Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Yesu pa Nkhani Yokhala Maso

Tsanzirani Yesu pa Nkhani Yokhala Maso

Tsanzirani Yesu pa Nkhani Yokhala Maso

“Khalani maso ndipo pempherani.”​—MAT. 26:41.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi mapemphero athu angasonyeze bwanji kuti tili maso?

Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili maso mu utumiki?

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala maso tikakumana ndi mayesero, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

1, 2. (a) Kodi ndi mafunso ati amene tingafunse pa nkhani ya kukhala maso kwa Yesu? (b) Kodi Yesu, yemwe ndi munthu wangwiro, angakhale chitsanzo chabwino kwa anthu opanda ungwiro? Perekani chitsanzo.

MWINA munadzifunsapo kuti: ‘Kodi n’zotheka kukhala maso ngati Yesu?’ Chifukwatu Yesu anali munthu wangwiro. Komanso nthawi zina ankatha kudziwa bwinobwino zam’tsogolo ngakhale zimene zidzachitike patapita zaka masauzande. Choncho mungadzifunsenso kuti: ‘Kodi iye ankafunikadi kukhala maso?’ (Mat. 24:37-39; Aheb. 4:15) Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kuona kuti malangizo a m’nkhaniyi ndi a panthawi yake ndiponso ofunika kuwatsatira mwamsanga. Tiyeni tione.

2 Kodi munthu wangwiro angakhale chitsanzo chabwino kwa anthu opanda ungwiro? Inde. Tikutero chifukwa chakuti n’zotheka kuphunzira zinthu kuchokera kwa mphunzitsi wabwino. Mwachitsanzo, taganizirani za munthu amene akuyamba kumene kuphunzira kuponya muvi ndi uta. Poyamba, iye akhoza kumaphonya kwambiri ndipo angafunike kuphunzitsidwa komanso kuchita khama. Kuti zinthu zimuyendere amayang’anitsitsa mmene mphunzitsi wake akuponyera. Amaona mmene mphunzitsi wakeyo akuimira, mmene akugwirira uta ndiponso mmene akukokera chingwe chake. Kenako munthuyo amapitiriza kuchita khama kuti adziwe kukoka bwino chingwe cha uta komanso zimene ayenera kuchita ngati kuli mphepo. Akamatsanzira zimene mphunzitsi wake akuchita, zinthu zimamuyendera moti nthawi iliyonse imene waponya muvi amaona kuti akumatsala pang’ono kubaya chinthu chimene akufunacho. Kuti tikhale Akhristu abwino, nafenso tiyenera kuchita khama kutsanzira Yesu ndiponso kutengera chitsanzo chake changwiro.

3. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankafunika kukhala maso? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

3 Koma kodi Yesu ankafunikadi kukhala maso? Inde. Mwachitsanzo, usiku woti iye aphedwa mawa lake, Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Mukhalebe maso pamodzi ndi ine.” Kenako ananena kuti: “Khalani maso ndipo pempherani kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.” (Mat. 26:38, 41) Ngakhale kuti Yesu ankakhala maso nthawi zonse, pa nthawi yovuta kwambiriyi anafunika kukhala maso kwambiri komanso kukhala pafupi ndi Atate ake wakumwamba. Iye ankadziwa kuti otsatira ake ankafunika kukhalanso maso pa nthawiyo komanso m’tsogolo. Tiyeni tione chifukwa chake Yesu amafuna kuti tikhale maso. Kenako, tiona njira zitatu zimene tingakhalire maso nthawi zonse ngati Yesu.

N’CHIFUKWA CHIYANI YESU AKUFUNA KUTI TIZIKHALA MASO?

4. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kusadziwa zakutsogolo ndi kufunika kokhala maso?

