Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Anthu Kuti ‘Adzuke ku Tulo’

Thandizani Anthu Kuti ‘Adzuke ku Tulo’

Thandizani Anthu Kuti ‘Adzuke ku Tulo’

“Nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale mu ola lakuti mudzuke ku tulo.”​—AROMA 13:11.

KODI MUNGAFOTOKOZE?

N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kukhala maso mwauzimu?

N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova ayenera kukhala tcheru komanso kumvetsera zolankhula za anthu amene amawalalikira?

Kodi kukhala okoma mtima ndiponso odekha n’kofunika bwanji mu utumiki wathu?

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu ambiri akufunikira kudzuka?

CHAKA chilichonse anthu ambiri amamwalira pa ngozi chifukwa chakuti dalaivala wa galimoto anayamba kuwodzera kapena kugona kumene. Ndiponso ena amachotsedwa ntchito chifukwa choti analephera kudzuka nthawi yabwino ndiye achedwa. Enanso amachotsedwa chifukwa chopezeka akugona pa nthawi ya ntchito. Koma kuwodzera mwauzimu kungabweretse mavuto aakulu kwambiri. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Wodala ndiye amene akhalabe maso.”​—Chiv. 16:14-16.

2 Pamene tsiku lalikulu la Yehova likuyandikira, anthu ambiri akugona mwauzimu. Ndipo atsogoleri ena a matchalitchi achikhristu anena kuti nkhosa zawo zili m’tulo tofa nato. Kodi kugona mwauzimu n’kutani? Nanga n’chifukwa chiyani Akhristu oona ayenera kukhala maso? Ndipo kodi tingathandize bwanji anthu ena kuti adzuke ku tulo tauzimu?

KODI TULO TAUZIMU N’CHIYANI?

3. Kodi tingamudziwe bwanji munthu amene akugona mwauzimu?

3 Anthu amene ali m’tulo sachita chilichonse. Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene ali m’tulo mwauzimu amakhala otanganidwa koma osati ndi zinthu zauzimu. Iwo amakhala otanganidwa kwambiri ndi nkhawa za moyo, zosangalatsa, kufuna kutchuka komanso kufuna chuma. Chifukwa chotanganidwa ndi zinthu zimenezi, saganiza zochita zinthu zauzimu. Koma anthu amene ali maso mwauzimu amadziwa kuti tikukhala “m’masiku otsiriza” ndipo amatanganidwa ndi kuchita chifuniro cha Mulungu.​—2 Pet. 3:3, 4; Luka 21:34-36.

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa malangizo akuti: “Tisapitirize kugona ngati mmene enawo akuchitira”?

4 Werengani 1 Atesalonika 5:4-8. Apa mtumwi Paulo analangiza Akhristu anzake kuti asapitirize “kugona ngati mmene enawo akuchitira.” Kodi iye ankatanthauza chiyani? Kunyalanyaza mfundo za Yehova za makhalidwe abwino ndi chinthu chimodzi chimene chingasonyeze kuti tikugona mwauzimu. Chinthu chinanso chosonyeza kuti tikugona ndicho kunyalanyaza mfundo yakuti nthawi yoti Yehova awononge anthu osaopa Mulungu yayandikira. Tiyenera kusamala kuti tisatengere maganizo ndiponso zochita za anthu amenewa.

5. Kodi ndi maganizo ati amene amasonyeza kuti munthu akugona mwauzimu?

5 Anthu ena amakhulupirira kuti kulibe Mulungu amene adzawaweruza chifukwa cha zochita zawo. (Sal. 53:1) Ena amaganiza kuti Mulungu alibe nafe ntchito anthufe ndiye palibe chifukwa choti ifenso tizimulambira. Koma ena amaganiza kuti akangokhala membala wa tchalitchi chinachake ndiye kuti akhoza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Anthu onse oterewa ali m’tulo tauzimu ndipo afunika kudzuka. Ndiye kodi tingawathandize bwanji?

IFEYO TIYENERA KUKHALABE MASO

6. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kuyesetsa kukhala maso mwauzimu?

