Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?

Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?

Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?

“Nthawi zonse muzitsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.”​—AEF. 5:10.

1, 2. (a) Kodi Mawu a Mulungu amasonyeza bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi moyo? (b) Kodi kudziwa kuti nthawi yosangalala ndi “mphatso yochokera kwa Mulungu,” kungatithandize kuchita zinthu m’njira yotani?

M’BAIBULO muli mawu ambiri osonyeza kuti Yehova samangofuna kuti tikhale ndi moyo, koma kuti tizisangalala nawo. Mwachitsanzo, lemba la Masalimo 104:14, 15 limanena kuti Yehova amachititsa “kuti chakudya chituluke m’nthaka, komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu. Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta, komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.” Yehova ndi amene amatipatsa chakudya chimene chimatithandiza kuti tizikhala ndi moyo. Amameretsa mbewu kuti tipeze chakudya, mafuta ndi vinyo. Ngakhale kuti vinyo sali m’gulu la zinthu zofunika kwambiri pa moyo, ‘amachititsa mtima kusangalala.’ (Mlal. 9:7; 10:19) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala ndiponso kuti mitima yathu izikhala yodzaza ndi “chimwemwe.”​—Mac. 14:16, 17.

2 Choncho tisamaone ngati talakwitsa ngati nthawi zina timakonza nthawi yosangalala. Mwina timakonza zokaona “mbalame zam’mlengalenga” ndi “maluwa akutchire,” komanso kuchita zinthu zina zimene zimatitsitsimula. (Mat. 6:26, 28; Sal. 8:3, 4) Kukhala ndi moyo wosangalala “ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlal. 3:12, 13) Kudziwa kuti nthawi yosangalala ndi mphatso, kungatithandize kuti tiziigwiritsa ntchito m’njira yosangalatsa amene anaipereka.

Pali Zosangalatsa Zosiyanasiyana Koma M’pofunika Malire

3. N’chifukwa chiyani anthu amasiyanasiyana posankha zosangalatsa?

3 Anthu amene amaona nthawi yosangalala moyenera amadziwa kuti pali zosangalatsa zosiyanasiyana zimene munthu angasankhe. Koma amadziwanso kuti sangathe kuchita zosangalatsa zonse. N’chifukwa chiyani zili choncho? Kuti tiyankhe funso limeneli, kusangalala tikuyerekezere ndi chakudya. Chakudya chimene anthu a m’dziko lina amachikonda, chimakhala chosiyana ndi chimene anthu a m’dziko linanso amakonda. N’chimodzimodzi ndi zosangalatsa. Mkhristu wa m’dziko lina angaone kuti kuchita zinthu zina zake n’kosangalatsa, pomwe Mkhristu wa m’dziko linanso akhoza kuona kuti n’kosasangalatsa. Ngakhale Akhristu okhala m’dera limodzi sangakonde kuchita zosangalatsa zofanana. Zimene wina akhoza kuona ngati n’zosangalatsa (mwina kupita kukacheza kunyumba kwa ena) Mkhristu wina akhoza kuona kuti n’zosasangalatsa. Kapena wina akhoza kuona kuti kupita kokawongola miyendo kwinaku akuona chilengedwe kungakhale kosangalatsa koma wina akhoza kuona kuti n’kotopetsa. Apa mfundo ndi yakuti, chakudya komanso zosangalatsa zilipo zambirimbiri koma anthu amakonda zosiyanasiyana.​—Aroma 14:2-4.

4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kumangochita zosangalatsa zilizonse? Perekani chitsanzo.

4 Ngakhale kuti zosangalatsa zilipo zosiyanasiyana, sizikutanthauza kuti tizingochita chilichonse chomwe chatisangalatsa. Kuti timvetse bwino zimenezi tiyeni tionenso chitsanzo cha chakudya chija. Ngakhale kuti tikhoza kufuna kudya zakudya zosiyanasiyana sitingadye mwadala chakudya choola. Kungakhale kupanda nzeru kudya chakudya chimenechi chifukwa chikhoza kutidwalitsa. Mofanana ndi zimenezi, timakonda zosangalatsa zosiyanasiyana zimene ndi zabwino, koma sitichita zosangalatsa zimene zingaike moyo wathu pa ngozi, zachiwawa kapena za makhalidwe oipa. Kuchita zosangalatsa ngati zimenezi n’kosemphana ndi mfundo za m’Baibulo ndipo kukhoza kutiwononga mwakuthupi komanso mwauzimu. Choncho kuti tichite zosangalatsa zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, tiyenera kudziwiratu pasadakhale ngati zosangalatsa zimene tasankhazo zili zabwino kapena zoipa. (Aef. 5:10) Kodi tingachite bwanji zimenezo?

