Msonkhano Wapadera Komanso Wosaiwalika
Msonkhano Wapadera Komanso Wosaiwalika
PA OCTOBER 2, 2010, M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anatsegula msonkhano wapachaka ndi mawu akuti: “Ndikukhulupirira kuti msonkhanowu ukatha, aliyense anena kuti, ‘Koma msonkhano umenewu, ee! Unali wapadera.’” Mawu amenewa anachititsa anthu ambirimbiri amene anasonkhana kukhala tcheru kwambiri. Msonkhano wapachaka umenewu wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, womwe ndi wa nambala 126, unachitikira ku Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ku Jersey City ku New Jersey m’dziko la United States. Kodi mfundo zikuluzikulu za pamsonkhano umenewu zinali zotani?
Nkhani yoyamba imene M’bale Lett anakamba inafotokoza za galeta la kumwamba la Yehova lotchulidwa m’buku la m’Baibulo la Ezekieli. Iye anakamba nkhani imeneyi mogwira mtima kwambiri. Galeta lalikulu ndiponso lochititsa kaso limeneli limaimira gulu la Mulungu lomwe Yehova akulitsogolera nthawi zonse. M’bale Lett ananena kuti mbali ya kumwamba ya gululi, yopangidwa ndi zolengedwa zauzimu, imayenda mofulumira kwambiri ngati mphezi chifukwa Yehova amaganizanso mofulumira. Nayonso mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova Mulungu ikuyenda. M’bale Lett anatchula zinthu zingapo zosangalatsa zimene zachitika m’mbali ya padziko lapansi ya gulu la Mulungu m’zaka za posachedwapa.
Mwachitsanzo, maofesi ena a nthambi awaphatikiza ndipo ntchito ya m’mayikowo ikuyang’aniridwa ndi ofesi imodzi. Zimenezi zikuthandiza kuti anthu amene poyamba ankatumikira pa Beteli m’mayikowo azigwira kwambiri ntchito yolalikira. M’bale Lett anapempha omvera kuti apitirize kupempherera Bungwe Lolamulira, lomwe limaimira kapolo wokhulupirika, kuti lipitirize kukhala lokhulupirika komanso lanzeru.—Mat. 24:45-47.
Malipoti Olimbikitsa Ndiponso Ndemanga Zogwira Mtima
M’bale Tab Honsberger, yemwe ali mu Komiti ya Nthambi ku Haiti, anapereka lipoti lomwe linakhudza mtima anthu omvera. Iye anafotokoza zimene zinachitika pambuyo pa chivomezi chimene chinachitika pa January 12, 2010, ku Haiti, chomwe chinapha anthu pafupifupi 300,000. Iye ananena kuti atsogoleri achipembedzo ankauza anthu kuti amene anaphedwa ndi chivomezi analangidwa ndi Mulungu chifukwa choti analibe chikhulupiriro koma Mulungu anateteza anthu abwino. Koma zimenezi zinali zosamveka chifukwa akaidi masauzande ambiri anapeza mwayi wothawa pamene mpanda wa ndende unagwa ndi chivomezicho. Anthu ambiri amtima wabwino a ku Haiti akulimbikitsidwa akamaphunzira chifukwa chenicheni chimene tikuvutikira masiku ano. M’bale Honsberger anafotokoza zimene m’bale wina wokhulupirika wa ku Haiti, amene mkazi wake anamwalira pa chivomezichi, ananena. M’baleyo anati: “Ndimalirabe ndipo sindidziwa kuti ndidzasiya liti koma ndimasangalala chifukwa cha chikondi chimene anthu m’gulu la Yehova amandisonyeza.
