Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mwana Amakonda Kuululira Ena za Atate’

‘Mwana Amakonda Kuululira Ena za Atate’

‘Mwana Amakonda Kuululira Ena za Atate’

“Atatewo palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atatewo.”​—LUKA 10:22.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

N’chifukwa chiyani Yesu anali woyenerera bwino kuululira ena za Atate ake?

Kodi Yesu anaulula bwanji za Atate kwa ena?

Kodi tingatsanzire Yesu m’njira ziti poululira ena za Atate?

1, 2. Kodi ndi funso liti limene limaimitsa mitu anthu ambiri ndipo n’chifukwa chiyani?

‘KODI Mulungu ndi ndani?’ Funso limeneli limaimitsa mitu anthu ambiri? Mwachitsanzo, anthu ambiri amene amati ndi Akhristu amakhulupirira kuti mwa Mulungu mmodzi muli Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera. Komabe ambiri amavomereza kuti chiphunzitso chimenechi n’chosamveka. Mtsogoleri wina wachipembedzo, yemwe amalembanso mabuku, ananena kuti n’zovuta kufotokoza chiphunzitso chimenechi chifukwa chakuti pali zinthu zina zimene munthu sangazimvetse. Ndiyeno anthu ambiri amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina amakhulupiriranso kuti kulibe Mulungu. Amanena kuti zinthu zodabwitsa zimene zili m’chilengedwe zinangokhalako mwangozi. Komatu Charles Darwin, yemwe analimbikitsa kwambiri chikhulupiriro chakuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, sananene kuti kulibe Mulungu. Iye anangonena kuti anthu alibe nzeru zokwanira kuti amvetse za Mulungu.

2 Anthu ambiri azikhulupiriro zosiyanasiyana amadzifunsa mafunso okhudza Mulungu. Koma akalephera kupeza mayankho ogwira mtima amangosiya. Zimenezi zikuonetseratu kuti Satana “wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira.” (2 Akor. 4:4) Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri sadziwa zoona zenizeni zokhudza Atate, yemwe ndi Mlengi wa zinthu zonse.​—Yes. 45:18.

3. (a) Kodi ndani anatiululira za Mlengi? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Koma n’zofunika kwambiri kuti anthu aphunzire zoona zenizeni zokhudza Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti anthu okhawo amene ‘amaitana pa dzina la Yehova’ ndi amene adzapulumuke. (Aroma 10:13) Kuitana pa dzina la Mulungu kumatanthauza kuphunzira za Yehova n’kumudziwa bwino. Yesu Khristu anathandiza ophunzira ake kudziwa Mulungu. Iye anawaululira za Atate ake. (Werengani Luka 10:22.) N’chifukwa chiyani Yesu anali woyenera kuposa aliyense kuulula za Atate ake? Ndipo kodi anachita bwanji zimenezi? Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yoululira ena za Atate? Tiyeni tikambirane mafunso amenewa.

YESU KHRISTU NDI WOYENERA KUPOSA ALIYENSE

4, 5. N’chifukwa chiyani Yesu anali woyenerera bwino kuposa aliyense kuululira ena za Atate ake?

4 Yesu anali woyenera kwambiri kuulula za Atate ake. Tikutero chifukwa chakuti zamoyo zonse zisanalengedwe, iye anakhala kumwamba monga mzimu ndiponso “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.” (Yoh. 1:14; 3:18) Zamoyo zonse zisanalengedwe, Mwana yekhayu ankakhala ndi Atate ake omwe ankamukonda kwambiri ndipo iye anaphunzira za Atatewo komanso makhalidwe Awo. Atatewa ndi Mwanayu anakhala limodzi kwa nthawi yaitali zedi ndipo ayenera kuti anakhala akucheza kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, iwo amakondana kwambiri. (Yoh. 5:20; 14:31) Izi zachititsa kuti Mwanayu aziwadziwa bwino kwambiri Atate.​—Werengani Akolose 1:15-17.

5 Atate anapereka kwa Mwanayo udindo womulankhulira monga “Mawu a Mulungu.” (Chiv. 19:13) Izi zinachititsa Yesu kukhala woyenera kwambiri kuululira ena za Atate ake. N’chifukwa chake Yohane analemba mu Uthenga Wabwino kuti Yesu, yemwe ndi “Mawu,” anali “pachifuwa cha Atate.” (Yoh. 1:1, 18) Ponena mawu amenewa, Yohane ankaganizira zimene zinkachitika m’masiku ake pa nthawi ya chakudya. Mlendo mmodzi ankakhala kutsogolo kwa mnzake pampando umodzi. Chifukwa chakuti ankayandikana, iwo ankatha kukambirana mosavuta. Ndiyeno ponena kuti Mwana anali “pachifuwa cha Atate” ndiye kuti ankakambirana zinthu zambiri.

