Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesetsani Kukhala pa Mtendere ndi Ena

Yesetsani Kukhala pa Mtendere ndi Ena

Yesetsani Kukhala pa Mtendere ndi Ena

“Tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.”​—AROMA 14:19.

1, 2. N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimakhala mwamtendere?

MASIKU ano, mtendere weniweni ukusowa m’dzikoli. Ngakhale anthu amene amachokera m’dziko limodzi ndiponso amene amalankhula chinenero chimodzi, nthawi zambiri sagwirizana. Iwo sagwirizana chifukwa choti amasiyana pa nkhani za chipembedzo, ndale, chuma kapena maphunziro. Koma mosiyana ndi zimenezi, anthu a Yehova ndi ogwirizana ngakhale kuti ndi ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.”​—Chiv. 7:9.

2 Mtendere umene tili nawo sikuti umangobwera wokha. Mtenderewu ulipo makamaka chifukwa chakuti tili “pa mtendere ndi Mulungu” popeza timakhulupirira Mwana wake amene anakhetsa magazi ake kuti aphimbe machimo athu. (Aroma 5:1; Aef. 1:7) Chinanso n’chakuti Mulungu woona amapereka mzimu woyera kwa atumiki ake okhulupirika ndipo mtendere ndi khalidwe lina limene mzimuwo umatulutsa. (Agal. 5:22) Chifukwa china n’chakuti ‘sitili mbali ya dzikoli.’ (Yoh. 15:19) Ife sitilowerera nkhani za ndale. Popeza kuti ‘tasula malupanga athu kuti akhale makasu a pulawo’ sitimenya nawo nkhondo.​—Yes. 2:4.

3. Kodi mtendere umene tingakhale nawo umatithandiza bwanji, nanga tikambirana chiyani m’nkhani ino?

3 Mtendere umene tingakhale nawo umatilimbikitsa kuchita zambiri osati kungopewa kuchitira ena zoipa. ‘Timakondana’ ngakhale kuti mu mpingo wa Mboni za Yehova muli anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana ndiponso zikhalidwe zosiyanasiyana. (Yoh. 15:17) Mtenderewu umatithandiza ‘kuchitira onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.’ (Agal. 6:10) Mtendere umene tili nawo ndi Yehova komanso ndi Akhristu anzathu ndi wamtengo wapatali ndipo tiyenera kuyesetsa kuti usasokonezeke. Tiyeni tikambirane zimene tingachite kuti tizikhala pa mtendere ndi ena mu mpingo.

Zimene Tingachite ‘Tikapunthwa’

4. Kodi tingatani kuti tikhalenso pa mtendere ndi munthu amene tamukhumudwitsa?

4 Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, analemba kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri. Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro.” (Yak. 3:2) Choncho Akhristu mu mpingo akhoza kusemphana maganizo. (Afil. 4:2, 3) Ngakhale zili choncho, anthu akhoza kuthetsa kusemphana maganizo popanda kusokoneza mtendere mu mpingo. Mwachitsanzo, tiyeni tione malangizo amene angatithandize ngati tazindikira kuti takhumudwitsa munthu wina.​—Werengani Mateyu 5:23, 24.

5. Kodi tingatani kuti tisunge mtendere ndi munthu amene watilakwira?

5 Nanga bwanji ngati munthu wina watilakwira pang’ono? Kodi tiziyembekezera kuti munthuyo abwere kudzatipepesa? Lemba la 1 Akorinto 13:5 limati: “[Chikondi] sichisunga zifukwa.” Munthu wina akatilakwira timasonyeza kuti tikufuna kusunga mtendere pomukhululukira n’kuiwala nkhaniyo. Tikatero, ndiye kuti ‘sitikusunga zifukwa.’ (Werengani Akolose 3:13.) Imeneyi ndi njira yabwino yothetsera mavuto ang’onoang’ono. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tikhale pa mtendere ndi Akhristu anzathu komanso kuti tikhale ndi mtendere wa m’maganizo. Mwambi wina wabwino kwambiri umati: “Kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa [munthu] kukhala wokongola.”​—Miy. 19:11.

