Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Malangizo Anzeru kwa Anthu Amene Sali Pabanja Ndiponso Amene Ali Pabanja

Malangizo Anzeru kwa Anthu Amene Sali Pabanja Ndiponso Amene Ali Pabanja

Malangizo Anzeru kwa Anthu Amene Sali Pabanja Ndiponso Amene Ali Pabanja

‘Ndikunena zimenezi kuti ndikulimbikitseni kuchita choyenera ndiponso kutumikira Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa.’​—1 AKOR. 7:35.

1, 2. N’chifukwa chiyani munthu afunikira kupeza malangizo a m’Baibulo othandiza pamene sali pabanja komanso pamene walowa m’banja?

KUCHITA zinthu ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzathu ndi chimodzi mwa zinthu zimene nthawi zina zimatichititsa kuti tikhale osangalala kwambiri. Koma nthawi zina kumachititsanso kuti tikhale okhumudwa kapena kuda nkhawa pa moyo wathu. Popeza timakumana ndi zoterezi tiyenera kupempha Mulungu kuti azititsogolera. Pali zifukwa zambiri zochititsa kuti tizifuna kuti iye azititsogolera. Mwachitsanzo, Mkhristu amene akuona kuti akhoza kukhala bwinobwino popanda kukwatira kapena kukwatiwa, akhoza kuganiza kuti achibale ake kapena anzake akumukakamiza kuti alowe m’banja. Komanso pali anthu ena amene amafuna kulowa m’banja koma sakupeza munthu wowayenera. Ena amafuna malangizo owathandiza kuti akhale mwamuna kapena mkazi wotha kusamalira bwino banja lake. Komanso Akhristu omwe ali pabanja ndi omwe sali pabanja amayesedwa kuti achite chiwerewere.

2 Kutsatira malangizo a Mulungu kumathandiza kuti tikhale osangalala. Kumathandizanso kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu. M’chaputala 7 cha kalata yake yoyamba yopita kwa Akorinto, Paulo anapereka malangizo kwa anthu okwatira ndi osakwatira. Iye ankafuna kulimbikitsa anthu “kuchita choyenera ndiponso kutumikira Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa.” (1 Akor. 7:35) Pamene mukuwerenga malangizo pa nkhani yofunikayi, muyenera kudziwa kuti kaya muli pabanja kapena ayi, mukhoza kugwiritsa ntchito mpata umenewu kutumikira Yehova.

Nkhani Yofunika Kwambiri Imene Aliyense Ayenera Kusankha Payekha

3, 4. (a) N’chiyani chimene chingachitike ngati mabwenzi kapena achibale akudera nkhawa kwambiri za munthu wina amene sanakwatire kapena kukwatiwa? (b) Kodi malangizo a Paulo angathandize bwanji munthu kukhala ndi maganizo oyenera okhudza banja?

3 Mofanana ndi Ayuda akale, anthu ambiri masiku ano amaona kuti ukwati ndi chinthu chofunika kwambiri. Mnyamata kapena mtsikana akapitirira msinkhu winawake asanalowe m’banja, anzake kapena achibale ake ena amayamba kumudera nkhawa ndipo amayamba kumupatsa malangizo. Pocheza naye, angamamulimbikitse kuti ayesetse kupeza mwamuna kapena mkazi womanga naye banja. Iwo angayambe kumufotokozera za mwamuna kapena mkazi amene akuona kuti angamuyenerere. Nthawi zina, ena mochenjera angakonze zoti anthu awiri amene sali pabanja akumane. Koma zoterezi zikachitika, zotsatira zake zimakhala zochititsa manyazi, zosokoneza ubwenzi ndiponso zopweteketsa mtima.

4 Paulo sanakakamize anthu kulowa kapena kusalowa m’banja. (1 Akor. 7:7) Iye ankatumikira Yehova bwinobwino opanda mkazi koma sankanyoza anthu ena amene ankafuna kukwatira kapena kukwatiwa. Masiku anonso Mkhristu aliyense ali ndi ufulu wosankha kukwatira kapena kusakwatira. Anthu ena sayenera kuumiriza anzawo kuchita zosiyana ndi zimene akufuna.

