Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ankayembekezera Mesiya

Anthu Ankayembekezera Mesiya

Anthu Ankayembekezera Mesiya

“Anthu anali kuyembekezera Khristu, ndipo onse anali kuganiza m’mitima yawo za Yohane kuti: ‘Kodi Khristu uja si ameneyu?’”​—LUKA 3:15.

1. Kodi abusa ena anamva uthenga wotani wochokera kwa mngelo?

KUNJA kunali kutada ndipo abusa anali kuyang’anira nkhosa zawo kubusa. Mwadzidzidzi mngelo wa Yehova anaima pafupi ndi abusawo ndipo kuwala kwa ulemerero wa Mulungu kunazungulira pamalo onsewo. Iwo anachita mantha koma anamvetsera uthenga wosangalatsa umene mngeloyo anapereka. Iye anati: “Musaope! Ine ndabwera kudzalengeza kwa inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu chimene anthu onse adzakhala nacho. Chifukwa lero wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.” Mwana amene mngeloyu ankanena ndi amene anali kudzakhala Khristu kapena kuti Mesiya. Mngeloyo anauza abusawo kuti mwanayo akamupeza modyeramo ziweto m’tauni yapafupi. Kenako mwadzidzidzi “khamu lalikulu lakumwamba” linayamba kutamanda Yehova n’kumanena kuti: “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.”​—Luka 2:8-14.

2. Kodi mawu akuti “Mesiya” amatanthauza chiyani ndipo anthu akanamudziwa bwanji?

2 Abusa achiyudawa ankadziwa kuti mawu akuti “Mesiya” kapena “Khristu” amatanthauza “Wodzozedwa.” (Eks. 29:5-7) Koma kodi akanatani kuti adziwe zambiri ndiponso kuti athandize ena kukhulupirira kuti mwana amene mngeloyu ankanena adzakhaladi Mesiya wosankhidwa ndi Yehova? Iwo akanachita zimenezi poona ngati zochita za mwanayo ndiponso zimene zinachitika pa moyo wake zikukwaniritsa maulosi a m’Malemba Achiheberi.

N’chifukwa Chiyani Anthu Anali Kuyembekezera Mesiya?

3, 4. Kodi ulosi wa Danieli 9:24, 25 unakwaniritsidwa bwanji?

3 Patapita zaka zambiri kuchokera pamene mngelo analankhula ndi abusawo, Yohane M’batizi anayamba ntchito yake yolalikira. Zimene ankanena ndiponso zimene ankachita zinachititsa anthu kuganiza kuti iyeyo anali Mesiya. (Werengani Luka 3:15.) N’kutheka kuti panali anthu ena amene ankadziwa molondola tanthauzo la ulosi wokhudza Mesiya wonena za “milungu 70.” Ngati ndi choncho, iwo ankadziwa nthawi imene Mesiya anali kubwera. Mawu ena a ulosiwu ndi akuti: “Kuchokera pamene mawu adzamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso, kufika pamene Mesiya Mtsogoleri adzaonekere, padzadutsa milungu 7, komanso milungu 62.” (Dan. 9:24, 25) Akatswiri ena amavomereza kuti milungu imeneyi ndi ya zaka. Mwachitsanzo, Baibulo lina limati: “Milungu 70 ya zaka yaikidwa.”​—Revised Standard Version.

4 Milungu 69 yotchulidwa pa Danieli 9:25 ndi zaka zokwana 483. Masiku ano, atumiki a Yehova amadziwa kuti milungu 69 imeneyi inayamba mu 455 B.C.E. M’chaka chimenechi, Mfumu Aritasasita ya Perisiya inauza Nehemiya kuti akakonze ndi kumanganso Yerusalemu. (Neh. 2:1-8) Milungu imeneyi inatha pambuyo pa zaka 483 mu 29 C.E. M’chaka chimenechi Yesu wa ku Nazareti anabatizidwa ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera kuti akhale Mesiya.​—Mat. 3:13-17. *

5. Kodi tikambirana maulosi ati?

5 M’Baibulo muli maulosi ambiri onena za Mesiya. Tsopano tiyeni tikambirane maulosi ena amene anakwaniritsidwa okhudza kubadwa kwa Yesu, zimene zinachitika ali mwana, ndiponso utumiki wake. Kukambirana zimenezi kutithandiza kuti tikhulupirire kwambiri maulosi amene ali m’Baibulo. Kutithandizanso kuona umboni wosatsutsika wosonyeza kuti Yesu analidi Mesiya amene anthu ankamuyembekezera kwa nthawi yaitali.