Ndili ndi chiyembekezo ndipo ndine wofunitsitsa kuuza anthu ena za chiyembekezochi.”M’bale Mark Sanderson, amene panopa akutumikira pa Beteli ku Brooklyn, anapereka lipoti lofotokoza za ku Philippines. Kale m’baleyu anali m’Komiti ya Nthambi ya kumeneko. Iye anasangalala kwambiri kufotokoza kuti kwa zaka 32 chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa Ufumu chakhala chikukwera komanso chiwerengero cha maphunziro a Baibulo n’chokwera kwambiri kuposa chiwerengero cha ofalitsa. Iye anafotokoza za m’bale wina dzina lake Miguel yemwe mdzukulu wake anaphedwa. Miguel anayesetsa kuti munthu amene anapha mdzukulu wakeyo amangidwe. Ndiyeno tsiku lina Miguel akulalikira m’ndende, anakumana ndi munthu amene anapha mdzukulu wakeyo. Ngakhale kuti Miguel anachita mantha, analankhula munthuyo modekha komanso mokoma mtima. Patapita nthawi, anayamba kuphunzira naye Baibulo ndipo munthuyo anayamba kukonda Yehova. Panopa ndi m’bale wobatizidwa. Tsopano iye ndi Miguel ndi mabwenzi apamtima ndipo Miguel akuyesetsa kuti mnzakeyo amasulidwe mwamsanga. *
Nkhani yotsatira inali yofunsa anthu. Amene anakamba ndi M’bale Mark Noumair, yemwe ndi mlangizi mu Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu. Iye anafunsa banja la Alex ndi Sarah Reinmueller, la David ndi Krista Schafer ndiponso banja la Robert ndi Ketra Ciranko. M’bale Alex Reinmueller ndi wothandiza Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku. Iye anafotokoza kuti anayamba kukonda kwambiri choonadi pamene ankachita upainiya ku Canada. Pa nthawiyo n’kuti ali ndi zaka 15 zokha ndipo nthawi zambiri ankapezeka kuti palibe woyenda naye mu utumiki moti ankayenda yekha. Atafunsidwa kuti atchule abale amene anamuthandiza kwambiri pa Beteli, M’bale Reinmueller anatchula abale atatu okhulupirika ndipo anafotokoza mmene m’bale aliyense anamuthandizira kuti akule mwauzimu. Sarah, yemwe ndi mkazi wa M’bale Reinmueller, ananena kuti ankagwirizana kwambiri ndi mlongo wina amene anapirira zaka zambirimbiri m’ndende ku China chifukwa cha chikhulupiriro chake. Sarah ananenanso kuti pemphero lamuthandiza kudalira Yehova.
M’bale David Schafer, yemwe ndi wothandiza Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa, anayamikira mayi ake chifukwa cha chikhulupiriro chawo cholimba. Ananenanso kuti abale ena amene ankagwira ntchito yodula mitengo, anamulimbikitsa kuti ayambe upainiya wothandiza ali wamng’ono. Mkazi wake Krista ananena monyadira kuti anathandizidwa ndi anthu achikulire a m’banja la Beteli omwe ankatsatira mawu a Yesu oti tizikhala ‘okhulupirika pa chinthu chaching’ono.’—Luka 16:10.
M’bale Robert Ciranko, yemwe ndi wothandiza Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku, analankhula za makolo a bambo ake ndi mayi ake amene anasamukira ku United States
kuchokera ku Hungary ndipo anali Akhristu odzozedwa. Ali mnyamata anachita chidwi atapezeka pa misonkhano yachigawo yaikulu kwambiri ya m’ma 1950, ndipo anazindikira kuti gulu la Yehova ndi lalikulu kwambiri osati mpingo wawo wokha. Mkazi wake Ketra ananena kuti anaphunzira kukhala wokhulupirika pa nthawi imene ankachita upainiya mu mpingo umene munali mpatuko ndiponso mavuto ena. Iye anapirira ndipo kenako anapemphedwa kukatumikira monga mpainiya wapadera ku mpingo wina kumene ankasangalala chifukwa chakuti abale ndi alongo ankagwirizana kwambiri.Kenako M’bale Manfred Tonak anapereka lipoti lonena za ku Ethiopia. Dziko limeneli linayamba kudziwika kalekale moti limatchulidwa m’Baibulo. Panopa m’dzikoli muli ofalitsa uthenga wabwino oposa 9,000. Ambiri mwa ofalitsawa amakhala mumzinda wa Addis Ababa kapena pafupi ndi mzindawu, womwe ndi likulu la dzikoli. Koma madera akutali akufunika ofalitsa Ufumu ambiri. Chifukwa cha zimenezi, Mboni za ku Ethiopia zimene zikukhala kumayiko ena zinapemphedwa kuti zipite kukalalikira kumadera ena akutali a m’dzikolo. Abale ndi alongo ambiri anapita ndipo analimbikitsa kwambiri Mboni za m’dzikoli komanso anapeza anthu achidwi.
