Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Mungatijambule?”

“Kodi Mungatijambule?”

“Kodi Mungatijambule?”

Pambuyo pa tsiku lachiwiri la msonkhano wachigawo, Josué amene amatumikira pa Beteli ku Mexico ankangoyenda kuti aone malo mumzinda wa Querétaro. Ndiyeno anakumana ndi Javier ndi Maru omwe ndi banja. Iwo amachokera ku Colombia, ndipo anapempha Josué kuti awajambule chithunzi. Chifukwa chakuti Josué ndi anzake ankaoneka bwino ndiponso anavala mabaji a msonkhano wachigawo, banjalo linawafunsa ngati iwo anabwera ku mwambo wotsekera maphunziro enaake kapena ku mwambo wina wapadera. Josué anawafotokozera kuti abwera kudzachita msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ndipo anawapempha kuti adzamvetsere nawo msonkhanowo pa tsiku Lamlungu.

Banjalo linafotokoza kuti silingakwanitse kubwera chifukwa analibe zovala zoyenera ku msonkhano. Choncho Josué anangowapatsa dzina lake ndi nambala ya foni ya ku ofesi ya nthambi kumene ankatumikira.

Patadutsa miyezi inayi, Josué anadabwa Javier atamuimbira foni. Banjali linapitadi kukachita nawo msonkhano wachigawo ndiyeno ankafuna kuti apeze wa Mboni woti azidzaphunzira nawo ku Mexico City kumene ankakhala. Nthawi yomweyo, Javier ndi Maru anayamba kuphunzira Baibulo ndiponso kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Patangotha miyezi 10, iwo anakhala ofalitsa osabatizidwa. Ngakhale kuti anasamukira ku Toronto ku Canada, anapitirizabe kupita patsogolo mwauzimu mpaka anabatizidwa.

Kenako Josué analandira kalata yochokera kwa Javier yomufotokozera zimene zinamuchititsa kuti aphunzire choonadi. Iye analemba kuti: “Tisanapite ku msonkhano wachigawo, ndinkakambirana ndi mkazi wanga kuti tifunika kuti Mulungu azititsogolera pa moyo wathu. Mmene munavalira tsiku limene lija, tinaona kuti munkachokeradi ku msonkhano wofunika kwambiri. Ndiyeno titapita ku msonkhano wachigawo tinachita chidwi ndi mmene anatilandirira mwachikondi, kutipatsa malo okhala ndiponso kutithandiza mmene tingapezere malemba m’Baibulo. Tinachitanso chidwi ndi khalidwe la onse amene anali pa msonkhanowo. Zinalibe kanthu kuti tinavala zovala zosayenera monga anthu oti tinali paulendo wokaona malo.”

Josué anaona kuti mawu amene mfumu yanzeru Solomo inalemba ndi oona. Iye analemba kuti: “Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino, kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzachite bwino.” (Mlal. 11:6) Nanunso mungabzale mbewu ngati mumayesetsa kuitanira anthu ku msonkhano wachigawo kapena kuti adzamvetsere nkhani ya onse. Yehova angakugwiritsireni ntchito kuti muthandize anthu amene ali ndi njala komanso ludzu la zinthu zauzimu ngati mmene analili Javier ndi Maru.​—Yes. 55:1.

[Chithunzi patsamba 32]

Kuchokera kumanzere: Alejandro Voeguelin, Maru Pineda, Alejandro Pineda, Javier Pineda ndi Josué Ramírez ku Beteli ya ku Mexico