Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Intaneti Mwanzeru

Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Intaneti Mwanzeru

Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Intaneti Mwanzeru

ZAKA za m’mbuyomu, zinthu zinasintha kwambiri anthu atayamba kusindikiza mabuku pogwiritsa ntchito makina. Nkhani zinayamba kufalitsidwa kwambiri padzikoli. Kusintha kumeneku n’kofanana ndi kumene kwachitika panopa chifukwa cha kubwera kwa Intaneti. Kubwera kwa Intaneti kwathandiza kwambiri kuti nkhani zizifalitsidwanso kwambiri padziko lonse. Mukamafufuza zinthu pa Intaneti mukhoza kupeza mfundo, ziwerengero ndiponso maganizo osiyanasiyana okhudza nkhani zosiyanasiyana.

Kulankhulana ndi mphatso yapadera imene Mlengi anatipatsa. Kumatithandiza kufotokoza ndiponso kumva nkhani kapena maganizo a ena. Yehova ndi amene anayamba kulankhulana ndi anthu ndipo anawapatsa malangizo omveka bwino owathandiza kukhala ndi moyo wosangalala. (Gen. 1:28-30) Koma zimene zinachitika pa chiyambi cha anthu zikusonyeza kuti munthu akhoza kugwiritsa ntchito molakwika mphatso ya kulankhulana. Satana anauza Hava zinthu zabodza. Hava anakhulupirira zimene Satana ananena ndipo anauzanso Adamu. Zotsatira zake zinali zakuti Adamu anabweretsa mavuto kwa anthu onse.​—Gen. 3:1-6; Aroma 5:12.

Kodi zimenezi zikukhudzana bwanji ndi Intaneti? Intaneti ingatithandize kudziwa ndiponso kuchita zinthu zofunika komanso kuchita zinthu mofulumira. Koma ikhozanso kutiwonongera nthawi, kutichititsa kuyamba makhalidwe oipa komanso tikhoza kupezapo zinthu zabodza. Tiyeni tikambirane zimene tingachite kuti tizigwiritsa ntchito bwino Intaneti.

Kodi N’zoona Kapena Zonama?

Si bwino kuganiza kuti zonse zimene timawerenga kapena kuona pa Intaneti ndi zabwino. Munthu akalemba pa Intaneti zinthu zimene akufuna kufufuza, Intanetiyo imabweretsa zonse, zabwino ndi zoipa zomwe. Tingayerekeze Intaneti ndi gulu la anthu limene limakafufuza bowa wosiyanasiyana, kaya wabwino kapena wakupha, kenako n’kutipatsa kuti tidye. Kodi mungayambe kudya bowa uliwonse musanatsimikizire kuti ndi wabwino? Ayi. Tikalemba pa Intaneti zimene tikufuna kudziwa, Intanetiyo imagwiritsa ntchito makompyuta ambirimbiri kuti ipeze zinthu zambiri zokhudza zimene tikufuna kudziwazo. Zinthuzo zingakhale zabwino kwambiri kapena zoipa kwambiri. Tiyenera kukhala ozindikira kuti tisiyanitse zabwino ndi zoipa mmene munthu amasiyanitsira gaga ndi mphale popeta. Ngati sititero, tikhoza kuipitsa maganizo athu ndi zinthu zabodza.

Mu 1993, magazini ina yotchuka inajambula agalu awiri akuyang’ana kompyuta. Ndiye galu wina anauza mnzake kuti: “Mukamacheza pa Intaneti, palibe amene amadziwa zoti ndiwe galu.” Kalelo, Satana anagwiritsa njoka kuti “acheze” ndi Hava n’cholinga choti Havayo asamuzindikire. Iye anamuuza kuti akhoza kufanana ndi Mulungu. Masiku ano, munthu aliyense amene ali ndi Intaneti akhoza kunamizira kuti ndi katswiri pa zinthu zinazake. Angachite izi popanda kutchula ngakhale dzina lake. Pa Intaneti palibe malamulo oletsa munthu wina aliyense kulembapo nkhani, mfundo zake, maganizo ake kapena kuikapo zithunzi.

