Ankalalikira Mawu a Mulungu Molimba Mtima
Ankalalikira Mawu a Mulungu Molimba Mtima
Mabuku athu, monga lakuti “Kuchitira Umboni Mokwanira” za Ufumu wa Mulungu, amasonyeza kuti Akhristu oona amakhala olimba mtima kwambiri akamatsutsidwa. Mofanana ndi Akhristu a nthawi ya atumwi, timapempha Yehova kuti atipatse mzimu wake komanso kuti atithandize kuti tilalikire mawu ake molimba mtima.—Mac. 4:23-31.
Ponena za ntchito yathu yolalikira pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, m’bale wina analemba kuti: “Atumiki a Yehova ankafalitsa mwakhama gawo 7 la buku lakuti Studies in the Scriptures, lomwe linali ndi mutu wakuti The Finished Mystery. Bukuli linagawiridwa kwa anthu ochuluka kwambiri. Ndiyeno mu 1918, kapepala ka Uthenga wa Ufumu Nambala 1 kanatulutsidwa. Kenako kunatuluka kapepala ka Uthenga wa Ufumu Nambala 2, kamene kanafotokoza chifukwa chake akuluakulu a boma ankadana ndi buku lakuti The Finished Mystery. Ndiyeno kunadzatuluka Uthenga wa Ufumu Nambala 3. Akhristu odzozedwa okhulupirika anachita khama kwambiri kufalitsa timapepala timeneti. Panafunika chikhulupiriro komanso kulimba mtima kuti afalitse timapepalati.
Masiku ano, ofalitsa Ufumu amaphunzitsidwa mmene angalalikirire koma kalelo izi sizinkachitika kwenikweni. M’bale wina wochokera ku Poland, amene amakhala ku United States, anafotokoza zimene zinamuchitikira pa tsiku limene anayamba kulowa mu utumiki wakumunda mu 1922. Iye anati: “Tsiku limenelo sindinkadziwa zoti ndinene komanso sindinkadziwa bwino chingelezi. Ndiyeno ndinaima ndekhandekha pakhomo la ofesi ina ya dokotala n’kugogoda. Kenako nesi anatsegula chitseko. Sindimaiwala zimene zinachitika chifukwa chakuti ndinkafunitsitsa kulankhula naye komanso ndinkachita mantha. Pamene ndinkatsegula chikwama changa, mabuku onse anagwera pansi pafupi ndi mapazi a nesiyo. Kaya ndinalakhula zotani, koma chimene ndikukumbukira n’chakuti ndinamupatsa buku. Pamene ndinkachoka ndinali ndi mphamvu ndithu ndipo ndinkaona kuti Yehova wandidalitsa. Tsiku limeneli ndinagawira mabuku ambiri pamsewu umenewu, womwe unkadutsa kumene kunali mashopu ndi maofesi.”