6. Kodi tingachite chiyani ngati munthu wina watilakwira ndipo zikutivuta kungoiwala?

6 Nanga bwanji ngati munthu wina watilakwira ndipo zikutivuta kungoiwala nkhaniyo. Si nzeru kumangouza aliyense nkhaniyo. Miseche ya mtundu umenewu imasokoneza mtendere mu mpingo. Kodi tingathetse bwanji nkhani yotereyi mwamtendere? Lemba la Mateyu 18:15 limati: “Ngati m’bale wako wachimwa, upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo.” N’zoona kuti lemba la Mateyu 18:15-17 limanena za machimo akuluakulu koma mfundo ya pa vesi 15 ikhoza kutithandizanso pa zochitika zina. Choncho tiyenera kukumana ndi munthu amene watilakwira patokha n’kukambirana naye mwachikondi n’cholinga choti tikhazikitse mtendere. *

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthetsa mavuto mwamsanga?

7 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndipo musam’patse malo Mdyerekezi.” (Aef. 4:26, 27) Nayenso Yesu ananena kuti: “Thetsa nkhani mofulumira ndi munthu wokuimba mlandu.” (Mat. 5:25) Choncho tiyenera kuthetsa nkhani mwamsanga kuti tikhazikitse mtendere. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? Kupanda kutero, vutolo likhoza kukula ngati bala limene silinathiridwe mankhwala. Tisalole kunyada, nsanje kapena kukondetsa zinthu zakuthupi kutilepheretsa kuthetsa nkhani mwamsanga.​—Yak. 4:1-6.

Zimene Tingachite Ngati Vutolo Likukhudza Anthu Ambiri

8, 9. (a) M’nthawi ya Paulo, kodi Akhristu mu mpingo wa ku Roma ankasemphana maganizo pa nkhani iti? (b) Kodi Paulo anapereka malangizo otani pa vuto lawoli?

8 Nthawi zina mavuto a mu mpingo amakhudza anthu ambiri osati awiri okha. Izi ndi zimene zinachitikira Akhristu a ku Roma omwe Paulo anawalembera kalata. Panali kusemphana maganizo pakati pa Akhristu achiyuda ndi Akhristu a mitundu ina. Anthu ena mu mpingo anali ndi chikumbumtima champhamvu ndipo ankanyoza anthu amene anali ndi chikumbumtima chofooka, kapena kuti amene chikumbumtima chawo chinkawaletsa kuchita zinthu zambiri ngakhale kuti zinthuzo n’zosaletsedwa m’Baibulo. Nawonso anthu a chikumbumtima chofookawa ankaweruza anzawo pa zinthu zimene aliyense ali ndi ufulu wosankha. Kodi Paulo anawapatsa malangizo ati?​—Aroma 14:1-6.

9 Paulo anapereka malangizo kwa magulu onse awiri. Iye analangiza anthu amene anazindikira zoti sayenera kutsatira Chilamulo cha Mose kuti asanyoze abale awo. (Aroma 14:2, 10) Maganizo onyoza ena akanatha kukhumudwitsa okhulupirira amene ankaona kuti n’kulakwa kudya zinthu zoletsedwa m’Chilamulo. Paulo anawalangiza kuti: “Siyani kuwononga ntchito ya Mulungu chifukwa cha zakudya basi. . . . Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.” (Aroma 14:14, 15, 20, 21) Paulo analangizanso Akhristu amene anali ndi chikumbumtima chofooka kuti asamaweruze anthu amene ali ndi maganizo osiyana ndi awo. (Aroma 14:13) Iye anawauza kuti: “Musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.” (Aroma 12:3) Atapereka malangizo kwa anthu onsewa, Paulo analemba kuti: “Choncho, tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.”​—Aroma 14:19.

10. Mofanana ndi Akhristu mu mpingo wa ku Roma, kodi chofunika n’chiyani kuti tithetse mavuto masiku ano?

10 Sitikukayikira kuti Akhristu mu mpingo wa ku Roma anatsatira malangizo a Paulo ndipo anasintha. Pakabuka mavuto pakati pa Akhristu masiku ano, tikhoza kuwathetsa mwabata tikafufuza ndiponso kutsatira malangizo a m’Malemba. Mofanana ndi Akhristu a ku Roma, anthu akasemphana maganizo, onse ayenera kusintha kuti ‘asunge mtendere pakati pawo.’​—Maliko 9:50.

Kodi Akulu Angathandize Bwanji?

