Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Mpingo Kukhalabe ndi Maganizo Abwino

Thandizani Mpingo Kukhalabe ndi Maganizo Abwino

Thandizani Mpingo Kukhalabe ndi Maganizo Abwino

“Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu, chifukwa muli ndi maganizo abwino.”​—AFIL. 4:23.

KODI TINGALIMBIKITSE BWANJI MAGANIZO ABWINO MU MPINGO . . .

tikakhala ndi abale athu auzimu?

pochita khama mu utumiki wa kumunda?

poulula machimo akuluakulu amene ena achita?

1. Kodi mipingo ya ku Filipi ndi Tiyatira inayamikiridwa chifukwa chiyani?

AKHRISTU oyambirira a ku Filipi anali osauka. Ngakhale zinali choncho, iwo anali owolowa manja ndipo anapereka chitsanzo chabwino chokonda okhulupirira anzawo. (Afil. 1:3-5, 9; 4:15, 16) N’chifukwa chake Paulo, potsiriza kalata imene anawalembera, ananena kuti: “Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu, chifukwa muli ndi maganizo abwino.” (Afil. 4:23) Chifukwa chakuti Akhristu a ku Tiyatira nawonso anali ndi mzimu wofananawo, Yesu atapatsidwa ulemerero wake anawauza kuti: “Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zapanopa n’zambiri kuposa zoyamba zija.”​—Chiv. 2:19.

2. Kodi tingathandize bwanji kuti anthu mu mpingo wathu akhale ndi maganizo abwino?

2 Masiku anonso, mpingo uliwonse wa Mboni za Yehova umakhala ndi mzimu kapena khalidwe linalake. Mipingo ina imadziwika ndi khalidwe la ubwenzi ndi mzimu wachikondi. Ina imachita bwino kwambiri pa ntchito yolalikira za Ufumu ndiponso kukonda utumiki wa nthawi zonse. Munthu aliyense akamayesetsa kukhala ndi maganizo abwino zimathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana ndipo umakula mwauzimu. (1 Akor. 1:10) Koma maganizo osayenera angachititse mpingo kuwodzera mwauzimu, kukhala wosasangalatsa ndiponso kulekerera zoipa. (1 Akor. 5:1; Chiv. 3:15, 16) Kodi mpingo wanu ndi wotani? Kodi inuyo mungathandize bwanji kuti mpingo wanu ukhale ndi maganizo abwino?

MUZILIMBIKITSA MAGANIZO ABWINO MU MPINGO

3, 4. Kodi tingatamande bwanji Yehova “mu mpingo waukulu”?

3 Wamasalimo anaimba kuti: “Ndidzakutamandani [Yehova] mu mpingo waukulu. Ndidzakutamandani pakati pa anthu ambiri.” (Sal. 35:18) Wamasalimoyu nthawi zonse ankatamanda Yehova pamene anali ndi atumiki anzake. Misonkhano ya mpingo imene timakhala nayo mlungu uliwonse, kuphatikizapo Phunziro la Nsanja ya Olonda, imatipatsa mwayi wosonyeza khama lathu pamene tikufotokoza chikhulupiriro chathu popereka ndemanga. Tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayesetsa kutenga nawo mbali pa misonkhano? Kodi ndimakonzekera bwino ndi kupereka mayankho mogwira mtima? Monga mutu wa banja, kodi ndimathandiza ana anga kukonzekera ndemanga pasadakhale ndiponso kuwaphunzitsa kuyankha m’mawu awoawo?’

4 Wamasalimo Davide anafotokoza kugwirizana pakati pa kuimba ndi kukhala ndi mtima wokhazikika. Iye anati: “Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu, Mtima wanga wakhazikika. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani.” (Sal. 57:7) Nyimbo zimene timaimba pamisonkhano yathu zimatipatsa mwayi ‘woimba nyimbo zotamanda’ Yehova ndi mtima wokhazikika. Ngati sitikudziwa nyimbo zina, tingachite bwino kuyeserera kuimba nyimbozo pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. Tiyeni titsimikize ‘kuimbira Yehova moyo wathu wonse ndiponso kumutamanda nthawi yonse ya moyo wathu.’​—Sal. 104:33.

5, 6. Kodi tingakhale bwanji ochereza komanso owolowa manja ndipo zimenezi zimathandiza bwanji mu mpingo?

