Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mzimu wa Mulungu Unkatsogolera Akhristu Oyambirira Ndipo Ukutsogoleranso Akhristu Masiku Ano

Mzimu wa Mulungu Unkatsogolera Akhristu Oyambirira Ndipo Ukutsogoleranso Akhristu Masiku Ano

Mzimu wa Mulungu Unkatsogolera Akhristu Oyambirira Ndipo Ukutsogoleranso Akhristu Masiku Ano

“Ntchito zonsezi, mzimu umodzimodziwo ndiwo umazichita.”​—1 AKOR. 12:11.

1. Kodi m’nkhani ino tikambirana chiyani?

TSIKU la Pentekosite wa m’chaka cha 33 C.E., ndi tsiku losaiwalika chifukwa panachitika zinthu zapadera. (Mac. 2:1-4) Pa tsiku limeneli, Mulungu anayamba kugwiritsa ntchito mzimu woyera m’njira yatsopano kuti atsogolere anthu ake. M’nkhani yapita ija tinakambirana mmene mzimu wa Mulungu unathandizira anthu okhulupirika akale kugwira ntchito zovuta kwambiri. Koma kodi njira imene mzimu wa Mulungu unathandizira anthu Chikhristu chisanayambe inasiyana bwanji ndi njira imene unathandizira anthu Chikhristu chitangoyamba? Nanga Akhristu masiku ano angathandizidwe bwanji ndi mzimu wa Mulungu? Tiyeni tikambirane zimenezi.

“Ndinetu Kapolo wa Yehova!”

2. Kodi Mariya anaona bwanji umboni wakuti mzimu woyera ulipo?

2 Mariya anali nawo m’gulu la anthu amene anasonkhana m’chipinda cham’mwamba ku Yerusalemu pamene analandira mzimu woyera. (Mac. 1:13, 14) Koma zaka zoposa 30 izi zisanachitike, Mariya anali kuona ntchito ya mzimu wa Yehova m’njira yapadera kwambiri. Mwachitsanzo, Yehova anasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba kubwera padziko lapansi. Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti Mariya akhale ndi pakati ngakhale kuti anali namwali.​—Mat. 1:20.

3, 4. Kodi Mariya anasonyeza mtima wotani ndipo tingamutsanzire bwanji?

3 N’chifukwa chiyani Mulungu anasankha Mariya kulandira mwayi wamtengo wapatali umenewu? Mngelo atafotokoza kuti Mariya adzabereka Mwana wa Mulungu, Mariya anati: “Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” (Luka 1:38) Mawu a Mariyawa akusonyeza mtima umene anali nawo womwe Mulungu anali atauoneratu. Zimene anayankha nthawi yomweyo zikusonyeza kuti anali wokonzeka kuchita chifuniro cha Mulungu pa nkhaniyi. Iye sanadere nkhawa zimene anthu ena angaganize iye akakhala ndi pakati. Sanaderenso nkhawa zimene Yosefe anganene. Ponena kuti anali kapolo wa Yehova, Mariya anasonyeza kuti ankakhulupirira Mulungu ndi mtima wonse monga Mbuye wake.

4 Kodi nthawi zina mumaona kuti maudindo amene muli nawo m’gulu la Mulungu simungakwanitse kuwasamalira? Aliyense wa ife ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova adzasamalira zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake? Kodi ndimasonyezadi mtima wofuna kutumikira Mulungu?’ Dziwani kuti Mulungu amapereka mzimu wake kwa anthu amene amamukhulupirira ndi mtima wonse komanso amene amazindikira chifuniro chake.​—Mac. 5:32.

Petulo Anathandizidwa ndi Mzimu Woyera

5. Kodi Petulo anali ataona kale mzimu woyera ukugwira ntchito m’njira zotani tsiku la Pentekosite mu 33 C.E. lisanafike?

5 Mofanana ndi Mariya, nayenso Petulo anali ataona mzimu woyera wa Mulungu ukugwira ntchito, tsiku la Pentekosite mu 33 C.E. lisanafike. Yesu anapereka kwa iye limodzi ndi atumwi ena mphamvu yotulutsa ziwanda. (Maliko 3:14-16) Ngakhale kuti Malemba safotokoza zambiri pa nkhaniyi, zikuoneka kuti Petulo anagwiritsa ntchito mphamvu imeneyi. Mphamvu ya Mulungu inaonekeranso pamene Yesu anaitana Petulo kuti ayende panyanja ya Galileya ndipo Petulo anayendadi. (Werengani Mateyu 14:25-29.) N’zodziwikiratu kuti Petulo ankadalira mzimu woyera kuti umuthandize kuchita zinthu zamphamvu. Koma kuyambira pa Pentekosite, mzimuwo unalinso kudzathandiza Petulo ndi ophunzira anzake m’njira zinanso.

