Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzirani Kukhala Maso Kuchokera kwa Atumwi a Yesu

Phunzirani Kukhala Maso Kuchokera kwa Atumwi a Yesu

“Mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”​—MAT. 26:38.

1-3. Kodi atumwi analephera bwanji kukhalabe maso usiku woti Yesu aphedwa mawa lake ndipo n’chiyani chikusonyeza kuti iwo anaphunzirapo pa zimene analakwitsa?

TAGANIZIRANI zimene zinachitika pa usiku woti Yesu aphedwa mawa lake. Iye anapita kumalo amene ankawakonda kwambiri, otchedwa munda wa Getsemane, omwe anali kum’mawa kwa Yerusalemu. Anapita kumeneku ndi atumwi ake okhulupirika. Chifukwa cha nkhawa ndi chisoni zimene zinali mumtima mwake, iye anafunika malo apayekha kuti akapemphere.​—Mat. 26:36; Yoh. 18:1, 2.

2 Anatenga atumwi ake atatu, Petulo, Yakobo ndi Yohane n’kupita nawo chapatali pang’ono m’mundamo. Kenako anawauza kuti: “Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.” Atatero, anapita kukapemphera. Pobwera anapeza anzake aja ali m’tulo tofa nato. Kachiwirinso anawauza kuti: “Khalani maso.” Komabe anawapeza akugona kawiri konse. Pa nthawi ina usiku womwewo, atumwi onse analephera kukhala maso mwauzimu. Iwo anamuthawa Yesu n’kumusiya yekha.​—Mat. 26:38, 41, 56.

3 Ndithudi atumwiwa anadzimvera chisoni chifukwa cholephera kukhalabe maso. Mofulumira, amuna okhulupirikawa anaphunzira kuchokera pa zimene analakwitsa. Ndipo buku la Machitidwe limasonyeza kuti iwo anadzapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhalabe maso. Kukhulupirika kwawo kunathandiza Akhristu anzawo kukhalanso okhulupirika. Panopa, kuposa ndi kale lonse, tikufunika kukhala maso. (Mat. 24:42) Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene tikuphunzira m’buku la Machitidwe pa nkhani yokhala maso.

ANAKHALA MASO KUTI ADZIWE KUMENE ANGAKALALIKIRE

4, 5. Kodi mzimu woyera unatsogolera motani Paulo ndi anzake pa ntchito yawo?

4 Choyambirira, atumwi anali maso kwambiri kuti adziwe kumene anayenera kukalalikira. Lemba lina limatiuza mmene Yesu anagwiritsira ntchito mzimu woyera umene Yehova anamupatsa kuti atsogolere Paulo ndi anzake pa ulendo wina wovuta kwambiri. (Mac. 2:33) Tiyeni tione mmene anayendera.​—Werengani Machitidwe 16:6-10.

5 Paulo, Sila ndi Timoteyo ananyamuka kuchokera kumzinda wa Lusitara, chakum’mwera kwa Galatiya. Pambuyo pa masiku angapo, anafika kumsewu wina waukulu ku Roma umene umalowera chakumadzulo kudera la ku Asia komwe kunkakhala anthu ambiri. Iwo ankafuna kudutsa msewu umenewu n’cholinga choti akafike kumizinda imene kunali anthu ambiri oti amve za Khristu. Koma chinthu china chinawaimitsa panjira. Vesi 6 limati: “Iwo anapita ku Fulugiya ndiponso m’dziko la Galatiya, chifukwa mzimu woyera unawaletsa kulankhula mawu opatulika m’chigawo cha Asia.” Mzimu woyera unawaletsa kukalalikira m’chigawo cha Asia koma Baibulo silifotokoza mmene unachitira zimenezi. Mosakayikira anali Yesu amene anagwiritsira ntchito mzimu wa Mulungu kutsogolera Paulo ndi anzake kuti akalalikire kudera lina.

6, 7. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira Paulo ndi anzake atafika pafupi ndi Bituniya? (b) Kodi atumwiwo anasankha kuchita chiyani, ndipo zotsatira zake zinali chiyani?

