Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutumikira Yehova Kwandibweretsera Chimwemwe

Kutumikira Yehova Kwandibweretsera Chimwemwe

Kutumikira Yehova Kwandibweretsera Chimwemwe

Yosimbidwa ndi Fred Rusk

Ndidakali wamng’ono ndinazindikira kuti mawu a Davide a pa Salimo 27:10 ndi oona. Lembali limati “Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya, Yehova adzanditenga.” Yembekezerani ndikuuzeni mmene zinakhalira.

N DINAKULIRA ku Georgia, m’dziko la United States ndipo ndinkakhala kumunda wa thonje wa agogo anga. Pa nthawi imeneyi chuma cha dziko chinali chitalowa pansi kwambiri m’ma 1930. Mayi anga anamwalira pa nthawi imene ankabereka mng’ono wanga. Mng’ono wangayonso anamwalira pa nthawi yomweyo. Bambo anga anasokonezeka kwambiri ndi imfayi ndipo anasamuka kupita kumzinda wina wakutali kukafufuza ntchito n’kundisiya ndi agogo anga aamuna. Pa nthawiyo agogo anga aakazi anali atamwaliranso. Kenako ankafuna kuti ndipite ndizikakhala nawo kumzindawo koma zinalephereka.

Azichemwali a bambo anga ndi amene ankasamalira pakhomo. Ngakhale kuti agogo angawo sanali m’chipembedzo chilichonse, ana awo aakaziwa ankalimbikira kupita kutchalitchi cha Baptist. Chifukwa choti ndinkaopa kumenyedwa, ndinakakamizika kuti ndizipita kutchalitchi Lamlungu lililonse. Kuyambira ndili wamng’ono sindinkakonda zachipembedzo. Chomwe ndinkakonda ndi kuphunzira ndi kuchita masewera basi.

Tsiku Limene Linasintha Moyo Wanga

Tsiku lina masana m’chaka cha 1941 ndili ndi zaka 15, bambo wina wachikulire anabwera kwathu ndi mkazi wake. Anthu anandiuza kuti iwo ndi “amalume anga” koma kwenikweni anali achimwene a agogo anga aakazi. Dzina lawo ndi a Talmadge Rusk. Ndinali ndisanamvepo za iwo koma ndinauzidwa kuti iwo ndi akazi awo ndi a Mboni za Yehova. Zimene iwo anafotokoza zokhudza cholinga cha Mulungu choti anthu akhale padziko lapansi kosatha, zinali zosiyana kwambiri ndi zimene ndinamva kutchalitchi. Pafupifupi aliyense m’banja lathu anatsutsa zimene ankanena moti anawaletsa kubweranso kunyumba kwathu. Komabe azakhali anga a Mary, omwe ndi ine timangosiyana zaka zitatu, analandira Baibulo ndiponso mabuku ena ofotokoza Baibulo.

Azakhaliwa anakhulupirira kuti apeza choonadi cha m’Baibulo ndipo anabatizidwa mu 1942 n’kukhala a Mboni za Yehova. Iwo anakumana ndi zimene Yesu ananena zoti: “Adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.” (Mat. 10:34-36) Iwo ankatsutsidwa modetsa nkhawa ndi achibale athu. Azakhali ena aakulu omwe ankachita nawo ndale m’derali anakawaneneza a Talmage kwa meya ndipo anamangidwa. Iwo anaimbidwa mlandu wofalitsa nkhani popanda chilolezo.

M’nyuzipepala ina munalembedwa nkhaniyi ndipo inanena kuti meyayo, yemwenso anali woweruza anauza anthu a mumzindawo kuti: “Mabuku amene munthu uyu akufalitsa . . . ndi oopsa kwambiri.” Amalume angawa anawina mlanduwu pambuyo pochita apilo koma anali atakhala m’ndende masiku 10.

