Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kale Lathu

Kusunga Zinthu Zathu Zamtengo Wapatali

Kusunga Zinthu Zathu Zamtengo Wapatali

ANTHU a Yehova ali ndi mbiri yochititsa chidwi kwambiri pa nkhani yomutumikira. Mbiri yochititsa chidwiyi tingaipeze m’mabuku athu, zithunzi, makalata, kuchokera kwa anthu amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali, kuchokera ku zinthu zakale zokhudza kulambira kwathu, ntchito yathu yolalikira kapena kuchokera ku mbali zina za mbiri yathu. Koma kodi kusunga zinthu zakalezi ndiponso kufufuza za mbiri yathu kuli ndi phindu lotani? Kale mitu ya mabanja achiisiraeli ankayenera kudziwitsa ana awo za malamulo ndiponso ntchito zotamandika za Yehova n’cholinga choti anawo “azidzadalira Mulungu.”​—Sal. 78:1-7.

Kuyambira kale, kufufuza m’zinthu zakale kwathandiza pokwaniritsa cholinga cha Yehova. Mwachitsanzo, pamene adani anayesa kuletsa ntchito yomanganso kachisi ku Yerusalemu, Mfumu Dariyo inalamula kuti anthu afufuze m’zolemba zakale zosungidwa ku likulu la Mediya ku Ekibatana. Kumeneko kunapezeka chikalata chochokera kwa Mfumu Koresi chololeza kuti Ayuda akagwire ntchito yomangayi ku Yerusalemu. (Ezara 6:1-4, 12) Chifukwa chopeza chikalatachi, kachisi anamangidwanso mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Nayenso Luka anagwiritsa ntchito zolemba zakale polemba uthenga wake wabwino. Iye anafufuza “zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi.”​—Luka 1:1-4.

Bungwe Lolamulira lili ndi chidwi kwambiri m’mbiri ya gulu lathu. M’bale wina wa m’Bungwe Lolamulira anasonyeza kuti m’pofunika kwambiri kuti tizisunga, kulemba ndiponso kuuza anthu ena za zinthu zakale zochokera m’mbiri ya gulu lathu la Mboni za Yehova. Iye anati, “Kuti tidziwe kumene tikupita, tiyenera kudziwa kumene tachokera.” Choncho dipatimenti yatsopano yoona zosunga zinthu zakale yakhazikitsidwa ku likulu lathu ku Brooklyn, New York ndipo Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku ndi imene imaiyang’anira.

ZITHUNZI NDIPONSO ZINTHU ZINA ZAMTENGO WAPATALI

Zinthu zakale zimaiwalika pakapita nthawi ndipo ambiri a ife timadandaula kuti sitinasunge zinthu za banja lathu zomwe zingatikumbutse zakalezo. M’dipatimenti yatsopanoyi, anthu akugwira mwakhama ntchito yosunga ndiponso kulemba zinthu zotikumbutsa kale lathu losangalatsa. Zithunzi zosungidwa m’dipatimentiyi tingazione ngati zithunzi zakale za banja lathu. M’dipatimentiyi akusunganso mabuku akale, nkhani zosangalatsa zosimbidwa ndi anthu omwe anaona okha zochitika zakale ndiponso zinthu zina zambiri zamtengo wapatali. Zinthu zimenezi zili ngati chuma chathu ndipo zimatithandiza kudziwa za mbiri ya gulu lathu la Mboni za Yehova. Zimatithandizanso kuyembekeza ndi chikhulupiriro chonse tsogolo labwino limene banja lathu lauzimu lidzakhale nalo.

Tikufuna kuti mudziwe zimene zikusungidwa m’dipatimenti yatsopanoyi choncho m’magazini ena a Nsanja ya Olonda yophunzira muzikhala nkhani yatsopano yakuti “Kale Lathu.” Mwachitsanzo, m’magazini yotsatira mudzakhala nkhani yokhala ndi zithunzi imene idzafotokoza za kanjinga konyamulira sutikesi. Idzayankhanso mafunso awa: Kodi ndani ankakagwiritsa ntchito? Nanga ankakagwiritsa ntchito liti? Kodi ankakagwiritsa ntchito yotani?

