Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Amuna Kukula Mwauzimu

Thandizani Amuna Kukula Mwauzimu

Thandizani Amuna Kukula Mwauzimu

“Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”​—LUKA 5:10.

1, 2. (a) Kodi amuna ambiri anatani Yesu atawalalikira? (b) Kodi tikambirana chiyani mu nkhani ino?

PA ULENDO wake wolalikira m’Galileya, Yesu ndi ophunzira ake anakwera ngalawa n’kupita kumalo kopanda anthu. Koma khamu la anthu linawatsatira wapansi. Anthu amene anabwera tsiku limenelo anali “amuna pafupifupi 5,000 osawerengera akazi ndi ana aang’ono.” (Mat. 14:21) Nthawi inanso, anthu ambiri anatsatira Yesu kuti achiritsidwe matenda awo komanso kumumva akuphunzitsa. Panali “amuna 4,000, osawerengera akazi ndi ana aang’ono.” (Mat. 15:38) Zikuoneka kuti amuna ambiri anali m’gulu la anthu amene ankabwera kwa Yesu kuti azidzamvetsera zimene ankaphunzitsa. Yesu anayembekezera kuti anthu ambiri azibwerabe chifukwa chakuti pambuyo pothandiza ophunzira ake kugwira nsomba mozizwitsa, iye anauza wophunzira wake Simon kuti: ‘Kuyambira lero muzisodza anthu amoyo.’ (Luka 5:10) Izi zinatanthauza kuti ophunzira ake anafunika kuponya maukonde awo m’nyanja ya anthu n’kusodza anthu kuphatikizapo amuna ambiri.

2 Masiku anonso, amuna ambiri amasonyeza chidwi ndi uthenga wa m’Malemba umene timawalalikira ndipo timaphunzira nawo Baibulo. (Mat. 5:3) Komabe, amuna ambiri amalephera kukula mwauzimu. Kodi tingawathandize bwanji? Yesu sankangolalikira kwa amuna okhaokha, koma nthawi zina ankafotokoza zinthu zimene amuna a nthawi yake ankada nazo nkhawa. Pogwiritsa ntchito chitsanzo chake, tiyeni tione mmene tingathandizire amuna kuthana ndi zinthu zitatu zimene zimawadetsa nkhawa masiku ano. Zinthu zimenezi ndi (1) nkhawa yofuna kupeza ndalama, (2) kuda nkhawa chifukwa cha zimene ena anganene komanso (3) kudzikayikira.

Nkhawa Yofuna Kupeza Ndalama

3, 4. (a) Kodi amuna ambiri amadera nkhawa za chiyani? (b) N’chifukwa chiyani amuna ena amaganiza kuti kufunafuna ndalama n’kofunika kwambiri kuposa zinthu zauzimu?

3 Mlembi wina anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.” Koma Yesu anamuyankha kuti: “Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.” Izi zinachititsa kuti mlembiyo aiganizirenso nkhani imeneyo. Popeza sankadziwa kumene kuchokere chakudya kapena pamene agone, mlembiyo anada nkhawa ndipo Malemba sasonyeza kuti anadzakhala wotsatira Khristu.​—Mat. 8:19, 20.

4 Amuna ambiri amadera nkhawa kwambiri zinthu zakuthupi poyerekezera ndi zauzimu. Ambiri amafuna kukhala ophunzira kwambiri ndi kupeza ntchito ya malipiro apamwamba ndipo amaona kuti zinthu zimenezi ndi zofunika kwambiri. Iwo amaganiza kuti kufunafuna ndalama ndi kofunika kwambiri kuposa zimene angapeze akamaphunzira Malemba ndiponso kukhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu. Mwina angayamikire zimene angaphunzire m’Baibulo koma ‘nkhawa za m’nthawi ino, komanso chinyengo champhamvu cha chuma,’ zimasokoneza chidwi chawo. (Maliko 4:18, 19) Taonani mmene Yesu anathandizira otsatira ake kuti azitha kuona zomwe zinali zofunika kwambiri pa moyo wawo.

5, 6. Kodi n’chiyani chinathandiza Andireya, Petulo, Yakobo ndi Yohane kudziwa ntchito yofunika kwambiri?