11. Kodi mkulu ayenera kuchita chiyani ngati Mkhristu akufuna kumuuza za vuto limene ali nalo ndi Mkhristu wina?

11 Kodi akulu ayenera kutani ngati Mkhristu akufuna kuwauza za vuto limene ali nalo ndi wachibale kapena Mkhristu mnzake? Lemba la Miyambo 21:13 limati: “Aliyense wotseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka, nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.” Mkulu sayenera ‘kutseka khutu lake.’ Komabe mwambi wina umachenjeza kuti: “Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, koma mnzake amabwera n’kumufufuzafufuza.” (Miy. 18:17) Mkulu ayenera kumvetsera mwachifundo, koma ayenera kusamala kuti asakhale ku mbali ya munthu amene akunena vutolo. Pambuyo pomvetsera nkhaniyo, angachite bwino kufunsa munthu wodandaulayo ngati wakambirana ndi munthu amene wamukhumudwitsayo. Mkuluyo akhozanso kukambirana naye mfundo za m’Malemba zimene ayenera kutsatira kuti asunge mtendere.

12. Perekani zitsanzo zosonyeza kuopsa kochita zinthu mopupuluma tikangomva munthu wina akudandaula za mnzake.

12 M’Baibulo muli zitsanzo zitatu zosonyeza kuti si bwino kuchita zinthu mopupuluma titangomva mbali imodzi ya nkhani. Potifara anakhulupirira bodza la mkazi wake lakuti Yosefe amafuna kumugwirira. Potifara anakwiya kwambiri ndipo anatsekera Yosefe m’ndende. (Gen. 39:19, 20) Mfumu Davide inakhulupiriranso bodza limene Ziba ananena loti Mefiboseti anali ku mbali ya adani a Davide. Mopupuluma Davide anayankha kuti: “Taona, zonse zimene zinali za Mefiboseti ndi zako.” (2 Sam. 16:4; 19:25-27) Mfumu Aritasasita inauzidwa kuti Ayuda akumanganso mpanda ku Yerusalemu ndipo akufuna kupandukira Ufumu wa Perisiya. Mfumuyo inakhulupirira bodzali n’kulamula kuti Ayudawo asiye ntchito yawo yomanga. Chifukwa cha zimenezi, Ayuda anasiya kumanga kachisi wa Mulungu. (Ezara 4:11-13, 23, 24) Akulu achikhristu angachite bwino kutsatira malangizo amene Paulo anapereka kwa Timoteyo oti azipewa kuweruziratu asanamvetse nkhani yonse.​Werengani 1 Timoteyo 5:21.

13, 14. (a) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati anthu asemphana maganizo? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize akulu kuweruza bwino nkhani zokhudza okhulupirira anzawo?

13 Ngakhale pamene tikuganiza kuti tamvetsa mbali zonse za nkhani inayake, tiyenera kuzindikira kuti “ngati wina akuganiza kuti akudziwa za chinachake, sanachidziwebe mokwanira.” (1 Akor. 8:2) Kodi tikudziwadi zinthu zonse zimene zinayambitsa vutolo? Kodi tikuwadziwadi bwinobwino anthu amene akhudzidwa ndi vutoli? Akulu akamaweruza ayenera kusamala kuti asapusitsidwe ndi chinyengo kapena mphekesera. Komanso sayenera kungokhulupirira munthu chifukwa choti ndi wachuma. Woweruza amene Mulungu wasankha, yemwe ndi Yesu Khristu, amaweruza mwachilungamo. Iye saweruza “potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake.” (Yes. 11:3, 4) M’malomwake Yesu amatsogoleredwa ndi mzimu wa Yehova. Akulu achikhristu nawonso ali ndi mwayi wotsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.

14 Akulu asanaweruze nkhani zokhudza Akhristu anzawo, ayenera kupempha Yehova kuti awathandize ndi mzimu wake. Iwo angathandizidwe ndi mzimuwo akamafufuza m’Mawu a Mulungu ndiponso m’mabuku ochokera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.​—Mat. 24:45.

Tiyenera Kukhalabe pa Mtendere ndi Mulungu

15. Ngati Mkhristu wadziwa kuti wina wachita tchimo lalikulu, kodi ayenera kuchita chiyani?

15 Akhristufe timalimbikitsidwa kuyesetsa kukhala pa mtendere ndi ena. Komabe Baibulo limanenanso kuti: “Nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere.” (Yak. 3:17) Kukhala amtendere kukubwera pambuyo pa kukhala oyera. Mawu akuti kukhala oyera akutanthauza kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amaona kuti ndi abwino ndiponso kutsatira mfundo zake zolungama. Mkhristu akadziwa kuti mnzake wachita tchimo lalikulu ayenera kumulimbikitsa kukaulula kwa akulu. (1 Akor. 6:9, 10; Yak. 5:14-16) Ngati mnzakeyo sakukaulula, Mkhristu amene akudziwa za tchimolo ayenera kukauza akulu. Kulephera kuchita zimenezi chifukwa chofuna kukhalabe pa mtendere ndi munthuyo kumachititsa kuti tigawane naye machimo.​—Lev. 5:1; werengani Miyambo 29:24.