4 Mwachidule, tinganene kuti Yesu akufuna kuti tizikhala maso chifukwa cha zimene sitidziwa komanso zimene timadziwa. Kodi pamene Yesu anali padziko lapansi pano ankadziwa zinthu zonse zakutsogolo? Ayi, chifukwa iye ananena kuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mat. 24:36) Pa nthawiyo, Yesu yemwe ndi “Mwana” sankadziwa nthawi imene mapeto a dziko loipali adzafike. Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Kodi pali zinthu zina za m’tsogolo zimene sitikudziwa? Ee zilipo. Sitidziwa tsiku limene Yehova adzatumize Mwana wake kuti adzawononge dziko loipali. Tikanadziwa tsikulo, kodi bwenzi zili zofunika kukhala maso? Malinga ndi zimene Yesu ananena, mapeto adzafika modzidzimutsa, choncho m’pofunika kukhala maso nthawi zonse.​Werengani Mateyu 24:43.

5, 6. (a) Kodi kudziwa za m’tsogolo ndiponso zolinga za Mulungu kumatilimbikitsa kukhala maso m’njira yotani? (b) Kodi kudziwa zolinga za Satana kukugwirizana bwanji ndi kufunika kokhala maso?

5 Koma Yesu ankadziwa zinthu zambiri zochititsa chidwi zakutsogolo zimene anthu ambiri sankadziwa. Ngakhale kuti sitidziwa zonse zimene Yesu amadziwa, iye watiphunzitsa zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu ndiponso zimene Ufumuwu udzachite posachedwapa. Tikakhala kusukulu, kuntchito kapena mu utumiki, timaona anthu ambiri amene ali mu mdima chifukwa chosadziwa choonadi. Chimenechitu ndi chifukwa china chotilimbikitsa kukhala maso. Mofanana ndi Yesu, tifunika kukhala maso nthawi zonse n’kumagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene ungapezeke kuti tiuze anthu za Ufumu wa Mulungu. Tiziyesetsa kugwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene ungapezeke chifukwa miyoyo ya anthu ili pa chiswe.​—1 Tim. 4:16.

6 Pali chinthu chinanso chimene Yesu ankadziwa chomwe chinamuchititsa kukhala maso. Iye ankadziwa kuti Satana ankafunitsitsa kumuyesa, kumuzunza ndiponso kumuchititsa kuti asakhale wokhulupirika kwa Mulungu. Mdani woipa ameneyu ankakhala maso nthawi zonse kuti apeze “nthawi ina yabwino” yoti ayesenso Yesu. (Luka 4:13) Yesu ankakhala tcheru nthawi zonse. Iye ankakhala wokonzeka podziwa kuti nthawi ina iliyonse akhoza kuyesedwa, kutsutsidwa kapena kuzunzidwa. Nafenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Tikudziwa kuti Satana ali ngati “mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akhristu onse kuti: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso.” (1 Pet. 5:8) Kodi tingachite bwanji zimenezi?

MMENE TINGAKHALIRE MASO PA NKHANI YA KUPEMPHERA

7, 8. Kodi Yesu anapereka malangizo otani pa nkhani ya pemphero ndipo iye anapereka chitsanzo chotani?

7 Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana kwambiri pakati pa kukhala maso mwauzimu ndi kupemphera. (Akol. 4:2; 1 Pet. 4:7) Atangouza ophunzira ake kuti akhale maso limodzi naye, Yesu anati: “Khalani maso ndipo pempherani kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.” (Mat. 26:41) Kodi iye ankafuna kuti ophunzira akewo achite zimenezi pa nthawi yovuta yokhayo? Ayi. Iye ankafuna kuti azichita zimenezi tsiku lililonse.

