Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndi Cholowa Changa

Yehova Ndi Cholowa Changa

Yehova Ndi Cholowa Changa

“Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Isiraeli.”​—NUM. 18:20.

1, 2. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kwa Alevi panthawi imene mafuko ankalandira cholowa cha malo m’Dziko Lolonjezedwa? (b) Kodi Yehova anawalonjeza chiyani Alevi?

AISIRAELI atatenga mbali yaikulu ya Dziko Lolonjezedwa, Yoswa anayamba kugawa malo kuti akhale cholowa cha mafuko a Isiraeli. Anagwira ntchito imeneyi limodzi ndi Mkulu wa Ansembe Eleazara ndiponso atsogoleri a mafuko. (Num. 34:13-29) Komabe Alevi sanalandire nawo cholowa cha malo. (Yos. 14:1-5) Kodi n’chifukwa chiyani fuko la Levi silinalandire gawo, kapena kuti cholowa cha malo, m’Dziko Lolonjezedwa? Kodi Mulungu anawaiwala?

2 Tikhoza kupeza mayankho a mafunso amenewa pa zimene Yehova anauza Alevi. Posonyeza kuti sanawaiwale, Yehova anawauza kuti: “Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Isiraeli.” (Num. 18:20) Mawu akuti: ‘Ine ndine cholowa chako,’ ndi olimbikitsa kwambiri. Kodi mungamve bwanji Yehova atakuuzani mawu amenewa? Mwina mungaganize kuti, ‘Kodi n’zotheka munthu ngati ine kuuzidwa ndi Wamphamvuyonse mawu amenewa?’ Mungadzifunsenso kuti, ‘Kodi masiku ano n’zotheka Yehova kukhala cholowa cha Mkhristu aliyense wopanda ungwiro?’ Mafunso amenewa ndi ofunika kwambiri chifukwa akukhudza inuyo komanso anthu amene mumawakonda. Choncho tiyeni tikambirane zimene Mulungu ankatanthauza ponena mawu amenewa. Kukambirana zimenezi kutithandiza kudziwa mmene Yehova angakhalire cholowa cha Akhristu masiku ano. Komanso zitithandiza makamaka kudziwa kuti iye angakhale cholowa chanu, kaya mukuyembekezera kukakhala kumwamba kapena kukhala m’Paradaiso padziko lapansi.

Yehova Ankasamalira Alevi

3. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Mulungu asankhe Alevi kumutumikira pa udindo wapadera?

3 Yehova asanapereke Chilamulo kwa Aisiraeli, mitu ya mabanja inkatumikira monga ansembe. Pamene Mulungu anapereka Chilamulo, anakonza zoti m’fuko la Levi muzichokera ansembe ndiponso othandiza awo. Kodi n’chiyani chinachititsa zimenezi? Mulungu atawononga ana aamuna oyamba kubadwa a ku Iguputo, iye anapatula ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli kuti akhale ake. Kenako iye anasankha kuti atenge Alevi “m’malo mwa ana aamuna onse oyamba kubadwa a Isiraeli.” Popeza kuti chiwerengero cha ana aamuna a mafuko ena a Aisiraeli chinali chachikulu kuposa cha Alevi, panafunika kuperekedwa ndalama m’malo mwa ana onse amene ‘anapitirira chiwerengero cha Alevi.’ (Num. 3:11-13, 41, 46, 47) Zitatero, Alevi anayamba kutumikira Mulungu wa Isiraeli pa udindo wawo wapadera.

4, 5. (a) Kodi Mulungu anakhala bwanji cholowa cha Alevi? (b) Kodi Mulungu ankasamalira bwanji Alevi?