6 Kuti tithe kudzutsa anthu ena, ifeyo tiyenera kukhalabe maso. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Mawu a Mulungu amasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kugona mwauzimu ndi “ntchito za mdima” monga maphwando aphokoso kumwa mwauchidakwa, chiwerewere, khalidwe lotayirira, mikangano ndi nsanje. (Werengani Aroma 13:11-14.) Kupewa makhalidwe amene tatchulawa n’kovuta kwambiri. M’pofunika kwambiri kukhala tcheru. Munthu amene akuona kuti akhoza kuyendetsa galimoto ali ndi tulo amaika moyo wake pa ngozi. Choncho Mkhristu afunika kusamala chifukwa kugona mwauzimu ndi koopsa kwambiri.

7. Kodi chingachitike n’chiyani ngati tikuona molakwika anthu a m’gawo lathu?

7 Mwachitsanzo Mkhristu angaganize kuti anthu onse m’gawo lake sakufuna kumva uthenga wabwino ndipo sangasinthe. (Miy. 6:10, 11) Iye angaganize kuti, ‘Ngati palibe munthu amene akufuna kumva uthenga, palibenso chifukwa choyesetsera kupeza anthu kapena kuwathandiza.’ N’zoona kuti anthu ambiri panopa akugona mwauzimu koma akhoza kusintha maganizo ngati zinthu zina zitasintha pa moyo wawo. Anthu ena amadzuka ku tulo n’kuyamba kumvetsera uthenga wathu. Anthu oterewa tingawathandize ngati ifeyo tili maso ndipo tikuyesetsa kugwiritsa ntchito njira zatsopano komanso zokopa zolalikirira uthenga wa Ufumu. Chinthu china chimene chingatithandize kukhala maso ndicho kukumbukira zimene zimachititsa utumiki wathu kukhala wofunika kwambiri.

N’CHIYANI CHIMACHITITSA UTUMIKI WATHU KUKHALA WOFUNIKA KWAMBIRI?

8. N’chifukwa chiyani utumiki wathu wachikhristu uli wofunika kwambiri?

8 Tizikumbukira kuti kaya anthu amve kapena ayi, ntchito yathu yolalikira imalemekeza Yehova ndiponso ikuthandiza kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. Posachedwapa, anthu amene samvera uthenga wabwino adzalandira chilango. Ndipo anthu adzaweruzidwa malinga ndi zimene amachita akamva uthenga wabwino. (2 Ates. 1:8, 9) Kungakhale kulakwa kwambiri ngati Mkhristu angamaganize kuti palibe chifukwa chochitira khama pa ntchito yolalikira chifukwa “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) Tisaiwale kuti Mawu a Mulungu amatiuza kuti anthu amene adzaweruzidwe monga “mbuzi” adzapita ku “chiwonongeko chotheratu.” Ntchito yathu imasonyeza kuti Mulungu ndi wachifundo chifukwa imathandiza anthu kuti asinthe n’kukhala oyenera kulandira “moyo wosatha.” (Mat. 25:32, 41, 46; Aroma 10:13-15) Kodi tikapanda kulalikira, anthu adzamva bwanji uthenga umene ungawathandize kupeza moyo?

9. Kodi kulalikira uthenga wabwino kwakuthandizani bwanji inuyo ndiponso anthu ena?

9 Kulalikira uthenga wabwino kumatithandizanso ifeyo. (Werengani 1 Timoteyo 4:16.) Mwina inuyo panokha mwaona kuti kulankhula za Yehova komanso zimene Ufumu wake udzachite kumalimbitsa chikhulupiriro chanu komanso kumathandiza kuti muzikonda kwambiri Mulungu. N’kutheka kuti kwakuthandizaninso kukhala ndi makhalidwe abwino. Kusonyeza kuti mwadzipereka kwa Mulungu polalikira kumathandizanso kuti muzikhala osangalala. Anthu amene amaphunzitsa ena choonadi amasangalala kwambiri kuona mmene mzimu wa Mulungu wathandizira anthuwo kusintha moyo wawo.