Gwiritsani Bwino Ntchito Nthawi Imene Simuli Pabanja

5, 6. N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti kukhala osakwatira ndi kwabwino?

5 Chochititsa chidwi ndi mawu a Paulo kwa Akorinto n’chakuti anafotokoza ubwino wa kusakwatira kapena kusakwatiwa. (Werengani 1 Akorinto 7:8.) Ngakhale kuti iye sanakwatire, sankadziona kuti ndi wapamwamba poyerekezera ndi anthu okwatira. Iye sankachita zinthu ngati mmene amachitira atsogoleri a matchalitchi achikhristu amene sakwatira. M’malomwake, mtumwiyu anafotokoza zinthu zabwino zimene atumiki osakwatira amasangalala nazo. Kodi kusakwatira kuli ndi ubwino wotani?

6 Mkhristu amene sali pabanja savutika kuchita utumiki winawake m’gulu la Yehova umene anthu apabanja sangakwanitse kuchita. Paulo anali ndi mwayi wokhala ‘mtumwi wotumidwa kupita kwa mitundu ina.’ (Aroma 11:13) Werengani Machitidwe chaputala 13 mpaka 20 kuti muone zimene iye ndi amishonale anzake ankachita polalikira m’madera atsopano komanso kukhazikitsa mipingo yatsopano m’malo osiyanasiyana. Pa utumiki wake, Paulo anapirira mavuto osiyanasiyana moti ndi anthu ochepa kwambiri masiku ano amene angakumane ndi mavuto oterowo. (2 Akor. 11:23-27, 32, 33) Koma chifukwa chakuti Paulo ankathandiza ena kukhala otsatira a Yesu, mavutowo sankamudetsa nkhawa. (1 Ates. 1:2-7, 9; 2:19) Kodi iye akanakhala kuti ndi wokwatira akanatha kuchita zonsezi? N’zokayikitsa.

7. Perekani chitsanzo cha Mboni zimene sizili pabanja zomwe zagwiritsira ntchito mpata umenewu kupititsa patsogolo ntchito yolalikira.

7 Akhristu ambiri amene sali pabanja, amagwiritsa ntchito mpata umenewu kupititsa patsogolo zinthu zaufumu. Sara ndi Limbania ndi mbeta ndipo ndi apainiya ku Bolivia. Iwo anasamukira kumudzi wina kumene anthu sanalalikidwepo kwa zaka zambiri. Kumudzi umenewo kulibe magetsi koma zimenezi siziwadetsa nkhawa. Iwo anati: “Popeza kuti kulibe mawailesi kapena ma TV, anthu sasokonezedwa ndi zinthu ngati zimenezi choncho nthawi zambiri amakhala akuwerenga.” Anthu ena m’mudzimo ankawasonyeza mabuku ena ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova amene ankawerenga koma oti anasiya kalekale kusindikizidwa. Pafupifupi nyumba iliyonse, anthu ankachita chidwi, choncho alongowo anavutika kufikira nyumba zonse m’gawolo. Mayi wina wachikulire anawauza kuti: “Ee! Mpaka inu a Mboni za Yehova mwafika kuno? Mapeto ayandikira basi.” Posapita nthawi anthu ena anayamba kumapezeka pamisonkhano ya mpingo.

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti ndi bwino kutumikira Mulungu pa nthawi imene munthu sanakwatire kapena kukwatiwa? (b) Kodi Akhristu osakwatira amakhala ndi mwayi wochita chiyani?

8 N’zoona kuti Akhristu okwatira amasangalalanso akamalalikira uthenga wabwino m’madera amene moyo wake umakhala wovuta. Komabe utumiki wina umene apainiya osakwatira amachita umakhala wovuta kwa okwatira kapena amene ali ndi ana. Pamene Paulo ankalembera mipingo makalata, ankadziwa kuti pali ntchito yambiri yofunika kugwira polalikira uthenga wabwino. Iye ankafuna kuti anthu onse azisangalala ngati mmene iye ankachitira. N’chifukwa chake Paulo ananena za ubwino wotumikira Yehova uli wosakwatira.

