Kale Lathu
‘Kankachititsa Kuti Ndizionekera Patali’
Mlongo Charlotte White anali mu utumiki wa nthawi zonse ndipo atafika mumzinda wa Louisville, ku Kentucky m’dziko la United States anthu anadabwa naye chifukwa anatenga kanjinga konyamulira sutikesi.
Mlongo White anadabwitsa anthu mumzindawu m’chaka cha 1908 pamene anabwera ndi chinthu chachilendo kwambiri chomwe chinali kanjinga konyamulira sutikesi. Mlongoyu anati, “Kanjingaka kankachititsa kuti ena apeze chokamba ndipo kankachititsa kuti ndizionekera patali.”
Mboni za Yehova, zomwe pa nthawiyo zinkatchedwa Ophunzira Baibulo, zinaona kuti ndi bwino kuuza ena choonadi chamtengo wapatali chimene zinaphunzira m’Malemba. Anthu ambiri anaphunzira za Baibulo kuchokera m’mabuku achingelezi akuti Millennial Dawn, amene ankadziwikanso kuti Studies in the Scriptures. Akhristu amene anali ofunitsitsa komanso amene akanakwanitsa ankayenda maulendo ataliatali kudutsa m’matawuni ndi m’midzi n’kumapereka mabuku amenewa kwa anthu ofunitsitsa kuwawerenga.
Mu 1908, Mlongo White limodzi ndi anthu ena akhama olengeza za Ufumu anapereka mabukuwa, omwe onse pamodzi ankakhalapo 6. Mabukuwa ankakhala ndi chikuto chansalu ndipo ankawagawira pa chopereka chosakwana madola awiri a ku United States. Sankagawira mabukuwa nthawi yomweyo, m’malo mwake ankangolemba anthu amene akuwafuna n’kudzawabweretsera pa tsiku la malipiro n’cholinga choti adzakhale ndi kandalama koti adzapereke. Munthu wina wotsutsa anadandaula kuti anthu amene ankalandira mabukuwa ankapereka ndalama zochepa kwambiri.
Malinda Keefer amakumbukira kuti nthawi zina anthu ankaodetsa mabuku pafupifupi 200 kapena 300 mlungu uliwonse. Koma chidwi chimene anthu anali nacho pa mabuku amenewa chinabweretsanso vuto
lina. Buku la nambala 6 linali la masamba 740. Ndemanga ina ya mu Nsanja ya Olonda inati: ‘Mabuku 50 ankalemera makilogalamu 18 ndiye zinali zovuta kuti anthu anyamule,’ makamaka alongo.Pofuna kuthana ndi vuto limeneli, M’bale James Cole anakonza kanjinga konyamulira sutikesi. Ataona kuti chintchito chonyamula makatoni a mabuku chatha, m’baleyu anati: “Mabuku sakundipweteketsanso mapewa.” Ndiyeno anakaonetsa kanjingaka pa msonkhano wa Ophunzira Baibulo umene unachitikira ku Cincinnati, Ohio m’chaka cha 1908. Abale ndi alongo anasangalala kwambiri. M’mbali mwa kanjingaka analembamo mawu achingelezi akuti Dawn-Mobile chifukwa chakuti kwenikweni ankanyamulira mabuku akuti Millennial Dawn. Apa tsopano ntchito yonyamula masutikesi odzaza ndi mabuku inafewetsedwa chifukwa munthu akakazolowera ankangoyendetsa ndi dzanja limodzi. Munthu ankatha kukatalikitsa kapena kukafupikitsa ndipo matayala ake ankayenda bwinobwino m’tinjira mmene munkadutsa ngolo. Munthu akaweruka ankatha kukapindapinda kuti athe kukanyamula n’kumapita kunyumba wapansi kapena pa kasitima kakang’ono kapamtunda.
Alongo amene anali mu utumiki wa nthawi zonse ankalandira kanjingaka. Koma ena ankagula madola awiri ndi hafu a ku United States. Mlongo Keefer, yemwe amusonyeza pachithunzipa, ankatha kuyendetsa kanjinga kameneka bwinobwino ndi dzanja limodzi ataikapo sutikesi yodzaza ndi mabuku kwinaku atanyamula chikwama china cha mabuku. Kutawuni ina ya ku Pennsylvania ku United States, kumene kunali mgodi, mlongoyu anapeza anthu ambiri omvetsera bwino moti pa tsiku lokapereka mabuku ankayenda maulendo atatu kapena anayi kudutsa pamlatho.
Cha m’ma 1980, woyendetsa ndege wina anapanga chikwama cha matayala chomwe ndi chofala kwambiri masiku ano. Zikwama zoterezi zimapezeka kwambiri m’mabwalo a ndege ndi m’misewu ya m’matawuni akuluakulu. Koma zaka 100 zapitazo, Ophunzira Baibulo akhama ndi amene ankachititsa chidwi anthu ambiri akamayendetsa kanjinga kawo konyamulira mabuku kwinaku akumwaza mbewu zamtengo wapatali za choonadi cha m’Baibulo.
[Mawu Otsindika patsamba 32]
Pa tsiku lokapereka mabuku Mlongo Keefer ankayenda maulendo atatu kapena anayi kudutsa pamlatho
[Mawu Otsindika patsamba 32]
Kanachepetsa vuto limene tinkakumana nalo pokapereka mabuku