6 Kodi Paulo ndi anzake analowera kuti? Vesi 7 limafotokoza kuti: “Atafika ku Musiya anayesetsa kuti apite ku Bituniya, koma mzimu wa Yesu sunawalole.” Ataletsedwa kukalalikira ku Asia, Paulo ndi anzake analowera chakumadzulo kuti akalalikire m’mizinda ya ku Bituniya. Komabe atatsala pang’ono kufika ku Bituniya kachiwirinso Yesu anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuwaletsa kuti asalalikire kumeneko. Pa nthawiyi amunawa ayenera kuti anazunguzika. Iwo ankadziwa uthenga woti alalikire ndiponso njira zolalikirira koma sankadziwa kumene angakalalikire. Tikhoza kunena kuti iwo anagogoda khomo lolowera ku Asia koma silinatseguke. Anagogodanso khomo lolowera ku Bituniya koma silinatsegukenso. Kodi iwo anangosiya kugogoda? Ayi sanasiye.

7 Pa nthawiyi, zimene amunawa anasankha kuchita zingaoneke zosamveka. Vesi 8 limatiuza kuti: “Analambalala Musiya ndi kukafika ku Torowa.” Choncho iwo anabwerera kulowera chakumadzulo. Anayenda mtunda wokwana makilomita 563 kudutsa mizinda ingapo mpaka anakafika ku Torowa kumene kunali njira yolowera ku Makedoniya. Kumeneku Paulo ndi anzake anagogodanso ndipo tsopano khomo linawatsegukira. Pofotokoza zimene zinachitika Vesi 9 limati: “Ndiyeno usiku Paulo anaona masomphenya. Munthu wina wa ku Makedoniya anaimirira ndi kumupempha kuti: ‘Wolokerani ku Makedoniya kuno mudzatithandize.’” Apa tsopano Paulo anadziwa kumene angapite kuti akalalikire. Mosazengereza, iye limodzi ndi amuna amene anali nawo anawolokera ku Makedoniya.

8, 9. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yonena za ulendo wa Paulo?

8 Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi? Onani kuti mzimu wa Mulungu unatsogolera Paulo pamene ananyamuka kupita kukalalikira ku Asia. Kenako unamutsogoleranso atayandikira Bituniya. Komanso Paulo atafika ku Torowa, m’pamene mzimuwu unamutsogolera kupita ku Makedoniya. Monga mutu wa mpingo, masiku anonso Yesu angatitsogolere chimodzimodzi. (Akol. 1:18) Mwachitsanzo, mwina inuyo munaganizapo zotumikira monga mpainiya kapena mumafuna kusamukira kumene kukufunikira olalikira uthenga ambiri. Yesu angakuthandizeni pogwiritsa ntchito mzimu wa Mulungu koma kokha ngati inuyo mutachitapo kanthu kuti mukwaniritse cholinga chanucho. Mwachitsanzo, munthu akhoza kukhotetsa galimoto kumanja kapena kumanzere pokhapokha ngati ikuyenda. N’chimodzimodzinso Yesu. Iye akhoza kutitsogolera pamene tikufuna kuwonjezera utumiki wathu koma pokhapokha ngati tikuchita zinthu zotithandiza kukwaniritsa zolinga zimene tili nazo.

9 Koma bwanji ngati zimene mukuyesetsa kuti muchite sizikutheka nthawi yomweyo? Kodi muyenera kuleka n’kumaganiza kuti mzimu wa Mulungu sukukutsogolerani? Kumbukirani kuti poyamba zinthu sizinachitike mmene Paulo ankafunira. Komabe anapitiriza kufunafuna ndi kugogoda mpaka anapeza khomo limene linatseguka. Ngati tingapitirize kufunafuna “khomo lalikulu la mwayi wautumiki,” ifenso tidzadalitsidwa.​—1 Akor. 16:9.

KHALANI MASO KUTI MUSANYALANYAZE KUPEMPHERA

10. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti kulimbikira kupemphera n’kofunika kuti tikhalebe maso?