8 Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yopemphera. Pajatu tsiku lina anakhala akupemphera kwa Atate ake usiku wonse. Ndiye tangoganizani zimene zinachitika. (Werengani Luka 6:12, 13.) Yesu anali mumzinda wa Kaperenao, womwe ankakonda kukhala akakhala ku Galileya, ndipo unali mwezi wa March kapena April. Dzuwa litayamba kulowa, Yesu anakwera phiri la pafupi ndi nyanja ya Galileya. Ali paphirilo, n’kutheka kuti akayang’ana m’munsi ankaona kuwala kwa nyali za ku Kaperenao ndiponso kumidzi ina yapafupi. Koma pamene Yesu anayamba kupemphera, maganizo ake onse anali pa kulankhula ndi Yehova. Iye anachita zimenezi kwa nthawi yaitali. Sanaone kuti nyali zakutalizo zikuzima, mwezi ukudutsa kumwamba kapena nyama zakuthengo zomwe zimatuluka usiku zikusokosera. Iye ayenera kuti ankauza Yehova za zinthu zofunika kwambiri zimene ankayenera kuchita. Iye ankafunika kusankha atumwi 12. Taganizirani mmene Yesu ankauzira Atate ake maganizo ake onse ndiponso nkhawa imene anali nayo pa wophunzira wake aliyense. Ayeneranso kuti ankachonderera Yehova kuti amutsogolere n’kumupatsa nzeru posankha zochita pa nkhani imeneyi.

9. Kodi nkhani yoti Yesu anapemphera usiku wonse ikutiphunzitsa chiyani?

9 Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yesu? Kodi ndiye kuti tiyenera kupemphera kwa maola ambirimbiri? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti ponena za ophunzira ake, Yesu anati: “Mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Mat. 26:41) Komabe tikhoza kutsanzira Yesu. Mwachitsanzo, kodi timapemphera kwa Atate wathu wakumwamba tisanasankhe pa nkhani iliyonse imene ingakhudze mwauzimu ifeyo, banja lathu kapena Akhristu anzathu? Kodi mapemphero athu amasonyeza kuti timadera nkhawa abale ndi alongo athu? Kodi timapemphera mochokera mumtima mwathu m’malo mongonena zinthu mwachizolowezi? Onaninso kuti Yesu ankayesetsa kupeza mpata wokhala payekha kuti auze Atate ake zakukhosi kwake. Masiku ano, moyo ndi wopanikiza kwambiri choncho n’zosavuta kuti titanganidwe mpaka kufika poiwala zinthu zofunika kwambiri. Koma kupeza nthawi yoti tikhale patokha n’kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kungatithandize kwambiri kukhala maso mwauzimu. (Mat. 6:6, 7) Tikatero, tidzayandikira kwambiri Yehova, tidzakhala ofunitsitsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye ndipo tidzapewa chilichonse chimene chingasokoneze ubwenziwu.​—Sal. 25:14.

MMENE TINGAKHALIRE MASO PA NTCHITO YOLALIKIRA

10. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene Yesu ankakhalira tcheru kuti apeze mipata yochitira umboni.

10 Yesu ankakhala maso pa ntchito imene Yehova anamupatsa. Pali ntchito zina zimene munthu angazigwire bwinobwino uku akuganizira zinthu zina. Koma pali ntchito zina zomwe zimafuna kuti munthu akhale maso n’kuika maganizo onse pa zimene akuchita. Umu ndi mmene zilili ndi ntchito yathu yolalikira. Yesu ankakhala maso pogwira ntchito imeneyi ndipo ankagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti alalikire uthenga wabwino. Mwachitsanzo, iye ndi ophunzira ake atayenda m’mawa wonse n’kufika m’tawuni ya Sukari, ophunzira ake anapita kukagula chakudya. Yesu anakhala pafupi ndi chitsime cha mumzindawo kuti apumule. Komabe iye anali maso n’cholinga choti agwiritse ntchito mpata uliwonse pochitira umboni. Ndiyeno kunafika mkazi wachisamariya kudzatunga madzi. Apa Yesu akanatha kungogona kuti apumule bwinobwino. Akanapeza ndithu zifukwa zoti asalankhulane ndi mayiyo. Koma iye anakambirana ndi mayiyo ndipo anamuphunzitsa choonadi mogwira mtima moti anthu ambiri a mumzindawo anayamba kukhulupirira. (Yoh. 4:4-26, 39-42) Nafenso tingachite bwino kutsanzira Yesu n’kumayesetsa kugwiritsa ntchito mpata uliwonse umene ungapezeke kuti tiuze anthu amene timakumana nawo uthenga wabwino.