4 Kodi Yehova anakhala bwanji cholowa cha Alevi pamene anawasankha kuti amutumikire pa udindo umenewu? Pamene Yehova ananena kuti akhale cholowa chawo ankatanthauza kuti m’malo mowapatsa malo monga cholowa, awapatsa utumiki wamtengo wapatali kwambiri. Cholowa chawo chinali “unsembe wa Yehova.” (Yos. 18:7) Chaputala 18 cha Numeri chimatithandiza kudziwa kuti iwo ankapezabe zofunika pa moyo. (Werengani Numeri 18:19, 21, 24.) Alevi ankayenera kupatsidwa “chakhumi chilichonse mu Isiraeli monga cholowa chawo chifukwa cha utumiki wawo.” Ankayenera kulandira gawo limodzi pa magawo 10 a zokolola ndiponso ziweto za Aisiraeli. Nawonso Alevi ankayenera kupereka gawo limodzi “labwino koposa” pa magawo 10 a zimene ankalandira n’cholinga choti asamalire ansembe. * (Num. 18:25-29) Ansembe ankapatsidwanso “zopereka zonse zopatulika” zimene ana a Isiraeli ankapereka kwa Mulungu kumalo ake olambirira. Choncho panali zifukwa zomveka zoti ansembe azikhulupirira kuti Yehova awasamalira.

5 Zikuoneka kuti m’Chilamulo cha Mose munali lamulo loti Aisiraeli azipereka chakhumi china. Mabanja achiisiraeli ankachigwiritsa ntchito kuti akhale ndi chakudya ndiponso zakumwa komanso kuti asangalale pa misonkhano yopatulika chaka chilichonse. (Deut. 14:22-27) Koma chakhumichi chinkagwiranso ntchito ina. Aisiraeli ankachita chikondwerero cha chaka cha Sabata pambuyo pa zaka 7 zilizonse. Kumapeto kwa chaka chachitatu ndiponso cha 6, Aisiraeli ankagwiritsa ntchito chakhumichi pothandiza osauka ndiponso Alevi. N’chifukwa chiyani Alevi ankalandira nawo chakhumichi? N’chifukwa chakuti ‘analibe gawo kapena cholowa’ mu Isiraeli.​—Deut. 14:28, 29.

6. Popeza Alevi sanapatsidwe malo mu Isiraeli monga cholowa chawo, kodi iwo ankakhala kuti?

6 Mwina mungadabwe kuti, ‘Ngati Alevi analibe malo awoawo, kodi ankakhala kuti?’ Mulungu anawapatsa pokhala. Iye anawapatsa mizinda 48 komanso malo ake odyetserako ziweto. Mizinda imeneyi inaphatikizapo mizinda 6 yothawirako. (Num. 35:6-8) Choncho Alevi anali ndi malo okhala pa nthawi imene sanali kutumikira pamalo opatulika a Mulungu. Yehova ankasamalira kwambiri anthu amene anadzipereka kuti amutumikire. Ndiyeno kodi Alevi anasonyeza bwanji kuti Yehova ndi cholowa chawo? Anasonyeza zimenezi pamene anakhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zowapatsa chilichonse chimene ankafunikira komanso kuti anali wofunitsitsa kuwasamalira.

7. Kodi Alevi ankafunika kuchita chiyani kuti Yehova akhale cholowa chawo?

7 Chilamulo sichinkanena kuti munthu amene walephera kupereka chakhumi alangidwe. Koma anthu akanyalanyaza kupereka chakhumi, ansembe ndi Alevi ankavutika ngati mmene zinachitikira m’nthawi ya Nehemiya. Pa nthawiyo, Alevi anafika mpaka posiya utumiki wawo kuti akalime kuminda yawo. (Werengani Nehemiya 13:10.) Choncho zikuonekeratu kuti Aisiraeli akapanda kumvera Chilamulo cha Yehova, Alevi sankasamalidwa. Kuwonjezera pamenepa, ansembe ndi Alevi nawonso ankafunika kukhulupirira Yehova komanso njira zake zowasamalirira.

