Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kukhalabe Maso’?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kukhalabe Maso’?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kukhalabe Maso’?

OPHUNZIRA a Yesu anamufunsa funso lakuti: ‘Kodi chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?’ (Mateyu 24:3) Poyankha funso limeneli, Yesu anafotokoza momveka bwino zinthu zosiyanasiyana komanso zosavuta kuzindikira zomwe zidzakhale chizindikiro. Zinthu zimenezi zafotokozedwa mu chaputala 24 cha Mateyu, chaputala 13 cha Maliko komanso chaputala 21 cha Luka. Komabe iye anawachenjezanso kuti: “Khalanibe maso.”​—Mateyu 24:42.

Ndiye ngati chizindikiro chinali chosavuta kuchidziwa, n’chifukwa chiyani Yesu anawachenjeza kuti akhalebe maso? Pali zifukwa ziwiri. Choyamba n’chakuti anthu ena angayambe kusokonezedwa ndi zinthu zina zomwe zingawachititse kuti ayambe kunyalanyaza chenjezoli moti angasiye kukhala maso n’kuyamba kufa mwauzimu. Chachiwiri n’choti Mkhristu angathe kuona umboni woti tili m’masiku otsiriza koma osakhudzidwa chifukwa cha mmene zinthu zilili kumene akukhala. Mwina angaganize kuti “chisautso chachikulu,” ndiponso kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu zili kutali, choncho palibe chifukwa choti iye ‘azikhalabe maso.’​—Mat. 24:21.

“Anthu Ananyalanyaza Zimene Zinali Kuchitika”

Yesu anakumbutsa otsatira ake za anthu a m’masiku a Nowa. Anthu ankaona Nowa akulalikira, ndiponso akumanga chingalawa chachikulu kwambiri. Ankaonanso chiwawa chikuchitika. Koma ambiri “ananyalanyaza zimene zinali kuchitika.” (Mat. 24:37-39) Masiku anonso anthu ambiri amanyalanyaza zinthu. Mwachitsanzo, mumsewu mumakhala zikwangwani zouza anthu kuti achepetse liwiro. Komabe anthu ambiri amanyalanyaza zimenezi. Izi zimachititsa kuti akuluakulu aboma aike mahampu m’misewu n’cholinga choti oyendetsa galimoto achepetse liwiro. Zofanana ndi zimenezi zingachitikenso ndi Mkhristu yemwe amangoona zizindikiro zoti tili m’masiku otsiriza koma n’kumapitirizabe kukhala ndi moyo wosalabadira zimenezi. Izi n’zimene zinachitikira mtsikana wina wa ku West Africa dzina lake Arielle.

Arielle ankakonda kuonera mpira wa azimayi pa TV. Sukulu yake itakonza timu, iye ankalakalaka kusewera ndipo izi zinapangitsa kuti aiwale kufunika kokhala maso mwauzimu. Iye analembetsa kuti azisewera pagolo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anati: “Atsikana ena amene ndinkasewera nawo ankachita zibwenzi ndi anyamata osuta ndiponso ogwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo. Iwo ankandiseka chifukwa chosachita nawo zimenezo ndipo ine ndinkaganiza kuti ndikhoza kupirira bwinobwino zomwe zinkachitikazi. Komabe mpirawo ndi umene unayamba kuwononga moyo wanga wauzimu. Nthawi zonse ndinkangoganizira za mpira basi. Ndikakhala m’Nyumba ya Ufumu, maganizo anga ankachoka pa misonkhano n’kumaganizira za m’bwalo la mpira. Makhalidwe anga achikhristu anayambanso kuwonongeka. Sikuti zinathera pongosangalala ndi kusewera mpirawo koma ndinayambanso mzimu wa mpikisano. Zimenezi zinandipangitsa kuti ndithere nthawi yaitali ndikukonzekera masewerawo n’cholinga choti tikawine basi moti nkhani yowina mpikisano inkandidetsa nkhawa kwambiri. Kuwonjezera pamenepo ndinafika posiya kucheza ndi anthu.

“Tsiku lina ndinazindikira kuti zinthu zafika poipa kwambiri. Timu imene tinkasewera nayo inafunika kumenya penati. Ndinachalira kuti ndiugwire. Ndinangozindikira kuti ndapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuti ndigwire mpirawo. Apa m’pamene ndinazindikira kuti ee, moyo wanga wauzimu wasokonekera. Kodi ndinachita chiyani kuti ndiukonze?

“Ndinali nditaonera DVD yakuti, Young People Ask​—What Will I Do With My Life? * Koma ndinaganiza zoioneranso mwachifatse. Ndipotu vuto langa linali lofanana ndi la André, mnyamata yemwe ali mu sewero limeneli. Mu seweroli, mkulu uja anauza André kuti awerenge ndi kuganizira mawu a pa Afilipi 3:8. Ndinaganizira kwambiri mawu amenewo kenako ndinasiya kusewera mpira.

“Zimenezi zinandithandiza kwambiri. Mzimu wa mpikisano komanso nkhawa yofunitsitsa kuwina zinathera pomwepo. Ndinayamba kukhala wosangalala komanso kugwirizana ndi anzanga achikhristu. Chidwi changa chomvetsera pa misonkhano chinabwerera ndipo ndinkasangalala nayo. Ndinayambanso kuchita bwino mu utumiki. Panopo ndimakonda kulembetsa upainiya wothandiza.”

