Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Tonthozani Anthu Onse Olira’

‘Tonthozani Anthu Onse Olira’

‘Tonthozani Anthu Onse Olira’

“Yehova wandidzoza kuti . . . ndikatonthoze anthu onse olira.”​—YES. 61:1, 2.

1. Kodi Yesu ankachita chiyani kwa anthu olira ndipo n’chifukwa chiyani?

PA NTHAWI ina Yesu Khristu anati: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yoh. 4:34) Pogwira ntchito imene Mulungu anamupatsa, Yesu anasonyeza makhalidwe abwino a Atate wake. Limodzi mwa makhalidwe amenewa ndi kukonda kwambiri anthu. (1 Yoh. 4:7-10) Mtumwi Paulo anafotokoza njira ina imene Yehova amasonyezera khalidwe limeneli. Ananena kuti Iye ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akor. 1:3) Yesu anasonyeza chikondi chimenechi pamene anachita zimene ulosi wa Yesaya unanena. (Werengani Yesaya 61:1, 2.) Ali musunagoge wa ku Nazarete, Yesu anawerenga ulosi umenewu kenako n’kusonyeza kuti mawuwa ankanena za iye. (Luka 4:16-21) Pa utumiki wake wonse, Yesu ankatonthoza olira, kuwalimbikitsa komanso kuwakhazika mtima pansi.

2, 3. N’chifukwa chiyani otsatira Khristu ayenera kumutsanzira potonthoza ena?

2 Otsatira onse a Yesu ayenera kumutsanzira potonthoza ena. (1 Akor. 11:1) Paulo ananena kuti: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.” (1 Ates. 5:11) Panopa tifunikadi kutonthoza ena chifukwa chakuti anthufe tikukhala ‘m’nthawi yapadera komanso yovuta.’ (2 Tim. 3:1) Anthu ambiri amtima wabwino padziko lonse amakhumudwitsidwa ndiponso kupsetsedwa mtima ndi zochita komanso zolankhula za anthu ena.

3 Pajatu Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza ano anthu ambiri adzakhala “odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” Makhalidwe amenewa akuwonjezeka chifukwa chakuti ‘anthu oipa ndi onyenga akuipiraipirabe.’​—2 Tim. 3:2-4, 13.

4. Kodi zinthu zasintha bwanji m’dzikoli masiku ano?

4 Zonsezi siziyenera kutidabwitsa chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amanena momveka kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Mawu akuti “dziko lonse” akunena mbali zake zandale, zachipembedzo, zamalonda ndiponso njira zake zofalitsira nkhani. Mpake kuti Satana Mdyerekezi amatchedwa “wolamulira wa dziko” komanso “mulungu wa nthawi ino.” (Yoh. 14:30; 2 Akor. 4:4) Zinthu zikupitirizabe kuipa kwambiri m’dzikoli chifukwa panopa Satana ndi wokwiya kwambiri. Iye akuchita zimenezi chifukwa akudziwa kuti kwangotsala nthawi yochepa kwambiri kuti Yehova amusiyitse kulamulira dzikoli. (Chiv. 12:12) N’zolimbikitsa kudziwa kuti nthawi imene Mulungu walola kuti Satana ndi dongosolo lake zikhalepo yatsala pang’ono kutha. Komanso, nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova imene Satana anayambitsa idzathetsedwa posachedwapa.​—Genesis chaputala 3; Yobu chaputala 2.

Uthenga Wabwino Ukulalikidwa Padziko Lonse

5. Kodi ulosi wonena za ntchito yolalikira ukukwaniritsidwa bwanji masiku otsiriza ano?

5 Zinthu zimene Yesu analosera zikukwaniritsidwa masiku ano. Iye ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:14) Ntchito yolalikira Ufumu wa Mulungu padziko lonse ikugwiridwa kwambiri kuposa kale lonse. Masiku ano, a Mboni za Yehova oposa 7,500,000 amene ali m’mipingo yoposa 107,000 padziko lonse amalalikira za Ufumu wa Mulungu. Iwo amatsanzira Yesu yemwe ankalalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu umenewu. (Mat. 4:17) Chifukwa cha ntchito yathu yolalikirayi, anthu ambiri olira akutonthozedwa. M’zaka ziwiri zapitazi anthu okwana 570,601 abatizidwa n’kukhala Mboni za Yehova.

6. Kodi munganene chiyani za mmene ntchito yathu yolalikira ikupitira patsogolo?

6 Kudziwa kuti Mboni za Yehova zikumasulira ndiponso kufalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 500, kungatithandize kuona kuti ntchito yolalikira ikupita patsogolo. Zimenezi sizinachitikepo m’mbuyo monsemu. Ntchito imeneyi yomwe mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova ikuchita ikukulirakulira kuposa ndi kale lonse. M’dziko loipa limene Satana akulilamulira, ntchito imeneyi sikanatheka popanda kuthandizidwa ndi mphamvu ya mzimu woyera ya Mulungu. Chifukwa chakuti uthenga wabwino waufumu ukulalikidwa padziko lonse kumene kuli anthu, Malemba akumatonthoza osati okhulupirira anzathu okha koma ngakhale anthu olira amene amalandira uthenga wa Ufumu.

Tizitonthoza Akhristu Anzathu

7. (a) N’chifukwa chiyani sitingayembekezere kuti Yehova achotse zinthu zonse zimene zimativutitsa panopa? (b) Timadziwa bwanji kuti n’zotheka kupirira chizunzo komanso masautso?

7 M’dzikoli mmene muli zoipa komanso mavuto ambirimbiri, sitingapewe kukumana ndi mavuto. Komabe sitingayembekezere kuti Mulungu achotse chilichonse chimene chimachititsa kuti anthu azivutika pokhapokha ayambe wachotsa dongosolo loipali. Koma panopa pamene tikukumana ndi chizunzo, tiyenera kudziwa kuti timakhala tikuyesedwa ngati tidzakhalebe okhulupirika kwa Yehova ndiponso ngati tidzapitirize kukhala ku mbali ya ulamuliro wake. (2 Tim. 3:12) Chifukwa chothandizidwa komanso kutonthozedwa ndi Atate wathu wakumwamba tidzachita mofanana ndi Akhristu odzozedwa a ku Tesalonika. Iwo anapirira komanso kusonyeza chikhulupiriro pamene anakumana ndi mazunzo komanso masautso.​—Werengani 2 Atesalonika 1:3-5.

8. Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti Yehova amatonthoza atumiki ake?

8 N’zosakayikitsa kuti Yehova amatonthoza atumiki ake. Mwachitsanzo, pamene Mfumukazi Yezebeli inkafuna kupha mneneri Eliya, iye anachita mantha kwambiri moti anathawa kenako n’kufika ponena kuti akufuna atangofa. Koma m’malo modzudzula Eliya, Yehova anamutonthoza ndi kumulimbikitsa kuti apitirize kutumikira monga mneneri. (1 Maf. 19:1-21) Umboni woti Yehova amatonthoza anthu ake umaonekanso pa zimene anachitira mpingo woyambirira wachikhristu. Mwachitsanzo timawerenga za nthawi imene “mpingo mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba.” Komanso pamene “unali kuyenda moopa Yehova ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera, mpingowo unali kukulirakulira.” (Mac. 9:31) Ifenso timayamikira kwambiri chifukwa chakuti ‘timalimbikitsidwa ndi mzimu woyera.’

9. Kodi kuphunzira za Yesu kungatitonthoze bwanji?

9 Monga Akhristu, timatonthozedwa tikamaphunzira za Yesu komanso kutsatira mapazi ake. Yesu anati: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Kuphunzira za mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu komanso kutsanzira chitsanzo chake chabwino kungatitonthoze tikamakumana ndi mavuto.