5 Andireya ndi m’bale wake Simoni Petulo ankagwira limodzi ntchito yausodzi. N’chimodzimodzinso ndi Yohane ndi Yakobo omwe ankagwira ntchito ndi bambo awo Zebedayo. Bizinezi ya anthu onsewo inkayenda bwino moti analemba anthu ena antchito. (Maliko 1:16-20) Andireya ndi Yohane atamva koyamba za Yesu kuchokera kwa Yohane M’batizi, anatsimikizira ndi mtima wonse kuti anali atapeza Mesiya. Andireya anapita kukauza m’bale wake Simoni Petulo ndipo mwina n’zimenenso Yohane anachita ndi m’bale wake Yakobo. (Yoh. 1:29, 35-41) M’miyezi yotsatira, onse anayi anali kutsatira Yesu pamene ankalalikira ku Galileya, Yudeya ndi Samariya. Kenako anadzabwereranso ku mabizinezi awo ausodzi. Iwo ankasangalala kumvetsera zinthu zimene Yesu ankaphunzitsa koma sankaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri kuposa ntchito zina.

6 Kenako pa nthawi ina, Yesu anaitana Petulo ndi Andireya kuti amutsatire n’kukhala “asodzi a anthu.” Kodi anthu awiriwa anatani ataitanidwa? Baibulo limati: “Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatira.” Ndi zimenenso Yakobo ndi Yohane anachita. Iwonso “nthawi yomweyo anasiya ngalawa ija ndi bambo awo n’kumutsatira.” (Mat. 4:18-22) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti amuna amenewa ayambe ntchito yolalikira nthawi zonse? Kodi iwo anavomera chifukwa chongotengeka maganizo? Ayi. Anthuwa anali atamva ulaliki wa Yesu miyezi ingapo izi zisanachitike. Anaonanso iye akuchita zozizwitsa, akuchita zinthu mwachilungamo komanso anadzionera okha mmene anthu ankachitira chidwi ndi uthenga umene iye ankalalikira. Choncho zimenezi zinachititsa kuti azikhulupirira kwambiri Yehova.

7. Kodi tingathandize bwanji anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kukhulupirira kuti Yehova amasamalira anthu ake?

7 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pothandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti azikhulupirira kwambiri Yehova? (Miy. 3:5, 6) Izi zimadalira kwambiri njira zimene timaphunzitsira. Pamene tikuphunzitsa, tingachite bwino kunena za malonjezo a Mulungu oti adzatidalitsa kwambiri tikamaika zinthu zaufumu patsogolo. (Werengani Malaki 3:10; Mateyu 6:33.) N’zoona kuti tingagwiritse ntchito malemba posonyeza kuti Yehova amasamalira anthu ake, koma chofunika kwambiri ndi chitsanzo chathu. Kuwafotokozera zimene takumana nazo kungathandize anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti azidalira kwambiri Yehova. Tikhozanso kukambirana nawo nkhani zolimbikitsa za anthu ena zimene tawerenga m’mabuku athu. *

8. (a) N’chifukwa chiyani zili zofunika kuti munthu amene akuphunzira Baibulo ‘alawe kuti aone kuti Yehova ndi wabwino’? (b) Kodi tingathandize bwanji munthu amene tikuphunzira naye Baibulo kuona yekha kuti Yehova ndi wabwino?

8 Kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro cholimba pamafunika zinthu zambiri osati kungowerenga kapena kumva mmene Yehova anadalitsira anthu ena. Munthu amene akuphunzira Baibulo ayeneranso kuona yekha umboni woti Yehova ndi wabwino. Wamasalimo anaimba kuti: “Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.” (Sal. 34:8) Kodi tingathandize bwanji munthu amene timaphunzira naye kuti aone kuti Yehova ndi wabwino? Tiyerekeze kuti wophunzira akudera nkhawa za ndalama komanso akuyesetsa kuti asiye chizolowezi chinachake choipa monga kusuta, kutchova juga kapena kuledzera. (Miy. 23:20, 21; 2 Akor. 7:1; 1 Tim. 6:10) Zingakhale bwino kumuphunzitsa kuti azipempha thandizo la Yehova polimbana ndi chizolowezicho n’cholinga choti aone kuti Yehovayo ndi wabwino. Tingalimbikitsenso wophunzira wathu kuti aziona zinthu zauzimu kukhala zofunika kwambiri. Angachite zimenezi pokhala ndi nthawi yophunzira Baibulo mlungu ndi mlungu komanso kukonzekera ndi kupezeka pa misonkhano yachikhristu. Chikhulupiriro chake chidzalimba kwambiri akamaona Yehova akumudalitsa.

Kuda Nkhawa Chifukwa cha Zimene Ena Anganene

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani Nikodemo komanso Yosefe wa ku Arimateya sananene kwa anthu ena kuti anali ophunzira a Yesu? (b) N’chifukwa chiyani masiku ano amuna ena amaopa kukhala otsatira a Khristu?