Kubadwa Kwake Ndiponso Zimene Zinachitika Ali Mwana

6. Kodi lemba la Genesis 49:10 linakwaniritsidwa bwanji?

6 Mesiya adzabadwira mu fuko la Yuda. Atatsala pang’ono kufa, Yakobo anadalitsa ana ake ndipo analosera kuti: “Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda, ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.” (Gen. 49:10) Mawu akuti “Silo” amatanthauza “Mwini wake.” Aphunzitsi achiyuda ambiri m’mbuyomu ankanena kuti mawu akuti “Silo” amanena za Mesiya. Kalelo, mfumu inkakhala ndi ndodo yachifumu ndiponso chibonga cha wolamulira posonyeza kuti ndi yoyenera kulamulira komanso kuuza anthu zochita. Kuyambira ndi ulamuliro wa Mfumu Davide, yemwe anali m’fuko la Yuda, ndodo yachifumu ndiponso chibonga cha wolamulira zinakhala ndi fuko limeneli. Mfumu yomaliza ya m’fuko la Yuda padziko lapansi inali Zedekiya. Koma ulosi wa Yakobo unanena za mfumu ina pambuyo pa Zedekiya. Mfumu imeneyi idzalamulira kosatha. Ndipo Mulungu anauza Zedekiya kuti mfumuyi ndi imene ili yoyenerera mwalamulo. (Ezek. 21:26, 27) Pambuyo pa Zedekiya, Yesu yekha ndi mbadwa ya Davide imene inalonjezedwa kulandira ufumuwu. Yesu asanabadwe mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha konse.” (Luka 1:32, 33) Choncho Silo ayenera kukhala Yesu Khristu amene anali mbadwa ya Yuda ndiponso ya Davide.​—Mat. 1:1-3, 6; Luka 3:23, 31-34.

7. Kodi Mesiya anabadwira kuti ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zochititsa chidwi?

7 Mesiya adzabadwira ku Betelehemu. Mneneri Mika analemba kuti: “Iwe Betelehemu Efurata, ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda. Komabe mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli, amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.” (Mika 5:2) Mesiya anali kudzabadwira ku Yudeya m’tauni ya Betelehemu, imene pa nthawi ina inkatchedwa Efurata. Chochititsa chidwi n’chakuti Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu, ndiponso Yosefe, yemwe anali bambo ake omulera, ankakhala ku Nazareti. Koma anapita ku Betelehemu kukalembetsa mu kaundula chifukwa chomvera lamulo la mfumu yachiroma ndipo Yesu anabadwira kumeneko m’chaka cha 2 B.C.E. (Mat. 2:1, 5, 6) Apatu ulosi unakwaniritsidwa ndendende.

8, 9. Kodi ndi zinthu ziti zokhudza kubadwa kwa Mesiya ndiponso zimene zinachitika pambuyo pake zomwe zinaloseredwa?

8 Namwali ndi amene adzabereke Mesiya. (Werengani Yesaya 7:14.) Lembali limanena kuti mtsikana adzabereka mwana wamwamuna. Pa Chiheberi mawu amene amatanthauza kuti namwali ndi bethulah. Koma pa vesili anagwiritsa ntchito mawu akuti almah omwe amatanthauza “mtsikana.” Komabe Baibulo linagwiritsa ntchito mawu amenewa ponena za Rabeka asanakwatiwe. (Gen. 24:16, 43) Mzimu woyera wa Mulungu unatsogolera Mateyu kulemba kuti ulosi wa pa Yesaya 7:14 unakwaniritsidwa pamene Yesu anabadwa. Mateyu sanagwiritse ntchito mawu achigiriki otanthauza “mtsikana.” Iye anagwiritsa ntchito mawu achigiriki akuti parthenos, amene amatanthauza “namwali.” Mateyu ndi Luka analemba kuti Mariya anali namwali ndipo anatenga pakati chifukwa cha mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu.​—Mat. 1:18-25; Luka 1:26-35.

9 Mesiya akadzabadwa ana ang’onoang’ono adzaphedwa. Mesiya atabadwa kunachitika zinthu zofanana ndi zimene zinachitika ku Iguputo zaka zambirimbiri m’mbuyomo. Farao analamula kuti anthu azitaya makanda aamuna achiheberi mumtsinje wa Nailo. (Eks. 1:22) Ulosi wa pa Yeremiya 31:15, 16 umanena za “Rakele akulirira ana ake” chifukwa chakuti adani ake amulanda anawo. Kulira kwake kunkamvekera kutali mpaka kumzinda wa Rama, womwe unali kudera la Benjamini kumpoto kwa Yerusalemu. Mateyu analemba kuti ulosi umenewu unakwaniritsidwa pamene Mfumu Herode inalamula kuti ana onse ang’onoang’ono aamuna a ku Betelehemu aphedwe. (Werengani Mateyu 2:16-18.) Tangoganizirani chisoni chimene anthu m’derali anali nacho pa nthawi imeneyi.

