chauzimu chochuluka. Akuchita zimenezi chifukwa chokonda kwambiri “gulu lonse la abale.”​—Mat. 24:45; 1 Pet. 2:17.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova