Tiyeni Tisangalale Limodzi
Tiyeni Tisangalale Limodzi
MASIKU ano, kukhala munthu wosangalala ndiponso wachimwemwe kukuvuta kwambiri. Ambiri akumaona kuti n’zovuta kukhala pansi kuti azicheza n’kumauzana zinthu zosangalatsa. Chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zotangwanitsa makamaka m’mizinda ikuluikulu, anthu ambiri akumakhala nthawi yaitali ali okhaokha ndipo izi zikuchititsa kuti azisungulumwa.
Pulofesa wina, yemwe ndi katswiri wa maphunziro a maganizo a anthu, dzina lake Alberto Oliverio, ananena kuti: “Anthu anazolowera kukhala osungulumwa ndipo moyo umene anthu okhala m’nyumba zikuluzikulu amakhala, umawachititsa kuti azingochita zinthu zaokha. Nthawi zambiri moyo wotanganidwa ndi zinthu zako umachititsa kuti tisamasamale za anthu ena monga amene timagwira nawo ntchito, aneba athu kapena munthu amene amagulitsa musitolo imene timakagulako zinthu.” Kusungulumwa kotereku n’kumene nthawi zambiri kumayambitsa matenda ovutika maganizo.
Koma zimenezi si zimene zimachitika pakati pa Akhristu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Muzikhala okondwera nthawi zonse.” (1 Ates. 5:16) Pali zifukwa zambiri zotichititsa kuti tisangalale komanso kukondwera limodzi ndi anzathu. Timalambira Yehova yemwe ndi Mulungu Wam’mwambamwamba, timadziwa choonadi cha m’Baibulo, tili ndi chiyembekezo chodzapulumuka n’kudzapeza moyo wosatha komanso tingathandize ena kupeza madalitso amenewa.—Sal. 106:4, 5; Yer. 15:16; Aroma 12:12.
Kukhala osangalala komanso kusangalala ndi anthu ena ndi zizindikiro za Akhristu oona. Choncho n’zosadabwitsa kuti Paulo analembera Afilipi kuti: “Ndine wokondwa ndipo ndikukondwera ndi inu nonse. Tsopano inunso khalani okondwa ndipo sangalalani limodzi ndi ine.” (Afil. 2:17, 18) M’mawu ochepawa Paulo ananena kawiri konse za kukhala okondwa ndiponso kusangalala limodzi ndi ena.
Akhristu ayenera kusamala kuti asamakhale moyo wodzipatula. Munthu wodzipatula sangasangalale ndi okhulupirira anzake. Kodi tingatsatire bwanji malangizo a Paulo akuti ‘tipitirize kukondwera mwa Ambuye’ ndi abale athu?—Afil. 3:1.
Sangalalani ndi Okhulupirira Anzanu
Pamene Paulo ankalemba kalata kwa Afilipi ayenera kuti anali kundende ku Roma. Iye anamangidwa chifukwa chogwira ntchito yolalikira. (Afil. 1:7; 4:22) Ngakhale zinali choncho, kumangidwa sikunachititse kuti changu chake potumikira Mulungu chizirale. M’malomwake, iye anasangalala kutumikira Yehova mmene akanathera n’kumadzikhuthula ngati “nsembe yachakumwa.” (Afil. 2:17) Zimene Paulo ankachita zikusonyeza kuti munthu sasangalala chifukwa cha zimene zikuchitika pa moyo wake. Ngakhale kuti anatsekeredwa m’ndende, iye anati: “Ndipitiriza kukondwera.”—Afil. 1:18.
Paulo anali atayambitsa mpingo ku Filipi choncho anali ndi chikondi chapadera ndi abale ake a ku Filipi amenewa. Iye ankadziwa kuti kugawana nawo chimwemwe chimene chimapezeka potumikira Yehova kungawalimbikitsenso kuchita zambiri. Choncho iye analemba kuti: “Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti zondichitikira zija, zathandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino m’malo moulepheretsa. Moti, kumangidwa kwanga chifukwa cha Khristu, kwadziwika ndi aliyense pakati pa Asilikali Oteteza Mfumu ndi ena onse.” (Afil. 1:12, 13) Kuwauza mawu olimbikitsa amenewa inali njira imodzi imene Paulo anasonyezera kuti ankasangalala komanso kukondwera ndi abale ake. Komanso Afilipiwo ayenera kuti anasangalalanso ndi Paulo. Koma kuti asangalale chonchi, ankafunika kuti asamadandaule ndi zimene Paulo ankakumana nazo. M’malomwake anafunikira kutsatira chitsanzo chake. (Afil. 1:14; 3:17) Nawonso Afilipi ankapempherera Paulo ndiponso kumuthandiza m’njira zosiyanasiyana.—Afil. 1:19; 4:14-16.
