Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiyeni Tithamange Mpikisano Mopirira

Tiyeni Tithamange Mpikisano Mopirira

Tiyeni Tithamange Mpikisano Mopirira

“Tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.”​—AHEB. 12:1.

1, 2. Kodi mtumwi Paulo anayerekezera moyo wachikhristu ndi chiyani?

CHAKA chilichonse m’madera ambiri mumachitika mipikisano yothamanga. Cholinga cha akatswiri amene amachita nawo mipikisanoyi ndi kulandira mphoto. Komabe ena amadziwa kuti sapambana. Kwa anthu oterewa, kungothamanga kokhako mpaka kukamaliza nawo chimakhala chinthu chonyaditsa.

2 M’Baibulo, moyo wachikhristu amauyerekezera ndi mpikisano wothamanga. M’kalata yake yoyamba, mtumwi Paulo anafotokoza mfundo imeneyi kwa Akhristu anzake a ku Korinto wakale. Iye analemba kuti: “Kodi simukudziwa kuti ochita mpikisano wa liwiro amathamanga onse, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphoto? Thamangani m’njira yoti mukalandire mphotoyo.”​—1 Akor. 9:24.

3. N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti mmodzi yekha ndiye amalandira mphoto?

3 Kodi Paulo ankatanthauza kuti munthu mmodzi yekha pa Akhristu onsewo ndi amene adzalandire mphoto ya moyo wosatha, pomwe ena onsewo sadzalandira chilichonse? Ayi si choncho. Othamanga pa mpikisano ankakonzekera kwambiri ndiponso ankachita khama n’cholinga choti alandire mphoto. Paulo ankafunanso kuti Akhristu anzake achite khama kwambiri pa mpikisanowu. Izi zikanawathandiza kuti adzalandire mphoto ya moyo wosatha. Choncho pa mpikisano umene Akhristu akuthamanga, onse amene amamaliza amalandira mphoto.

4. Kodi tiyenera kudziwa chiyani zokhudza mpikisano womwe tikuthamanga?

4 Mawu amene Paulo ananenawa ndi olimbikitsa, koma ndi otipangitsanso kuganizira kwambiri za moyo wathu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti mphoto ya moyo wosatha kumwamba kapena m’Paradaiso padziko lapansi ndi yamtengo wapatali kuposa chilichonse. Moyo wathu monga Akhristu uli ngati ulendo wautali kwambiri wokhala ndi zinthu zosokoneza ndiponso zoopsa zambirimbiri. (Mat. 7:13, 14) Koma n’zomvetsa chisoni kuti ena afooka mwinanso kusiya kuthamanga ndipo ena agwa. Kodi ndi zinthu zoopsa ziti zimene tingakumane nazo pa mpikisanowu? Kodi tingatani kuti tizipewe? Nanga tingatani kuti timalize bwinobwino n’kulandira mphoto?

Tiyenera Kupirira Kuti Tipambane

5. Kodi pa Aheberi 12:1, Paulo ananena chiyani chokhudza mpikisano wothamanga?

5 Paulo ananenanso za mpikisano wothamanga m’kalata yake yopita kwa Akhristu achiheberi ku Yerusalemu ndi Yudeya. (Werengani Aheberi 12:1.) Iye ananena zifukwa zothamangira pa mpikisanowu komanso zimene munthu angachite kuti apambane. Choyamba tikambirana chifukwa chimene Paulo analembera kalatayi ndiponso zimene ankafuna kuti Aheberiwo achite. Kenako tikambirana zimene tikuphunzira pa mawu akewo.

6. Kodi Akhristu anakumana ndi mavuto otani kuchokera kwa atsogoleri achipembedzo?

6 Akhristu oyambirira, makamaka amene ankakhala ku Yerusalemu ankakumana ndi mavuto ambirimbiri. Iwo ankazunzidwa ndi atsogoleri a chipembedzo achiyuda omwe ankakakamiza anthu kuti aziwatsatira. Pafupifupi zaka 30 izi zisanachitike, atsogoleri a zipembedzo anali atachitanso chimodzimodzi kwa Yesu pomunamizira kuti anali woukira boma komanso pomupha ngati chigawenga. Pa nthawiyi, iwo ankafuna kuletsa anthu kulalikira za Yesu. M’buku la Machitidwe muli nkhani zambirimbiri zosonyeza mmene atsogoleriwa ankazunzira Akhristu. Iwo anayamba zimenezi pasanapite nthawi kuchokera pamene zozizwitsa zinachitika m’chaka cha 33 C.E. Izi zinachititsa kuti moyo wa Akhristu okhulupirika ukhale wovuta kwambiri.​—Mac. 4:1-3; 5:17, 18; 6:8-12; 7:59; 8:1, 3.

7. Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti nthawi imene Akhristu amene Paulo anawalembera kalata ikhale yovuta?

7 Pamene izi zinkachitika n’kuti nthawi za Ayuda zitatsala pang’ono kutha. Yesu anali atauza otsatira ake za kuwonongedwa kwa mtundu wa Yuda wosakhulupirika. Iye anawauzanso zinthu zomwe zidzachitike chiwonongekocho chikadzayandikira ndipo anawapatsa malangizo okhudza zimene angachite kuti apulumuke. (Werengani Luka 21:20-22.) Kodi iwo anayenera kuchita chiyani? Yesu anawachenjeza kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa.”​—Luka 21:34.

8. Kodi n’chiyani chinapangitsa Akhristu ena kubwerera m’mbuyo potumikira Yehova?

8 Paulo analembera kalata Akhristu achiheberiwo patadutsa zaka pafupifupi 30 kuchokera pamene Yesu ananena mawu amenewa. Kodi Akhristuwo anatani patapita nthawi yaitali? Chifukwa cha mavuto ena ndiponso kudera nkhawa zinthu zofunika pa moyo, ena anasiya kuphunzira za Yehova ndiponso kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Iye. (Aheb. 5:11-14) Akhristu ena ayenera kuti ankaganiza kuti zinthu ziziwayendera bwino akamangotsatira zochita za Ayuda anzawo. Iwo ankaganiza kuti palibe vuto ndi zimenezi chifukwa chakuti Ayudawo ankakhulupirirabe Mulungu ndiponso kutsatira mfundo zambiri za m’Chilamulo cha Mose. Mu mpingo munalinso anthu ena amene ankakakamiza anzawo kutsatira Chilamulo cha Mose ndi miyambo ina yachiyuda. Kodi Paulo ananena chiyani pofuna kulimbikitsa Akhristu anzake kuti akhale maso mwauzimu n’kumathamanga mpikisano mopirira?

9, 10. (a) Kodi kumapeto kwa chaputala 10 cha Aheberi, Paulo ananena kuti Akhristu achiheberi ankafunika kuchita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani Paulo analemba za atumiki ena akale okhulupirika?

9 Yehova anauzira Paulo kulemba kalata yolimbikitsa Akhristu achiheberi. M’chaputala 10 cha kalata yake, Paulo anawauza kuti Chilamulo cha Mose chinali “mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zikubwera.” Iye anafotokozanso momveka bwino kuti nsembe ya Yesu yokha ndi imene ingathandize kuti machimo awo akhululukidwe. Chakumapeto kwa chaputalachi, Paulo analangiza anthuwo kuti: “Mukufunika kupirira, kuti mutachita chifuniro cha Mulungu, mudzalandire zimene Mulungu walonjeza. Pakuti ‘kwatsala kanthawi kochepa kwambiri,’ ndipo ‘amene akubwerayo afika ndithu, sachedwa ayi.’”​—Aheb. 10:1, 36, 37.

10 Ndi mawu amenewa, Paulo analimbikitsa Akhristu achiheberi kupirira. M’chaputala 12 iye anawalimbikitsanso kuchita zimenezi powauza kuti ‘athamange mopirira mpikisano umene anawaikira.’ Koma asananene zimenezi, Paulo anauziridwa ndi Mulungu kuti awalembere nkhani ina imene ili m’chaputala 11. M’chaputala chimenechi, iye anafotokoza tanthauzo la kukhulupirira Mulungu moona ndipo anawalembera zimene anthu amene anali ndi chikhulupiriro choona anachita. N’chifukwa chiyani ananena za chikhulupiriro asanabwereze kunena za kupirira? Iye ankafuna kuti Akhristuwo azindikire kuti munthu amafunika kupirira ndiponso kulimba mtima kuti asonyeze kuti amakhulupiriradi Yehova. Iye anatchula amuna ndi akazi ambirimbiri amene anakhala okhulupirika kwa Yehova ngakhale pa nthawi imene anakumana ndi mavuto. Chitsanzo chawo chikanathandiza Akhristuwo kupirira mavuto. Atafotokoza zinthu zosonyeza chikhulupiriro zimene atumiki a Yehova amenewa anachita, Paulo anauza Akhristu achiheberi kuti: “Chifukwa chakuti tili ndi mtambo wa mboni waukulu chonchi wotizungulira, tiyeninso tivule cholemera chilichonse ndi tchimo limene limatikola mosavuta lija. Ndipo tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.”​—Aheb. 12:1.