Mmene Azakhali Anandithandizira

Azakhali anga a Mary ankandiuza zinthu zina zimene ankakhulupirira komanso anayamba kulalikira kwa anthu ena oyandikana nawo. Tsiku lina ndinapita nawo kwa bambo wina yemwe ankaphunzira nawo Baibulo komanso yemwe anali atalandira buku lomwe linkatchedwa The New World. * Mkazi wake anatiuza kuti mwamuna wake anali atachezera usiku wonse akuliwerenga. Ngakhale kuti pa nthawiyo sindinkafuna kukhala m’chipembedzo chilichonse, ndinkakhulupirira kwambiri zimene ndinkaphunzira. Ndinatsimikizira kuti Mboni za Yehova ndi anthu a Mulungu osati chifukwa cha zimene ndinkaphunzira koma mmene anthu ankazunzira Mbonizo.

Mwachitsanzo, tsiku lina ndikuchoka kokapalira munda wa tomato, Ine ndi a Mary tinapeza kuti azakhali anga aakulu atatu awotcha mabuku a azakhali angawo, kuphatikizapo galamafoni ndi nkhani zochokera m’Baibulo zomwe zinajambulidwamo. Zimenezi zinandikwiyitsa koma mmodzi wa azakhali anga omwe anawotcha katunduyo ananena kuti: “Uzatithokoza m’tsogolomu chifukwa cha zimene tachitazi.”

A Mary anauzidwa kuti achoke kunyumba kwathu mu 1943 chifukwa chakuti anakana kusiya chikhulupiriro chawo komanso kusiya kulalikira kwa anthu oyandikana nawo. Komabe pa nthawi imeneyi ndinasangalala kudziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, ndiponso kuti iye ndi wachikondi, wachifundo komanso saotcha athu m’moto wa helo. Ndinaphunziranso kuti Yehova ali ndi gulu lachikondi ngakhale kuti ndinali ndisanapite ku msonkhano uliwonse.

Tsiku lina ndikutchetcha ndinangoona anthu awiri akufika pa galimoto n’kundifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe Fred?’ Nditadziwa kuti anali a Mboni za Yehova ndinawauza kuti: “Bwanji ndikwere nawo galimotoyo tipite pa malo ena ake abwino kuti tikakambirane.” A Mary ndi amene anakonza zoti anthuwa andipeze. M’modzi mwa anthuwo anali Shield Toutjian yemwe anali mtumiki woyendayenda. Iye anandilimbikitsa kwambiri n’kundipatsanso malangizo auzimu omwe anali a pa nthawi yake. Ndiyeno achibale anga aja anayambanso kuzunza ineyo chifukwa choikira kumbuyo mfundo zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira.

A Mary ankakhala ku Virginia ndipo anandilembera kalata yonena kuti ngati ndikufunitsitsa kutumikira Yehova, ndipite ndizikakhala nawo. Ndinangoona ngati ndinyamuke nthawi yomweyo. Ndiyeno Lachisanu madzulo mu October 1943 ndinatenga katundu wanga n’kumuika m’bokosi n’kukamangirira mumtengo winawake kutali ndi kwathu. Ndiyeno Loweruka ndinakatsitsa bokosilo n’kuzemba kupita kukakwera galimoto yopita m’tauni. Ndikupita kumzinda wa Roanoke ndinapeza a Mary ali kunyumba ya a Edna Fowlkes.

Kukula Mwauzimu, Kubatizidwa Kenako Kutumikira pa Beteli

Edna anali mlongo wodzozedwa wachifundo kwambiri ndipo tingamuyerekezere ndi Lidiya. Mlongoyu ankachita lendi nyumba ina ndipo anaitana a Mary kuti azikakhala nawo. Ankakhalanso ndi alamu ake omwe anali ndi ana aakazi awiri. Anawo anali Gladys ndi Grace Gregory omwe anadzakhala amishonale. Panopa Gladys ali ndi zaka za m’ma 90 ndipo akutumikira pa nthambi ya ku Japan.