10, 11. Kodi ndani amene angatonthoze ena mu mpingo?

10 Mu mpingo tilinso ndi mwayi wotonthozedwa ndi okhulupirira anzathu. Mwachitsanzo, taganizirani mmene akulu mu mpingo amathandizira anthu amene ali ndi mavuto. Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu analemba kuti: “Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupempherere.” Kodi zimenezi zikanathandiza bwanji? “Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.” (Yak. 5:14, 15) Komabe, anthu ena mu mpingo angatonthoze Akhristu anzawo.

11 Nthawi zambiri akazi akakumana ndi mavuto, amamasuka kuuza akazi anzawo. Kawirikawiri alongo achikulire amene amadziwa zambiri angapereke malangizo abwino kwa alongo achitsikana. Mwina alongo achikulirewa amene ndi anzeru anakumanapo ndi mavuto ofanana ndi amene alongo achitsikanawo akukumana nawo. Chifundo ndiponso makhalidwe ena amene akazi amakhala nawo zingathandize kwambiri kuti atonthoze ena. (Werengani Tito 2:3-5.) Choncho n’zotheka kuti akulu komanso anthu ena atonthoze ena ndipo ayenera ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wachisoni’ mu mpingo. (1 Ates. 5:14, 15) Ndi bwinonso kukumbukira kuti Mulungu “amatitonthoza m’masautso athu onse, kuti tithe kutonthoza amene ali m’masautso amtundu uliwonse.”​—2 Akor. 1:4.

12. N’chifukwa chiyani kupezeka ku misonkhano yachikhristu kuli kofunika kwambiri?

12 Kupezeka pa misonkhano yachikhristu ndi njira yabwino komanso yofunika kwambiri imene tingapezere chitonthozo. Tikutero chifukwa chakuti kumakhala malangizo a m’Baibulo amene amatilimbikitsa. M’Baibulo timawerenga kuti Yudasi ndi Sila ‘analimbikitsa abale ndi mawu ambiri ndipo anawapatsa mphamvu.’ (Mac. 15:32) Nafenso tingachite bwino kucheza komanso kulimbikitsa abale ndi alongo athu mu mpingo misonkhano isanayambe komanso ikatha. Choncho ngati tikukumana ndi mavuto sitiyenera kudzipatula chifukwa kuchita zimenezi sikungathetse vutolo. (Miy. 18:1) M’malomwake tingachite bwino kumvera malangizo ouziridwa a mtumwi Paulo akuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.”​—Aheb. 10:24, 25.

Mawu a Mulungu Azikutonthozani

13, 14. Fotokozani mmene Malemba angatitonthozere.

13 Kaya ndife Akhristu obatizidwa kapena tangoyamba kumene kuphunzira za Mulungu ndi zolinga zake, tikhoza kutonthozedwa kwambiri ndi Mawu a Mulungu. Paulo analemba kuti: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa chiyembekezo chifukwa malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.” (Aroma 15:4) Malemba Opatulika amatitonthoza komanso kutichititsa kuti ‘tikhale oyenerera bwino ndi okonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Tim. 3:16, 17) Kudziwa zolondola ponena za cholinga cha Mulungu komanso kukhala ndi chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo, zingatitonthoze kwambiri. Choncho tiyeni tigwiritse bwino ntchito Mawu a Mulungu komanso mabuku ofotokoza Baibulo kuti titonthozedwe komanso kuthandizidwa m’njira zosiyanasiyana.

