Zimene Zasintha M’magazini Yophunzira
Zimene Zasintha M’magazini Yophunzira
Tasintha zinthu zina m’magazini yophunzira n’cholinga choti izioneka yosangalatsa komanso kuti izikuthandizani kwambiri pophunzira Mawu a Yehova omwe ndi choonadi chamtengo wapatali.—Sal. 1:2; 119:97.
Zaka zinayi zapitazo tinayamba kusindikiza magazini a mitundu iwiri. Ina yogawira ndipo ina ndi yoti tiziphunzira ifeyo, Mboni za Yehova, limodzi ndi ophunzira Baibulo athu amene akupita patsogolo.
Ponena za magazini yophunzira, Mkhristu wina amene watumikira Yehova kwa nthawi yaitali analemba kuti: “Nditangoona magazini yophunzira yoyambirira, ndinaona kuti ndi yabwino komanso yofika pa mtima. Nkhani zake zofotokoza choonadi chozama cha m’Baibulo zinandifika pa mtima kwambiri. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cholandira magazini imeneyi.” M’bale wina analemba kuti: “Ndikufuna kuti ndizikhala ndi nthawi yambiri yophunzira nkhani za m’magazini yophunzira ndipo ndizigwiritsa ntchito Baibulo la malifalensi.” Tikuganiza kuti nanunso mumayamikira kwambiri magaziniyi.
Monga mukudziwa, Nsanja ya Olonda yakhala ikufalitsidwa kuyambira chaka cha 1879 ndipo izi zatheka chifukwa cha mzimu wa Yehova ndiponso madalitso ake. (Zek. 4:6) Pa zaka 133 zimenezi, takhala tikusintha maonekedwe a tsamba loyambirira la magaziniyi. Kuyambira chaka chino cha 2012 patsamba loyamba pazikhala chithunzi cha anthu akulalikira ndipo izi zizitikumbutsa ntchito imene Mulungu watipatsa yochitira umboni mokwanira za Ufumu wa Yehova. (Mac. 28:23) Chithunzichi chizipezekanso patsamba 2 pomwe pazikhala mawu ofotokoza zimene zikuchitika komanso kumene zikuchitikira. Choncho, chaka chonsechi tidzakhala tikukumbutsidwa kuti anthu a Yehova akulalikira uthenga wabwino “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mat. 24:14.
Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zasintha pa magaziniyi? Bokosi la mafunso obwereza lizikhala kumayambiriro kwa nkhani yophunzira iliyonse. Izi zithandiza kuti mudziwiretu mfundo zikuluzikulu zimene muyenera kufufuza mukamaphunzira nkhaniyo. Ochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ayenera kugwiritsabe ntchito mafunso amenewa pa mapeto pa phunziro lililonse pofuna kubwereza mfundo za m’phunzirolo. Muona kuti malo a m’mphepete mwa masamba ndi okulirapo ndiponso manambala a masamba ndi a ndime alembedwa moti azioneka bwinobwino.
Monga tanenera, m’magazini ino muzikhalanso nkhani yatsopano ya mutu wakuti, “Kale Lathu.” Nkhani imeneyi izisonyeza kusintha kumene kwakhala kukuchitika m’mbiri ya Mboni za Yehova. Izikhalanso ndi mbiri ya moyo wa Akhristu ena ndipo mutu wake uzikhala wakuti, “Anadzipereka ndi Mtima Wonse.” Nkhani zimenezi zizifotokoza chimwemwe chimene abale ndi alongo athu apeza chifukwa chotumikira kumadera amene kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri.
Tikukhulupirira kuti muzisangalala kwambiri kuphunzira Mawu a Mulungu pogwiritsa ntchito magazini imeneyi.
Ofalitsa
[Chithunzi patsamba 3]
1879
[Chithunzi patsamba 3]
1895
[Chithunzi patsamba 3]
1931
[Chithunzi patsamba 3]
1950
[Chithunzi patsamba 3]
1974
[Chithunzi patsamba 3]
2008