Musakhale ngati “Hava wa pa Intaneti.” Muzikhala osamala kwambiri ndi zimene mukuwerenga pa Intaneti. Musanayambe kuzikhulupirira, ndi bwino kudzifunsa kuti: (1) Kodi ndani walemba zimenezi? Kodi ndi woyeneradi kuzilemba? (2) N’chifukwa chiyani walemba nkhani imeneyi? N’chiyani chimene chamuchititsa kuilemba? Kodi walemba mokondera? (3) Kodi zimene walembazo wazitenga kuti? Kodi walemba kumene anatenga mfundo zake kuti anthu atsimikizire ngati zili zoona? (4) Kodi nkhaniyi si yakalekale? Mtumwi Paulo anapatsa Timoteyo malangizo amene akhoza kutithandizanso masiku ano. Iye analemba kuti: “Sunga bwino chimene chinaikidwa m’manja mwako. Pewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zinthu zoyera. Upewenso mitsutso pa zimene ena monama amati ndiye ‘kudziwa zinthu.’”​—1 Tim. 6:20.

Kodi Imakuthandizani Kukhala ndi Nthawi Yambiri Kapena Imakuwonongerani Nthawi?

Tikamagwiritsa ntchito Intaneti mwanzeru, ikhoza kutithandiza kuti tisawononge nthawi, mphamvu kapena ndalama. Tikhoza kugula zinthu mosavuta tili kunyumba kwathu. Kuyerekeza mitengo ya zinthu pa Intaneti kungatithandize kuti tisawononge ndalama. Kutumiza kapena kutenga ndalama kubanki kudzera pa Intaneti kwafewetsa zinthu pa moyo wa anthu ambiri. Anthu akhozanso kulipira zinthu ali kunyumba kwawo. Intaneti imathandiza munthu kukonzekera ulendo mofulumira ndiponso kuguliratu tikiti pa mtengo wabwino. Ingatithandizenso kupeza mosavuta manambala a foni ndi maadiresi ndiponso kudziwa misewu imene tingadutse kuti tikafike kumalo enaake. Maofesi a nthambi a Mboni za Yehova padziko lonse amagwiritsa ntchito Intaneti kuti achite zinthu ngati zimenezi pofuna kuti asawononge nthawi, ndalama ndiponso kuti achepetse anthu ogwira ntchito.

Koma pali vuto lina limene tiyenera kuliganizira. Vutoli ndi nthawi imene munthu angawononge pa Intaneti. M’malo mogwiritsa ntchito Intaneti pa zinthu zoti ziwathandize, anthu ena amangoiona ngati malo osewerera. Iwo amawononga nthawi yambiri pa Intaneti pochita masewera, kugula zinthu, kucheza, kutumiza mauthenga ndiponso kufufuza zinthu. Kenako amayamba kunyalanyaza zinthu zofunika kwambiri zokhudza banja lawo, anzawo komanso mpingo. Amafika poti safuna kuchoka pa Intaneti. Mwachitsanzo, kafukufuku amene anachitika m’chaka cha 2010 anasonyeza kuti achinyamata oposa 18 pa 100 alionse ku Korea ali ndi vuto losafuna kuchoka pa Intaneti. Anthu ochita kafukufuku ku Germany ananena kuti “akazi ambiri akudandaula kuti amuna awo ali ndi vuto losafuna kuchoka pa Intaneti.” Mkazi wina anadandaula kuti vutoli lasintha kwambiri mwamuna wake mpaka lafika powononga banja lawo.

Ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova inalandira kalata yochokera kwa munthu wina amene ananena kuti anali ndi vutoli. Nthawi zina iye ankakhala pa Intaneti kwa maola 10 pa tsiku. Iye ananena kuti “poyamba, ankaona kuti palibe vuto lililonse.” Koma ananenanso kuti: “Patapita nthawi, ndinayamba kusiya pang’onopang’ono kusonkhana ndiponso kupemphera.” Akapita ku misonkhano, ankakhala wosakonzekera ndiponso ankangolakalaka zoti “ayambenso kugwiritsa ntchito Intaneti.” Koma n’zosangalatsa kuti iye anazindikira kuopsa kwa vuto lake ndipo anayesetsa kusintha. Tiyeni tiyesetse kuti tisafike pokhala ndi vuto losafuna kuchoka pa Intaneti.