Ndili kunyumba ya Edna, ndinkapita ku misonkhano mokhazikika ndipo anandiphunzitsa kulalikira. Popeza ndinali ndi ufulu wophunzira Mawu a Mulungu komanso kupezeka pa misonkhano ya mpingo ndinayamba kufunitsitsa kukula mwauzimu. Pa June 14, 1944 ndinabatizidwa. A Mary limodzi ndi Gladys komanso Grace anayamba upainiya ndipo atapemphedwa kuti akatumikire kumpoto kwa Virginia, anavomera. Iwo anathandiza kwambiri kukhazikitsa mpingo wa ku Leesburg. Kumayambiriro kwa 1946, ndinayamba kuchita upainiya pafupi ndi kumene alongowa ankatumikira. Pa nyengo imeneyi tinapitira limodzi ku msonkhano wa mayiko ku Cleveland, Ohio womwe unachitika pa August 4 mpaka 11.

Pa msonkhano umenewu, M’bale Nathan Knorr amene ankayang’anira ntchito ya gulu la Mulungu ananena kuti pakukonzedwa zoti awonjezere nyumba za Beteli ya ku Brooklyn. Ina mwa ntchitoyi inali yomanga nyumba yatsopano yogona ndiponso kuwonjezera nyumba yosindikizira mabuku. Panafunika achinyamata ambiri kuti athandize pa ntchitoyi. Ndinaganiza kuti umenewu ndi mwayi wanga woti nditumikire Yehova. Ndinalemba kalata yofunsira utumikiwu ndipo patangopita miyezi yochepa, ndinalandira kalata pa December 1, 1946, yondiitana kuti ndipite ku Beteli.

Patapita chaka chimodzi m’bale wina dzina lake Max Larson, amene ankayang’anira ntchito yosindikiza mabuku anabwera pa desiki yanga m’dipatimenti yotumiza ndi kulandira makalata. Iye anandiuza kuti abale asankha zoti ndizikatumikira m’dipatimenti ya utumiki. Pa utumiki umenewu, ndinaphunzira mmene ndingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo ndiponso mmene gulu la Mulungu limagwirira ntchito. Izi zinachitika kwenikweni pamene ndinkagwira ntchitoyi ndi woyang’anira m’dipatimentiyi dzina lake T. J. (Bud) Sullivan.

Bambo anga ankabwera kudzandiona ku Beteli. Pamene anali achikulire iwo anayamba kukonda zachipembedzo. Atabwera kudzandiona ulendo womaliza mu 1965, ananena kuti: “Ukhoza kubwera kumadzandiona koma ine sindidzabweranso kudzakuona.” Ndinapitadi kukawaona maulendo angapo asanamwalire. Bambowo ankaganiza kuti adzapita kumwamba. Koma ine ndikuona kuti Yehova akuwakumbukira ndipo mwina adzawaukitsa kuti akhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi osati kumwamba kumene ankaganiza kuti adzapita.

Misonkhano Ina Komanso Ntchito Yomanga Yosaiwalika

Misonkhano ikuluikulu inkandithandiza kwambiri kuti mipingo ikule komanso kuti ineyo ndikule mwauzimu. Izi zinkatero m’ma 1950, makamaka ikachitikira ku Yankee Stadium mumzinda wa New York. Umodzi wa misonkhano imeneyi unachitika mu 1958, ku Yankee Stadium ndi ku Polo Grounds pa nthawi yofanana, ndipo kunasonkhana anthu okwana 253,922 ochokera m’mayiko 123. Pali chinthu chimodzi chimene chinachitika pa msonkhanowu chomwe sindiiwala. Ndikuthandizira mu ofesi yoyang’anira msonkhanowu, M’bale Knorr anabwera akufulumira kwambiri n’kunena kuti: “Fred, ndinaiwala kupezeratu m’bale woti akakambe nkhani kwa apainiya amene asonkhana muholo yodyerayo. Tathamanga ukawalankhule. Ungopita ukakambe nkhani yabwino kwambiri, zikakhala mfundo zake uziziganizira munjira popita muholoyo, wamva?” Ndinapemphera kangapo uku ndikuthamangira kuholoyo ndipo ndinakafika ndikupumira m’mwamba.