MUZIKHALA TCHERU

10, 11. (a) Kodi Yesu ndi Paulo anasonyeza bwanji kuti anali tcheru komanso kuti anali ndi chidwi? (b) Fotokozani mmene kukhala maso komanso kuchita chidwi zingathandizire kuti utumiki wathu upite patsogolo.

10 Pali njira zambiri zimene tingathandizire anthu kuti akhale ndi chidwi ndi uthenga wabwino. Choncho atumiki achikhristu ayenera kukhala tcheru ndiponso kuchita chidwi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yesu. Popeza kuti Yesu anali munthu wangwiro, iye anatha kuzindikira zinthu ngati mkwiyo wa mumtima mwa Mfarisi, kulapa kwenikweni kwa mkazi wochimwa ndiponso mtima wodzipereka wa mkazi wamasiye. (Luka 7:37-50; 21:1-4) Yesu ankathandiza aliyense mwauzimu mogwirizana ndi vuto lake. Sikuti mtumiki wa Mulungu amafunika kukhala wangwiro kuti azindikire mmene angathandizire anthu. Mtumwi Paulo anatha kusintha ulaliki wake n’cholinga choti ugwirizane ndi anthu osiyanasiyana amene ankakumana nawo.​—Mac. 17:22, 23, 34; 1 Akor. 9:19-23.

11 Tikamayesetsa kukhala tcheru ndiponso kuchita chidwi ngati mmene anachitira Yesu ndi Paulo, tikhoza kupeza njira zatsopano zothandizira anthu amene timakumana nawo kuti azichita chidwi ndi uthenga wathu. Mwachitsanzo, pamene mukukumana ndi anthu yesani kuona zinthu zimene zingakuthandizeni kudziwa chikhalidwe chawo, zimene amakonda komanso ngati ali ndi banja kapena ayi. Mwina mungaone zimene akuchita pa nthawiyo n’kuwayamikira mwaulemu. Kenako mungayambe kukambirana nawo.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi zimene timakambirana ndi munthu amene tikuyenda naye mu utumiki?

12 Munthu amene amakhala tcheru amapewa zododometsa. Tikakhala mu utumiki timalimbikitsana kwambiri pa nthawi imene tikucheza ndi munthu amene tikuyenda naye. Koma tiyenera kukumbukira kuti cholinga cha ulendo wathuwo ndi kulalikira kwa anthu ena. (Mlal. 3:1, 7) Choncho tiyenera kuonetsetsa kuti zokambirana zathu tikachoka panyumba ina kupita ina zisakhale zosokoneza utumiki wathu. Kukambirana mfundo zimene tikufuna kukauza anthu kungatithandize kuti maganizo athu onse akhale pa kulalikira. Ngakhale kuti nthawi zina foni ya m’manja imatithandiza mu utumiki, tiyenera kusamala kuti isasokoneze zokambirana zathu ndi mwininyumba.

MUZICHITA CHIDWI NDI ANTHU

13, 14. (a) Kodi tingatani kuti tidziwe zimene munthu ali nazo chidwi? (b) N’chiyani chingachititse anthu kuyamba kuchita chidwi ndi zinthu zauzimu?

13 Atumiki atcheru komanso amene ali maso amamvetsera kwambiri pamene anthu amene akumana nawo mu utumiki akulankhula. Kodi ndi mafunso ati amene mungafunse n’cholinga choti munthu amene mwakumana naye afotokoze zimene zili mu mtima mwake? Kodi iye akufuna kudziwa chifukwa chake pali zipembedzo zambiri? Kodi akudera nkhawa chifukwa choti m’dera limene akukhala muli chiwawa kapena chifukwa chakuti maboma akulephera kuthetsa mavuto? Kodi mungamuthandize kuchita chidwi ndi zinthu zauzimu pokambirana naye zinthu zamoyo zogometsa kwambiri zimene Mulungu analenga? Kapena kodi mungamufotokozere mmene malangizo a m’Baibulo amathandizira anthu? Nkhani ya pemphero imachititsa chidwi anthu a mtundu uliwonse, ngakhale amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu. Anthu ambiri amafuna kudziwa ngati pali winawake amene amamva mapemphero. Ena amadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu amamva mapemphero onse? Ngati ayi, kodi tingatani kuti Mulungu azimva mapemphero athu?’