10. Kodi lemba la Hoseya 11:1 linakwaniritsidwa bwanji pa Yesu?

10 Mofanana ndi Aisiraeli, Mesiya adzaitanidwa kuti atuluke mu Iguputo. (Hos. 11:1) Herode asanalamule zoti anawo aphedwe, mngelo anauza Yosefe kuti atenge Mariya ndi Yesu n’kuthawira ku Iguputo. Anakhala kumeneko “mpaka kumwalira kwa Herode, kuti zimene Yehova analankhula kudzera mwa mneneri wake [Hoseya] zikwaniritsidwe. Iye anati: ‘Ndinaitana mwana wangayu kuti atuluke mu Iguputo.’” (Mat. 2:13-15) N’zoonekeratu kuti zinali zosatheka kuti Yesu achititse kuti maulosi okhudza kubadwa kwake ndiponso moyo wake ali mwana akwaniritsidwe.

Mesiya Anayamba Kugwira Ntchito Yake

11. Kodi njira ya Wodzozedwa wa Yehova inakonzedwa bwanji?

11 Wodzozedwa wa Mulungu asanafike, njira idzakonzedwa. Malaki analosera kuti “mneneri Eliya” ndi amene adzachite zimenezi. Iye adzakonzekeretsa mitima ya anthu kuti adzalandire Mesiya. (Werengani Malaki 4:5, 6.) Ndiyeno Yesu ananena kuti “Eliya” ameneyu ndi Yohane M’batizi. (Mat. 11:12-14) Nayenso Maliko ananena kuti utumiki wa Yohane unakwaniritsa ulosi wa Yesaya wonena za kukonza njira. (Yes. 40:3; Maliko 1:1-4) Si Yesu amene anachititsa kuti Yohane agwire ntchito yofanana ndi imene Eliya anagwira n’cholinga choti amukonzere njira. Mulungu ndi amene ankafuna kuti anthu adzazindikire Mesiya. Choncho Mulungu ndi amene anasankha Yohane kuti agwire ntchito yofanana ndi ya Eliya n’cholinga choti anthu adzalandire Mesiya.

12. Kodi ndi ntchito yapadera iti imene Mulungu anapatsa Mesiya?

12 Mesiya adzadziwika chifukwa cha ntchito yapadera imene Mulungu adzamupatse. Yesu ali m’sunagoge wa ku Nazareti kumene anakulira, anawerenga mu mpukutu wa Yesaya mawu akuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu, ndi kudzalalikira chaka chovomerezeka kwa Yehova.” Yesu ananena kuti ulosiwu unkanena za iyeyo. Iye analidi Mesiya. N’chifukwa chake ananena kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”​—Luka 4:16-21.

13. Kodi Yesaya analosera chiyani za utumiki wa Yesu ku Galileya?

13 Ulosi wonena za utumiki wa Mesiya ku Galileya. Yesaya analosera za “dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali” ndiponso “Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.” Iye anati: “Anthu amene anali kuyenda mu mdima, aona kuwala kwakukulu. Anthu amene anali kukhala m’dziko la mdima wandiweyani, kuwala kwawawalira.” (Yes. 9:1, 2) Yesu anayamba utumiki wake ku Galileya m’tauni ya Kaperenao. Iye anaphunzitsanso ku Zebuloni ndiponso ku Nafitali. Yesu anaphunzitsa anthu a kumeneko mfundo za choonadi. Choncho anawathandiza kuona kuwala kwauzimu. (Mat. 4:12-16) Ku Galileya n’kumene Yesu anapereka ulaliki wake wa paphiri, kusankha atumwi ake ndiponso kuchita chozizwitsa chake choyamba. Zikuonekanso kuti ku Galileya n’kumene Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa ophunzira ake oposa 500. (Mat. 5:1–7:27; 28:16-20; Maliko 3:13, 14; Yoh. 2:8-11; 1 Akor. 15:6) Choncho pamene Yesu analalikira ‘kudziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali’ anakwaniritsa ulosi wa Yesaya. Koma Yesu analalikiranso uthenga wa Ufumu kumadera ena a ku Isiraeli.

Maulosi Ena Okhudza Mesiya

14. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji lemba la Salimo 78:2?