11, 12. (a) Kodi Yesu anatani pamene anthu ena ankafuna kumusokoneza pa ntchito yake? (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yopewa kuchita zinthu mopitirira malire?

11 Nthawi zina, ngakhale anthu amene anali ndi zolinga zabwino anachita zinthu zimene zikanasokoneza Yesu pa utumiki wake. Mwachitsanzo, Yesu ali ku Kaperenao, gulu la anthu linachita naye chidwi kwambiri chifukwa choti ankachiritsa anthu mozizwitsa. Chifukwa cha zimenezi, iwo ankafuna kuti Yesu azikhalabe komweko. Izitu zinali zomveka. Komabe ntchito ya Yesu inali yolalikira kwa anthu onse amene anali ngati “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli” osati a mumzinda umodzi okha. (Mat. 15:24) Choncho anauza anthuwo kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:40-44) Apa zikuonekeratu kuti maganizo a Yesu anali pa utumiki basi ndipo sanalole chilichonse kumusokoneza.

12 Kodi Yesu anali wakhama pa ntchito yake moti analibiretu nthawi yopumula kapena yosangalala? Kapena kodi anali kutanganidwa kwambiri ndi ntchitoyo moti sankadziwa kapena kuchita chidwi ndi zimene mabanja anali kukumana nazo? Ayi. Yesu anali chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yopewa kuchita zinthu mopitirira malire. Iye ankapeza nthawi yosangalala pamodzi ndi anzake. Iye ankachita chidwi kwambiri ndi mabanja ndipo ankawachitira chifundo chachikulu komanso ankasonyeza chikondi kwa ana.​—Werengani Maliko 10:13-16.

13. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yokhala maso komanso kupewa kuchita zinthu mopitirira malire pogwira ntchito yolalikira za Ufumu?

13 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani ya kusalola zinthu kumusokoneza pa ntchito yake komanso kupewa kuchita zinthu mopitirira malire? Sitidzalola kuti dzikoli litisokoneze pa ntchito yathu. Mwina anzathu kapena achibale athu amene amatifunira zabwino angatilimbikitse kuti tisiye kuchita zambiri mu utumiki kapena kuti tichite zinthu zimene iwo amaona kuti n’zofunika. Koma ngati tikutsanzira Yesu, timaona kuti utumiki wathu uli ngati chakudya chathu. (Yoh. 4:34) Ntchito yathu yolalikira ili ngati chakudya chifukwa imatilimbitsa mwauzimu ndiponso imatipatsa chimwemwe. Koma sikuti timachita zinthu mopitirira malire mpaka kufika podzilanga kapena podziona kuti ndife olungama kuposa ena. Mofanana ndi Yesu, timafuna kukhala atumiki osangalala komanso osachita zinthu mopitirira malire. Pajatu timatumikira “Mulungu wachimwemwe.”​—1 Tim. 1:11.

MMENE TINGAKHALIRE MASO TIKAKUMANA NDI MAYESERO

14. Kodi tiyenera kupewa chiyani tikakumana ndi mavuto? Perekani chifukwa.

14 Monga taonera kale, Yesu anapereka mwamphamvu malangizo onena za kukhala maso pa nthawi imene anakumana ndi mayesero aakulu. (Werengani Maliko 14:37.) Nafenso kuposa ndi kale lonse, tiyenera kutengera chitsanzo chimenechi tikakumana ndi mavuto. Anthu ambiri akakumana ndi mayesero amaiwala mfundo yoona ndiponso yofunika kwambiri imene inatchulidwa kawiri m’buku la Miyambo yakuti: “Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.” (Miy. 14:12; 16:25) Tikamadalira nzeru zathu pamene takumana ndi mavuto aakulu, ndiye kuti ifeyo komanso anzathu amene timawakonda tikhoza kukhala pa ngozi.