5. Kodi tingadziwe bwanji ngati zosangalatsa zomwe timakonda zikugwirizana ndi mfundo za Mulungu?

5 Kuti zosangalatsa zikhale zopindulitsa komanso zosangalatsa Yehova, ziyenera kukhala zogwirizana ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu. (Sal. 86:11) Kuti tidziwe ngati zosangalatsa zomwe timakonda zikugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo tiyenera kudzifunsa mafunso atatu. Mafunso ake ndi akuti: Kodi zosangalatsa zimene ndikufuna kuchita n’zotani? Kodi ndizizichita liti? Nanga ndizichita ndi ndani? Tiyeni tikambirane zinthu zimenezi chilichonse pachokhapachokha.

Kodi Zosangalatsazo N’zotani?

6. Kodi tiyenera kupewa zosangalatsa zotani ndipo n’chifukwa chiyani?

6 Tisanayambe kuchita zosangalatsa zimene tasankha, tiyenera kudzifunsa kaye kuti, ‘Kodi zosangalatsa zimene ndikufuna kuchitazo n’zotani?’ Pamene tikufufuza yankho la funso limeneli, ndi bwino kukumbukira kuti pali magulu awiri a zosangalatsa. Gulu loyamba ndi la zinthu zimene tiyenera kukaniratu. Gulu lachiwiri ndi la zinthu zimene tikhoza kusankha kuchita kapena ayi. Tiyeni tikambirane za gulu loyamba. M’dziko loipali, zosangalatsa zambiri zimaphwanya mfundo za m’Baibulo kapena malamulo a Mulungu. (1 Yoh. 5:19) Akhristu oona amakana kwamtuwagalu zosangalatsa zoterezi. Zosangalatsa zimenezi zikuphatikizapo zinthu zankhanza, zamizimu, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, zolaula, zachiwawa kapena zinthu zimene zimalimbikitsa makhalidwe ena oipa. (1 Akor. 6:9, 10; werengani Chivumbulutso 21:8.) Kaya tili pamalo ati, tikakana zosangalatsa zimenezi timasonyeza Yehova kuti ‘tikunyansidwa ndi choipa.’​—Aroma 12:9; 1 Yoh. 1:5, 6.

7, 8. Kodi tingadziwe bwanji kuti zosangalatsa zimene tasankha ndi zabwino kapena zoipa? Perekani chitsanzo.

7 Gulu lachiwiri ndi la zosangalatsa zimene Mawu a Mulungu sanena mwachindunji kuti ndi zoipa. Choncho tisanasankhe zosangalatsa zomwe zili m’gulu limeneli, tiyenera kuona ngati zikugwirizana ndi zimene Yehova amaona kuti ndi zabwino. (Miy. 4:10, 11) Kenako tingasankhe zomwe tikuona kuti zitisiya tili ndi chikumbumtima chabwino. (Agal. 6:5; 1 Tim. 1:19) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Taganizirani izi: Tisanayambe kudya chakudya choti sitinadyepo, timayenera kudziwa kaye zinthu zimene aika mu chakudyacho pokonza. Choncho tisanayambe zosangalatsa zilizonse tiyenera kufufuza kaye kuti n’zotani.​—Aef. 5:17.

8 Mwina mumakonda kuchita masewera olimbitsa thupi. Masewera amenewa amakhala osangalatsa kwambiri. Koma bwanji ngati mumakonda zosangalatsa zina chifukwa chakuti posewera anthu amachita zinthu monga kusonyeza kwambiri mtima wampikisano, amaika moyo wawo pa ngozi, amakonda kuvulazana, amasangalala monyanyira, kapena amasonyeza kuti amakonda kwambiri dziko lawo? Ngati zoterezi n’zimene zimachitika pa masewera amene mumakonda, dziwani kuti zimene mumakonda si zogwirizana ndi mmene Yehova amaganizira komanso si zogwirizana ndi uthenga wa mtendere ndi wachikondi womwe timalalikira kwa ena. (Yes. 61:1; Agal. 5:19-21) Koma ngati zosangalatsazo zili ndi zinthu zabwino ndiponso zogwirizana ndi mfundo za Yehova ndiye kuti zikhoza kukhala zopindulitsa ndiponso zosangalatsa.​—Agal. 5:22, 23; werengani Afilipi 4:8.

Kodi Ndizizichita Liti?