10 Tsopano tiyeni tione phunziro lachiwiri limene tikupeza kuchokera kwa Akhristu oyambirirawa pa nkhani ya kukhala maso. Iwo anali maso ndipo sankanyalanyaza kupemphera. (1 Pet. 4:7) Kupemphera nthawi zonse n’kofunika kuti tikhalebe maso. Kumbukirani kuti kumunda wa Getsemane kuja, adani ake asanamugwire, Yesu anauza atumwi ake atatu kuti: “Khalani maso ndipo pempherani kosalekeza.”​—Mat. 26:41.

11, 12. Kodi Herode anazunza bwanji Akhristu kuphatikizapo Petulo ndipo n’chifukwa chiyani ankachita zimenezo?

11 Petulo amene analipo pa nthawiyo anaona mmene mapemphero ochokera pansi pa mtima amathandizira. (Werengani Machitidwe 12:1-6.) Mavesi oyambirira a nkhaniyi amatiuza zimene Herode anachita pozunza Akhristu n’cholinga choti Ayuda azimukonda. Iye ankadziwa bwino kuti Yakobo anali mtumwi amene ankachitira limodzi zinthu ndi Yesu. Choncho iye anamupha “ndi lupanga.” (Vesi 2) Izi zinachititsa kuti mpingo utaye mtumwi wokondedwa ndipo chimenechi chinali chiyeso chachikulu.

12 Kodi kenako Herode anachita chiyani? Vesi 3 limanena kuti: “Ataona kuti zimenezi zasangalatsa Ayuda, anamanganso Petulo.” Koma m’mbuyomo atumwi ena anatulutsidwa m’ndende m’njira yodabwitsa. Ndipo Petulo anali mmodzi mwa iwo. (Mac. 5:17-20) Herode ankadziwa zimenezi choncho anachita zonse zimene akanatha kuti Petulo asathawe. Iye anaonetsetsa kuti pali “magulu anayi a asilikali, kuti azisinthana pomulondera. Gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Cholinga cha Herode chinali chakuti adzamuonetse kwa anthu pambuyo pa pasika.” (Vesi 4) Ndiye tangoganizani. Herode analamula kuti Petulo amangiriridwe kwa Asilikali awiri ndipo tsiku lililonse asilikali 16 ankasinthana usana ndi usiku n’cholinga choti asathawe basi. Herode ankafuna kuti adzamuonetse kwa Ayuda pambuyo pa Pasika n’kumupha kuti awasangalatse. Kodi Akhristu anzake anatani zinthu zitafika pamenepa?

13, 14. (a) Kodi mpingo unachita chiyani Petulo atamangidwa? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Akhristu anzake a Petulo anachita pa nkhani ya pemphero?

13 Mpingo unadziwa zoyenera kuchita. Vesi 5 limati: “Petulo anakhala akusungidwa m’ndendemo, koma mpingo unali kumupempherera mosalekeza kwa Mulungu ndi mtima wonse.” Iwo anapemphera ndi mtima wonse kuti m’bale wawo wokondedwa athandizidwe ndi Mulungu. Iwo sanataye mtima chifukwa choti Yakobo anaphedwa kapena kuganiza kuti mapemphero awo sangayankhidwe. Iwo ankadziwa kuti mapemphero a anthu okhulupirika ndi amtengo wapatali kwa Yehova. Iye amayankha mapemphero ngati ali ogwirizana ndi chifuniro chake.​—Aheb. 13:18, 19; Yak. 5:16.

14 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Akhristu anzake a Petulo anachita? Munthu amene ali maso samangopempherera nkhani zokhudza iyeyo koma amapemphereranso abale ndi alongo ena. (Aef. 6:18) Kodi mukudziwa za abale ndi alongo amene akukumana ndi mayesero? Ena akuzunzidwa, ena saloledwa ndi boma kuti azilalikira ndipo m’madera ena mukuchitika masoka achilengedwe. Ndi bwino kuwatchula anthu oterewa m’mapemphero. Mwinanso mukudziwa anthu ena amene akukumana ndi mavuto osaonekera kwambiri. Mwina angakumane ndi mavuto a m’banja, kukhumudwitsidwa kapena matenda. Mungachite bwino kuganizira za anthu amene mungawatchule mwachindunji m’mapemphero anu kwa Yehova, yemwe ndi “Wakumva mapemphero.”​—Sal. 65:2.

