Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Okhulupirika Akale Amene Anatsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu

Anthu Okhulupirika Akale Amene Anatsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu

Anthu Okhulupirika Akale Amene Anatsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu

“Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, watumiza ine ndiponso watumiza mzimu wake.”​—YES. 48:16.

1, 2. Kodi chofunika n’chiyani kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro, ndipo kodi kuphunzira za atumiki okhulupirika akale kungatilimbikitse bwanji?

KUYAMBIRA m’nthawi ya Abele anthu akhala akusonyeza chikhulupiriro, komabe “chikhulupiriro sichikhala ndi anthu onse.” (2 Ates. 3:2) Ndiye n’chifukwa chiyani anthu amakhala ndi chikhulupiriro ndipo n’chiyani chimawathandiza kukhalabe okhulupirika? Tikudziwa kuti munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva kuchokera m’Mawu a Mulungu. (Aroma 10:17) Chikhulupiriro ndi khalidwe limene mzimu wa Mulungu umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Choncho kuti tikhale ndi chikhulupiriro, timafunika mzimu woyera.

2 Kungakhale kulakwitsa kuganiza kuti amuna ndi akazi amene amasonyeza chikhulupiriro, ndiye kuti anabadwa choncho. Baibulo limanena za atumiki okhulupirika omwe anali anthu “monga ife tomwe.” (Yak. 5:17) Iwo anali anthu omwe ankadzikayikira, ankakhala ndi nkhawa ndiponso ankalephera kuchita zinthu zina, “koma anapatsidwa mphamvu,” ndi mzimu wa Mulungu kuti athe kulimbana ndi mavuto. (Aheb. 11:34) Kukambirana mmene mzimu wa Yehova unathandizira anthu amenewa kungatilimbikitse kuti tikhalebe okhulupirika nthawi yovuta ino pamene chikhulupiriro chathu chikuyesedwa kwambiri.

Mzimu wa Mulungu Unathandiza Mose

3-5. (a) Kodi timadziwa bwanji kuti Mose ankachita zinthu mothandizidwa ndi mzimu woyera? (b) Kodi chitsanzo cha Mose chimatiuza chiyani pa nkhani ya mmene Yehova amaperekera mzimu wake?

3 Pa anthu onse amene anali ndi moyo padziko lapansi mu 1513 B.C.E., Mose “anali munthu wofatsa kwambiri.” (Num. 12:3) Mtumiki wa Mulungu wofatsayu anapatsidwa udindo waukulu kwambiri wosamalira mtundu wa Isiraeli. Mzimu wa Mulungu unathandiza Mose kulosera, kuweruza, kulemba mabuku, kutsogolera anthu komanso kuchita zozizwitsa. (Werengani Yesaya 63:11-14.) Komabe pa nthawi ina, Mose anadandaula poona kuti udindo wakewo ndi chimtolo chimene sangathe kuchisenza. (Num. 11:14, 15) Ndiyeno Yehova anatenga “gawo lina la mzimu” umene unali pa Mose n’kuupereka kwa anthu ena 70 kuti amuthandize udindo wakewo. (Num. 11:16, 17) N’zoona kuti Mose ankaona kuti udindo wake ndi wolemera, koma sikuti ankachita zinthu zonse mwa mphamvu yake. N’chimodzimodzinso ndi anthu 70 amene anasankhidwa kuti azimuthandiza.

4 Yehova anapatsa Mose mzimu woyera wokwanira kuti umuthandize kukwanitsa ntchito imene anapatsidwa. Atamuchepetsera ntchito yoti agwire, Mose ankathandizidwabe ndi mzimu woyera wokwanira kuti agwire bwino ntchito yake. Mose sankasowa mzimu woyera wokwanira ndipo amuna 70 enawo sankakhala ndi mzimu woyera wochuluka kwambiri. Yehova amapereka mzimu woyera umene timafuna kuti tikwanitse kum’tumikira pa udindo uliwonse. Iye “akafuna kupereka mzimu wake sachita kuyeza pamuyezo” koma amapereka “kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo.”​—Yoh. 1:16; 3:34.