5 Kuchereza abale ndi alongo athu ndi njira ina imene tingalimbikitsire chikondi mu mpingo. M’chaputala chomaliza cha kalata yake imene analembera mpingo wa Aheberi, Paulo anawalimbikitsa kuti: “Mupitirize kukonda abale. Musaiwale kuchereza alendo.” (Aheb. 13:1, 2) Kuitana oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo kapena anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse kuti mudzadye nawo limodzi chakudya kunyumba kwanu ndi njira yabwino kwambiri imene mungasonyezere kuchereza alendo. Mungathe kuitananso akazi amasiye, banja lokhala ndi kholo limodzi kapena anthu ena amene angapindule. Mungawaitane kudzadya nawo limodzi kapena kudzakhala nawo pa kulambira kwanu kwa pabanja.

6 Paulo analangiza Timoteyo kuti alimbikitse ena “kuti azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawira ena, ndiponso asunge maziko abwino a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.” (1 Tim. 6:17-19) Paulo anali kulimbikitsa Akhristu anzake kuti akhale owolowa manja. Ngakhale pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto a zachuma tingathe kukhala owolowa manja. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndiyo kutenga anthu ovutika kuyenda popita mu utumiki wakumunda kapena kumisonkhano. Kodi anthu amene amafuna thandizo pa zinthu ngati zimenezi ayenera kukhala ndi maganizo otani? Iwo ayenera kuchita zilizonse zimene angathe posonyeza kuyamikira. Mwachitsanzo, ngati abale akuwatenga pa galimoto, akhoza kupereka zimene angathe podziwa kuti mtengo wa mafuta komanso wosamalira galimoto ukukwera. Kupatula nthawi yocheza ndi abale ndi alongo athu kungawathandizenso kumva kuti timawawerengera ndiponso timawakonda. Nthawi zonse tikamachitira zabwino “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro” ndiponso kukhala okonzeka kugawana nawo nthawi yathu ndi chuma chathu, timayamba kuwakonda kwambiri komanso timalimbikitsa maganizo abwino mu mpingo.​—Agal. 6:10.

7. Kodi kusunga zinsinsi za anthu ena kumathandiza bwanji kuti anthu mu mpingo akhale ndi maganizo abwino?

7 Tiyeni tione zinthu zina zimene zingathandize kuti mu mpingo mukhale chikondi. Zinthu zake ndi kukhala bwenzi lenileni ndiponso kusunga zinsinsi. (Werengani Miyambo 18:24.) Mabwenzi enieni amasungirana chinsinsi. Abale athu akatifotokozera zakukhosi kwawo komanso zimene zili mumtima mwawo sitiyenera kuuza anthu ena. Tikatero, ubwenzi wathu umalimba kuposa poyamba. Tiyeni tizikondana mu mpingo n’kumakhala ngati anthu a banja limodzi. Tizikhala odalirika ndipo tisamangonenanena nkhani zachinsinsi za anthu ena.​—Miy. 20:19.

MUZIGWIRA NTCHITO YOLALIKIRA MWAKHAMA

8. Kodi Akhristu a ku Laodikaya analandira malangizo otani nanga n’chifukwa chiyani?

8 Yesu anauza mpingo wa ku Laodikaya kuti: “Ndikudziwa ntchito zako, kuti si iwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha. Choncho, chifukwa choti ndiwe wofunda, osati wotentha kapena wozizira, ndikulavula m’kamwa mwanga.” (Chiv. 3:15, 16) Akhristu a ku Laodikaya sankachita khama pa utumiki wawo. Zimenezi zinakhudzanso ubwenzi wawo mu mpingo. Choncho, Yesu anawalangiza mwachikondi kuti: “Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho, khala wodzipereka ndipo ulape.”​—Chiv. 3:19.