9 Mlongo wina wosakwatiwa ku United States analemba kuti: “Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu wosakwatira sangakhale wosangalala. Koma ine ndazindikira kuti munthu amakhala wosangalala kwambiri ngati ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ngakhale kuti munthu wosakwatira amakumana ndi mavuto ena, amakhala ndi mwayi wamtengo wapatali.” Ponena za kukhala wosangalala, mlongoyu analemba kuti: “Kukhala wosakwatiwa sikuletsa munthu kukhala wosangalala. M’malomwake, ndi nthawi imene munthu amasangalala kwambiri. Ndikudziwa kuti Yehova amakonda aliyense kaya akhale wokwatira kapena wosakwatira.” Panopa mlongoyu akutumikira kudera lina kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Ngati ndinu wosakwatira kapena wosakwatiwa kodi mungagwiritse ntchito mpata umene muli nawo kuti muwonjezere nthawi yoti muziphunzitsa anthu choonadi? Nanunso mudzaona kuti kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa ndi mphatso ya mtengo wapatali yochokera kwa Yehova.

Amene Akufuna Kukwatira Kapena Kukwatiwa

10, 11. Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu amene akufuna kukwatira koma sanapezebe munthu wowayenera?

10 Pambuyo pokhala osakwatira kwa nthawi ndithu, atumiki a Yehova ambiri amasankha kupeza mwamuna kapena mkazi woti akwatirane naye. Chifukwa chakuti amadziwa kufunika kokhala ndi malangizo, iwo amapempha Yehova kuti awathandize kupeza munthu wowayenera.​—Werengani 1 Akorinto 7:36.

11 Ngati mumafuna kukwatira kapena kukwatiwa ndi munthu amene amafuna kutumikira Yehova ndi mtima wonse muyenera kutchula zimenezi m’mapemphero anu. (Afil. 4:6, 7) Kaya mudikira kwa nthawi yaitali bwanji, simuyenera kutaya mtima. Muzidalira Mulungu wathu wachikondi ndipo iye adzakuthandizani mogwirizana ndi zimene mumafuna.​—Aheb. 13:6.

12. N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kuganizira mozama ngati munthu wina wamufunsira kuti amange naye banja?

12 Mkhristu amene sali pabanja koma amene akufuna kukhala pabanja angafunsiridwe ndi munthu amene ndi wofooka mwauzimu kapena wosakhulupirira. Ngati zimenezi zingakuchitikireni, kumbukirani kuti mavuto amene mungadzakumane nawo chifukwa chosasankha bwino adzakhala opweteka koopsa kuposa kusungulumwa kumene mumamva pamene simunakwatire kapena kukwatiwa. Munthu akakwatira ayenera kudziwa kuti adzakhala ndi mnzakeyo mpaka kalekale, pamavuto kapena pa mtendere. (1 Akor. 7:27) Musalole kungokwatira kapena kukwatiwa ndi aliyense chifukwa choganiza kuti nthawi ikupita. Mukatero mukhoza kudzanong’oneza bondo m’tsogolo.​—Werengani 1 Akorinto 7:39.

Konzekerani Zimene Mungakumane Nazo M’banja

13-15. Kodi ndi zinthu zofunika kwambiri ziti zimene anthu omwe akufuna kukwatirana ayenera kukambirana kaye adakali pachibwenzi?

13 Ngakhale kuti Paulo ananena kuti ndi bwino kutumikira Yehova usanakwatire kapena kukwatiwa, iye sankanyoza anthu amene akufuna kukhala pabanja. M’malomwake, malangizo ake ouziridwa amathandiza anthu okwatirana kuti azithana ndi mavuto amene amakumana nawo ndiponso kuti banja lawo lisasokonezeke.