9 Amuna ena amadera nkhawa zimene ena anganene, choncho amasankha kusakhala otsatira a Yesu. Mwachitsanzo, Nikodemo komanso Yosefe wa ku Arimateya sanafune kuuza anthu ena kuti ndi ophunzira a Yesu. Iwo ankaopa zimene Ayuda anzawo anganene kapena kuchita akadziwa zimenezo. (Yoh. 3:1, 2; 19:38) Panali chifukwa chomveka chimene ankaopera. Atsogoleriwo ankadana kwambiri ndi Yesu moti ankachotsa musunagoge wina aliyense amene ankakhulupirira Yesu.​—Yoh. 9:22.

10 M’madera ena masiku ano, munthu amene amasonyeza kuti amakonda Baibulo, Mulungu kapena nkhani zachipembedzo, akhoza kuzunzidwa ndi anthu amene amagwira nawo ntchito, anzake kapena achibale ake. M’madera ena ngakhale kungonena zoti ukufuna kusintha chipembedzo, imakhala nkhani yoopsa kwambiri. Zimakhala zovuta kwambiri ngati munthuyo amagwira ntchito yausilikali, yandale kapena ngati ndi wodalirika pa ntchito zina m’deralo. Mwachitsanzo, mwamuna wina wa ku Germany ananena kuti: “Zimene a Mboni za Yehova mumaphunzitsa za Baibulo zimakhala zoona. Koma ineyo nditati ndikhale wa Mboni lero, ndiye kuti pofika mawa aliyense akhala atadziwa. Ndiye nanga anthu okhala nawo pafupi, anthu kuntchito, komanso anthu ena amene amacheza ndi banja lathu? Ee! Ndikaganiza zimenezi ndimaona kuti zingandivute kwambiri.”

11. Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kuti asamaope anthu?

11 Ngakhale kuti atumwi a Yesu sanali amantha, iwo ankaopabe anthu. (Maliko 14:50, 66-72) Kodi Yesu anawathandiza bwanji kuti apitirize kudziwa choonadi ngakhale kuti anthu ankawatsutsa kwambiri? Yesu anachita zinthu zingapo powathandiza kuti adzapirire mayesero amene adzakumane nawo. Iye anawauza kuti: “Ndinu odala anthu akamadana nanu, kukusalani, kukunyozani ndi kukana dzina lanu n’kumanena kuti ndi loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu.” (Luka 6:22) Yesu anauza otsatira ake kuti adzanyozedwa “chifukwa cha Mwana wa munthu.” Koma anawatsimikizira kuti Mulungu adzawathandiza ngati azimupempha kuti awathandize ndiponso kuwalimbikitsa. (Luka 12:4-12) Yesu analimbikitsanso anthu ena kuti azigwirizana ndi ophunzira ake.​—Maliko 10:29, 30.

12. Kodi tingathandize bwanji ophunzira Baibulo kuti asamaope anthu?

12 Nafenso tiyenera kuthandiza munthu amene timaphunzira naye Baibulo kuti asamaope anthu. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kumuthandiza kudziwa zimene angachite anthu ena akamamutsutsa. (Yoh. 15:19) Mwachitsanzo, anthu amene amagwira naye ntchito ndiponso anzake ena angamamufunse mafunso kapena kutsutsa zimene iye amakhulupirira. Choncho mungachite bwino kukambirana naye mayankho osavuta koma ogwira mtima ochokera m’Baibulo. Komanso mungachite bwino kumacheza naye monga mnzanu ndiponso kumuthandiza kuti adziwane ndi Akhristu ena, makamaka amene amakonda zinthu zofanana ndi zimene iye amakonda. Chinthu chofunika kwambiri kuposa zonsezi ndi kumuphunzitsa kupemphera nthawi zonse kuchokera pansi pa mtima. Izi zingamuthandize kuti ayandikire kwambiri Mulungu komanso kuti azimuona kuti iye ndi Thanthwe komanso Pothawirapo pake.​—Werengani Salimo 94:21-23; Yakobo 4:8.

Kudzikayikira

13. N’chifukwa chiyani kudzikayikira kumachititsa kuti amuna ena asafune kuphunzira choonadi?

13 Amuna ena safuna kuchita zinthu zauzimu chifukwa chakuti satha kuwerenga, satha kulankhula momasuka kapena chifukwa chakuti ndi amanyazi. Ena akakhala pa gulu samasuka kufotokoza maganizo awo kapena mmene akumvera. Akaganiza zophunzira, kupereka ndemanga pa misonkhano yachikhristu kapena kulalikira amaona kuti ndi chintchito. M’bale wina ananena kuti: “Ndili wamng’ono ndinkati ndikakhala mu utumiki n’kufika pakhomo la munthu, ndinkanamizira kugogoda kenako n’kuthawa mwakachetechete kuti wina asandimve kapena kundiona. . . . Ndinkachita zimenezi chifukwa ndinkachita manyazi kwambiri ndi ntchito yomayenda khomo ndi khomo.”