Mlongo wina anati: “Cha m’ma 1933 abale ambiri ankagwiritsa ntchito magalimoto okhala ndi zokuzira mawu polalikira uthenga wa Ufumu.” Tsiku lina, mlongoyu ankalalikira limodzi ndi banja lina kudera la mapiri ku California m’dziko la United States. Mlongoyu anati: “M’baleyo anapita pamwamba penipeni pa phiri ndi galimoto yokhala ndi zokuzira mawu ndipo ife tinakhala cha m’munsi mwake. Ndiyeno ataika chimbale cha zimene anajambula, uthenga wake unkamveka ngati ukuchokera kumwamba. Anthu a m’tauniyo anayesetsa kumufufuza koma sanam’peze. Atamaliza uthenga umene unali pa chimbalecho, tinapita kukalalikira. Ndinalalikira nthawi zinanso ziwiri ndi abale okhala ndi galimoto la zokuzira mawu koma kunena zoona anthu ambiri sankafuna kumva
uthenga wathu. Ngakhale zinali choncho, sakanachitira mwina koma kumvabe uthengawo chifukwa chakuti unkamveka m’nyumba zawo. Tinaona kuti nthawi zonse Yehova amagwiritsa ntchito njira yoyenera pa nthawi yoyenera. Pankafunika kulimba mtima ndithu kuti tichite zimenezi koma nthawi zonse zinkatiyendera ndipo dzina la Yehova linkalemekezedwa.”M’zaka za m’ma 1930 ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1940, mu utumiki tinkagwiritsa ntchito magalamafoni ndi nkhani za Baibulo zojambulidwa. Mlongo wina anati: “Mlongo wina wachitsikana ankalalikira kunyumba ndi nyumba pogwiritsa ntchito galamafoni. Atafika panyumba ina n’kutsegula galamafoni, bambo wa panyumbayo analusa kwambiri moti anamenya theche galamafoniyo ndipo inagwa pakhonde n’kugwera pansi. Koma chodabwitsa n’chakuti palibe chimbale chilichonse chimene chinasweka. Azibambo ena atatu amene ankadya nkhomaliro m’galimoto ina yoimika ataona zimenezi, anaitana mtsikanayo kuti adzamve uthengawo ndipo analandira mabuku. Izi zinathandiza kuti asadandaule kwambiri ndi nkhanza zimene bambo uja anam’chitira.” Panafunika kulimba mtima kuti apirire mavuto amenewa.
Mlongo yemweyu ananena kuti: “Ndikukumbukira nthawi imene tinayamba kugawira magazini mumsewu mu 1940. Poyamba tinkalalikira tikuyenda gulu. Abale ndi alongo ankandondozana atakolekera zikwangwani zolembedwa kuti ‘Chipembedzo Ndi Msampha Ndiponso Malonda Achinyengo’ komanso chakuti ‘Tumikirani Mulungu ndi Khristu Mfumu.’ Tinkagawiranso timapepala kwa anthu amene timakumana nawo. Pankafunika kulimba mtima ndithu kuti tichite zimenezi koma zinathandiza kuti anthu adziwe za dzina la Yehova komanso za anthu ake.”
Mlongo wina anati: “Kugawira magazini m’timatauni ting’onoting’ono kunali kovuta. Pa nthawi imeneyi anthu ambiri ankadana ndi Mboni. . . . Munthu ankafunika kulimba mtima kuti aime pa kona penapake atatenga magazini n’kumatchula mokweza mawu enaake amene tinkawagwiritsa ntchito. Koma pafupifupi Loweruka lililonse tinkapita kolalikira. Nthawi zina anthu ankatilandira bwino ndithu. Koma nthawi zina gulu la anthu linkatiukira moti tinkathawa kuti asativulaze.”
Nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse Mboni za Yehova zinkazunzidwa kwambiri koma zinkalalikirabe molimba mtima. Pa masiku 43, kuyambira pa December 1, 1940, kufika pa January 12, 1941, panali ntchito yapadera yolalikira. Pa nthawiyi, ofalitsa pafupifupi 50,000 ku United States anagawira timabuku pafupifupi 8 miliyoni. Imeneyi ankaitchula kuti Nthawi Yochitira Umboni “Molimba Mtima.”
Abale ndi alongo achikulire ambiri amene ali m’gulu la Yehova amakumbukira mavuto osiyanasiyana amene anakumana nawo omwe anachititsa kuti akhale olimba mtima. Ena amakumbukira kuti kwa zaka zambiri ankalimba mtima ndi mawu omwe ankakonda kunena akuti, Pitikitsani adani kuchipata. Sitikudziwa kuti m’tsogolomu tizidzagwiritsa ntchito njira zotani polalikira. Koma Yehova adzatithandiza kuti tipitirize kulalikira mawu ake ndi chikhulupiriro komanso molimba mtima.
[Mawu Otsindika patsamba 9]
Kulimba mtima n’kofunika nthawi zonse pogwira ntchito yolalikira za Ufumu