Pamene mipingo inayamba kuchuluka ku New York City m’ma 1950 ndi 1960, maholo amene tinkachita lendi n’kumawagwiritsa ntchito ngati Nyumba za Ufumu anayamba kuchepa. Choncho kuyambira mu 1970 mpaka mu 1990, nyumba zitatu zinagulidwa ku Manhattan n’kuzikonza kuti zikhale malo olambirira. Ndinasankhidwa kukhala tcheyamani wa makomiti oyang’anira ntchito imeneyi ndipo ndikukumbukira mmene Yehova anadalitsira mipingo pa ntchitoyi. Ndalama zinapezeka ndipo ntchito inagwiridwa bwino kwambiri moti panopa nyumba zimenezi zikugwirabe ntchito monga malo olambirira.

Zinthu Zina Zimene Zinasintha pa Moyo Wanga

Tsiku lina mu 1957 ndikupita kukagwira ntchito ndinadutsa pamalo ena oimika magalimoto pakati pa Nyumba za Beteli ndi nyumba zosindikizira mabuku. Ndiyeno mvula inayamba kugwa. Kenako ndinaona kamtsikana kokongola kwambiri kamene kanali katangobwera kumene kudzatumikira pa Beteli kakuyenda kutsogolo kwanga. Kanalibe ambulera ndiye tinafunditsana ambulera wangayo. Apa m’pamene tinadziwana ndi Marjorie ndipo tinakwatirana mu 1960. Kuyambira nthawi imene tinakwatiranayi takhala tikutumikira Yehova limodzi kwina kulikonse kaya pamavuto kapena pamtendere. Mu September 2010, tinakwanitsa zaka 50 tili m’banja.

Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene tinakwatirana, M’bale Knorr anandiuza kuti abale asankha zoti ndikakhale mlangizi ku Sukulu ya Giliyadi. Uwu unali mwayi waukulu kwambiri. Kuyambira mu 1961 kufika mu 1965 kunali makalasi 5 otenga nthawi yaitali ophunzitsa abale a panthambi kuti azitha kuyendetsa bwino ntchito za panthambipo. Chakumapeto kwa 1965, anachepetsa nthawi ya makalasiwa kufikanso pa miyezi 5 ndipo tinayambanso kuphunzitsa amishonale.

Mu 1972, ndinasinthidwa kuchoka ku Sukulu ya Giliyadi kupita ku Dipatimenti Yoyankha Makalata ndipo ndinali woyang’anira m’dipatimentiyi. Kufufuza ndi kuyankha mafunso komanso nkhani zina zovuta kwandithandiza kumvetsa bwino ziphunzitso za m’Mawu a Mulungu komanso mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zapamwamba za Mulungu wathu pothandiza ena.

Mu 1987, ndinasinthidwanso kupita ku Dipatimenti Yopereka Chidziwitso cha Zachipatala yomwe inali itangoyamba kumene. Panakonzedwa maphunziro a akulu amene anali m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala. Maphunzirowa anali othandiza akuluwo kuti azikambirana bwino ndi ogwira ntchito zothandiza anthu ovutika, madokotala ndiponso oweruza n’cholinga choti amvetse mfundo za m’Malemba zimene timakhulupirira pa nkhani ya magazi. Vuto lalikulu linali lakuti madokotala ambiri ankangopereka magazi kwa ana popanda chilolezo cha makolo ndipo nthawi zambiri ankangotenga chilolezo kukhoti.

Madokotala ambiri akauzidwa za njira zina zachipatala zosagwiritsa ntchito magazi ankanena kuti njira zimenezo sizipezeka kapena ankanena kuti n’zodula kwambiri. Dokotala wina wopanga opaleshoni atayankha choncho ndinamuuza kuti, “Tatambasulani mkono wanu.” Atatambasula, ndinamuuza kuti, “Chomwe mwagwiracho n’chothandiza kwambiri kuti mupange opaleshoni popanda kuthira magazi.” Zimene ndinamuuzazi zinamuthandiza kudziwa kuti kugwiritsira ntchito bwino mpeni wochitira opaleshoni kumathandiza kuti magazi ambiri asatayike.