6, 7. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachititsa kuti ubwenzi wa Mwana ndi Atate uzilimba kwambiri?

6 Atate ndi Mwanayu anayamba kukondana kwambiri. “Tsiku ndi tsiku, [Mulungu] anali kusangalala kwambiri” ndi Mwanayo. (Werengani Miyambo 8:22, 23, 30, 31.) M’pake kuti ubwenzi wa awiriwa unkalimba kwambiri pamene ankagwira ntchito limodzi ndiponso pamene Mwanayo ankaphunzira komanso kutengera makhalidwe a Atatewo. Ndiyeno angelo ndiponso anthu atalengedwa, Mwanayo anayamba kuona mmene Yehova ankachitira zinthu ndi aliyense. Izi ziyenera kuti zinachititsa kuti adziwe kwambiri makhalidwe a Mulungu.

7 Kenako Satana anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Pa nthawi imeneyi, Mwanayo anali ndi mwayi woona mmene Yehova amasonyezera chikondi, chilungamo, nzeru ndiponso mphamvu pamene zinthu zavuta kwambiri. Mosakayikira, izi zinathandiza kuti nayenso Yesu adzathane ndi mavuto amene anadzakumana nawo pa utumiki wake padziko lapansi.​—Yoh. 5:19.

8. Kodi nkhani za m’Mauthenga Abwino zimatithandiza bwanji kumvetsa makhalidwe a Atate?

8 Chifukwa choti ankadziwana bwino ndi Yehova, palibe aliyense amene anafotokoza bwino za Atate kuposa Mwanayu. Palibe njira ina yabwino kwambiri yodziwira Atate kuposa kuphunzira zimene Mwana wake wokondedwa anaphunzitsa ndi kuchita. Mwachitsanzo, zikanakhala zovuta kwambiri kumvetsa tanthauzo la mawu oti “chikondi” pongowerenga mu dikishonale. Koma tikaganizira nkhani za m’Mauthenga Abwino zofotokoza zimene Yesu anachita mu utumiki komanso mmene ankathandizira anthu ena, tikhoza kuzindikira tanthauzo la mawu oti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8, 16) N’chimodzimodzinso ndi makhalidwe ena a Mulungu amene Yesu anawasonyeza kwa ophunzira ake ali padziko lapansi.

MMENE YESU ANAULULIRA ATATE AKE

9. (a) Kodi Yesu anaulula za Atate ake m’njira ziwiri ziti? (b) Perekani chitsanzo cha mmene Yesu anaululira za Atate ake kudzera m’zimene ankaphunzitsa.

9 Kodi Yesu anaulula bwanji za Atate ake kwa ophunzira ake komanso kwa Akhristu ena onse? Iye anachita zimenezi kudzera m’zimene ankaphunzitsa komanso m’zochita zake. Choyamba, tiyeni tikambirane zimene Yesu ankaphunzitsa. Zimene Yesu ankaphunzitsa otsatira ake zinkasonyeza kuti ankadziwa kwambiri maganizo, mtima ndiponso njira za Atate ake. Mwachitsanzo, iye anayerekezera Atate ake ndi m’busa wa nkhosa amene amasiya nkhosa zambiri kuti akafufuze imodzi imene yasochera. Iye ananena kuti m’busayo akaipeza “amakondwera kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zosasochera zija.” Kodi ankatanthauza chiyani? Yesu anafotokoza kuti: “Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.” (Mat. 18:12-14) Kodi tikuphunzira chiyani za Yehova m’fanizo limeneli? Nthawi zina mukhoza kumadzimva kuti ndinu wopanda pake ndipo palibe akukuwerengerani. Koma dziwani kuti Atate wanu wakumwamba amakukondani kwambiri ndipo amakufunirani zabwino. Iye amaona kuti ndinu ‘mmodzi wa tiana’ take.