6. Kodi mzimu wa Mulungu unathandiza Petulo kuchita chiyani pa Pentekosite m’chaka cha 33 C.E. ndiponso pambuyo pake?

6 Pa nthawi ya Chikondwerero cha Pentekosite mu 33 C.E., Petulo ndi anzake anapatsidwa mphamvu zozizwitsa moti anatha kulankhula zinenero za alendo amene anabwera ku Yerusalemu. Kenako Petulo anatsogolera polankhula ndi khamu la anthu limene linasonkhana. (Mac. 2:14-36) Nthawi zina Petulo ankachita mantha komanso ankachita zinthu mopupuluma. Koma atalandira mzimu woyera anayamba kulalikira molimba mtima ngakhale kuti ena ankamuzunza ndiponso kumuopseza kuti asiye. (Mac. 4:18-20, 31) Mulungu anamuthandizanso kuti adziwe zinthu zachinsinsi. (Mac. 5:8, 9) Iye anapatsidwanso mphamvu youkitsa anthu.​—Mac. 9:40.

7. Kodi ndi zinthu ziti zimene Yesu ankaphunzitsa zimene Petulo anayamba kuzimvetsa pambuyo poti wadzozedwa?

7 Tsiku la Pentekosite lisanafike, Petulo anali atamvetsa mfundo zambiri zachoonadi zimene Yesu ankaphunzitsa. (Mat. 16:16, 17; Yoh. 6:68) Komabe panali mfundo zina zimene Yesu anaphunzitsa zomwe Petulo anali asanazimvetsebe tsikuli lisanafike. Mwachitsanzo, Petulo sankadziwa zoti Yesu adzaukitsidwa ndi thupi lauzimu pakapita masiku atatu. Sankadziwanso zoti Khristu azidzalamulira ali kumwamba. (Yoh. 20:6-10; Mac. 1:6) Petulo sankadziwa n’komwe zoti anthu ena adzakhala ndi thupi lauzimu n’kumakalamulira mu Ufumu wakumwamba. Koma atabatizidwa ndi mzimu woyera n’kukhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba, anayamba kumvetsa mfundo zimene Yesu anaphunzitsa pa nkhani imeneyi.

8. Kodi odzozedwa limodzi ndi “nkhosa zina” ali ndi mwayi wodziwa zinthu ziti?

8 Mfundo zimene ophunzira a Yesu ankalephera kuzimvetsa, anayamba kuzimvetsa atalandira mzimu woyera. Olemba Malemba Achigiriki Achikhristu anauziridwa kulemba mfundo zochititsa chidwi zofotokoza cholinga cha Yehova. (Aef. 3:8-11, 18) Masiku ano, Akhristu odzozedwa limodzi ndi “nkhosa zina” amadyera limodzi mwauzimu n’kumaphunzira mfundo zachoonadi zimenezi. (Yoh. 10:16) Kodi mumaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kwambiri kuthandizidwa ndi mzimu woyera kuti mudziwe ndiponso kumvetsa Mawu a Mulungu?

Paulo ‘Anadzazidwa ndi Mzimu Woyera’

9. Kodi ndi zinthu ziti zomwe Paulo anakwanitsa kuchita mothandizidwa ndi mzimu woyera?

9 Patapita pafupifupi chaka chimodzi kuchokera pa Pentekosite mu 33 C.E., munthu winanso analandira mphatso ya Mulungu ya mzimu woyera. Munthu wake anali Saulo yemwe anadzakhala Paulo. Mzimu unamuthandizanso m’njira imene nafenso tikupindula nayo masiku ano. Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba mabuku 14 a Baibulo. Mofanana ndi Petulo, mzimu wa Mulungu unathandiza Paulo kumvetsa ndiponso kulemba momveka bwino za chiyembekezo chopita kumwamba n’kukakhala ndi moyo wosakhoza kufa kapena kuwonongeka. Mothandizidwa ndi mzimu woyera, Paulo anachiritsa odwala, kutulutsa ziwanda ndiponso kuukitsa akufa. Koma Paulo anapatsidwa mphamvu ndi mzimu woyera kuti achite zinthu zina zofunika kwambiri. Atumiki a Mulungu amalandiranso mphamvu ya mzimu woyera umenewu masiku ano ngakhale kuti salandira mozizwitsa.