Mofanana ndi zithunzi zakale za banja lathu, zinthu zimene zikusungidwa m’dipatimentiyi zimatithandiza kudziwa zambiri zokhudza mbiri yathu ndiponso anthu auzimu a m’mbuyomu. Zimatidziwitsa za chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima kwa abale athu akale komanso za zinthu zosangalatsa ndiponso zovuta zimene anthu amakumana nazo potumikira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi. Zimatithandizanso kudziwa mmene Mulungu amatsogolerera ndiponso kuthandiza anthu ake nthawi zonse. (Deut. 33:27) Ndife otsimikiza kuti Yehova adzadalitsa khama lathu pa ntchito yosunga bwino zinthu zochokera m’mbiri ya gulu lathu. Adzatero chifukwa chodziwa kuti zimenezi zingatilimbikitse ndiponso kutithandiza kukhala ogwirizana pochita chifuniro chake.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 31]

Tione Zimene Amachita

Alembi, ojambula zithunzi, ofufuza ndiponso ena amagwiritsa ntchito zinthu zakale pokonza mabuku achikhristu, ma DVD kapena zinthu zina zophunzitsa Baibulo. Choncho a m’dipatimenti yatsopanoyi amayesetsa kwambiri kusonkhanitsa ndiponso kusunga bwino zinthu zakale zosiyanasiyana. Amazipeza kuchokera ku maofesi a nthambi, madipatimenti ena a Beteli, mipingo, anthu ndiponso mabungwe a dzikoli. Tiyeni tione zina zimene amachita m’dipatimentiyi.

Amalandira Zinthu ndi Kuziona Bwinobwino: Nthawi ndi nthawi, dipatimentiyi imalandira zinthu zosiyanasiyana. Zinthu zambiri zimachokera kwa anthu amene banja lawo lakhala likutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri. Anthuwo amapereka mokoma mtima zinthu zimenezi kapena amakazisiya ku Beteli mongowabwereka. Kenako akazilandira ku Beteli, amaziona bwinobwino ndiponso kuziyerekeza ndi zinthu zina. Zimenezi zimathandiza kuti tidziwe za mbiri yathu ndiponso anthu a m’mbiriyo.

Amalemba Mndandanda: M’dipatimentiyi muli zinthu masauzande ambiri ndipo zina ndi zakale kwambiri moti zakhalapo zaka zoposa 100. Popeza kuti zinthuzi zimakhala zosiyanasiyana kwambiri, zonse ziyenera kulembedwa bwinobwino pa mndandanda kuti anthu akadzafuna kuzigwiritsa ntchito azidzazipeza mosavuta.

Amazikonza ndi Kuziteteza: Mabuku amene angawonongeke mosavuta ndiponso zinthu zina zakale zimakonzedwa ndiponso kutetezedwa bwino kwambiri. Mapepala, zithunzi, nkhani zochokera m’nyuzipepala, mafilimu ndiponso mawu a anthu zimajambulidwanso m’njira yoti anthu akhoza kuziona kapena kuzimvetsera pa kompyuta. Choncho anthu akafuna kuzigwiritsa ntchito amangoona pa kompyuta m’malo mogwira zinthu zenizenizo zomwe ndi zamtengo wapatali kwambiri ndiponso zikhoza kuwonongeka.

Amazisunga Pabwino Ndipo Angazipezenso Mosavuta: Amasunga zinthuzi mwadongosolo kwambiri ndiponso pamalo otetezeka. Amachita zimenezi kuti zisatayike kapena kuwonongeka chifukwa cha kuwala kapena chinyezi. Akukonza zoti munthu akhoza kufufuza pa kompyuta ndi kupeza mosavuta zinthu zakale zimenezi zomwe zachokera m’kale lathu.

[Zithunzi patsamba 32]

1. Chithunzi chosonyeza “Sewero la pa Kanema la Chilengedwe.” 2. M’ndandanda wolembetsera mabuku. 3. Galimoto yokhala ndi zokuzira mawu. 4. Chikuto cha Nsanja ya Olonda ya April 15, 1912. 5. Chikalata chonena za kumangidwa kwa J. F. Rutherford. 6. Maikolofoni a wailesi ya WBBR. 7. Galamafoni. 8. Chikwama chonyamulira mabuku. 9. Notsi za winawake. 10. Telegalamu yopita kwa J. F. Rutherford.