9. Kodi yankho la funso lakuti, ‘Kodi zosangalatsa ndizizichita liti?’ lingatithandize kudziwa chiyani?

9 Funso lachiwiri limene mungadzifunse ndi lakuti, ‘Kodi zosangalatsazo ndizizichita liti? Kodi ndizitenga nthawi yaitali bwanji ndikuchita zosangalatsazo?’ Yankho la funso lakuti, kodi zosangalatsa zimene ndimafuna n’zotani? lingatiuze zimene timaona kuti ndi zovomerezeka ndi zimene timaona kuti n’zosavomerezeka. Koma yankho la funso lakuti kodi zosangalatsa ndizizichita liti? lingatithandize kudziwa zimene timaona kuti n’zofunika pa moyo wathu. Ndiyeno n’chiyani chingatithandize kudziwa kuti zosangalatsa zimene timakonda timaziika pamalo oyenera?

10, 11. Kodi mawu a Yesu a pa Mateyu 6:33 angatithandize bwanji kuona nthawi imene tingathere tikuchita zosangalatsa?

10 Yesu Khristu anauza otsatira ake kuti: ‘Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.’ (Maliko 12:30) Choncho kukonda Yehova kuyenera kukhala chinthu choyamba pa moyo wathu. Timasonyeza zimenezi tikamatsatira malangizo a Yesu akuti: “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mat. 6:33) Kodi mawu a Yesu amenewa, angatithandize bwanji kuika zosangalatsa pamalo oyenera pa moyo wathu? Kodi angatithandize bwanji kudziwa kuchuluka kwa nthawi imene tingatenge tikuchita zosangalatsazo?

11 Onani kuti Yesu akutiuza kuti tiyenera ‘kupitiriza kufunafuna ufumu choyamba.’ Iye sananene kuti pitirizani kufunafuna ufumu wokha.’ N’zoonekeratu kuti Yesu ankadziwa kuti pali zinthu zina zimene timafunafuna pa moyo kuwonjezera pa kufunafuna Ufumu. Ankadziwa kuti tingafunike nyumba, chakudya, zovala, maphunziro, ntchito, zosangalatsa ndi zinthu zina. Komabe, pa zinthu zonse zimene tiyenera kufunafuna, zinthu zaufumu ziyenera kukhala pamalo oyamba. (1 Akor. 7:29-31) Choncho mfundo imeneyi iyenera kutilimbikitsa kuti pochita zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo zosangalatsa, tizikumbukira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi zokhudza ufumu. Ngati tingachite zimenezi, ndiye kuti zosangalatsa zochepa zimene tingapange zikhoza kukhala zothandiza.

12. Kodi mfundo yopezeka pa Luka 14:28 ingagwiritsidwe ntchito bwanji posankha zosangalatsa?

12 Choncho ndi bwino kudziwiratu kuti titaya nthawi yaitali bwanji tikuchita zosangalatsa, tisanayambe kuzichita. (Luka 14:28) Tiyenera kudziwa kuti tiziwononga nthawi yaitali bwanji tikuchita zosangalatsa zimene tikufuna kuchita. Sitiyenera kutha nthawi yambiri tikuchita zosangalatsa mpaka kusowa nthawi yochitira zinthu zofunika kwambiri monga kuphunzira Baibulo patokha, kupanga kulambira kwa pabanja, kupita ku misonkhano kapena kulalikira. (Maliko 8:36) Koma ngati zosangalatsa zimatithandiza kuti tipitirize kuchita zinthu za Ufumu, ndiye kuti tingachite bwino kugwiritsira ntchito nthawi yathu pa zinthu zopindulitsa zimenezo.

Kodi Ndizichita ndi Ndani?

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kusankha mosamala anthu amene tikufuna kukasangalala nawo limodzi?

13 Funso lachitatu limene mungadzifunse ndi lakuti, ‘Kodi zosangalatsazo ndizichita ndi ndani?’ Ndi bwino kudzifunsa funso limeneli. Chifukwa chiyani? Chifukwa zosangalatsa kuti zikhale zabwino kapena ayi, zimadalira anthu amene tikuchita nawo zosangalatsazo. Chakudya chimakoma ngati munthu akudya ndi anzake apamtima. Zosangalatsa zimakomanso ngati munthu akuzichita ndi mabwenzi ake abwino. Choncho, n’zomveka kuti ambiri a ife, makamaka achinyamata, timakonda kuchita zinthu zosangalatsa tili limodzi ndi anthu ena. Komabe kuti zosangalatsa zikhale zopindulitsa, ndi bwino kudziwiratu anthu amene tikufuna kuchita nawo zosangalatsazo komanso anthu amene tifunikira kuwapewa.​—2 Mbiri 19:2; werengani Miyambo 13:20; Yak. 4:4.

14, 15. (a) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yosankha mabwenzi abwino? (b) Kodi tingadzifunse mafunso ati okhudza mabwenzi athu?