Kodi nafenso timakhala okondwera ngati Paulo? Kodi timayesetsa kuona zinthu zabwino zimene zimachitika pa moyo wathu komanso mu utumiki wathu? Tikamacheza ndi abale athu, ndi bwino kumakambirana mokondwera za ntchito yolalikira. Kuti tichite zimenezi sikuti tizichita kudikira kuti tikhale ndi chokumana nacho chosangalatsa kwambiri. Mwina tinatha kukopa chidwi cha munthu kuti ayambe kumvetsera uthenga wa Ufumu. Kapena tinakambirana bwino ndi mwininyumba vesi lina la m’Baibulo. Apo ayi, mwina anthu m’dera lina anatizindikira kuti ndife a Mboni za Yehova ndipo zimenezi zinapereka umboni wabwino. Kukambirana ndi ena zinthu ngati zimenezi kungatithandize kuti tizisangalala limodzi.
Anthu a Yehova ambirimbiri amadzimana zinthu zambiri n’cholinga choti agwire ntchito yolalikira. Apainiya, oyang’anira oyendayenda, atumiki a pa Beteli, amishonale komanso Akhristu amene amatumikira m’mayiko ena, amachita khama kwambiri mu utumiki wa nthawi zonse ndipo amachita zimenezi mosangalala. Kodi timasangalala komanso kukondwera limodzi nawo? Ngati ndi choncho, tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira ‘antchito anzathu pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu.’ (Akol. 4:11) Tikakhala pa misonkhano ya mpingo kapena misonkhano ikuluikulu, tiziyamikira anthu amenewa ndi mtima wonse. Tiyeneranso kutsanzira khama lawo. Komanso tingachite bwino kupeza “mpata” womvetsera zinthu zimene amakumana nazo ndiponso mawu awo olimbikitsa. Tingachite zimenezi powaitana kunyumba kwathu kuti tidzacheze mwinanso kudya nawo limodzi.—Afil. 4:10.
Sangalalani Limodzi ndi Amene Akukumana ndi Mayesero
Kupirira pozunzidwa komanso kulimbana ndi mayesero, zinathandiza Paulo kuti apitirizebe kukhala wokhulupirika kwa Yehova. (Akol. 1:24; Yak. 1:2, 3) Podziwa kuti abale a ku Filipi akhoza kukumana ndi mavuto omwewo komanso kuti angalimbikitsidwe podziwa kuti iye anapirira mayesero, Paulo anaona kuti ndi bwino kukondwera nawo. Choncho iye analemba kuti: “Inu munapatsidwa mwayi. Osati mwayi wokhulupirira Khristu wokha, komanso wovutika chifukwa cha iye. Ndiye chifukwa chake inunso muli ndi mavuto ofanana ndi amene munawaona kwa ine, ndiponso amene mukumva kuti ndikukumana nawo panopa.”—Afil. 1:29, 30.
Masiku anonso Akhristu amatsutsidwa chifukwa cha ntchito yawo yolalikira. Nthawi zina amachitiridwa nkhanza koma nthawi zina amatsutsidwa m’njira zosachita kuonekera. Mwina anganamiziridwe ndi anthu ampatuko, angadedwe ndi achibale awo, apo ayi anganyozedwe ndi anzawo ku ntchito kapena kusukulu. Yesu ananena kuti sitiyenera kudabwa kapena kukhumudwa ndi mayesero ngati amenewa. M’malomwake tiyenera kusangalala. Iye ananena kuti: “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba.”—Mat. 5:11, 12.
Sitiyenera kuchita mantha tikamva kuti abale athu akuzunzidwa koopsa m’mayiko ena. M’malomwake tiyenera kusangalala chifukwa cha kupirira kwawo. Tiyenera kupempha Yehova kuti awathandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti apitirize kupirira. (Afil. 1:3, 4) N’zoona kuti pali zinthu zochepa zimene tingachitire abale athu amenewa koma tikhoza kuthandiza Akhristu mu mpingo wathu amene akukumana ndi mayesero. Tiyenera kuwasonyeza chikondi komanso kuwathandiza. Tingapeze nthawi yosangalala nawo powaitana nthawi ndi nthawi pa kulambira kwathu kwapabanja, kuyenda nawo mu utumiki wakumunda komanso kuwatenga tikamapita kokacheza malo ena osangalatsa.
Tili ndi zifukwa zambiri zosangalalira limodzi. Tiyeni tipewe mtima wokonda kudzipatula umene wafala m’dzikoli, ndipo tipitirize kusangalala ndi abale athu. Tikamachita zimenezi tidzathandiza kuti mu mpingo mukhale chikondi komanso mgwirizano. Zimenezi zidzathandizanso kuti tizisangalala kwambiri ndi ubale wathu wachikhristu. (Afil. 2:1, 2) Choncho, tiyeni tizitsatira malangizo a Paulo akuti: “Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye. Ndibwerezanso, Kondwerani.”—Afil. 4:4.
[Mawu a Chithunzi patsamba 6]
Globe: Courtesy of Replogle Globes