14 Anthu ena omwe akufuna kukwatirana angafunike kusintha maganizo awo pa zimene akuyembekezera m’banja. Pamene ali pa chibwenzi angayambe kuganiza kuti iwo amakondana kuposa anthu ena onse ndiponso kuti akakwatirana sadzakhala ndi mavuto. Iwo amalowa m’banja atatengeka ndi chikondi ndipo amakhulupirira kuti palibe chilichonse chimene chingasokoneze banja lawo losangalala. Kuganiza choncho n’kudzinamiza. Chikondi chomwe anthu amene alowa m’banja amasonyezana n’chosangalatsa kwambiri koma sichingathetse mavuto amene mwamuna ndi mkazi amakumana nawo m’banja.​—Werengani 1 Akorinto 7:28. *

15 Anthu ena amene angokwatirana kumene amadabwa kapenanso kukhumudwa akasiyana maganizo ndi mnzawo pa nkhani zofunika kwambiri. Anthu okwatirana angasiyane maganizo pa kagwiritsidwe ntchito ka ndalama, malo okhala, ndiponso kuti azipita kangati kokaona achibale. Munthu aliyense amakhala ndi khalidwe lina limene limakhumudwitsa mnzake. Pamene muli pa chibwenzi n’zosavuta kunyalanyaza zinthu zofunika ngati zimenezi, koma pakapita nthawi zikhoza kuyambitsa mavuto m’banja. Choncho ndi bwino kukambirana nkhani zofunika ngati zimenezi mudakali pa chibwenzi.

16. N’chifukwa chiyani okwatirana ayenera kukambirana mmene angathetsere bwino mavuto awo?

16 Kuti zinthu ziziyenda bwino m’banja, anthu okwatirana ayenera kulimbana ndi mavuto mogwirizana. Iwo ayenera kugwirizana polanga ana komanso posamalira makolo okalamba. Mavuto a m’banja sayenera kusokoneza ubwenzi wawo. Anthu okwatirana akamatsatira malangizo a m’Baibulo amathana bwinobwino ndi mavuto, amapirira mavuto amene sakutha ndipo amakhala limodzi mosangalala.​—1 Akor. 7:10, 11.

17. Kodi ndi “zinthu za dziko” ziti zimene okwatirana ayenera kuziyembekezera kuti zidzawadetsa nkhawa?

17 Paulo ananenanso mfundo ina yofunika yokhudza banja pa 1 Akorinto 7:32-34. (Werengani.) M’pomveka kuti anthu amene ali pabanja “amadera nkhawa zinthu za dziko” monga chakudya, zovala, malo ogona ndi zinthu zina zomwe si zauzimu. N’chifukwa chiyani zili choncho? M’bale akakhala wosakwatira amachita zambiri mu utumiki. Koma akakwatira amafunika kugwiritsa ntchito nthawi ina ndiponso mphamvu zake kuti asamalire mkazi wake n’cholinga choti akondweretse mkazi wakeyo. N’chimodzimodzinso ndi mlongo, nayenso amafunika kukondweretsa mwamuna wake. Popeza Yehova ndi wanzeru kwambiri, amadziwa zimenezi. Iye amadziwa kuti mwamuna ndi mkazi amafunika kugwiritsa ntchito mphamvu ndi nthawi imene ankagwiritsa ntchito mu utumiki, pa nthawi imene sanali pabanja, kuti asamalire mwamuna kapena mkazi wake.

18. Kodi okwatirana ayenera kusintha zinthu ngati ziti zomwe ankachita asanakwatirane?

18 Koma tikuphunziraponso zinthu zina. Taona kuti anthu amene ali pabanja ayenera kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zina zimene m’mbuyomu ankagwiritsa ntchito potumikira Mulungu kuti asamalirane. Choncho ayenera kuchita zomwezo ndi nthawi komanso mphamvu zimene ankagwiritsa ntchito pocheza kapena pochita zosangalatsa asanalowe m’banja. Kodi mkazi angamve bwanji ngati mwamuna wake amakondabe kuchita masewera olimbitsa thupi ndi anzake? Nanga mwamuna angamve bwanji ngati mkazi wake amathera nthawi yambiri akucheza ndi anzake? Mwamuna kapena mkazi amene amatsala yekhayo angayambe kusungulumwa, kukhala wosasangalala ndiponso kuona kuti sakukondedwa. Zimenezi zikhoza kupewedwa ngati anthu amene alowa m’banjawo akuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wawo.​—Aef. 5:31.