14 Mesiya azidzagwiritsa ntchito mafanizo. M’salimo lina, Asafu anaimba kuti: “Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mwambi.” (Sal. 78:2) Kodi tikudziwa bwanji kuti mawu a ulosi amenewa akunena za Yesu? Timadziwa chifukwa cha zimene Mateyu ananena. Mateyu atafotokoza mafanizo a Yesu oyerekezera Ufumu ndi kanjere ka mpiru ndiponso zofufumitsa, iye analemba kuti: “[Yesu] sanalankhule nawo chilichonse popanda fanizo, kuti zikwaniritsidwe zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri amene anati: ‘Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mafanizo, ndidzafalitsa zinthu zobisika kuchokera pa chiyambi cha dziko lapansi.’” (Mat. 13:31-35) Choncho mafanizo ndi njira imodzi imene Yesu anagwiritsa ntchito kuti aphunzitse mogwira mtima.

15. Kodi lemba la Yesaya 53:4 linakwaniritsidwa bwanji?

15 Mesiya adzanyamula matenda athu. Yesaya analosera kuti: “Zoonadi, iye anatinyamulira matenda athu ndipo anatisenzera zowawa zathu.” (Yes. 53:4) Apongozi a Petulo atadwala, Yesu anawachiritsa ndipo kenako anachiritsanso anthu ena amene anabwera kunyumbako. Mateyu ananena kuti Yesu anachita zimenezi kuti “zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti: ‘Iye anatenga matenda athu n’kunyamula zowawa zathu.’” (Mat. 8:14-17) Koma si nthawi yokhayo pamene Yesu anathandiza odwala. Baibulo limasonyeza kuti pali nthawi zina zambiri pamene Yesu anachiritsa anthu.

16. Kodi mtumwi Yohane anasonyeza bwanji kuti Yesu anakwaniritsa ulosi wa pa Yesaya 53:1?

16 Anthu ambiri sadzakhulupirira Mesiya ngakhale kuti adzachita zabwino zambiri. (Werengani Yesaya 53:1.) Yohane anasonyeza kuti ulosiwu unakwaniritsidwa chifukwa iye analemba kuti: “Ngakhale kuti [Yesu] anachita zizindikiro zambiri pamaso [pa anthu], iwo sanali kukhulupirira iye, moti mawu a mneneri Yesaya anakwaniritsidwa. Iye anati: ‘Yehova, kodi ndani wakhulupirira zimene ife tamva? Ndipo kodi dzanja la Yehova laonetsedwa kwa ndani?’” (Yoh. 12:37, 38) Komanso pa nthawi imene mtumwi Paulo anali kulalikira, ndi anthu ochepa okha amene anakhulupirira uthenga wabwino wonena za Yesu, yemwe ndi Mesiya.​—Aroma 10:16, 17.

17. Kodi ulosi wa pa Salimo 69:4 unakwaniritsidwa bwanji?

17 Mesiya adzadedwa popanda chifukwa. (Sal. 69:4) Yesu anati: “Ndikanapanda kuchita pakati [pa anthu] ntchito zimene wina aliyense sanachitepo, akanakhala opanda tchimo, koma tsopano aona ndipo adana nane, ndi kudananso ndi Atate wanga. Zili choncho kuti mawu olembedwa m’Chilamulo akwaniritsidwe. Mawu ake ndi akuti, ‘Anadana nane popanda chifukwa.’” (Yoh. 15:24, 25) Mawu akuti “Chilamulo” nthawi zambiri amatanthauza Malemba onse. (Yoh. 10:34; 12:34) Mauthenga Abwino amatsimikizira kuti Yesu ankadedwa ndi anthu ambiri, makamaka ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda. Ndipotu Yesu ananena kuti: “Dziko lilibe chifukwa chodana ndi inu, koma limadana ndi ine, chifukwa ndimachitira umboni kuti dzikoli ntchito zake ndi zoipa.”​—Yoh. 7:7.

18. Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana zotani zimene zingatithandize kukhulupirira kwambiri kuti Yesu ndiye Mesiya?

18 M’nthawi ya Yesu, otsatira ake ankakhulupirira kuti iye analidi Mesiya chifukwa chakuti anakwaniritsa maulosi onse okhudza Mesiya opezeka m’Malemba Achiheberi. (Mat. 16:16) Monga taonera, maulosi ena anakwaniritsidwa pamene Yesu anali mwana ndiponso pa nthawi ya utumiki wake. M’nkhani yotsatira tidzakambirana maulosi ena onena za Mesiya. Kuganizira mozama maulosi amenewa kutithandiza kukhulupirira kwambiri kuti Yesu Khristu ndiyedi Mesiya amene anasankhidwa ndi Atate wathu wakumwamba, Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kuti mudziwe zambiri zokhudza “milungu 70,” onani mutu 11 m’buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli!

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndi maulosi ati okhudza kubadwa kwa Yesu amene anakwaniritsidwa?

• Kodi njira inakonzedwa bwanji Mesiya asanafike?

• Kodi Yesu anakwaniritsa maulosi ati a mu Yesaya chaputala 53?

[Mafunso]