Alevi Amene Anaona Kuti Yehova Ndi Cholowa Chawo

8. Kodi Asafu ankavutika maganizo ndi chiyani?

8 Yehova anali cholowa cha fuko lonse la Alevi. Komabe, Alevi ena ankanenanso mawu akuti “Yehova ndiye cholowa changa” posonyeza kuti paokha anali pa ubwenzi ndi Mulungu ndiponso kuti ankamukhulupirira. (Maliro 3:24) Mlevi wina amene ankatchula mawu amenewa anali woimba ndiponso wopeka nyimbo. Munthu ameneyu, timutchula kuti Asafu, ngakhale kuti mwina anali wina wa m’banja la Asafu. Asafu anali Mlevi yemwe ankatsogolera oimba m’masiku a Mfumu Davide. (1 Mbiri 6:31-43) Salimo 73 limanena kuti Asafu, kapena wina wa m’banja lake, anayamba kuchitira nsanje anthu oipa ndipo sankamvetsa kuti n’chifukwa chiyani anthu oipawo zinthu zikuwayendera bwino. Iye anafika mpaka ponena kuti: “Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe, ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.” Zikuoneka kuti iye anaiwala kuti kutumikira Yehova unali mwayi waukulu ndiponso kuti Yehova anali cholowa chake. Iye anali kuvutika kwambiri maganizo ‘kufikira pamene analowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.’​—Sal. 73:2, 3, 12, 13, 17.

9, 10. N’chifukwa chiyani Asafu ananena kuti Mulungu ndi ‘cholowa chake mpaka kalekale’?

9 Asafu atalowa m’malo opatulika, anayamba kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Mwina nanunso zimenezi zinakuchitikirani. N’kutheka kuti nthawi inayake munaiwala kuti kutumikira Yehova ndi mwayi wamtengo wapatali ndipo munayamba kuganizira kwambiri za kufunafuna chuma. Koma kupita ku misonkhano ndiponso kuphunzira Mawu a Mulungu kunakuthandizani kuyambanso kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Asafu anazindikira zimene zidzachitikire anthu oipa. Iye anaganiziranso zinthu zabwino zimene anali nazo chifukwa chotumikira Mulungu ndipo anazindikira kuti Yehova amugwira dzanja lake lamanja n’kumutsogolera. Choncho Asafu anauza Yehova kuti: “Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha.” (Sal. 73:23, 25) Kenako ananena kuti Mulungu ndi cholowa chake. (Werengani Salimo 73:26.) Wamasalimo ankadziwa kuti ngakhale ‘thupi lake ndi mtima wake zitalefuka,’ Mulungu adzakhala ‘cholowa chake mpaka kalekale.’ Iye ankakhulupiriranso ndi mtima wonse kuti Yehova adzamukumbukira chifukwa choti iye ndi mnzake. Yehova sadzaiwala utumiki umene Asafu anachita mokhulupirika. (Mlal. 7:1) Kudziwa zimenezi kunali kotonthoza kwambiri kwa Asafu. Iye anaimba kuti: “Kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.”​—Sal. 73:28.

10 Pamene Asafu ananena kuti Yehova anali cholowa chake sankangoganiza za zinthu zakuthupi zimene analandira monga Mlevi. Kwenikweni iye ankanena za mwayi wake wotumikira Yehova ndiponso wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Wam’mwambamwamba. (Yak. 2:21-23) Kuti apitirize kukhala pa ubwenzi umenewu, wamasalimoyu ankafunikira kupitiriza kukhulupirira Yehova ndiponso kumudalira. Asafu anayenera kukhulupirira kuti Mulungu adzamudalitsa pomupatsa tsogolo labwino ngati apitiriza kumumvera. Nanunso mungakhulupirire kuti Wamphamvuyonse adzakudalitsani ngati mmene anachitira ndi Asafu.