15, 16. (a) Fotokozani mmene mngelo wa Yehova anapulumutsira Petulo m’ndende. (Onani chithunzi m’munsimu.) (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Yehova anachita populumutsa Petulo n’zolimbikitsa kwambiri?

15 Ndiyeno kodi zinthu zinamuthera bwanji Petulo? Ali m’tulo pakati pa asilikali awiri, zinthu zodabwitsa zinachitika. (Werengani Machitidwe 12:7-11.) Ndiye taganizirani zimene zinachitika. Mwadzidzidzi m’chipinda chimene anatsekeredwacho munawala kwambiri. Ndiyeno mngelo anaimirira chapafupi koma asilikali aja sanamuone. Mngeloyo anadzutsa Petulo mwachangu ndipo maunyolo onse amene anam’mangira anagwa pansi. Kenako mngeloyo anatulutsa Petulo m’chipindacho n’kudutsa naye pakati pa asilikali amene anali kunja mpaka kutuluka pachipata chachitsulo chomwe “chinawatsegukira chokha.” Atangotuluka m’ndendemo, mngeloyo anamuchokera. Uku kunali kumasulidwa kwa Petulo.

16 N’zolimbikitsa kwambiri tikaganizira mphamvu zimene Yehova ali nazo populumutsa atumiki ake. Masiku ano, sitiyembekezera kuti Yehova azitipulumutsa modabwitsa. Koma tikudziwa kuti Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti athandize anthu ake masiku ano. (2 Mbiri 16:9) Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake woyera, umene ndi wamphamvu kwambiri, kuti atithandize kupirira vuto lililonse. (2 Akor. 4:7; 2 Pet. 2:9) Posachedwapa, Yehova adzapatsa Mwana wake mphamvu yomasula anthu mamiliyoni ambiri ku imfa. (Yoh. 5:28, 29) Ngati timakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu tidzakhala olimba mtima kwambiri tikamakumana ndi mavuto masiku ano.

ANKACHITIRA UMBONI MOKWANIRA NGAKHALE KUTI ANKAKUMANA NDI MAVUTO

17. Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yolalikira mwakhama?

17 Tsopano tiyeni tione chinthu chachitatu chimene tikuphunzira kwa atumwi a Yesu pa nkhani ya kukhala maso. Iwo ankachitirabe umboni mokwanira ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Kulalikira mwakhama n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale maso. Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Iye anagwira ntchito mwakhama kwambiri, anayenda maulendo ataliatali ndipo anakhazikitsa mipingo yambirimbiri. Iye anapiriranso mavuto ambiri koma sanasiye kulalikira mwakhama.​—2 Akor. 11:23-29.

18. Kodi Paulo anapitiriza bwanji kuchitira umboni atamangidwa ku Roma?

18 M’buku la Machitidwe, nkhani yomaliza yonena za Paulo imapezeka m’chaputala 28. Paulo anafika ku Roma kuti akazengedwe mlandu pamaso pa Nero. Iye anatsekeredwa m’ndende ndipo mwina anamangiriridwa kwa msilikali. Koma izi sizinalepheretse mtumwi wakhamayu kulalikira. Iye anapezabe njira zochitira umboni. (Werengani Machitidwe 28:17, 23, 24.) Patadutsa masiku atatu Paulo anaitanitsa akuluakulu a Ayuda kuti awalalikire. Ndiyeno litafika tsiku limene anapangana iye anachitira umboni mokwanira. Vesi 23 limati: “Pamenepo iwo [Ayuda a kumeneko] anapangana naye tsiku, ndipo anabwera mwaunyinji kumene iye anali kukhala. Chotero kuyambira m’mawa mpaka madzulo, anawafotokozera nkhani yonse pochitira umboni mokwanira za ufumu wa Mulungu. Anachitira umboniwo mwa kugwiritsa ntchito mfundo zokopa zokhudza Yesu, kuchokera m’chilamulo cha Mose ndi mu Zolemba za aneneri.”