“Mtambo wa Mboni”

11. Kodi kuganizira chitsanzo cha “mtambo wa mboni waukulu” kungatithandize bwanji?

11 Sikuti ‘mtambo wa mboni waukuluwu’ ndi anthu omwe ankangoonerera anthu akuthamanga ayi. Koma iwo ankathamanga nawo mu mpikisanowo mpaka kukamaliza. Ngakhale kuti iwo anamwalira, mophiphiritsira angatengedwe kukhala akatswiri amene akuthandiza ena omwe angoyamba kumene kuthamanga. Ndiye tangoyerekezerani mmene wothamanga watsopano angamvere poona kuti anthu akumuchemerera ndipo amene akumuchemererawo ndi akatswiri. Iye akhoza kuyesetsa kwambiri kuti apambane. Mtambo wa mboniwu umasonyeza kuti ngakhale titakumana ndi mavuto ambiri, tikhoza kupambana n’kulandira mphoto. Choncho kuganizira kwambiri chitsanzo cha “mtambo wa mboni” kukanathandiza Akhristu achiheberi kukhala olimba mtima ndiponso ‘kuthamanga mpikisano mopirira.’ Ifenso tikamaganizira chitsanzo chimenechi tikhoza kuchita chimodzimodzi.

12. Kodi zitsanzo za anthu okhulupirika amene Paulo ananena zikutiphunzitsa chiyani?

12 Moyo wa anthu ambiri okhulupirika amene Paulo anawatchula si wosiyana kwambiri ndi wathu. Mwachitsanzo, Nowa ankakhala pa nthawi imene dziko linatsala pang’ono kuwonongedwa ndi Chigumula. Ifenso tikukhala m’nthawi imene dzikoli latsala pang’ono kuwonongedwa. Yehova anauza Abulahamu ndi Sara kuti achoke kwawo n’cholinga choti azimutumikira. Iye anawalonjeza kuti adzakhala makolo a mtundu wa anthu omwe adzamutumikire ndipo iwo ankayembekezera kukwaniritsidwa kwa lonjezoli. Yehova amatipemphanso kuti tidzikane tokha n’cholinga choti tikhale naye pa ubwenzi wabwino ndipo walonjeza kuti adzatidalitsa. Mose anayenda m’chipululu choopsa kwambiri popita ku Dziko Lolonjezedwa. Ifenso tili pa ulendo m’dziko loipali ndipo tikukalowa m’dziko latsopano. Choncho tiyenera kuganizira kwambiri za moyo wa anthu okhulupirikawa. Tingachite zimenezi potsanzira zinthu zosangalatsa Yehova zimene anachita n’kumapewa zinthu zokhumudwitsa Yehova zimene anachita.​—Aroma 15:4; 1 Akor. 10:11.

Zimene Zinawathandiza Kumaliza Mpikisano

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu zimene Nowa anauzidwa kuchita zinali zovuta, ndipo n’chiyani chinamuthandiza kuti achite zonse zimene Yehova anamuuza?

13 Kodi n’chiyani chimene chinathandiza atumiki a Yehova amenewa kupirira n’kupambana pa mpikisanowu? Taonani zimene Paulo analemba zokhudza Nowa. (Werengani Aheberi 11:7.) Nowa anali asanaone ‘chigumula chamadzi padziko lapansi chikuwononga chamoyo chilichonse.’ (Gen. 6:17) Zoterezi zinali zisanachitikepo ndipo panalibe amene ankaganiza kuti zingachitike. Ngakhale zinali choncho, Nowa sanaganize kuti n’zosatheka. Iye anatero chifukwa chakuti ankakhulupirira kuti chilichonse chimene Yehova wanena chidzachitika. Nowa sanaone kuti Mulungu wamupempha kuchita zinthu zovuta. Iye anatsatira zimene Mulungu analamula ndipo “anachitadi momwemo.” (Gen. 6:22) Tangoganizirani zimene Nowa anauzidwa kuchita. Iye anayenera kumanga chingalawa, kusonkhanitsamo zinyama, kusunga chakudya choti azikadya ndi banja lake komanso cha zinyama. Anayeneranso kulalikira uthenga wochenjeza anthu ndiponso kuyesetsa kuti banja lake likhale lolimba mwauzimu. Iyitu sinali ntchito yamasewera. Koma chikhulupiriro ndiponso kupirira kwa Nowa zinathandiza kuti iye ndi banja lake apulumuke ndiponso adalitsidwe.