Nkhani ina yochititsa chidwi inali yosiyirana. Nkhaniyi inafotokoza za Mboni za Yehova ku Russia ndiponso milandu imene Mbonizo zinkazengedwa. M’bale Aulis Bergdahl wa m’Komiti ya Nthambi ku Russia, anafotokoza mbiri ya Mboni za Yehova m’dzikolo makamaka mumzinda wa Moscow. M’bale Philip Brumley wa mu Dipatimenti ya Zamalamulo ku nthambi ya United States anafotokoza zochitika zosangalatsa za miyezi ya posachedwapa. Iye anafotokoza zimene zinachitika pamene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linkazenga milandu 9 imene Mboni za Yehova zinasumiridwa. Oweruza onse m’khotili anavomereza kuti milandu yonse 9 inali yopanda umboni. Poweruza ina ya milanduyi, khotilo linafotokoza zifukwa zosonyeza kuti milanduyo inali yabodza. Ngakhale kuti sitikudziwa kuti zotsatirapo zake zidzakhala zotani, M’bale Brumley anasonyeza kuti zimene khotili linagamula zikhoza kuthandizanso pa milandu ya m’mayiko ena.
Pambuyo pa nkhani yosangalatsayi, M’bale Lett analengeza kuti khotilo lasankha kuti lingazenge mlandu wakalekale wokhudza misonkho wa pakati pa boma la France ndi Mboni za Yehova. Khoti limeneli limalemekezedwa kwambiri padziko lonse ndipo limavomereza kuzenga milandu yochepa kwambiri. Panopo khotilo lazenga milandu 39 ya Mboni za Yehova ndipo milandu 37 yaweruzidwa mokomera Mboni za Yehova. M’bale Lett analimbikitsa anthu a Mulungu onse kuti azipempha Yehova Mulungu kuti athandize pa mlandu wa ku France umenewu.
M’bale Richard Morlan ndi amene anapereka lipoti lomaliza. Iye ndi mlangizi wa Sukulu Yophunzitsa Akulu ndipo analankhula mogwira mtima za sukuluyo ndiponso mmene ikuthandizira akulu.
Nkhani Zina Zimene a M’Bungwe Lolamulira Anakamba
M’bale Guy Pierce wa m’Bungwe Lolamulira anakamba mogwira mtima nkhani yonena za lemba la chaka cha 2011 lakuti: ‘Pezani chitetezo m’dzina la Yehova.’ (Zef. 3:12) Iye ananena kuti nthawi ino ndi yosangalatsa kwambiri kwa anthu a Yehova koma ndi nthawinso yovuta yofunika kuganiza mwanzeru. Tsiku lalikulu la Yehova likuyandikira. Komabe anthu amaganiza kuti zinthu monga chipembedzo chonyenga, mabungwe andale kapena chuma zingawateteze. Anthu ena amangokhalira kuchita zinthu zosangalatsa n’cholinga choti aiwale zinthu zoipa zimene zikuchitika m’dzikoli. Koma kuti tipeze chitetezo chenicheni tiyenera kuitana pa dzina la Yehova. Zimenezi zimatanthauza kuti tiyenera kudziwa Yehova, kumulemekeza kwambiri, kumukhulupirira ndiponso kumukonda ndi moyo wathu wonse.
