Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
• Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene zingatithandize kupewa mtima wofuna kuchita chinyengo?
Zinthu zake ndi izi: (1) Tiziopa Mulungu moyenera. (1 Pet. 3:12) (2) Tikhale ndi chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo. (3) Tiziyesetsa kukhala okhutira ndi zimene tili nazo.—4/15, tsamba 6 ndi 7.
• Kodi munthu amene amaona kutumikira Mulungu kukhala kofunika kwambiri amakhala wokhwimitsa zinthu kapena wosapeza nthawi yosangalala?
Ayi. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Iye ankasangalala kudya limodzi ndi anthu ena. Timadziwa kuti sanali munthu wokhwimitsa zinthu kapena wosaseka ndi anthu chifukwa chakuti anthu ena komanso ana ankamasuka naye.—4/15, tsamba 10.
• Kodi mwamuna ndi mkazi wake angachite chiyani ngati chikondi chawo chayamba kuchepa mwana akabadwa?
Ayenera kuchita zinthu zosonyeza kuti akukondanabe. Mwamuna ayenera kuyesetsa kuthandiza mkazi wake kuti nkhawa zimene ali nazo zithe. Onse awiri ayenera kuyesetsa kukambirana momasuka za mmene akumvera ndiponso zofuna zawo.—5/1, tsamba 12 ndi 13.
• Kodi mtengo wa maolivi wotchulidwa mu chaputala 11 cha Aroma umaimira chiyani?
Fanizo la mtengowu limanena za mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu yomwe ndi Isiraeli wauzimu. Muzu wa mtengo wa maolivi wophiphiritsirawu umaimira Yehova ndipo thunthu lake limaimira Yesu. Ayuda ambiri atakana Yesu, anthu a mitundu ina anakhala okhulupirira ndipo analumikizidwa kumtengowu n’cholinga choti chiwerengero cha mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu chikwanire.—5/15, tsamba 22-25.
• Kodi ndi uthenga wabwino uti umene tiyenera kulalikira kwa anthu osauka?
Uthenga wabwino umenewu ndi wakuti: Mulungu wasankha Yesu kukhala Mfumu. Yesu ndi Wolamulira amene angathetsedi umphawi. Tikutero chifukwa choti adzalamulira anthu onse ndipo ali ndi mphamvu zotha kusintha zinthu. Iye amachitiranso chifundo anthu osauka ndipo angathe kuchotsa chimene chimayambitsa umphawi, chomwe ndi mtima wodzikonda umene anthufe timabadwa nawo.—6/1, tsamba 7.
• Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anauza Kayafa kuti: “Mwanena nokha?”—Mat. 26:63, 64.
Mawu akuti “mwanena nokha” ayenera kuti anali okuluwika komanso odziwika bwino kwa Ayuda ndipo ankatanthauza kuti zimene zanenedwazo ndi zoona. Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe, anafunsa Yesu ngati anali Khristu, Mwana wa Mulungu. Yankho la Yesu lakuti: “Mwanena nokha” linasonyeza kuti anavomera.—6/1, tsamba 18.
• Kodi ana amene Yesu akanadzakhala nawo amawerengeredwanso kuti ndi mbali ya dipo limene Yesu anapereka?
Ayi. Ngakhale kuti Yesu akanatha kukhala ndi mbadwa zangwiro mabiliyoni ambiri, mbadwa zimene akanakhala nazozo sizinali mbali ya dipo. Moyo wangwiro wa Yesu wokha unali wofanana ndendende ndi moyo wa Adamu. (1 Tim. 2:6)—6/15, tsamba 13.
• Kodi Akhristu angasonyeze bwanji kuti akumvera chenjezo lonena za aphunzitsi onyenga limene lili m’lemba la Machitidwe 20:29, 30?
Sayenera kulandira aphunzitsi onyenga m’nyumba zawo kapena kuwapatsa moni. (Aroma 16:17; 2 Yoh. 9-11) Iwo sawerenga mabuku a ampatuko, kuonera mapulogalamu awo pa TV kapena kuwerenga zimene alemba pa Intaneti.—7/15, tsamba 15 ndi 16.
• Kodi ndani ayenera kuphunzitsa ana zokhudza Mulungu?
Baibulo limalangiza kuti bambo ndi mayi ayenera kuphunzitsa ana. (Miy. 1:8; Aef. 6:4) Ofufuza apeza kuti pamene makolo onse awiri amaphunzitsa ana, anawo amapindula kwambiri.—88/1, tsamba 6 ndi 7.