Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zomwe Mungachite Kuti Muzipindula Ndiponso Kusangalala Mukamaphunzira Baibulo

Zomwe Mungachite Kuti Muzipindula Ndiponso Kusangalala Mukamaphunzira Baibulo

Zomwe Mungachite Kuti Muzipindula Ndiponso Kusangalala Mukamaphunzira Baibulo

Kodi tingatani kuti tizisangalala tikamaphunzira Baibulo? Nanga tingatani kuti tizipindula kwambiri pophunzira? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zofunika kwambiri kuti tizipindula kwambiri tikamaphunzira Baibulo.

1 KUPEMPHERA: Choyamba tiyenera kupemphera. (Sal 42:8) N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyenera kuona kuti kuphunzira Mawu a Mulungu ndi mbali ya kulambira kwathu. Choncho tiyenera kupempha Yehova kutithandiza kuti tikhale ndi maganizo oyenera ndiponso kuti atipatse mzimu wake woyera. (Luka 11:13) Barbara, yemwe wakhala akuchita umishonale kwa nthawi yaitali anati: “Ndimapemphera nthawi zonse ndisanayambe kuwerenga kapena kuphunzira Baibulo. Ndikatero, ndimamva kuti Yehova ali nane ndipo akusangalala ndi zimene ndikuchita.” Kupemphera tisanayambe kuphunzira kumathandiza kuti titseguke maganizo ndiponso mtima n’cholinga choti tipindule mokwanira ndi chakudya chauzimu cha mwanaalirenji chimene tikulandira.

2 KUSINKHASINKHA: Chifukwa cha kusowa nthawi anthu ambiri amangowerenga Mawu a Mulungu koma osaikapo maganizo awo onse. Koma izi zimachititsa kuti asapindule kwambiri ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Carlos, amene watumikira Yehova kwa zaka zoposa 50, amaona kuti kupatula nthawi yosinkhasinkha zimene waphunzira n’kothandiza kwambiri. Iye anati: “Masiku ano ndimangowerenga masamba ochepa okha m’Baibulo, mwina awiri basi. Ndiyeno nthawi yambiri ndimakhala ndikusinkhasinkha zimene ndawerengazo n’cholinga choti ndiganizire bwinobwino zimene ndikuphunzira pa nkhaniyo.” (Sal. 77:12) Tikamapatula nthawi yosinkhasinkha timadziwa molondola chifuniro cha Mulungu.​—Akol. 1:9-11.

3 KUGWIRITSA NTCHITO ZIMENE TAPHUNZIRA: Tikazindikira ubwino wa chinthu, timapindula nacho kwambiri. Izi n’zimene zimachitika ndi kuphunzira Baibulo. M’bale wina wachinyamata dzina lake Gabriel, amene ali ndi ndandanda yabwino yophunzira Baibulo, anati: “Kuphunzira Baibulo kumandithandiza kuti ndizilimbana ndi mavuto amene ndimakumana nawo tsiku ndi tsiku. Kumandithandizanso kuti ndikhale woyenera kuthandiza ena. Ndimayesetsa kugwiritsa ntchito pa moyo wanga zonse zimene ndaphunzira.” (Deut. 11:18; Yos. 1:8) M’Baibulo muli chuma chamtengo wapatali chimene tiyenera kuchifufuza. Tikachipeza tizichigwiritsa ntchito pa moyo wathu.​—Miy. 2:1-5.

KUBWEREZA: Nzeru zonse zimachokera kwa Yehova ndipo iye watipatsa mwayi waukulu zedi wophunzira nzeru zimenezo. (Aroma 11:33) Choncho nthawi ina mukamadzaphunzira Baibulo mudzaonetsetse kuti mwayamba ndi kupemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi maganizo oyenera komanso akupatseni mzimu wake woyera. Kenako mudzapeze nthawi yosinkhasinkha zimene mwawerenga. Muzionetsetsanso kuti mukugwiritsa ntchito pa moyo wanu zimene mwaphunzira. Mukamachita zimenezi, muzipindula ndiponso kusangalala kwambiri mukamaphunzira Baibulo.