10. Kodi mzimu woyera unathandiza bwanji Paulo kulankhula molimba mtima?

10 Paulo “atadzazidwa ndi mzimu woyera” anadzudzula mwamphamvu munthu wamatsenga. Kodi zimenezi zinakhudza bwanji bwanamkubwa wa ku Kupuro amene analipo? Iye analandira choonadi chifukwa “anadabwa kwambiri ndi zimene anaphunzira zokhudza Yehova.” (Mac. 13:8-12) Apa zikuonekeratu kuti Paulo ankadziwa kuti mzimu woyera wa Mulungu ndi umene ungamuthandize kuti athe kulankhula choonadi. (Mat. 10:20) Kenako iye anapempha Akhristu a mpingo wa ku Efeso kuti azimupempherera kuti am’patse mphamvu yoti ‘azitha kulankhula.’​—Aef. 6:18-20.

11. Kodi Paulo ankatsogoleredwa bwanji ndi mzimu wa Mulungu?

11 Sikuti mzimu woyera unkangomuthandiza Paulo kulankhula. Nthawi zina unkamuletsa kulankhula m’madera ena. Paulo ankatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu pa maulendo ake aumishonale. (Mac. 13:2; Werengani Machitidwe 16:6-10.) Yehova akutsogolerabe ntchito yolalikira pogwiritsa ntchito mzimu wake. Mofanana ndi Paulo, atumiki onse omvera a Yehova amayesetsa kulengeza choonadi molimba mtima ndiponso mwakhama. Masiku ano, Mulungu akutitsogolera ndi mzimu wake mosiyana ndi mmene ankachitira m’nthawi ya Paulo. Koma ndife otsimikiza kuti Yehova akugwiritsa ntchito mzimu wake kuti anthu onse ofunitsitsa alandire choonadi.​—Yoh. 6:44.

“Ntchito Zosiyanasiyana”

12-14. Kodi mzimu wa Mulungu umagwira ntchito mofanana kwa atumiki ake onse? Fotokozani.

12 Timalimbikitsidwa kwambiri tikamawerenga nkhani zosonyeza mmene Yehova ankadalitsira mpingo wa Akhristu odzozedwa, utangoyamba. Kumbukirani zimene Paulo anauziridwa kulemba m’kalata yake yopita kwa Akorinto zokhudza mphatso za mzimu zosiyanasiyana zimene anthu analandira m’nthawi yake. Iye anati: “Tsopano mphatso zilipo zamitundumitundu, koma mzimu ndi umodzi, ndipo pali mautumiki osiyanasiyana, koma Ambuye ndi mmodzi. Palinso ntchito zosiyanasiyana, koma Mulungu amene amachita ntchito zonsezo mwa anthu onse ndi mmodzi.” (1 Akor. 12:4-6, 11) Apa mfundo ndi yakuti mzimu woyera umagwira ntchito pa atumiki a Mulungu m’njira zosiyanasiyana mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Akhristu a “kagulu ka nkhosa” ndiponso a “nkhosa zina” angalandire mzimu woyera. (Luka 12:32; Yoh. 10:16) Koma sikuti umachititsa anthu mu mpingo kuchita zinthu zofanana.

13 Mwachitsanzo, akulu amaikidwa ndi mzimu woyera. (Mac. 20:28) Koma sikuti Akhristu onse amene adzozedwa ndi mzimu woyera ndi akulu mu mpingo. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Mfundo ndi yakuti mzimu wa Mulungu umagwira ntchito pa anthu mu mpingo m’njira zosiyanasiyana.

14 Mzimu umene umachititsa Akhristu odzozedwa kutsimikiza kuti ndi ana a Mulungu ndi umenenso Yehova anagwiritsa ntchito poukitsa Mwana wake wobadwa yekha kuti akakhale ndi moyo wosafa kumwamba. (Werengani Aroma 8:11, 15.) Mzimu umenewu ndi umene Yehova anagwiritsanso ntchito polenga zinthu zonse. (Gen. 1:1-3) Yehova anagwiritsanso ntchito mzimu woyera womwewu kuti Bezaleli agwire ntchito yokhudza chihema, kuti Samisoni akhale wamphamvu kwambiri ndiponso kuti Petulo ayende pamadzi. Tisaganize kuti kukhala ndi mzimu wa Mulungu n’kofanana ndi kudzozedwa ndi mzimuwu. Kudzozedwa ndi mzimu woyera ndi ntchito yapadera imodzi yokha imene mzimuwu umagwira ndipo Mulungu ndi amene amasankha anthu oti adzozedwe.