Yehova Amafuna Tizikhala ndi Makhalidwe Oyera

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani anthu a pabanja afunika kuyesetsa kupewa chiwerewere? (b) Kodi pamakhala vuto lotani ngati mwamuna ndi mkazi wake amasiyana kwa nthawi yaitali?

19 Atumiki a Yehova amafunika kupewa chiwerewere. Anthu ena amakwatira kuti apewe mavuto pa nkhani imeneyi. Koma sikuti munthu akakwatira ndiye kuti basi watetezeka ku khalidwe la chiwerewere. Kalekale, anthu ankakhala otetezeka ngati ali m’kati mwa mpanda wa mzinda. Munthu amene watuluka mumpandamo pa nthawi imene achifwamba avuta ankaberedwa kapena kuphedwa. N’chimodzimodzinso ndi ukwati. Anthu amene ali pabanja amakhala otetezeka ngati akutsatira malangizo amene Mulungu, amene anayambitsa banja, anapereka okhudza kugonana.

20 Paulo anafotokoza malangizo amenewa pa 1 Akorinto 7:2-5. Munthu amayenera kugonana ndi mwamuna kapena mkazi wake basi osati ndi munthu wina. Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kupatsana “mangawa” chifukwa ndi zimene okwatiranawo amafunika kuchitirana. Komabe anthu ena okwatirana amasiyana kwa nthawi yaitali. Mwina amachita zimenezi chifukwa choti wina wapita ku tchuthi kapena kukagwira ntchito kumalo enaake kutali. Izi zimachititsa kuti asapatsane “mangawa.” Ndiye tangoganizani mavuto amene angakhalepo ngati wina ‘walephera kudzigwira’ n’kukopeka ndi maganizo a Satana mpaka kufika pochita chigololo. Yehova amadalitsa mitu ya mabanja imene imasamalira mabanja awo popanda kuika ukwati wawo pangozi.​—Sal. 37:25.

Ubwino Womvera Malangizo a M’Baibulo

21. (a) N’chifukwa chiyani zimavuta kusankha kukhala wokwatira kapena wosakwatira? (b) Kodi malangizo a pa 1 Akorinto chaputala 7 ndi othandiza bwanji?

21 Kusankha kukwatira kapena kusakwatira ndi chimodzi mwa zinthu zovuta kwambiri kuchita pa moyo wa munthu. Anthu onse ndi opanda ungwiro ndipo izi n’zimene zimayambitsa kusagwirizana pakati pa anthu. Choncho ngakhale anthu amene akudalitsidwa ndi Yehova nthawi zina amakhumudwa kaya akhale okwatira kapena osakwatira. Ngati mutagwiritsa ntchito malangizo a nzeru opezeka pa 1 Akorinto chaputala 7 mukhoza kupewa mavuto. Kaya muli pabanja kapena ayi mukhoza ‘kuchita bwino’ pamaso pa Yehova. (Werengani 1 Akorinto 7:37, 38.) Kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wa munthu. Ngati ubwenzi umenewu utapitirira mukhoza kudzapeza moyo m’dziko latsopano. M’dziko limenelo, kuchita zinthu ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzathu sikudzakhalanso kovuta ngati mmene zilili masiku ano.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Werengani buku lakuti Chinsinsi cha chimwemwe cha Banja mutu 2 ndime 16 mpaka 19.

Kodi Mungayankhe?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kuumiriza ena kukwatira kapena kukwatiwa?

• Ngati ndinu mtumiki wa Yehova wosakwatira, kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu?

• Kodi Akhristu omwe ali pachibwenzi angakonzekere bwanji mavuto a m’banja?

• Kodi ukwati umateteza munthu kuti asachite chiwerewere? Fotokozani.

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 14]

Akhristu osakwatira omwe amathera nthawi yawo yambiri mu utumiki amakhala osangalala

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi anthu ena amafunika kusintha zinthu ziti akalowa m’banja?