5 Kodi pali mayesero amene mukupirira? Kodi mumaona kuti maudindo anu akuwonjezeka moti mukusowa nthawi? Kodi mukuvutika kusamalira banja lanu mwakuthupi komanso mwauzimu chifukwa cha kukwera mitengo kwa zinthu kapena matenda? Kodi muli ndi maudindo akuluakulu mu mpingo? Dziwani kuti Mulungu akhoza kukuthandizani ndi mzimu wake kuti mukwanitse kuthana ndi vuto lililonse.​—Aroma 15:13.

Mzimu Woyera Unathandiza Bezaleli

6-8. (a) Kodi mzimu wa Mulungu unathandiza kuti Bezaleli ndi Oholiabu achite chiyani? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Bezaleli ndi Oholiabu ankatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu? (c) N’chifukwa chiyani nkhani ya Bezaleli ili yolimbikitsa?

6 Bezaleli anali mtumiki wa Yehova yemwe analipo m’nthawi ya Mose. Zimene zinachitikira mtumiki ameneyu zingatithandize kumvetsa bwino mmene mzimu wa Mulungu ungatithandizire. (Werengani Ekisodo 35:30-35.) Bezaleli anasankhidwa kuti atsogolere pa ntchito yokonza chihema. Kodi iye anali ndi luso lokhudza ntchitoyi asanasankhidwe? Mwina anali nalo koma zikuoneka kuti ntchito yomwe ankagwira asanayambe izizi inali youmba njerwa za Aiguputo. (Eks. 1:13, 14) Ndiyeno kodi Bezaleli anakwanitsa bwanji ntchito yovuta imeneyi? Yehova ‘anam’patsa mzimu wake kuti akhale wanzeru, wozindikira, wodziwa zinthu, ndi kuti akhale mmisiri waluso pa ntchito ina iliyonse. Anam’patsa mzimuwo kutinso akhale wotha kulinganiza kapangidwe ka zinthu . . . ndiponso wodziwa kupanga mwaluso zinthu zina zilizonse.’ Kaya Bezaleli anali ndi luso lotani poyambapo mfundo ndi yakuti mzimu woyera unamuthandiza. N’chimodzimodzinso ndi Oholiabu. Bezaleli ndi Oholiabu ayenera kuti anamvetsa bwino zimene Mulungu ankafuna pa ntchito yawo chifukwa chakuti anaigwira bwino komanso ankaphunzitsa anthu ena zoyenera kuchita.

7 Umboni wina wosonyeza kuti Bezaleli ndi Oholiabu ankatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu ndi wakuti zimene anapanga zinali zolimba kwambiri moti zinkagwiritsidwabe ntchito patapita zaka 500. (2 Mbiri 1:2-6) Masiku ano anthu amene amapanga zinthu amasayina mayina awo kuti atchuke koma Bezaleli ndi Oholiabu sanachite zimenezo. Iwo anafuna kuti ulemerero wonse wa zimene anapangazo upite kwa Yehova.​—Eks. 36:1, 2.

8 Masiku ano, tikhoza kupemphedwanso kuti tigwire ntchito zina zofuna luso. Mwina tingapemphedwe kuthandiza pa ntchito ya zomangamanga, yosindikiza mabuku, yokonzekera misonkhano ikuluikulu, yopereka chithandizo pakagwa tsoka kapena yokambirana ndi madokotala ndiponso anthu ena ogwira ntchito kuchipatala mfundo za m’Malemba zimene timakhulupirira pa nkhani ya magazi. Nthawi zina ntchito zoterezi zimagwiridwa ndi anthu amene anaphunzira luso lokhudza zimenezi koma nthawi zina amakhala Akhristu ongodzipereka oti alibe luso limenelo. Mzimu wa Mulungu ndi umene umawathandiza kuti akwanitse zimenezi. Kodi inuyo munakanapo zinthu zina m’gulu la Yehova poona kuti pali anthu ena amene angachite bwino kuposa inuyo? Kumbukirani kuti mzimu wa Yehova ukhoza kukuthandizani kuti mugwire bwinobwino ntchito imene Yehova wakupatsani.