14 Tingaphunzire zambiri tikamaona mmene ofalitsa aluso amayambira kukambirana ndi anthu mu utumiki. Onani zimene amachita kuti asapanikize anthu ndi mafunso kapena kuwafunsa mafunso ochititsa manyazi. Onaninso mmene mawu awo ndiponso nkhope zawo zimasonyezera kuti akufunitsitsa kumvetsa maganizo a mwininyumba.​—Miy. 15:13.

KHALANI OKOMA MTIMA NDIPONSO ALUSO

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okoma mtima polalikira?

15 Kodi mumamva bwanji wina akakudzutsani ku tulo? Anthu ambiri samva bwino ngati wina wawadzutsa modzidzimutsa. Aliyense amafuna kudzutsidwa monyengerera. Ndi mmene zililinso ndi kudzutsa anthu ku tulo tauzimu. Mwachitsanzo, kodi muyenera kuchita chiyani ngati munthu wina wakwiya chifukwa choti mwamufikira ndi uthenga wabwino? Mokoma mtima mungasonyeze kuti mwamvetsa maganizo ake. Mungamuyamikire kuti walankhula moona mtima kenako mungachoke mwaulemu. (Miy. 15:1; 17:14; 2 Tim. 2:24) Mukatero munthuyo akhoza kudzalandira bwino m’bale kapena mlongo amene angadzamufikirenso m’tsogolo.

16, 17. Kodi tingasonyeze bwanji kuzindikira mu utumiki?

16 Nthawi zina mukhoza kukambiranabe ndi munthu amene sakufuna kuti mumulalikire. Munthu wina akhoza kunena kuti: “Ine sindikufuna. Ndili ndi chipembedzo changa.” Apo ayi anganene kuti: “Aa inetu za Mbonizo sizindisangalatsa.” Angatero pongofuna kuti tisakambirane naye. Koma mukayesetsa mwaluso ndiponso mokoma mtima mwina mungathe kufunsa funso limene lingathandize mwininyumbayo kuchita chidwi ndi zinthu zauzimu.​—Werengani Akolose 4:6.

17 Ngati tapeza anthu amene akunena kuti atanganidwa ndi bwino kuwasiya osawakakamiza. Koma nthawi zina mukhoza kuona kuti n’zotheka kulankhula mwachidule mfundo zogwira mtima. Abale ena, mu mphindi imodzi yokha, amatha kutsegula Baibulo, kuwerenga lemba lochititsa chidwi ndiponso kusiyira mwininyumba funso loti adzayankhe nthawi ina. Ulaliki wawo wachidule umathandiza kwambiri moti mwininyumba amazindikira kuti ali ndi nthawi yokwanira yoti akambirane mwachidule. Ngati n’kotheka muziyesa kuchita zimenezi.

18. Kodi tingatani kuti tizilalikira mwamwayi m’njira yogwira mtima?

18 Tikakhala okonzeka kulalikira mwamwayi tikhoza kuthandiza anthu amene timakumana nawo pochita zinthu zathu za tsiku ndi tsiku kuti achite chidwi ndi uthenga wabwino. Abale ndi alongo ambiri amanyamula mabuku, magazini kapena timapepala m’thumba kapena m’chikwama. Iwo amakonzekeranso lemba limodzi loti akambirane ndi munthu ngati mpata utapezeka. Mukhoza kufunsa woyang’anira utumiki kapena apainiya a mu mpingo wanu kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi.

KUTHANDIZA ACHIBALE PANG’ONOPANG’ONO KUTI AKHALE NDI CHIDWI

19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwa ulesi pamene tikuthandiza achibale athu?

19 Mwachibadwa, timafuna kuthandiza achibale athu kuti ayambe kuphunzira choonadi. (Yos. 2:13; Mac. 10:24, 48; 16:31, 32) Tikaona kuti zimene tayesa kuchita kuti tiwathandize sizinaphule kanthu, tingagwe ulesi. Tikhoza kumaganiza kuti palibe chimene tinganene kapena kuchita chomwe chingasinthe maganizo awo. Koma dziwani kuti zinthu zina zikhoza kuwachititsa kusintha. Apo ayi, inuyo mukhoza kuphunzira luso lina pophunzitsa choonadi moti mukhoza kuwafika pa mtima.

20. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mwanzeru pokambirana ndi achibale athu?

20 Tiziganizira mmene achibale athu akumvera tikamayesa kuwathandiza. (Aroma 2:4) Tiyenera kuwalankhula mokoma mtima ngati mmene timachitira ndi anthu amene timakumana nawo mu utumiki. Tiyenera kulankhula nawo modekha komanso mwaulemu. M’malo mowalalikira nthawi zonse tingachite bwino kuwafotokozera mmene choonadi chatithandizira. (Aef. 4:23, 24) Fotokozani momveka bwino zimene Yehova wachita ‘pokuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.’ (Yes. 48:17) Zochita zanu zizisonyeza kuti ndinu Mkhristu chifukwa zimenezo zingathandize achibale anu kuti amvetsere choonadi.

21, 22. Perekani chitsanzo chosonyeza ubwino wochita khama pothandiza achibale athu kuti aphunzire choonadi.

21 Posachedwapa mlongo wina analemba kuti: “Ndakhala ndikuyesetsa kuthandiza azichimwene ndi azichemwali anga 13 kuti aphunzire choonadi. Ndachita zimenezi powalankhula komanso powasonyeza khalidwe labwino. Sindinalolepo chaka kutha popanda kuwalembera makalata. Kwa zaka 30 m’banja mwathu Mboni ndinali ine ndekha.”

22 Mlongoyu anapitiriza kuti: “Tsiku lina ndinaimbira foni mchemwali wanga wina yemwe amakhala kutali kwambiri. Iye anandiuza kuti anapempha m’busa wa ku tchalitchi chake kuti aziphunzira naye Baibulo koma sizinatheke. Nditamuuza kuti ndikhoza kumuthandiza ananena kuti: ‘Koma dziwa kuti sindingayerekeze kukhala wa Mboni za Yehova.’ Ndinamutumizira buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndipo ndinkamuimbira foni pafupipafupi. Koma anali asanayambe kuliwerenga. Ndiyeno ndinamupempha kuti atenge bukulo ndipo kwa mphindi 15 tinawerenga ndi kukambirana malemba ena a m’bukulo. Izi zitachitika maulendo angapo, anayamba kufuna kuti tiziphunzira nthawi yochulukirapo. Kenako, iye ndi amene ankandiimbira foni kuti tiphunzire. Pena ankandiimbira ndisanadzuke ndipo nthawi zina ankaimba foni kawiri patsiku. Chaka chotsatira, iye anabatizidwa ndipo patangotha chaka chimodzi anayamba upainiya.”

23. N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwa ulesi pothandiza anthu kuti adzuke ku tulo tauzimu?

23 Kuti muthandize anthu kudzuka ku tulo tauzimu muyenera kukhala aluso komanso kupitiriza kuchita khama. Ubwino wake ndi wakuti anthu ambiri odzichepetsa amamvetsera tikamawathandiza kuti adzuke ku tulo. Pa avereji, mwezi uliwonse anthu oposa 20,000 amabatizidwa kukhala Mboni za Yehova. Choncho tiyeni tizitsatira malangizo amene Paulo anauza m’bale wina wa m’nthawi yake dzina lake Arikipo akuti: “Uonetsetse kuti utumiki umene unaulandira mwa Ambuye ukuukwaniritsa.” (Akol. 4:17) M’nkhani yotsatira tidzakambirana tanthauzo la kulalikira modzipereka.

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 13]

ZIMENE TINGACHITE KUTI TISAGONE MWAUZIMU

▪ Tizichita chifuniro cha Mulungu nthawi zonse

▪ Tizipewa kuchita ntchito za mdima

▪ Tiyenera kudziwa kuopsa kwa kugona mwauzimu

▪ Tiziona moyenera anthu a m’gawo lathu

▪ Tiziyesa kugwiritsa ntchito njira zatsopano polalikira

▪ Tizikumbukira kuti utumiki wathu ndi wofunika kwambiri