9. Kodi mmene timachitira mu utumiki wa kumunda zimakhudza bwanji mpingo?

9 Kuti tilimbikitse maganizo abwino mu mpingo tiyenera kugwira ntchito yolalikira mwakhama. Mpingo unakhazikitsidwa n’cholinga choti uzithandiza kufufuza anthu amtima wabwino ndiponso kuwalimbikitsa mwauzimu. Chotero tiyenera kugwira ntchito yolalikira mwakhama ngati mmene Yesu anachitira. (Mat. 28:19, 20; Luka 4:43) Tikamachita khama kwambiri mu utumiki m’pamene timakhalanso ogwirizana kwambiri monga “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Tikamaona mmene ena akuchitira mu utumiki pofotokoza zimene amakhulupirira komanso mmene amayamikirira zinthu zauzimu, timayamba kuwakonda ndiponso kuwalemekeza kwambiri. Kugwira ntchito “mogwirizana” mu utumiki wakumunda kumachititsanso kuti mu mpingo mukhale umodzi.​Werengani Zefaniya 3:9.

10. Kodi kukulitsa luso lathu mu utumiki kungathandize bwanji ena mu mpingo?

10 Tikamayesetsa kukulitsa luso mu utumiki, anthu ena mu mpingo amalimbikitsidwa. Tikamayesetsa kuchitira chifundo anthu amene timakumana nawo mu utumiki ndiponso kuwafika pa mtima, timasangalala ndiponso timalimbikitsidwa kuchita khama kwambiri.(Mat. 9:36, 37) Anthu akaona kuti ife tikusangalala komanso kuchita khama mu utumiki nawonso amayamba kuchita zomwezo. M’malo motumiza mmodzimmodzi kukalalikira, Yesu anatumiza ophunzira ake awiriawiri. (Luka 10:1) Sikuti zimenezi zinangochititsa kuti azilimbikitsana ndi kuthandizana koma zinachititsanso kuti onse azilimbikira pa ntchito yolalikira. Kodi simuyamikira kugwira ntchito ndi olengeza Ufumu akhama? Khama lawo limatilimbikitsa kuchita zambiri m’ntchito yathu yolalikira.​—Aroma 1:12.

MUZIPEWA KUNG’UNG’UDZA NDIPONSO KUCHITA ZOIPA

11. Kodi Aisiraeli a m’nthawi ya Mose anayamba kukhala ndi mtima wotani, nanga zotsatira zake zinali zotani?

11 Patangodutsa milungu yochepa kuchokera pamene Aisiraeli anakhazikitsidwa monga mtundu watsopano, iwo anayamba kukhala ndi mtima wosakhutira komanso kung’ung’udza. Zimenezi zinachititsa kuti apandukire Yehova ndi anthu amene ankamuimira. (Eks. 16:1, 2) Pa Aisiraeli onse amene anachoka ku Iguputo, ndi ochepa okha amene anakalowa m’Dziko Lolonjezedwa. Nayenso Mose sanaloledwe kulowa m’dzikolo chifukwa cha zimene anachita Aisiraeliwo atakhala ndi mtima woipa. (Deut. 32:48-52) Kodi masiku ano tingatani kuti tipewe maganizo oipa?

12. Kodi tingapewe bwanji mtima wong’ung’udza?

12 Tiyenera kupewa mtima wong’ung’udza. Ngakhale kuti kukhala odzichepetsa ndi kulemekeza amene ali ndi udindo kungatithandize kupewa khalidweli, tifunikanso kusankha bwino anthu amene timacheza nawo. Ngati sitisankha zosangalatsa zabwino, kapena ngati timathera nthawi yambiri tili ndi anzathu akuntchito kapena akusukulu amene satsatira mfundo zolungama tingayambe kukhala ndi maganizo oipa. Tiyenera kupewa kucheza kwambiri ndi anthu a maganizo oipa komanso amene amalimbikitsa mtima wosafuna kuuzidwa zochita.​—Miy. 13:20.

13. Kodi mtima wong’ung’udza umayambitsa mavuto auzimu ati mu mpingo?

13 Mtima wong’ungudza ukhoza kuyambitsa mavuto ena auzimu. Mwachitsanzo, ungachititse kuti mumpingo musowe mtendere ndi mgwirizano. Munthu akayamba kudandaula anzake zimakhala zopweteka komanso zimayambitsa mavuto monga miseche ndiponso kulalatirana. (Lev. 19:16; 1 Akor. 5:11) M’nthawi ya atumwi, anthu ena ong’ung’udza ‘ankanyalanyaza ulamuliro ndipo ankalankhula zonyoza amene ali ndi ulemerero.’ (Yuda 8, 16) N’zodziwikiratu kuti Mulungu sanasangalale ndi anthu amene ankang’ung’udza zokhudza oyang’anira mu mpingo.