Mzimu wa Mulungu Unathandiza Yoswa Kutsogolera Anthu a Mulungu

9. Kodi Aisiraeli anakumana ndi zotani atangotuluka kumene m’dziko la Iguputo, ndipo panali funso lotani?

9 Mzimu wa Mulungu unathandizanso munthu wina amene anakhalako nthawi ya Mose ndi Bezaleli. Anthu a Mulungu atangochoka ku Iguputo Aamaleki anawaukira. Choncho Aisiraeli anayenera kumenya nkhondo yawo yoyamba monga anthu omasulidwa ku ukapolo. Koma iwo sankadziwa kwenikweni za nkhondo. (Eks. 13:17; 17:8) Panafunika munthu woti atsogolere pa nkhondoyo. Koma kodi akanawatsogolera ndani?

10. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Aisiraeli apambane pa nkhondo imene Yoswa ankatsogolera?

10 Yoswa ndi amene anasankhidwa. Kodi iye akanafunsidwa kuti anene ntchito zimene ankazidziwa asanasankhidwe pa udindowu akananena za chiyani? Kodi akananena zoti anagwirapo ntchito ngati kapolo? Kuumba njerwa? Kapena kutola mana? N’zoona kuti agogo a Yoswa a Elisama anali mtsogoleri wa fuko la Efuraimu. Iwo anatsogolera asilikali 108,100 a chigawo chimodzi cha Isiraeli cha mafuko atatu. (Num. 2:18, 24; 1 Mbiri 7:26, 27) Koma Yehova anauza Mose kuti Yoswa ndi amene ayenera kutsogolera asilikali a Isiraeli pokagonjetsa adani. Sanasankhe Elisama kapena mwana wake Nuni. Nkhondoyi inatenga pafupifupi tsiku lonse lathunthu. Chifukwa chakuti Yoswa anali womvera kwambiri ndipo ankafunitsitsa kutsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, Aisiraeli anapambana nkhondo.​—Eks. 17:9-13.

11. N’chiyani chingatithandize kuti nafenso tikwanitse kuchita bwino utumiki wopatulika ngati mmene anachitira Yoswa?

11 Mose atamwalira, Yoswa ndi amene anali kutsogolera ana a Aisiraeli. Iye anali munthu “wodzazidwa ndi mzimu wa nzeru.” (Deut. 34:9) Mzimu woyera sunamuchititse kuti azilosera kapena kuchita zozizwitsa ngati mmene zinalili ndi Mose. M’malomwake unathandiza Yoswa kutsogolera Aisiraeli pa nkhondo yogonjetsa dziko la Kanani. Nafenso masiku ano tikhoza kumaona ngati kuti sitingakwanitse kuchita mautumiki ena opatulika. Koma mofanana ndi Yoswa, zinthu zikhoza kutiyendera bwino ngati titsatira malangizo a Mulungu.​—Yos. 1:7-9.

“Gidiyoni Anagwidwa ndi Mzimu wa Yehova”

12-14. (a) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene zinachitikira Aisiraeli kuti kagulu kawo ka asilikali 300 kanagonjetsa chigulu cha asilikali a Amidiyani? (b) Kodi Yehova analimbikitsa bwanji Gidiyoni? (c) Kodi Mulungu angatithandize bwanji masiku ano?

12 Yoswa atamwalira, Yehova anapitiriza kuonetsa mmene mphamvu zake zimathandizira anthu okhulupirika. M’Baibulo, buku la Oweruza lili ndi nkhani zambiri za anthu amene ‘anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu ndipo analimba mtima.’ (Aheb. 11:34) Mulungu anathandiza Gidiyoni ndi mzimu woyera kuti amenyere nkhondo anthu ake. (Ower. 6:34) Asilikali a Gidiyoni anasonkhana koma anali ochepa powayerekeza ndi asilikali a adani awo. Msilikali mmodzi wachiisiraeli anayenera kumenyana ndi asilikali 4 achimidiyani. Koma Yehova ankaona kuti asilikali achiisiraeliwo anali ochuluka kwambiri. Choncho anauza Gidiyoni kuti achepetse asilikaliwo maulendo awiri mpaka kufika poti msilikali mmodzi anafunika kumenyana ndi asilikali 450. (Ower. 7:2-8; 8:10) Asilikali ochepawa ndi amene Yehova anaona kuti ayenera kupita kokamenya nkhondo. Choncho panalibe munthu amene akanadzitama kuti ndi amene wachititsa kuti apambane.