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani Paulo ankachitira umboni mogwira mtima? (b) Kodi Paulo anatani pamene anthu ena anakana uthenga wabwino?

19 N’chifukwa chiyani Paulo ankachitira umboni mogwira mtima? Onani kuti vesi 23 likutchula zifukwa zingapo. (1) Ankafotokoza za Ufumu wa Mulungu ndi za Yesu Khristu. (2) Ankayesetsa kuti awafike pamtima omvera ake ‘pogwiritsa ntchito mfundo zokopa.’ (3) Ankakambirana nawo kuchokera m’Malemba. (4) Ankadzipereka kwambiri chifukwa anachitira umboni “kuyambira m’mawa mpaka madzulo.” Paulo anachitira umboni mwamphamvu koma si onse amene anamukhulupirira. vesi 24 limati: “Ena anayamba kukhulupirira zimene ananenazo, koma ena sanakhulupirire.” Anthu atayamba kusiyana maganizo, anabalalika.

20 Kodi Paulo anakhumudwa ataona kuti anthu ena sanakhulupirire uthenga wabwino? Ayi. Pa Machitidwe 28:30, 31 timawerenga kuti: “Paulo anakhalabe m’nyumba yake yolipira kwa zaka ziwiri zathunthu, ndipo onse obwera kudzamuona anali kuwalandira ndi manja awiri. Anali kuwalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuwaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu, mwaufulu wonse wa kulankhula popanda choletsa.” Mawu olimbikitsa amenewa ndi amene ali kumapeto kwenikweni kwa buku la Machitidwe.

21. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Paulo anachita ali pa ukaidi wosachoka panyumba?

21 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Paulo anachita? Pamene anali pa ukaidi wosachoka panyumba, Paulo sanathe kulalikira kunyumba ndi nyumba. Koma iye sanataye mtima, m’malomwake ankalalikira kwa anthu onse amene ankabwera kudzamuona. N’chimodzimodzi ndi atumiki a Mulungu masiku ano. Ena atsekeredwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro koma amalalikirabe ndipo amapitiriza kukhala osangalala. Abale athu ena sangathe kuchoka pakhomo kapena akukhala m’nyumba zosungira anthu chifukwa cha ukalamba kapena matenda. Iwo amayesetsa mmene angathere kulalikira kwa madokotala, anthu ogwira ntchito kumalowo, alendo ndiponso anthu ena. Iwo amafunitsitsa kuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu. Timayamikira kwambiri chitsanzo chawo.

22. (a) Ndi buku liti limene lingatithandize kupindula ndi buku la Machitidwe? (Onani bokosi pamwambapa.) (b) Kodi inuyo muyesetsa kuchita chiyani pamene mukuyembekezera mapeto a dziko loipali?

22 Pali zinthu zambiri zokhudza kukhala maso zimene tingaphunzire kwa atumwi ndiponso Akhristu oyambirira ena otchulidwa m’buku la Machitidwe. Pamene tikuyembekezera mapeto a dziko loipali, tiyeni tiyesetse mmene tingathere kutsanzira Akhristu oyambirirawa pa nkhani yolalikira molimba mtima ndiponso mwakhama. “Kuchitira umboni mokwanira” za Ufumu wa Mulungu masiku ano ndi mwayi waukulu zedi umene tili nawo.​—Mac. 28:23.

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 13]

NDASINTHA MMENE NDIMAONERA BUKU LA MACHITIDWE

Woyang’anira dera wina atawerenga buku lakuti “Kuchitira Umboni Mokwanira “za Ufumu wa Mulungu ananena kuti: “Ndasintha mmene ndimaonera buku la Machitidwe. Ndawerenga nkhani za mu Machitidwe nthawi zingapo koma zinali ngati ndinali kuziwerenga pa kuunika kwa kandulo nditavala magalasi a litsiro. Koma tsopano ndikumva kuti ndadalitsidwa kuona zinthu zabwino mu Machitidwe pa kuwala kwa dzuwa.”

[Chithunzi patsamba 12]

Mngelo anathandiza Petulo kudutsa pachipata chachikulu chachitsulo