Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Panopa Ndine Wolumala, Koma Sindidzakhala Chonchi Mpaka Kalekale”

“Panopa Ndine Wolumala, Koma Sindidzakhala Chonchi Mpaka Kalekale”

“Panopa Ndine Wolumala, Koma Sindidzakhala Chonchi Mpaka Kalekale”

Yosimbidwa ndi Sara van der Monde

Anthu amakonda kundiuza kuti, “Ee, koma Sara umamwetulira bwino. N’chiyani chimakuthandiza kukhala wosangalala nthawi zonse?” Ndimawauza kuti ndikuyembekeza zinthu zapadera. Mwachidule ndimangoti: “Panopa ndine wolumala koma sindidzakhala chonchi mpaka kalekale.”

NDINABADWA m’chaka cha 1974 ku Paris m’dziko la France. Panali mavuto ena pa nthawi imene ndinkabadwa ndipo anandipeza ndi matenda a mu ubongo olumalitsa ziwalo. Ndinkavutika kuyendetsa manja ndi miyendo komanso kulankhula. Ndinayambanso matenda a khunyu ndipo ndinkadwala matenda osiyanasiyana.

Ndili ndi zaka ziwiri, banja lathu linasamukira ku Melbourne m’dziko la Australia. Patangopita zaka ziwiri, bambo anga anatithawa n’kundisiya ndi amayi. Apa m’pamene ndinayamba kukonda kwambiri Mulungu. Mayi anga omwe ndi a Mboni, ankakonda kunditenga popita ku misonkhano yachikhristu kumene ndinadziwa kuti Mulungu amandikonda ndiponso kundisamalira. Kudziwa zimenezi komanso chikondi cha mayi anga zandithandiza kuti ndiziona kuti ndine wotetezeka ngakhale kuti zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wathu.

Mayi anga anandiphunzitsanso kupemphera kwa Yehova. Ndimaona kuti kupemphera n’kosavuta ndikakuyerekezera ndi kulankhula. Popemphera, sindivutika n’kutulutsa mawu. M’malomwake ndimangolankhula zomveka bwinobwino mumtima. Komanso popeza zolankhula zanga sizimveka bwinobwino, mtima wanga umakhala m’malo chifukwa choti ndimadziwa kuti Yehova amamvetsa chilichonse chimene ndimalankhula ngakhale za mumtima.​—Sal. 65:2.

Kupirira Vuto Langa

Pamene ndinali ndi zaka 5, matenda anga anafika poipa kwambiri moti ndinkafunika zitsulo zovala kuyambira m’miyendo kufika m’chiuno kuti ndiziyenda bwinobwino. Koma ndinkalephera kuyenda nazo bwinobwino. Pofika zaka 11 ndinkalephereratu kuyenda. Kenako ndinkavutikanso kukwera kapena kutsika pabedi moti panafunika chipangizo china choyendera magetsi kuti chizindikhazika pa njinga yanga.

N’zoona kuti nthawi zina ndimada nkhawa chifukwa choti ndine wolumala. Koma kenako ndimakumbukira mfundo imene banja lathu limayendera yakuti: “Osamadandaula ndi zimene sungathe kuchita. Uzingochita zokhazo zimene ungakwanitse.” Kuganizira zimenezi kwandithandiza kuti ndithe kuchita zinthu ngati kukwera hatchi, kuyendetsa boti, kupalasa bwato, kupita kukagona kumalo enaake osangalatsa ngakhalenso kuyendetsa galimoto kumalo amene kulibe magalimoto ambiri. Ndilinso ndi luso lojambula, kusoka, kuluka, kupeta nsalu ndi kuumba miphika.

Chifukwa chakuti ndinalumala kwambiri, anthu ena ankanena kuti sindingakwanitse kutumikira Mulungu monga munthu wabwinobwino. Nditafika zaka 18 aphunzitsi anga anandiuza kuti ndichoke kwathu n’cholinga choti ndisiye chipembedzo cha mayi anga. Aphunzitsiwo ananena kuti andipezera nyumba. Koma ndinawauza kuti sindidzasiya chikhulupiriro changa ndipo sindidzachoka kunyumba kwathu mpaka pamene ndidzaone kuti ndikhoza kudziimira pandekha.

Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene mphunzitsiyu ananena zimenezi, ndinabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Patangopita zaka ziwiri, ndinasamukira m’nyumba inayake yaing’ono. Ndimasangalala kukhala m’nyumba imeneyi chifukwa muli zonse zondithandiza pa vuto langa ndiponso ndikukhala mwaufulu.

Ndinangodabwa Munthu Wina Atandifunsira

Ndakumana ndi mayesero ambiri pa moyo wanga. Tsiku lina ndinangodabwa kuti mnyamata wina wolumala amene ndinkaphunzira naye limodzi sukulu anandifunsira. Poyamba ndinakopeka. Inunso mukudziwa kuti mtsikana aliyense amafuna mnzake woti amange naye banja. Koma sikuti ukwati wathu ukanakhala wosangalatsa chifukwa choti tonse ndi olumala ayi. Vuto lina linali lakuti mnyamatayo sanali wamboni. Tinkasiyana kwambiri zikhulupiriro, zochita ndiponso zolinga. Ndiye zinali zosatheka kukwatirana. Ndinali nditatsimikiza mumtima mwanga kumvera lamulo la Mulungu lakuti tizikwatira kapena kukwatiwa ndi Mkhristu mnzathu basi. (1 Akor. 7:39) Ndiyeno ndinamuuza mnyamatayo mwaulemu kuti zimenezo sizitheka.

Panopa ndikudziwa kuti ndinasankha bwino. Sindikayikira zoti ndidzasangalala kwambiri m’dziko latsopano limene Mulungu watilonjeza. (Sal. 145:16; 2 Pet. 3:13) Ndikufunitsitsa kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndiponso kusadandaula kwambiri kuti ndine wolumala.

Ndimalakalaka tsiku limene ndidzajowe kuchoka panjingayi n’kuyamba kuthamanga ngati kalulu. Pa nthawi imeneyo ndidzafuula kuti: “Ndinali wolumala koma tsopano ndine wabwinobwino, ndipo ndidzakhala chonchi mpaka kalekale.”