13 Gidiyoni ndi gulu lake la asilikali anali okonzeka kukamenya nkhondo. Kodi inuyo mukanakhala m’kagulu kakang’ono ka asilikaliwo, mukanalimba mtima poona kuti asilikali onse amantha kapena ofooka sapita nanu ku nkhondo? Kapena kodi mukanaopa poganiza kuti zinthu sizikakutherani bwino? N’zosachita kufunsa kuti Gidiyoni ankakhulupirira Mulungu. Iye anachita zimene anauzidwa. (Werengani Oweruza 7:9-14.) Yehova sanakwiye chifukwa chakuti Gidiyoni anapempha kuti amuonetse chizindikiro chotsimikizira kuti ali naye. (Ower. 6:36-40) M’malomwake, Mulungu analimbitsa chikhulupiriro cha Gidiyoni.

14 Mphamvu zopulumutsa za Yehova zilibe malire. Iye akhoza kupulumutsa anthu ake pa vuto lililonse ndipo akhoza kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito anthu ooneka ofooka kapena ooneka ngati sangathandize aliyense. Nthawi zina tingadzimve kuti adani athu ndi ambiri ndipo zinthu sizitiyendera bwino. Sitiyembekezera kuti Mulungu atipatsa chizindikiro chozizwitsa ngati mmene anachitira ndi Gidiyoni. Koma Mulungu amatitsogolera ndi kutilimbikitsa kudzera m’Mawu ake ndiponso mpingo umene umatsogoleredwa ndi mzimu wake. (Aroma 8:31, 32) Malonjezo amene Yehova wapereka amatitsimikizira kuti iye ndiyedi Mthandizi wathu wachikondi.

“Mzimu wa Yehova Unabwera pa Yefita”

15, 16. N’chifukwa chiyani mwana wa Yefita anavomera kudzipereka ndipo zimenezi zingalimbikitse bwanji makolo?

15 Tiyeni tionenso chitsanzo china. Pa nthawi imene Aisiraeli ankafuna kumenyana ndi Aamoni, mzimu wa Yehova “unabwera pa Yefita.” Chifukwa chakuti Yefita ankafunitsitsa kupambana nkhondoyo kuti dzina la Yehova lilemekezedwe, iye anachita lumbiro lovuta kwambiri kukwaniritsa. Iye analumbira kuti Mulungu akamuthandiza kugonjetsa Aamoni, munthu amene akayambe kutuluka pakhomo kukamuchingamira akamabwerera kunyumba akam’pereka kwa Yehova. Pobwerera kokagonjetsa Aamoni, mwana wake wamkazi ndi amene anathamanga kukamuchingamira. (Ower. 11:29-31, 34) Kodi Yefita anadabwa nazo zimenezi? Ayenera kuti sanadabwe chifukwa chakuti iye anali ndi mwana mmodzi yekha. Iye anakwaniritsa lumbiro lake kwa Yehova popereka mwana wakeyo kuti azikamutumikira kukachisi wake ku Silo. Popeza anali mtumiki wa Yehova wokhulupirika, mwana wa Yefitayo anaona kuti ndi bwino kuchitadi zimene bambo ake analumbira. (Werengani Oweruza 11:36.) Mzimu wa Yehova unathandiza anthu awiri onsewa.

16 Kodi zinatheka bwanji kuti mwana wa Yefitayu akhale ndi mtima wodzipereka chonchi? N’zoonekeratu kuti iye ankaona khama la bambo ake ndiponso kudzipereka kwawo kwa Mulungu. Zimenezi zinalimbitsa chikhulupiriro chake. Makolo, muyenera kudziwa kuti ana anu amaona chitsanzo chanu. Zimene mumasankha zimasonyeza kuti mumakhulupirira zimene mumanena. Ana anu amamva mapemphero anu ochokera pansi pa mtima, zimene mumaphunzitsa mogwira mtima ndiponso amaona chitsanzo chanu cha kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Akamaona zimenezi amakhala ndi mtima wofuna kutumikira Yehova. Zimenezi zimakhala zosangalatsa.