14 Yesu anapereka chitsanzo chabwino pogwiritsira ntchito Malemba kuti aphunzitse ndi kutonthoza ena. Nthawi ina pamene Yesu anaonekera kwa ophunzira ake awiri pambuyo poti waukitsidwa, iye ‘anawafotokozera Malemba momveka bwino.’ Zimene anawalankhula zinawakhudza mtima kwambiri. (Luka 24:32) Mtumwi Paulo anatsanzira chitsanzo cha Yesu ndipo ‘anakambirana ndi anthu mfundo za m’Malemba.’ Anthu a ku Bereya, amene ankamvetsera zimene Paulo ankalalikira, “analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku anali kufufuza Malemba mosamala.” (Mac. 17:2, 10, 11) Ndi chinthu chanzerudi kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kupindula nalo. Tiyeneranso kuwerenga mabuku achikhristu amene amatitonthoza ndi kutipatsa chiyembekezo m’nthawi yovuta ino.

Njira Zina Zimene Tingatonthozere Ena

15, 16. Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe tingachite kuti titonthoze ena?

15 Pali zinthu zosiyanasiyana zimene tingachite kuti titonthoze abale athu. Mwachitsanzo, tingathandize Akhristu achikulire kapena amene akudwala popita kukawagulira zinthu kumsika. Tingawathandizenso pogwira ntchito zina za pakhomo. Tikachita zimenezi tingawasonyeze kuti timawaganizira. (Afil. 2:4) Njira ina imene tingatonthozere abale athu ndiyo kuyamikira makhalidwe awo abwino monga chikondi, chikhulupiriro, kulimba mtima komanso zimene amachita pothana ndi mavuto.

16 Tikafuna kutonthoza achikulire, tingachite bwino kupita kokacheza nawo ndi kuwamvetsera akamafotokoza mbiri ya moyo wawo komanso madalitso amene apeza potumikira Yehova. Ndipotu zimenezi zingatilimbikitsenso ifeyo. Tikhozanso kuwerenga Baibulo kapena mabuku ena ofotokoza Baibulo limodzi ndi anthu amene tawachezera. Mwina tingakambirane nawo zimene zili m’Phunziro la Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Baibulo la Mpingo zimene zikuphunziridwa mlungu umenewo. Chinanso chimene tingachite ndi kuonera nawo DVD yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Tikhozanso kuwerenga kapena kuwauza nkhani zolimbikitsa zochokera m’mabuku athu.

17, 18. N’chifukwa chiyani tili ndi chidaliro choti Yehova adzatitonthoza ndi kutilimbikitsa monga atumiki ake okhulupirika?

17 Tikaona kuti pali Mkhristu mnzathu amene akukumana ndi mavuto, tingachite bwino kumutchula m’mapemphero athu. (Aroma 15:30; Akol. 4:12) Tikamayesetsa kupirira mavuto amene timakumana nawo komanso kufunafuna mipata yotonthozera ena, tikhoza kukhala ndi chikhulupiriro ngati chimene wamasalimo anali nacho. Iye anaimba kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” (Sal. 55:22) Yehova adzatitonthoza ndi kutithandiza nthawi zonse. Iye sangagwiritse mwala atumiki ake.

18 Mulungu anauza atumiki ake akale kuti: “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.” (Yes. 51:12) Yehova adzachitanso chimodzimodzi kwa ife ndipo adzadalitsa zonena zathu komanso zimene timachita potonthoza olira. Kaya tili ndi chiyembekezo cha moyo kumwamba kapena padziko lapansi, aliyense wa ife angalimbikitsidwe ndi mawu a Paulo amene ananena kwa Akhristu odzozedwa anzake kuti: “Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ndipo amatilimbikitsa m’njira yosalephera ndiponso anatipatsa chiyembekezo chabwino, mwa kukoma mtima kwakukulu, alimbikitse mitima yanu ndi kukulimbikitsani muntchito yabwino iliyonse ndiponso m’mawu.”​—2 Ates. 2:16, 17.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ntchito yathu yafika potani?

• Kodi ndi zinthu ziti zomwe tingachite kuti titonthoze ena?

• Kodi tili ndi umboni wotani wa m’Malemba wosonyeza kuti Yehova amatonthoza anthu ake?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi mumatonthoza anthu olira?

[Chithunzi patsamba 30]

Ana ndi akulu omwe angatonthozenso ena