16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehu anachita atakumana ndi Mfumu Yehoramu?

16 Nkhani ya m’Baibulo yokhudza Yehu imasonyeza kuti chilungamo cha Mulungu n’chofunika kuposa kusunga mtendere ndi munthu wochimwa. Yehu anatumidwa ndi Mulungu kuti akapereke chiweruzo kunyumba ya Mfumu Ahabu. Yehoramu anali mwana wa Ahabu ndi Yezebeli ndipo anali mfumu yoipa. Iye anakwera galeta lake n’kupita kukakumana ndi Yehu n’kumufunsa kuti: “Kodi ukubwerera zamtendere Yehu?” Kodi Yehu anayankha kuti chiyani? Iye anati: “Mtendere ungakhalepo bwanji pali dama la Yezebeli mayi ako ndi amatsenga ake ambirimbiri?” (2 Maf. 9:22) Nthawi yomweyo, Yehu anakoka uta wake n’kulasa Yehoramu mpaka muvi unatulukira pamtima. Mofanana ndi Yehu, akulu sayenera kulekerera anthu ochimwa mwadala amene sakulapa pofuna kukhalabe nawo pa mtendere. Iwo amawachotsa pofuna kuti mpingo upitirize kukhala pa mtendere ndi Mulungu.​—1 Akor. 5:1, 2, 11-13.

17. Kodi Akhristu onse angatani kuti asunge mtendere?

17 Nthawi zambiri abale akasemphana maganizo, nkhani zake zimakhala zing’onozing’ono zosafunika komiti ya chiweruzo. Choncho ndi bwino kungoiwala nkhani zoterezi. Mawu a Mulungu amati: “Wophimba machimo akufunafuna chikondi, ndipo amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.” (Miy. 17:9) Kutsatira mawu amenewa kungatithandize tonsefe kusunga mtendere mu mpingo ndiponso kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.​—Mat. 6:14, 15.

Mulungu Amadalitsa Anthu Amene Amayesetsa Kukhala pa Mtendere ndi Ena

18, 19. Kodi kuyesetsa kukhala pa mtendere ndi ena n’kofunika bwanji?

18 ‘Tikamatsatira zinthu zobweretsa mtendere,’ Yehova amatidalitsa kwambiri. Timakhalanso pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova tikamatsatira njira zake. Timasunganso mtendere ndiponso umodzi mu paradaiso wathu wauzimu. Kuyesetsa kukhala pa mtendere ndi anthu mu mpingo kumatithandizanso kuona mmene tingakhalire pa mtendere ndi anthu amene timawalalikira “uthenga wabwino wamtendere.” (Aef. 6:15) Timathanso ‘kukhala odekha kwa onse ndiponso ougwira mtima pokumana ndi zoipa.’​—2 Tim. 2:24.

19 Tisaiwalenso kuti padzakhala “kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) Izi zikadzachitika padzikoli padzakhala anthu mamiliyoni ambiri osiyanasiyana. Iwo adzakhala ochokera m’mayiko osiyanasiyana ndiponso amene anakhalako nthawi zosiyanasiyana ngakhale a pa nthawi imene “dziko linakhazikika.” (Luka 11:50, 51) Kuphunzitsa anthu amene adzaukitsidwe kuti atsatire njira za mtendere udzakhala mwayi waukulu. Zimene tikuphunzira panopa zokhudza kusunga mtendere zidzatithandiza kwambiri pa nthawi imeneyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kuti mumve malangizo a m’Malemba okhudza zimene mungachite pakachitika machimo akuluakulu monga kunena miseche yoipitsa mbiri ya munthu ndiponso chinyengo, onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1999, tsamba 17 mpaka 22.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi tingatani kuti tisunge mtendere ndi munthu amene tamukhumudwitsa?

• Kodi tingatani kuti tisunge mtendere ndi munthu amene watikhumudwitsa?

• Ngati anthu awiri ayambana, n’chifukwa chiyani sitiyenera kukhala ku mbali ya munthu mmodzi?

• N’chifukwa chiyani chilungamo n’chofunika kwambiri kuposa kusunga mtendere ndi munthu wochimwa?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 29]

Yehova amakonda anthu amene amakhululukira ena ndi mtima wonse