15. Kodi mutu wa banja ungayesedwe kuchita zotani pa nthawi ya mavuto a zachuma?

15 Mwachitsanzo, mwamuna yemwe ndi mutu wa banja akhoza kumavutika kuti apezere zosowa “anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira.” (1 Tim. 5:8) Mwina angamaganize zoyamba ntchito imene ingamuchititse kuti aziphonya misonkhano yachikhristu, asamachititse kulambira kwa pa banja mokhazikika, kapena asamalowe nawo mu utumiki wakumunda. Iye akadalira nzeru zake, akhoza kuganiza kuti angachite bwino kugwira ntchito imeneyi. Komatu zimenezi zikhoza kuchititsa kuti adwale kapena afe mwauzimu. Chofunika pamenepa ndi kutsatira malangizo a pa Miyambo 3:5, 6. Pa lembali Solomo anati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”

16. (a) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yodalira nzeru za Yehova osati luso lake lomvetsa zinthu? (b) Kodi amuna ambiri akutsanzira bwanji Yesu pa nkhani yodalira Yehova akakumana ndi mavuto?

16 Pa nthawi imene anakumana ndi mavuto, Yesu sanadalire m’pang’ono pomwe luso lake lomvetsa zinthu. Tangoganizani. Munthu amene anali wanzeru kuposa wina aliyense amene anakhalapo padziko anasankha kuti asadalire nzeru zake. Mwachitsanzo, pamene Satana ankamuyesa, iye ankayankha kuti: “Malemba amati.” (Mat. 4:4, 7, 10) Iye ankadalira nzeru za Atate ake pokana mayesero a Satana. Pochita zimenezi, Yesu anasonyeza kudzichepetsa, komwe ndi khalidwe limene Satana aliberetu komanso amadana nalo. Kodi ifeyo timatero? Mkhristu yemwe ndi mutu wa banja amenenso amatsatira Yesu pa nkhani yokhala maso, amalola kuti Mawu a Mulungu azimutsogolera makamaka pa nthawi imene akukumana ndi mavuto. Pa dziko lonse pali amuna achikhristu ambiri amene akuchita zimenezi. Nthawi zonse, iwo amaika patsogolo Ufumu wa Mulungu ndiponso kulambira koona osati zinthu zakuthupi. Apatu tingati amasamalira bwino kwambiri mabanja awo. Yehova amadalitsa ntchito yawo yopezera banja lawo zinthu zakuthupi ngati mmene analonjezera m’Mawu ake.​—Mat. 6:33.

17. N’chiyani chimakulimbikitsani kutsanzira Yesu pa nkhani yokhala maso?

17 Tafikapa, taona kuti Yesu ankakhala maso ndipo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri. Chitsanzo chakechi n’chothandiza kwambiri ndipo chikhoza kupulumutsa moyo wathu. Musaiwale kuti Satana amafuna kuti tizigona mwauzimu, tikhale ndi chikhulupiriro chofooka, tizichita mphwayi polambira Mulungu ndiponso kuti tikhale ndi mtima wogawanika. (1 Ates. 5:6) Musalole kuti iye apambane. Pitirizani kukhala maso ngati Yesu pa nkhani ya kupemphera, mu utumiki ndiponso pokumana ndi mayesero. Mukamachita zimenezi, mudzakhala ndi moyo wosangalala ndiponso wabwino kwambiri ngakhale panopa pamene tili m’masiku otsiriza a dziko loipali. Ngati mukhala maso ndiye kuti pa nthawi imene Ambuye adzafika kudzawononga dziko loipali, adzakupezani muli okonzeka komanso mukuchita chifuniro cha Atate ake. Yehova adzasangalala kwambiri kukupatsani mphoto chifukwa cha kukhulupirika kwanu.​—Chiv. 16:15.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 6]

Yesu analalikira mkazi amene anakumana naye pachitsime. Kodi inuyo mumagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene mwapeza?

[Chithunzi patsamba 7]

Kusamalira banja lanu mwauzimu kumasonyeza kuti muli maso