14 Zingakhale zothandiza kwambiri kutsatira chitsanzo cha Yesu pa nkhani yosankha mabwenzi. Yesu wakhala akukonda anthu kuchokera pamene dziko linalengedwa. (Miy. 8:31) Pamene anali padziko lapansi, iye ankachita zinthu zosonyeza kuti amakonda anthu onse. (Mat. 15:29-37) Komabe, Yesu ankadziwa kuti pali kusiyana pakati pokhala munthu waubwenzi ndi kukhala bwenzi lapamtima. Ngakhale kuti anali munthu waubwenzi kwa anthu onse, iye sanali bwenzi lapamtima la anthu onse. Pamene anali kulankhula kwa atumwi ake 11 okhulupirika, iye anati: “Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.” (Yoh. 15:14; 13:27, 30; onaninso Yoh. 13:27, 30.) Anthu amene Yesu ankasangalala nawo monga mabwenzi ake anali okhawo amene ankamutsatira ndiponso kutumikira Yehova.

15 Choncho, pamene mukufuna kusankha winawake kukhala bwenzi lanu lapamtima, ndi bwino kukumbukira mawu amene Yesu ananenawa. Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolankhula komanso zochita za munthu ameneyu zimasonyeza kuti amatsatira malamulo a Yehova ndi Yesu? Kodi amatsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo zomwe inenso ndimatsatira? Kodi ndikasankha kuti akhale mnzanga n’kumachita naye zosangalatsa, adzandithandiza kuti ndiziika zinthu zaufumu poyamba m’moyo wanga? Kodi adzandithandiza kukhala mtumiki wa Yehova wokhulupirika?’ Ngati mukutsimikizira kuti yankho lanu pa mafunso amenewa ndi loti inde, ndiye kuti mwapeza bwenzi labwino lomwe mukhoza kuchitira limodzi zosangalatsa.​—Werengani Masalimo 119:63; 2 Akor. 6:14; 2 Tim. 2:22.

Kodi Zosangalatsa Zathu Ndi Zoyenera?

16. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati pa nkhani ya zosangalatsa zomwe timakonda?

16 Takambirana zinthu zitatu zokhudza zosangalatsa. Taona kuti tiyenera kudziwa zosangalatsazo kuti n’zotani, nthawi imene timathera tikuzichita ndiponso amene timachita nawo. Kuti zosangalatsa zathu zikhale zopindulitsa, ziyenera kukhala zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Choncho, tisanachite zosangalatsa zilizonse tiyenera kuziona kaye ngati zili zabwino. Tikamafuna kudziwa kuti zosangalatsazo n’zotani, tingadzifunse kuti, ‘Kodi zosangalatsazo zili ndi zinthu zabwino kapena zoipa?’ (Miy. 4:20-27) Tikamafuna kudziwa kuti zosangalatsazo ndizizichita liti, tingadzifunse kuti, ‘Kodi zizidzanditengera nthawi yaitali bwanji? Kodi nthawi yomwe ndidzathere ndikuchita zinthu zimenezi idzakhala yopindulitsa?’ (1 Tim. 4:8) Tikamafuna kudziwa zoti ndizichita ndi ndani, tingadzifunse kuti, ‘Kodi anthu amene ndizidzachita nawo zosangalatsazo ndi abwino kapena oipa?’​—Mlal. 9:18; 1 Akor. 15:33.

17, 18. (a) Kodi tingadziwe bwanji ngati zosangalatsa zathu zili zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo kapena ayi? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza kuchita chiyani posankha zosangalatsa?

17 Ngati zosangalatsa zimene mumakonda sizikugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo zimene takambiranazi, ndiye kuti zosangalatsa zimenezo si zoyenera. Koma ngati tikutsimikizira kuti zosangalatsa zathu zikugwirizana ndi mfundo zitatu za m’Baibulo zimene takambiranazi, ndiye kuti n’zolemekeza Yehova komanso n’zopindulitsa.​—Sal. 119:33-35.

18 Choncho pa nkhani ya zosangalatsa, tiyeni tiyesetse kuchita zosangalatsa zabwino, pa nthawi yabwino ndiponso ndi anthu abwino. Tiyeni tikhale otsimikiza mtima kutsatira malangizo a m’Baibulo awa: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”​—1 Akor. 10:31.

Kodi Mungafotokoze?

Pa nkhani yokhudza zosangalatsa, kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo zopezeka m’Malemba otsatirawa:

Afilipi 4:8?

Mateyu 6:33?

Miyambo 13:20?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

N’zotani?

[Chithunzi patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Liti?

[Chithunzi patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ndi ndani?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo cha Yesu posankha mabwenzi ndiponso zosangalatsa?