Njira Zopangira Kulambira kwa Pabanja Kapena Kuphunzira Baibulo Patokha
Njira Zopangira Kulambira kwa Pabanja Kapena Kuphunzira Baibulo Patokha
KUMAYAMBIRIRO kwa 2009, mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse inasintha misonkhano yawo. Misonkhano iwiri inaphatikizidwa. Cholinga chake chinali chakuti tizigwiritsa ntchito nthawi imene tinkachita Phunziro la Buku la Mpingo kuti tizichita Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo patokha. Kodi mukugwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imeneyi? Kodi mukupindula kwambiri ndi kusinthaku?
Ena amadzifunsa kuti, ‘Kodi tiziphunzira chiyani pa Kulambira kwa Pabanja?’ Si cholinga cha Bungwe Lolamulira kusankhira banja lililonse zinthu zoti liziphunzira. Koma popeza zinthu zimasiyanasiyana pa moyo wathu, ndi bwino kuti mutu wa banja kapena munthu payekha azisankha zoyenera kuphunzira mlungu uliwonse.
Pa tsikuli, anthu ena amakonzekera misonkhano ya mpingo, koma pali zinthu zinanso zimene mungachite pa Kulambira kwa Pabanja. Ena amawerenga kapena kukambirana nkhani za m’Baibulo. Mabanja ena amene ali ndi ana aang’ono amachita sewero la nkhani ya m’Baibulo kuti anawo azipindula. Sikuti nthawi zonse tizingokhalira kuphunzira mwa mafunso ndi mayankho ngati kuti tili pa misonkhano ya mpingo. Kuchita zinthu ngati tikucheza pophunzira kumathandiza kuti aliyense azikhala womasuka ndi kutha kufotokoza maganizo ake. Kuphunzira mwa njira imeneyi kumathandiza kuti munthu azitha kuganiza mwanzeru ndipo phunzirolo limakhala losangalatsa komanso losaiwalika.
Pofotokoza zimene amachita pa Kulambira kwa Pabanja, Bambo wina wa ana atatu analemba kuti: “Zimene takhala tikukambirana ndi zokhudza zimene tawerenga m’Baibulo. Pamakhala machaputala amene aliyense amawerengeratu ndiye ana amasankha nkhani zina zoti afufuze n’kudzazifotokoza pa phunziro. Michael [wa zaka 7] amakonda kujambula chithunzi kapena kulemba timawu tochepa. David [wa zaka 13] ndi Kaitlyn [wa zaka 15] amatha kulemba nkhani ya m’Baibulo ngati kuti analipo pamene zinthuzo zinkachitika. Mwachitsanzo, pa nthawi ina tinawerenga za Yosefe akumasulira maloto a wophika mkate wa mfumu Farao ndi a woperekera chikho. Ndiyeno Kaitlyn analemba nkhani ngati kuti anali mkaidi m’ndendemo n’kumaona zinthuzo zikuchitika.”—Genesis chaputala 40.
Pa moyo wathu zinthu zimasiyanasiyana. Zimene zingagwire bwino ntchito kwa munthu wina kapena banja lina sizingagwirenso kwa ena. Bokosi limene lili patsamba 7 lili ndi njira zosiyanasiyana zimene tingagwiritse ntchito popanga Kulambira kwa Pabanja kapena pophunzira Baibulo patokha. Koma mukhoza kuwonjezeranso njira zina.
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 6, 7]
Kwa mabanja amene muli achinyamata:
• Mungawerenge ndi kukambirana buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa.
• Mungayerekezere kuti munalipo pamene nkhani ya m’Baibulo imene mukuwerenga inkachitika. (Werengani Nsanja ya Olonda ya May 15, 1996, tsamba 14, ndime 17 ndi 18.)
• Mungakambirane zolinga zing’onozing’ono ndi zikuluzikulu zimene banja lanu lingakhale nazo.
• Nthawi zina mungaonere vidiyo yokhudza nkhani za m’Baibulo ndi kukambirana zimene mwaonera.
• Mungakambirane nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yakuti “Zoti Achinyamata Achite.”
Kwa mabanja amene mulibe ana:
• Mungakambirane mitu 1, 3 ndiponso 11 mpaka 16 ya m’buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
• Mungakambirane zomwe mwapeza pofufuza nkhani zimene mwawerenga m’Baibulo.
• Mungakonzekere Phunziro la Baibulo la Mpingo kapena Phunziro la Nsanja ya Olonda
• Mungakambirane zimene banja lanu lingachite kuti liwonjezere utumiki
Kwa Akhristu amene sali pa banja kapena amene amuna kapena akazi awo si Mboni:
• Mungaphunzire mabuku atsopano amene mwalandira pa msonkhano wachigawo.
• Mungawerenge ma Yearbook atsopano ndiponso akale.
• Mungafufuze mayankho a mafunso amene anthu amafunsa kawirikawiri m’gawo lanu.
• Mungakonzekere zimene munganene mu utumiki wa kumunda.
Kwa mabanja amene muli ana aang’ono:
• Mungachite sewero la nkhani ya m’Baibulo.
• Mungachite masewera othandiza kukumbukira zinthu za m’Baibulo monga amene amapezeka mu Galamukani! patsamba 30 ndi 31.
• Nthawi zina, mungachite zinthu zosangalatsa kwambiri zimene zingathandize ana kuphunzira za Mulungu. (Werengani nkhani yakuti “Kuphunzira Baibulo M’malo Osonyezerako Nyama!” mu Galamukani! ya March 8, 1996, tsamba 16 mpaka 19.)
• Mungakambirane nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yakuti “Phunzitsani Ana Anu.”