14. Kodi Abulahamu ndi Sara anapirira zinthu zotani ndipo zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?

14 Kenako Paulo ananena kuti Abulahamu ndi Sara anali m’gulu la ‘mtambo wa mboni waukulu wotizungulira.’ Moyo wawo unasintha pamene Mulungu anawauza kuti achoke kwawo ku Uri. Iwo sankadziwa kuti kumene akupitako zinthu zikawathera bwanji. Koma ankakhulupirira kwambiri Yehova ndipo ankamumvera ngakhale pamene zinthu zinavuta. Chifukwa chakuti Abulahamu analolera kusiya zambiri kuti atumikire Yehova, Baibulo limati iye ndi ‘tate wa onse okhala ndi chikhulupiriro.’ (Aroma 4:11) Akhristu achiheberi ankadziwa za moyo wa Abulahamu ndi banja lake choncho Paulo anangotchula zinthu zina zikuluzikulu zimene anachita zosonyeza chikhulupiriro. Koma zimene Paulo ananena zimasonyeza bwinobwino kulimba kwa chikhulupiriro chawo. Ponena za iwo Paulo anati: “Onsewa [kuphatikizapo Abulahamu ndi banja lake] anafa ali ndi chikhulupiriro, ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali ndi kuwalandira, ndipo analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.” (Aheb. 11:13) Chifukwa chakuti ankakhulupirira Mulungu komanso anali naye pa ubwenzi wabwino, zinawathandiza kuthamanga mpikisano mopirira.

15. Kodi n’chiyani chinachititsa Mose kuti asankhe moyo umene anali nawo?

15 Mose ndi chitsanzo china cha mtumiki wa Yehova amene ali m’gulu la “mtambo wa mboni.” Iye anasiya moyo wa wofuwofu ndipo “anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu.” Kodi n’chiyani chinamupangitsa kuchita zimenezi? Paulo anayankha kuti: “Anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire. . . . Anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Werengani Aheberi 11:24-27.) Mose sanasokonezedwe ndi kuchita “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.” Iye ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu ndipo zimenezi zinamupangitsa kuti akhale wolimba mtima kwambiri komanso wopirira. Mose anachita zonse zimene akanatha kuti atulutse mtundu wa Isiraeli ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa.

16. Tikudziwa bwanji kuti Mose sanakwiye atauzidwa kuti sadzalowa nawo m’Dziko Lolonjezedwa?

16 Mofanana ndi Abulahamu, nayenso Mose sanaone malonjezo a Mulungu akukwaniritsidwa. Aisiraeli ali pafupi kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Mulungu anauza Mose kuti: “Pakuti udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa m’dziko limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli.” Izi zinachitika chifukwa chakuti iye ndi Aroni atapsetsedwa mtima ndi anthu osamvera, anachita zinthu “mosakhulupirika kwa [Mulungu] pakati pa ana a Isiraeli, kumadzi a pa Meriba.” (Deut. 32:51, 52) Kodi Mose anakwiya ndi zimenezi? Ayi sanakwiye. Tikutero chifukwa anapempha Yehova kuti adalitse Aisiraeli ndipo mawu ake omaliza anali akuti: “Ndiwe wodala Isiraeli iwe! Ndani angafanane ndi iwe, anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova, chishango chako chokuthandiza, amenenso ndi lupanga lako lopambana?”​—Deut. 33:29.

Zimene Tikuphunzira

17, 18. (a) Pamene tikuthamanga pa mpikisano wathu, kodi tikuphunzira chiyani kuchokera pa zitsanzo za “mtambo wa mboni”? (b) Kodi tiphunzira chiyani m’nkhani yotsatira?

17 Panopa taphunzira za moyo wa anthu amene ali m’gulu la ‘mtambo wa mboni wotizungulira.’ Zimenezi zatithandiza kudziwa kuti ngati tikufuna kuthamanga mpikisano mpaka kukamaliza, tiyenera kukhulupirira kwambiri Mulungu ndi malonjezo ake. (Aheb. 11:6) Chikhulupiriro chimenechi chiyenera kukhudza zochita zathu za tsiku ndi tsiku. Mosiyana ndi anthu opanda chikhulupiriro, ife atumiki a Yehova timaona za m’tsogolo. Timatha ‘kuona Wosaonekayo’ ndipo izi zimatithandiza kuthamanga mpikisano mopirira.​—2 Akor. 5:7.

18 Mpikisano umene Akhristu akuthamanga si wophweka. Komabe n’zotheka kumaliza mpikisanowu n’kukalandira mphoto. M’nkhani yotsatira tiphunzira zinthu zina zimene zingatithandize kupambana mpikisanowu n’kulandira mphoto.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani Paulo analemba nkhani zokhudza chikhulupiriro cha mboni zokhulupirika za m’nthawi yakale?

• Kodi chitsanzo cha “mtambo wa mboni waukulu wotizungulira” chingatithandize bwanji kuthamanga mpikisanowu mopirira?

• Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zitsanzo za mboni zokhulupirika monga Nowa, Abulahamu ndi Sara komanso Mose?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 19]

Abulahamu ndi Sara anasankha kusiya moyo wawo wabwino mumzinda wa Uri