Ngati zinthu zina zikukusokonezani ndi kukuchititsani kuti munyalanyaze chizindikiro chimene Yesu anapereka, muyenera kuchitapo kanthu mwamsanga ngati mmene anachitira Arielle. Mungayese kuchita zotsatirazi: Onani Watch Tower Publications Index yomwe mkulu wa mu sewero lija ananena kuti ndi mapu otithandiza kupeza chuma chobisika. Apo ayi mungayang’ane Mlozera Nkhani wa Magazini a Nsanja ya Olonda. Mukhoza kupeza malangizo abwino ndiponso zimene anthu ena anachita atakumana ndi mayesero. Kuti muzipindula kwambiri ndi misonkhano, muyenera kukonzekera bwinobwino ndiponso kulemba notsi. Ena aona kuti kukhala m’mipando ya kutsogolo kwawathandiza kuti azipindula ndi misonkhano. Ngati nkhaniyo ndi yokambirana ndi omvera yesetsani kupereka ndemanga yanu koyambirira. Kuwonjezera pamenepo, muyenera kukhala tcheru kuti muzimva nkhani zimene zangochitika kumene zomwe zili mbali ya chizindikiro cha “masiku otsiriza.”​—2 Tim. 3:1-5; 2 Pet. 3:3, 4; Chiv. 6:1-8.

“Khalani Okonzeka”

Chizindikiro cha masiku otsiriza chikukhudza ‘dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.’ (Mat. 24:7, 14) Anthu ena amakhala m’madera omwe kumachitika miliri, njala, zivomezi ndiponso zinthu zina zimene zinaloseredwa. Koma anthu ena amakhala m’madera omwe muli bata ndi mtendere. Ngati inuyo panokha simunaonepo zinthu zosonyeza chizindikiro cha masiku otsiriza, kodi ndi bwino kuganiza kuti chisautso chachikulu chili kutali? Ayi, kuchita zimenezi kungakhale kupanda nzeru.

Mwachitsanzo, taganizirani zimene Yesu ananena zokhudza “miliri ndi njala.” (Luka 21:11) Choyamba, iye sananene kuti zidzachitika m’madera onse pa nthawi imodzi kapena kuti kupha anthu mofanana. Iye ananena kuti zizichitika “m’malo osiyanasiyana.” Choncho sitingayembekezere kuti zinthu zofanana zizichitika padziko lonse nthawi imodzi. Chachiwiri, Yesu atanena za njala anasonyeza kuti otsatira ake ena ayenera kusamala kuti asamadye kwambiri. Iye anati: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri.” (Luka 21:34) Choncho Akhristu sayenera kuyembekezera kuti adzakumana ndi zinthu zonse zokhudza chizindikiro cha masiku otsiriza. Yesu ananena kuti: “Mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.” (Luka 21:31) Zipangizo zamakono zimatithandiza kuona zizindikiro zonse ngakhale kuti sizikuchitikira m’dera lathu.

Kumbukiraninso kuti Yehova anakhazikitsa ‘tsiku ndi ola’ lakuti chisautso chachikulu chiyambike. (Mat. 24:36) Choncho zochitika za padzikoli sizingasinthe tsikuli.

Yesu anachenjeza Akhristu kulikonse kuti: “Khalani okonzeka.” (Mat. 24:44) Tiyenera kukhala okonzeka nthawi zonse. N’zoona kuti sitingakhalire kuchita zinthu zauzimu tsiku lonse. Ndipotu palibe amadziwa zimene tidzakhala tikuchita pamene chisautso chachikulu chizidzayamba. Ena adzakhala ali kumunda ndipo ena akugwira ntchito zapakhomo. (Mat. 24:40, 41) Ndiyeno, kodi tingatani kuti tikhale okonzeka?

Emmanuel ndi Victorine limodzi ndi ana awo 6, amakhala kudera lina la ku Africa kumene chizindikiro cha masiku otsiriza sichionekera kwenikweni. Iwo anaganiza zomakambirana zinthu zauzimu tsiku lililonse n’cholinga choti azikhala okonzeka. Emmanuel anati: “Zinali zovuta kupeza nthawi yabwino kwa tonsefe. Kenako tinagwirizana kuti tizichita zimenezi kwa mphindi 30 kuyambira 6 koloko m’mawa. Timakambirana lemba la tsiku kenako n’kukonzekera ndime zingapo za Phunziro la Baibulo la Mpingo la mlungu umenewo.” Kodi kuchita zimenezi kwawathandiza kuti akhale maso? Inde kwawathandiza kwambiri. Emmanuel ndi Wogwirizanitsa Ntchito za Bungwe la Akulu mu mpingo wawo. Victorine amakonda kulembetsa upainiya wothandiza ndipo waphunzitsa choonadi anthu ambiri. Ana awo aakazi akupita patsogolo mwauzimu.

Yesu anatilangiza kuti: “Khalani maso, khalani tcheru.” (Maliko 13:33) Musalole zinthu zosokoneza kukuchititsani kuodzera mwauzimu. M’malomwake muzitsatira malangizo anzeru amene ali m’mabuku athu komanso amene timalandira pa misonkhano ya mpingo ngati mmene anachitira Arielle. Mofanana ndi banja la Emmanuel, tsiku lililonse muziyesetsa kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kukhala okonzeka komanso ‘kukhalabe maso.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Ili ndi sewero lofotokoza zimene achinyamata amakumana nazo akamayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Yehova.

[Chithunzi patsamba 4]

Kukambirana zinthu zauzimu kwathandiza Emmanuel ndi banja lake ‘kukhala okonzeka’