11. Kodi Yeremiya anafunsa funso lotani ndipo linayankhidwa bwanji?

11 Mlevi wina amene anaona kuti Yehova ndiye cholowa chake anali mneneri Yeremiya. Tiyeni tikambirane zimene iye ankatanthauza ponena mawu amenewa. Yeremiya ankakhala kumzinda wa Anatoti, womwe unali mzinda wa Alevi wa pafupi ndi Yerusalemu. (Yer. 1:1) Pa nthawi ina, nayenso Yeremiya ankafuna kudziwa kuti: N’chifukwa chiyani anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino pamene olungama akuvutika? (Yer. 12:1) Ataona zimene zinali kuchitika ku Yerusalemu ndiponso ku Yuda, ‘anadandaula’ kwa Yehova. Yeremiya ankadziwa kuti Yehova ndi wolungama. Yehova anayankha funso la Yeremiya pomuuza zimene anayenera kulosera ndiponso pokwaniritsa ulosiwo. Anthu amene anamvera Yehova ‘anapulumutsidwa’ koma anthu oipa amene zinthu zinkawayendera bwino sanamvere chenjezo la Yehova ndipo anawonongedwa.​—Yer. 21:9.

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani Yeremiya ananena kuti: “Yehova ndiye cholowa changa,” ndipo anali ndi mtima wotani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani mafuko onse a Isiraeli ankafunika kukhala ndi mtima wodikira?

12 Yeremiya anamva ngati anali kuyenda mu mdima pamene anali kuyang’ana dziko la kwawo litawonongedwa. Yehova ‘anamuchititsa kukhala ngati munthu woti anafa kalekale.’ (Maliro 1:1, 16; 3:6) Yeremiya anauza Aisiraeli kuti abwerere kwa Atate wawo wakumwamba, koma zoipa zawo zinachuluka kwambiri moti Mulungu analola kuti Yuda awonongedwe. Zimenezi zinamupweteka kwambiri Yeremiya ngakhale kuti iye sanali wolakwa. Pa nthawi yovutayi, mneneriyu anakumbukira chifundo cha Mulungu. Iye anati: “Ife sitinafafanizidwe.” N’zoona kuti chifundo cha Yehova chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse. Inali nthawi imeneyi pamene Yeremiya ananena kuti: “Yehova ndiye cholowa changa.” Iye anapitiriza kukhala ndi mwayi wotumikira Yehova monga mneneri.​Werengani Maliro 3:22-24.

13 Kwa zaka 70, Aisiraeli analibe kwawo chifukwa dziko lawo linali litawonongedwa. (Yer. 25:11) Koma mawu a Yeremiya akuti “Yehova ndiye cholowa changa” anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Mulungu ndi wachifundo ndipo izi zinachititsa kuti akhale ndi “mtima womudikira.” Cholowa cha mafuko onse a Isiraeli chinawonongedwa choncho iwo anafunika kukhala ndi mtima wodikira umene mneneriyu anali nawo. Ndi Yehova yekha amene akanawathandiza. Patapita zaka 70, anthu a Mulungu anabwezeretsedwa kudziko lawo ndipo anali ndi mwayi womutumikira ali kumeneko.​—2 Mbiri 36:20-23.

Anthu Ena Amene Yehova Anakhala Cholowa Chawo

14, 15. Kuwonjezera pa Alevi, ndaninso analola Yehova kuti akhale cholowa chake ndipo n’chifukwa chiyani?

14 Asafu ndi Yeremiya anali a fuko la Levi. Koma kodi ndi Alevi okha amene anali ndi mwayi wotumikira Yehova? Ayi. Davide, yemwe anadzakhala mfumu ya Isiraeli, anasonyeza kuti Mulungu ndi cholowa chake pamene ananena kuti Iye ndi “gawo langa m’dziko la amoyo.” (Werengani Salimo 142:1, 5.) Pa nthawi imene Davide ankalemba salimo limeneli sanali m’nyumba yachifumu kapena m’nyumba ina iliyonse. Iye anali atabisala m’phanga pothawa adani ake. Tikudziwa kuti Davide anabisala m’phanga kawiri. Ulendo wina anabisala pafupi ndi Adulamu ndipo ulendo wina m’chipululu cha Eni-gedi. N’kutheka kuti analemba Salimo 142 ali mu limodzi mwa mapanga awiriwa.