Kodi N’zoyenera Kapena Zosayenera?

Lemba la 1 Atesalonika 5:21, 22 limanena kuti: “Tsimikizirani zinthu zonse. Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino. Pewani zoipa zamtundu uliwonse.” Tiyenera kuona ngati zinthu zimene tapeza pa Intaneti zili zovomerezeka kwa Mulungu ndiponso ngati zili zogwirizana ndi mfundo zake zapamwamba. Zinthuzo zizikhala zoyenera kwa Akhristu osati zolimbikitsa makhalidwe oipa. Zinthu zolaula zafala kwambiri pa Intaneti moti ngati sitisamala tingakopeke nazo.

Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zinthu zimene ndikuonera ndingazibise patafika mwamuna kapena mkazi wanga, makolo anga kapena Akhristu anzanga?’ Ngati ndi choncho, ndi bwino kuti muzigwiritsa ntchito Intaneti pokhapokha ngati pali anthu ena. Intaneti yasintha kwambiri zinthu pa nkhani ya kulankhulana ndiponso kugula zinthu. Koma yayambitsanso njira yatsopano yoti anthu ‘azichita chigololo mumtima mwawo.’​—Mat. 5:27, 28.

Kodi Nditumizire Ena Kapena Ayi?

Munthu akamagwiritsa ntchito Intaneti amatha kulandira komanso kutumiza zinthu kwa anthu ena. Ngakhale kuti tili ndi ufulu wolandira zinthu ndiponso kutumiza, tili ndi udindo wotsimikizira kuti zinthuzo n’zoona komanso kuti sizilimbikitsa makhalidwe oipa. Kodi timatsimikizira kuti zinthu zimene timatumizira anthu ena n’zoona? Kodi tili ndi chilolezo chotumizira ena zinthuzo? * Kodi zinthuzo n’zothandiza ndiponso zolimbikitsa? Kodi cholinga chathu potumiza zinthuzo n’chiyani? Kodi tikungofuna kugometsa anthu ena?

Ngati tigwiritsa ntchito bwino Intaneti potumiza ndiponso kulandira mauthenga, ikhoza kutithandiza kwambiri. Koma tikhoza kumalandira mauthenga ambiri okhala ndi zinthu zambirimbiri zoti tiwerenge. Nanga kodi ifeyo timakondanso kutumizira anthu ambirimbiri nkhani zimene zangochitika kumene kapena nkhani zachabechabe zimene zimangowawonongera nthawi? Kuchita zimenezi n’kusaganiza bwino. Tisanatumize uthenga ndi bwino kuganizira cholinga choutumizira. Kodi tikufuna kuti munthu akalandira achite chiyani? M’mbuyomu, anthu ankalemberana makalata ndi achibale komanso anzawo pofuna kuwadziwitsa za moyo wawo. Ifenso tiyenera kukhala ndi cholinga chimenechi tikamatumiza mauthenga pa Intaneti. Komanso si bwino kutumizira anthu zinthu zimene tilibe nazo umboni.

Ndiyeno, kodi tiziigwiritsa ntchito bwanji Intaneti? Kodi tisamaigwiritse ntchito n’komwe? Nthawi zina zingakhale bwino kusiyiratu. Munthu amene tamutchula poyamba uja, yemwe kwa zaka zambiri anali ndi vuto losafuna kuchoka pa Intaneti, anachita zimenezi kuti athetse vutolo. Komabe Intaneti ikhoza kutithandiza ngati tilola ‘kuganiza bwino kutiyang’anira, ndiponso kuzindikira kutiteteza.’​—Miy. 2:10, 11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 N’chimodzimodzinso ndi zithunzi. Ngakhale kuti tingajambule zithunzi kuti tigwiritse ntchito, mwina sitingakhale ndi ufulu wozifalitsa n’kutchula mayina a anthu amene ali pa zithunzizo ndiponso kutchula kumene amakhala.

[Chithunzi patsamba 4]

Kodi mungatani kuti musapusitsidwe ndi zinthu zabodza pa Intaneti?

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi muyenera kuganizira chiyani musanatumize uthenga?