“Mzimu wa Yehova Unayamba Kugwira Ntchito” pa Samisoni

17. Kodi Samisoni anachita chiyani mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu?

17 Munthu wina amene anathandizidwa ndi mzimu wa Mulungu ndi Samisoni. Pa nthawi imene Aisiraeli anali akapolo a Afilisiti, “mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito” pa Samisoni kuti awapulumutse. (Ower. 13:24, 25) Mulungu anathandiza Samisoni kukhala ndi mphamvu zoposa wina aliyense. Afilisiti atauza Aisiraeli ena kuti agwire Samisoni, “mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo zingwe zimene anam’manga nazo manja zija zinaduka ngati ulusi wowauka ndi moto, moti zinadukaduka ndi kugwa.” (Ower. 15:14) Nthawi ina, Samisoni sanachite zinthu mwanzeru ndipo izi zinachititsa kuti thupi lake lifooke. Koma ngakhale pa nthawi imeneyo, Samisoni anapatsidwa mphamvu “mwa chikhulupiriro.” (Aheb. 11:32-34; Ower. 16:18-21, 28-30) Mzimu wa Yehova unkachititsa Samisoni kuchita zinthu zodabwitsa chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Zochitika zakale zimenezi zimatilimbikitsa kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero?

18, 19. (a) Kodi nkhani ya Samisoni imatitsimikizira chiyani? (b) Kodi kuphunzira nkhani za atumiki akale a Mulungu m’nkhani ino kwakuthandizani bwanji?

18 Mofanana ndi Samisoni, nafenso timadalira mzimu woyera womwewo. Timadalira mzimuwo pogwira ntchito ‘yolalikira kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira’ imene Yesu anapatsa otsatira ake. (Mac. 10:42) Kuti tikwanitse kugwira ntchito imeneyi, timafunikira maluso amene mwina mwachibadwa tilibe. Ndife osangalala kuti Yehova amatipatsa mzimu wake kuti utithandize kuchita zinthu zosiyanasiyana zimene timauzidwa kuchita. Choncho tikamatumikira Yehova, timakhala ndi maganizo a mneneri Yesaya yemwe anati: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, watumiza ine ndiponso watumiza mzimu wake.” (Yes. 48:16) Mzimu wa Mulungu ndi umene umatilimbikitsa kulalikira. Timafunitsitsa kulalikira chifukwa chakuti timadziwa zoti Yehova adzatithandiza kukhala ndi luso ngati mmene anachitira ndi Mose, Bezaleli ndi Yoswa. Timatenga “lupanga la mzimu lomwe ndilo mawu a Mulungu” podziwa kuti Yehova atipatsa mphamvu ngati mmene anachitira ndi Gidiyoni, Yefita ndiponso Samisoni. (Aef. 6:17, 18) Ngati timadalira Yehova kuti atithandize kuthana ndi mavuto, tikhoza kukhala amphamvu kwambiri ngati Samisoni koma mwauzimu.

19 Taona kuti Yehova amadalitsa anthu amene amakhala olimba mtima pa kulambira koona. Chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri tikamalola mzimu woyera wa Mulungu kutitsogolera pa moyo wathu. Zingakhale bwinonso kukambirana nkhani zina zochititsa chidwi zimene zalembedwa m’Malemba Achigiriki. Tidzaona mmene mzimu wa Yehova unathandizira atumiki a Mulungu pasanafike pa Pentekosite mu 33 C.E. komanso pambuyo pake. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zimenezi.

N’chifukwa chiyani n’zolimbikitsa kudziwa mmene mzimu wa Mulungu unathandizira anthu awa?

• Mose

• Bezaleli

• Yoswa

• Gidiyoni

• Yefita

• Samisoni

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Mzimu wa Mulungu ungatichititse kuti tikhale ndi mphamvu mwauzimu ngati mmene unachitira ndi Samisoni mwakuthupi

[Chithunzi patsamba 21]

Makolo, dziwani kuti chitsanzo chanu chabwino chingathandize ana anu kukhala ndi maganizo otumikira Yehova