15. Kodi kubatiza anthu ndi mzimu woyera kudzapitirira mpaka kalekale? Fotokozani.

15 Mzimu woyera wa Mulungu wakhala ukugwira ntchito m’njira zosiyanasiyana pa atumiki a Yehova okhulupirika kwa nthawi yonse imene Mulungu wakhala ndi atumiki okhulupirika. Choncho wakhala ukugwira ntchito kwa zaka masauzande anthu asanayambe kudzozedwa nawo. Pa Pentekosite mu 33 C.E., anthu anayamba kudzozedwa ndi mzimu koma sikuti zimenezi zidzapitirira mpaka kalekale. Kubatizidwa ndi mzimu kudzatha koma mzimu woyera udzapitiriza kutsogolera anthu a Mulungu n’cholinga choti apitirize kuchita chifuniro chake mpaka kalekale.

16. Kodi mzimu woyera ukuthandiza atumiki a Mulungu kuchita chiyani masiku ano?

16 Kodi ndi ntchito iti imene ikuchitika padziko lapansi motsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Yehova? Lemba la Chivumbulutso 22:17 limati: “Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: ‘Bwera!’ Aliyense wakumva anene kuti: ‘Bwera!’ Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.” Mzimu wa Mulungu umalimbikitsa Akhristu masiku ano kuti aziitana munthu “aliyense amene akufuna” kuti amwe madzi a moyo. Akhristu odzozedwa ndi amene akutsogolera pa ntchito imeneyi. Koma nawonso a nkhosa zina amagwira ntchito yoitana anthu imeneyi. Mzimu woyera umathandiza anthu a magulu awiri onsewa kugwira bwino ntchitoyi. Anthu a m’magulu awiriwa anasonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova pobatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” (Mat. 28:19) Onsewa amalola kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu pa moyo wawo ndipo amasonyeza makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Mofanana ndi Akhristu odzozedwa, a nkhosa zina amalola mzimu wa Mulungu kuwathandiza. Mothandizidwa ndi mzimuwo amayesetsa kutsatira mfundo zolungama za Yehova kuti akhale oyera.​—2 Akor. 7:1; Chiv. 7:9, 14.

Pitirizani Kupempha Mzimu Woyera

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi mzimu wa Mulungu?

17 Choncho kaya Mulungu wakupatsani chiyembekezo cha moyo wosatha kumwamba kapena padziko lapansi, Yehova akhoza kukupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti mukhalebe okhulupirika ndiponso mukalandire mphoto yanuyo. (2 Akor. 4:7) N’zoona kuti anthu ena angakunyozeni mukamalalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Koma musaiwale kuti “ngati anthu akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala chifukwa zikusonyeza kuti mzimu waulemerero, umene ndi mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.”​—1 Pet. 4:14.

18, 19. Kodi Yehova adzakuthandizani bwanji pogwiritsa ntchito mzimu wake, ndipo kodi inuyo mwatsimikiza kuchita chiyani pa nkhani imeneyi?

18 Mulungu amapereka mwaulere mzimu woyera kwa anthu amene amapempha kuchokera pansi pa mtima. Ungakuthandizeni kukhala ndi maluso ndiponso mtima wofuna kuchita zonse zimene mungathe mu utumiki wa Yehova. “Mulungu amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.” Mphatso yamtengo wapatali kwambiri ya mzimu woyera ndiponso khama lathu zikhoza kutithandiza “kugwira mwamphamvu mawu amoyo” ndiponso kupitiriza “kukonza chipulumutso [chathu], mwamantha ndi kunjenjemera.”​—Afil. 2:12, 13, 16.

19 Choncho, muzidalira kwambiri mzimu wa Mulungu ndiponso kuchita khama kwambiri pa utumiki uliwonse. Sonyezani luso lanu lonse pa ntchito imene mwapatsidwa ndipo muzidalira Yehova kuti akuthandizeni. (Yak. 1:5) Iye adzakupatsani zinthu zonse zimene zingakuthandizeni kumvetsa Mawu ake, kuthana ndi mavuto komanso kulalikira uthenga wabwino. Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.” (Luka 11:9, 13) Izi zikuphatikizapo kupempha mzimu woyera. Choncho pitirizani kupempha Yehova kuti mukhale m’gulu la atumiki ake otsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.

Kodi Mungafotokoze?

• Mofanana ndi Mariya, kodi tiyenera kusonyeza mtima wotani kuti tilandire madalitso?

• Kodi mzimu wa Mulungu unatsogolera bwanji Paulo?

• Kodi mzimu wa Mulungu ukutsogolera bwanji atumiki a Mulungu masiku ano?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 24]

Mzimu wa Mulungu unathandiza Paulo kulankhula mwamphamvu kwa munthu wamatsenga

[Chithunzi patsamba 26]

Masiku ano, mzimu woyera umagwira ntchito kwa Akhristu amene adzapite kumwamba ndi amene adzakhale padziko lapansi