14. N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu sanathe kuchiritsa mnyamata yemwe anali ndi chiwanda?

14 Taganizirani mmene ophunzira a Yesu anamvera chifukwa cholephera kuchiritsa mnyamata amene anali ndi chiwanda. Bambo a mnyamatayo anabwera kwa Yesu n’kunena kuti: “[Mwana wanga] ndi wakhunyu ndipo akuvutika kwambiri. Amagwera pamoto kawirikawiri ndiponso amagwera m’madzi kawirikawiri. Ndinabwera naye kwa ophunzira anu, koma alephera kumuchiritsa.” Yesu anatulutsa chiwandacho ndipo mwanayo anachira. Kenako ophunzirawo anapita kwa Yesu n’kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwanda chija?” Yesu anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro chanu. Pakuti ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.” (Mat. 17:14-20) Munthu amafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti athe kulimbana ndi mavuto amene angakhale ngati mapiri. Koma kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu atalephera kukhala ndi chikhulupiriro n’kuyamba kuganizira zimene amalephera? Akhoza kulephera kuthana ndi mavutowo n’kuyamba kumadzikayikira.

15, 16. Kodi tingathandize bwanji munthu amene tikuphunzira naye Baibulo kuti asamadzikayikire?

15 Njira imodzi imene tingathandizire munthu wodzikayikira ndiyo kumulimbikitsa kuganizira kwambiri za Yehova osati kudziganizira yekha. Petulo analemba kuti: “Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake. Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.” (1 Pet. 5:6, 7) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuthandiza ophunzira Baibulo athu kukonda zinthu zauzimu. Munthu amene amakonda zinthu zauzimu amaziona kuti ndi za mtengo wapatali. Amakonda Mawu a Mulungu ndipo amasonyeza “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Amakonda kupemphera. (Afil. 4:6, 7) Amadaliranso Mulungu kuti amupatse mphamvu ndiponso kumulimbitsa mtima. Izi zimamuthandiza kuti athe kulimbana ndi vuto lililonse komanso kuchita bwino utumiki uliwonse umene angalandire.​—Werengani 2 Timoteyo 1:7, 8.

16 Anthu amene timaphunzira nawo amafunika kuwathandiza kuwerenga, kukambirana ndi anthu komanso kukamba bwino nkhani. Ena angamaone ngati sangakwanitse kutumikira Mulungu chifukwa cha zinthu zoipa zimene ankachita asanayambe kuphunzira za Yehova. Anthu ngati amenewa amangofuna kuwathandiza mwachikondi komanso moleza mtima. Yesu ananena kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”​—Mat. 9:12.

‘Sodzani’ Amuna Ambiri

17, 18. (a) Kodi tingatani kuti tizipeza amuna ambiri mu utumiki? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

17 Baibulo lokha ndi limene lili ndi uthenga umene ungathandize kuti munthu akhaledi wosangalala. Choncho m’pofunika kuti tizithandiza amuna ambiri kuti aliphunzire. (2 Tim. 3:16, 17) Ndiyeno kodi tingachite chiyani kuti tizilalikira amuna ambiri? Njira yabwino imene tingachitire zimenezi ndi kumalalikira madzulo, masana a Loweruka kapena Lamlungu apo ayi masiku atchuthi pamene amuna ambiri amakhala pakhomo. Tikafika pakhomo tingachite bwino kupempha ngati tingalankhule ndi abambo. Tikhozanso kulalikira kwa amuna amene timagwira nawo ntchito kapena kwa amuna omwe si mboni koma akazi awo timasonkhana nawo.

18 Pamene tikulalikira kwa munthu aliyense amene takumana naye, sitikayikira zoti anthu amtima wabwino adzatimvetsera. Choncho tiyeni tiyesetse kuthandiza moleza mtima onse amene amakonda choonadi. Komabe kodi tingathandize bwanji amuna amene ndi obatizidwa kuti ayenerere maudindo m’gulu la Mulungu? Nkhani yotsatira idzayankha funso limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Werengani mabuku a Yearbook of Jehovah’s Witnesses komanso mbiri ya moyo wa anthu amene amalembedwa m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi amuna angathandizidwe bwanji kuona kuti zinthu zauzimu n’zofunika kwambiri?

• Kodi tingathandize bwanji atsopano kulimbana ndi vuto loopa anthu?

• N’chiyani chingathandize ena kuti athane ndi vuto lodzikayikira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 25]

Kodi mumayesetsa kuti mupeze amuna n’kuwauza uthenga wabwino?

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi mungathandize bwanji munthu amene mukuphunzira naye kuti akonzekere kulimbana ndi mayesero?