Kenako M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yogwira mtima ndiponso yochititsa munthu kuganiza mozama. Mutu wake unali wakuti, “Kodi Mwalowa Nawo mu Mpumulo wa Mulungu?” Iye ananena kuti mpumulo wa Mulungu sutanthauza kuti Mulungu anasiya kugwira ntchito. Tikutero chifukwa Yehova ndi Mwana wake “akugwirabe ntchito” pa tsiku lopuma lophiphiritsa limeneli pofuna kuti cholinga chake chokhudza zinthu zimene iye analenga padziko lapansi chikwaniritsidwe. (Yoh. 5:17) Ndiyeno kodi tingalowe bwanji mu mpumulo wa Mulungu? Tiyenera kupewa tchimo ndiponso ntchito zodzilungamitsa. Komabe pali zinanso zimene tiyenera kuchita. Tiyeneranso kusonyeza chikhulupiriro, kukumbukira nthawi zonse cholinga cha Mulungu ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi cholingacho. Ngakhale kuti nthawi zina zimakhala zovuta, tiyenera kutsatira malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa. M’bale Splane analimbikitsa kwambiri omvera kuti achite zonse zimene angathe kuti alowe mu mpumulo wa Mulungu.
Nkhani yomaliza imene inakambidwa ndi M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira inali ndi mutu wakuti, “Kodi Tikuyembekezera Chiyani?” M’bale Morris analankhula mwachikondi ngati mmene bambo amachitira ndi ana ake. Iye anakumbutsa omvera za maulosi amene panopa sanakwaniritsidwe ndipo anthu okhulupirika akuyembekezera mwachidwi kuti akwaniritsidwe. Ena mwa maulosi amenewa ndi onena za nthawi imene anthu azidzati “Bata ndi mtendere!” ndiponso onena za kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga. (1 Ates. 5:2, 3; Chiv. 17:15-17) M’bale Morris anachenjeza kuti tikaona zinthu zina zikuchitika padziko koma zimene sizikukwaniritsa maulosi amenewa, sitiyenera kunena kuti, “Aramagedo ikuyamba basi.” Iye analimbikitsa anthu kukhala osangalala, oleza mtima ndiponso kuyembekezera Yehova ngati mmene lemba la Mika 7:7 limanenera. Iye analimbikitsanso anthu kugwirizana kwambiri ndi Bungwe Lolamulira ngati mmene gulu la asilikali limachitira pa nkhondo likakumana ndi adani ambirimbiri. Iye ananenanso kuti: “Muchite zinthu mwamphamvu, inu nonse amene mukuyembekezera Yehova.”—Sal. 31:24.
Pomaliza, panali zilengezo zosangalatsa zimene zinali zapadera kwambiri. M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira analengeza kuti anali kukonza zoti Nsanja ya Olonda yophunzira iyambe kusindikizidwa m’Chingelezi chosavuta. Magazini imeneyi ithandiza anthu amene amavutika kumva Chingelezi. Ananena kuti ayesa kuchita zimenezi kwa kanthawi kuti aone ngati zingathandize. Kenako M’bale Stephen Lett analengeza kuti Bungwe Lolamulira lakonza zoti pakhale maulendo aubusa kwa oyang’anira zigawo ndi akazi awo ku United States. Analengezanso kuti Sukulu Yophunzitsa Utumiki yasinthidwa dzina kukhala Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira. Iye ananena kuti padzakhalanso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja. Sukulu imeneyi idzathandiza mabanjawo kuti athe kuchita zambiri m’gulu la Yehova. M’bale Lett analengezanso kuti Sukulu ya Oyang’anira Oyendayenda ndi Akazi Awo ndiponso Sukulu ya Abale a M’komiti ya Nthambi ndi Akazi Awo izidzachitika kawiri pa chaka ku Patterson. Padzakhalanso mwayi woti anthu amene analowa kale m’masukulu amenewa alowenso kachiwiri.
Anthu onse anakhudzidwa mtima pamene M’bale John E. Barr, yemwe anali ndi zaka 97 ndiponso anakhala m’Bungwe Lolamulira kwa nthawi yaitali, anamaliza msonkhanowu ndi pemphero lodzichepetsa ndiponso lochokera pansi pa mtima. * Anthu onse amene analipo anaona kuti msonkhanowu unalidi wapadera ndiponso wosaiwalika.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Werengani Yearbook ya 2011, tsamba 62 ndi 63.
^ ndime 20 M’bale Barr anamaliza moyo wake padziko lapansi pa December 4, 2010.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
Anthu onse anasangalala kumva ndemanga za anthu amene anafunsidwa
[Mawu Otsindika patsamba 20]
Yehova wadalitsa ntchito yolalikira ku Ethiopia