Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi n’zotheka kutchula chiwerengero cha maulosi onena za Mesiya amene ali m’Malemba Achiheberi?

Kuphunzira mosamala Malemba Achiheberi kungatithandize kudziwa maulosi ambiri amene Yesu Khristu anakwaniritsa. Maulosi amenewa ananeneratu zinthu monga kumene Mesiya anachokera, nthawi imene anaonekera padziko, zimene anachita, zimene anthu anamuchitira ndiponso ntchito imene Yehova Mulungu anafuna kuti agwire. Maulosi onsewa tikawaphatikiza, amatithandiza kuzindikira kuti Yesu ndiye Mesiya. Koma tiyenera kusamala ngati tikufuna kupeza chiwerengero cha maulosi onena za Mesiya amene ali m’Malemba Achiheberi.

Pali maulosi amene anthu ena savomereza zoti amanena za Mesiya. M’buku lina lonena za moyo wa Yesu, yemwe ndi Mesiya, Alfred Edersheim ananena zimene arabi analemba. (The Life and Times of Jesus the Messiah) Iwo ankanena kuti m’Malemba Achiheberi muli maulosi 456 onena za Mesiya, ngakhale kuti ena mwa maulosiwa satchula Mesiya mwachindunji. Koma tikaonetsetsa maulosi 456 amenewa, zimakayikitsa ngati ena mwa maulosiwo akunenadi za Yesu Khristu. Mwachitsanzo, Edersheim ananena kuti Ayuda ankaona kuti lemba la Genesis 8:11 ndi ulosi wonena za Mesiya. Iwo ankaona kuti “tsamba la mtengo wa maolivi limene njiwa inabweretsa linatengedwa kuphiri la Mesiya.” Edersheim anatchulanso lemba la Ekisodo 12:42. Pofotokoza maganizo olakwika a Ayuda pa lemba limeneli, iye analemba kuti: “Mesiya adzatuluka ku Roma ngati mmene Mose anatulukira m’chipululu.” Mosakayikira, akatswiri a maphunziro a Baibulo ndiponso anthu ena sangavomereze zimene Ayudawa ankanena komanso sangavomereze zoti malemba awiriwa akufotokozadi za Yesu Khristu.

Ngakhale titangoona maulosi amene Yesu Khristu anakwaniritsadi, zikhoza kukhala zovuta kuti tonse tigwirizane pa chiwerengero chimodzi. Mwachitsanzo, taganizirani za maulosi osiyanasiyana onena za Mesiya amene ali m’chaputala 53 cha Yesaya. Lemba la Yesaya 53:2-7 linalosera za Mesiya kuti: “Alibe maonekedwe alionse apamwamba . . . Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa . . . Anatinyamulira matenda athu . . . Iye anabayidwa chifukwa cha zolakwa zathu . . . Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa.” Ndiye funso ndi lakuti kodi mavesi onsewa akunena ulosi umodzi kapena mbali iliyonse ndi ulosi pawokha?

Taganiziraninso za lemba la Yesaya 11:1 lomwe limati: “Nthambi idzatuluka pachitsa cha Jese, ndipo mphukira yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso.” Ulosi umenewu umapezekanso pa vesi 10 ndipo mawu ake ndi ofanana. Ndiyeno kodi pamenepa tingati pali maulosi awiri kapena tingati ulosi umodzi wangobwerezedwa? Zimene tingasankhe pa maulosi a mu chaputala 53 ndi chaputala 11 cha Yesaya zingakhudze chiwerengero cha maulosi onena za Mesiya.

Choncho si bwino kuti tizilimbana ndi kudziwa chiwerengero chenicheni cha maulosi onena za Mesiya amene ali m’Malemba Achiheberi. Gulu la Yehova lalemba m’mabuku angapo mndandanda wa maulosi ambiri onena za Yesu ndiponso kukwaniritsidwa kwake. * Mndandanda umenewu ungatithandize ndiponso kutilimbikitsa tikamaugwiritsa ntchito pophunzira Baibulo patokha, pa banja komanso pamene tili mu utumiki. Kaya maulosi onena za Mesiya alipo angati, mfundo ndi yakuti onsewo amatipatsa umboni wosatsutsika wakuti Yesu ndiye Khristu, kapena kuti Mesiya.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani mabuku akuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsamba 200; Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 1223; Voliyumu 2, tsamba 387; ndi “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” tsamba 343 mpaka 344.