14, 15. (a) Kodi kulekerera machimo kungakhudze bwanji mpingo? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tadziwa zoti wina wachita tchimo lalikulu?

14 Kodi tiyenera kutani ngati tadziwa zoti Mkhristu wina akuchita machimo monga kuledzera, kuonera zolaula kapena chiwerewere? (Aef. 5:11, 12) Kulekerera machimo akuluakulu kungachititse kuti mzimu woyera wa Yehova usamagwire bwino ntchito pa mpingo komanso kungasokoneze mtendere wa mu mpingo. (Agal. 5:19-23) Akhristu a mu mpingo wa ku Korinto anafunika kuchotsa oipa. Masiku anonso tiyenera kusunga mpingo uli woyera komanso wa maganizo abwino pochotsa chilichonse chimene chingasokoneze mpingowo. Kodi inuyo mungachite chiyani kuti mu mpingo wanu mukhale mtendere?

15 Monga tanena kale, tiyenera kusunga chinsinsi ngati anthu ena atiuza zakukhosi kwawo kapena zimene zili mumtima mwawo. Kufalitsa nkhani zachinsinsi za anthu ena n’kulakwa kwambiri komanso ndi zopweteka. Ngakhale zili choncho, tiyenera kuuza akulu ngati munthu wina wachita tchimo lalikulu chifukwa chakuti ndi amene ali ndi udindo wa m’Malemba wothandiza anthu oterowo. (Werengani Levitiko 5:1.) Choncho ngati tadziwa zoti m’bale kapena mlongo wina wachita tchimo lalikulu tiyenera kumulimbikitsa kuti akauze akulu n’cholinga choti amuthandize. (Yak. 5:13-15) Ngati pakupita nthawi ndithu iye asanakanene, ifeyo tiyenera kukanena.

16. Kodi kuulula machimo akuluakulu kumathandiza bwanji kuti mpingo ukhale ndi maganizo abwino?

16 Anthufe timatsitsimulidwa mwauzimu mu mpingo wachikhristu choncho tiyenera kuuteteza pouza akulu za machimo akuluakulu. Ngati akuluwo atathandiza wochimwayo kuzindikira tchimo lake, iye n’kulapa ndiponso kulandira thandizo lauzimu, sangasokonezenso mpingo. Koma kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu wochimwayo sakulapa ndipo akukana thandizo limene akulu akumupatsa? Kuchotsa munthu wotereyu kumathandiza kuti ‘tiwononge’ kapena kuti tichotse zinthu zimene zingasokoneze mpingo wonse. (Werengani 1 Akorinto 5:5.) Kuti mpingo ukhale ndi maganizo abwino, aliyense ayenera kuchitapo kanthu, kugwirizana ndi akulu komanso kuteteza okhulupirira anzathu.

MUZILIMBIKITSA ‘UMODZI MWA MZIMU’

17, 18. N’chiyani chingatithandize kusunga ‘umodzi wathu mwa mzimu’?

17 Chifukwa ‘chopitiriza kulabadira zimene atumwi anali kuphunzitsa,’ otsatira a Yesu oyambirira anathandiza kuti anthu azigwirizana kwambiri mu mpingo. (Mac. 2:42) Iwo ankalemekeza kwambiri malangizo ochokera m’Malemba amene akulu anali kuwauza. Masiku anonso mipingo yonse imalimbikitsidwa kukhala yogwirizana chifukwa akulu amatsatira zimene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amanena. (1 Akor. 1:10) Tikamatsatira malangizo a m’Baibulo amene gulu la Yehova limapereka ndiponso kutsatira malangizo a akulu, timasonyeza kuti ‘tikuyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwamtendere monga chomangira chotigwirizanitsa.’​—Aef. 4:3.

18 Choncho tiziyesetsa kuthandiza mpingo kuti ukhale ndi maganizo abwino. Tikamachita zimenezi tingakhale otsimikizira kuti ‘kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhala nafe, chifukwa tili ndi maganizo abwino.’​—Afil. 4:23.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 19]

Kodi mumakonzekera ndemanga zogwira mtima kuti mulimbikitse maganizo abwino mu mpingo?

[Chithunzi patsamba 20]

Kuphunzira nyimbo zathu ndi kuzidziwa bwino kumalimbikitsa maganizo abwino mu mpingo