Kwa zaka 20 zapitazi, Yehova wadalitsa kwambiri khama limene abale achita pokambirana ndi madokotala komanso oweruza. Atayamba kumvetsa zimene timakhulupirira anthu amenewa anasintha mmene amaonera Mboni za Yehova. Iwo anadziwa kuti akatswiri a zachipatala anatulukira kuti njira zopangira opaleshoni popanda kuthira magazi n’zothandiza. Anadziwanso kuti pali madokotala ambiri komanso zipatala kumene odwala angatumizidwe kuti akalandire chithandizo choterechi.

Kuyambira mu 1996, ine ndi Marjorie takhala tikutumikira ku Watchtower Educational Center ku Patterson, mu mzinda wa New York. Malo amenewa ali pamtunda wa makilomita 110 kumpoto kwa Brooklyn. Ndinatumikira kwa nthawi yochepa mu Dipatimenti ya Utumiki ndipo kenako ndinkaphunzitsa abale ochokera m’maofesi a Nthambi komanso oyang’anira oyendayenda. Pa zaka 12 zapitazi, ndakhala ndikutumikiranso monga woyang’anira mu Dipatimenti Yoyankha Makalata imene inasamutsidwa kuchoka ku Brooklyn kupita ku Patterson.

Mavuto Aukalamba

Pamene ndafika zaka za m’ma 80, ntchito zina za pa Beteli zikundivuta kwabasi. Ndakhala ndikudwala khansa kwa zaka zoposa 10. Ndimaona kuti ndili ngati Hezekiya amene Yehova anatalikitsa moyo wake. (Yes. 38:5) Mkazi wanga amavutikanso ndi matenda a Alzheimer. Marjorie wakhala akutumikira Yehova mwachangu, kulangiza achinyamata komanso kundithandiza mokhulupirika kwambiri. Nthawi zonse ankakonda kuphunzira Baibulo ndiponso ankaphunzitsa bwino Baibulo. Pali anthu ambiri amene wawaphunzitsa choonadi ndipo omwe ndi anzathu mpaka pano.

Azakhali anga a Mary anamwalira mu March 2010, ali ndi zaka 87. Iwo anali katswiri pophunzitsa Mawu a Mulungu ndipo anathandiza anthu ena kuti ayambe kulambira Mulungu woona. Anatha zaka zambiri akuchita utumiki wa nthawi zonse. Ndimayamikira azakhali anga chifukwa chondiphunzitsa Mawu a Mulungu komanso kundithandiza kukhala mtumiki wa Mulungu wathu wachikondi Yehova ngati mmene iwo analili. A Mary anaikidwa pamodzi ndi amuna awo omwe ankatumikira monga m’mishonale m’dziko la Israel. Sindikukayikira kuti Yehova akuwakumbukira ndipo adzawaukitsa.

Ndikaganizira zaka 67 zimene ndakhala ndikutumikira Yehova, ndimayamikira kwambiri madalitso amene ndapeza. Kuchita chifuniro cha Yehova kwandibweretsera chimwemwe. Popeza ndimakhulupirira kuti Yehova ndi wokoma mtima, ndikuyembekezera zimene Mwana wake analonjeza zakuti: “Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kwambiri kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.”​Mat. 19:29.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Lofalitsidwa mu 1942 koma panopa linasiya kusindikizidwa.

[Chithunzi patsamba 19]

Mu 1928 ndili kufamu ya agogo anga ku Georgia m’dziko la United States.

[Chithunzi patsamba 19]

Azakhali anga a Mary ndi a Talmadge

[Chithunzi patsamba 20]

Azakhali anga a Mary ali ndi Gladys komanso Grace

[Chithunzi patsamba 20]

Pa ubatizo wanga pa June 14, 1944

[Chithunzi patsamba 20]

Ndili mu Dipatimenti ya Utumiki

[Chithunzi patsamba 21]

Ndili ndi azakhali anga pa msonkhano wa mayiko ku Yankee Stadium mu 1958

[Chithunzi patsamba 21]

Ndili ndi Marjorie pa tsiku la ukwati wathu

[Chithunzi patsamba 21]

Tili limodzi mu 2008