15 Ngati ndi choncho, ndiye kuti ndi nthawi imene Mfumu Sauli inkasakasaka Davide kuti imuphe. Davide anathawira kuphanga lovuta kukafikako. (1 Sam. 22:1, 4) N’kutheka kuti Davide ali kutchireko, ankaona kuti analibe mnzake amene angamuteteze. (Sal. 142:4) Nthawi imeneyi m’pamene Davide anapempha Mulungu kuti amuthandize.

16, 17. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa Davide kumva kuti analibe womuthandiza? (b) Kodi Davide anapempha thandizo kwa ndani?

16 Asanalembe Salimo 142, mwina Davide anamva zimene zinachitikira mkulu wa ansembe dzina lake Ahimeleki. Iye anathandiza Davide asakudziwa kuti Davideyo akuthawa Sauli. Chifukwa cha nsanje, Mfumu Sauli inalamula kuti Ahimeleki ndi banja lake aphedwe. (1 Sam. 22:11, 18, 19) Davide ankadziimba mlandu pa imfa ya anthuwo. Ankaona ngati kuti iye ndi amene anapha wansembe amene anamuthandiza. Kodi inuyo mukanakhala Davide, mukanamva choncho? Kuwonjezera pa zimenezi, Davide ankasowa mtendere chifukwa chakuti Sauli ankapitiriza kumusakasaka.

17 Pasanapite nthawi, mneneri Samueli, amene anadzoza Davide kuti adzakhale mfumu, anamwalira. (1 Sam. 25:1) Izi ziyenera kuti zinawonjezera maganizo a Davide oona kuti alibe womuthandiza. Komabe, Davide anadziwa kuti Yehova ndi amene angamuthandize. Davide sanali ndi mwayi wa utumiki wofanana ndi wa Alevi, koma anali atadzozedwa kuti achite utumiki wina. Iye anali kudzakhala mfumu ya anthu a Mulungu. (1 Sam. 16:1, 13) Choncho Davide ankapemphera kwa Mulungu ndi mtima wake wonse ndipo anapitiriza kumudalira. Nanunso muyenera kuona kuti Yehova ndi cholowa ndiponso chitetezo chanu pamene mukumutumikira mwakhama.

18. Kodi anthu amene takambirana m’nkhani ino anasonyeza bwanji kuti Yehova anali cholowa chawo?

18 Kodi Yehova anakhala bwanji cholowa cha atumiki ake amene takambirana m’nkhaniyi? Iye anawapatsa utumiki wapadera. Iwo ankadalira Mulungu kuti awasamalire pamene ankamutumikira. Alevi ndiponso Aisiraeli a mafuko ena, monga Davide, ankaona Mulungu kuti ndi cholowa chawo. Kodi inunso mungatani kuti Yehova akhale cholowa chanu? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kuti mumve mmene Yehova ankasamalirira ansembe, werengani buku lakuti Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 684.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Yehova anakhala bwanji cholowa cha Alevi?

• Kodi Asafu, Yeremiya ndi Davide anasonyeza bwanji kuti Yehova anali cholowa chawo?

• Kodi chofunika n’chiyani kuti Yehova akhale cholowa chanu?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Alevi sanalandire malo monga cholowa chawo. M’malomwake, Yehova anakhala cholowa chawo chifukwa anali ndi mwayi waukulu womutumikira

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi Yehova anakhala bwanji cholowa cha ansembe ndi Alevi?

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi n’chiyani chinathandiza Asafu kuti azionabe Yehova monga cholowa chake?