10. Kodi Yesu anaulula bwanji Atate ake kudzera m’zochita zake?

10 Njira yachiwiri imene Yesu anaululira za Atate kwa ophunzira ake inali kudzera m’zochita zake. M’pake kuti pa nthawi imene mtumwi Filipo anauza Yesu kuti: “Tionetseni Atatewo,” Yesu anayankha kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:8, 9) Tiyeni tione zinthu zina zimene Yesu anachita zosonyeza makhalidwe a Atate ake. Wakhate wina atapempha Yesu kuti amuchiritse, Yesu anakhudza munthuyo, yemwe anali “wakhate thupi lonse,” n’kunena kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” Wakhateyo atachiritsidwa ayenera kuti sanakayikire zoti Yehova ndi amene anachititsa kuti Yesu amuchiritse. (Luka 5:12, 13) Lazaro atamwalira, ophunzira ake ayenera kuti anaona kuti Atate ndi wachifundo kwambiri pamene Yesu ‘anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni’ komanso ‘akugwetsa misozi.’ Ngakhale kuti Yesu ankadziwa kuti akaukitsa Lazaro, zinamupweteka kwambiri kuona achibale komanso anzake a Lazaro akulira. (Yoh. 11:32-35, 40-43) Mwina inunso muli ndi nkhani zina m’Baibulo zokhudza zimene Yesu anachita zomwe zimakuchititsani kuona kuti Atate ndi wachifundo.

11. (a) Kodi zimene Yesu anachita poyeretsa kachisi zikusonyeza kuti Atate ndi otani? (b) Kodi nkhani imeneyi ndi yolimbikitsa bwanji kwa ife?

11 Kodi timaphunzira chiyani tikamawerenga zimene Yesu anachita poyeretsa kachisi? M’maganizo mwanu yesani kuona zotsatirazi zikuchitika. Yesu akupanga mkwapulo wazingwe ndipo akuthamangitsa anthu amene akugulitsa ng’ombe ndi nkhosa. Kenako akukhuthula makobidi a anthu osintha ndalama ndi kugubuduza matebulo awo. (Yoh. 2:13-17) Ophunzira ake ataona zimenezi anakumbukira mawu aulosi amene Mfumu Davide inanena akuti: “Kudzipereka kwambiri panyumba yanu kwandidya.” (Sal. 69:9) Zimene Yesu anachita molimba mtima zinasonyeza kuti iye anali wofunitsitsa kuikira kumbuyo kulambira koona. M’nkhani imeneyi tikuonanso makhalidwe a Atate. Imatikumbutsa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire zochotsera kuipa konse padziko lapansi komanso kuti amafunitsitsa kuchita zimenezi. Zimene Yesu anachitazi zimasonyeza bwino mmene Atate amamvera akaona zinthu zoipa zimene zafala padzikoli. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri pa nthawi imene ena atichitira zopanda chilungamo.

12, 13. Kodi tikuphunzira chiyani za Yehova tikaona mmene Yesu ankachitira ndi ophunzira ake?

12 Tiyeni tione chitsanzo china. Tikambirana mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake. Iwo ankakonda kukangana za amene ali wamkulu pakati pawo. (Maliko 9:33-35; 10:43; Luka 9:46) Popeza anakhala nthawi yaitali ndi Atate, Yesu ankadziwa mmene Yehova amaonera mtima wodzikuzawu. (2 Sam. 22:28; Sal. 138:6) Ndipotu Yesu anaona Satana Mdyerekezi akusonyeza mtima umenewu. Chifukwa chodzikuza, Satana ankafuna kwambiri kutchuka ndiponso maudindo. Choncho Yesu ayenera kuti anamva chisoni kwambiri kuona ophunzira ake amene wakhala akuwaphunzitsa akusonyeza mtima woipawu. Ngakhale ophunzira amene anawasankha kukhala atumwi ake anasonyeza mtima umenewu. Iwo sanasiye mpaka tsiku limene Yesu anaphedwa. (Luka 22:24-27) Koma Yesu anapitiriza kuwadzudzula mokoma mtima ndipo sanakayikire zoti pang’ono ndi pang’ono adzatengera mtima wake wodzichepetsa.​—Afil. 2:5-8.

13 Kodi mukuona makhalidwe a Atate pa zimene Yesu anachita pothandiza ophunzira ake moleza mtima kusintha makhalidwe awo oipa? Zimene Yesu anachita komanso kulankhula zimasonyeza kuti Atate sasiya anthu ake ngakhale kuti anthuwo amalakwitsa zinthu mobwerezabwereza. Kudziwa makhalidwe a Mulungu amenewa kuyenera kutithandiza kupemphera kwa iye kuti tilape tikalakwitsa zinazake.

MWANAYO ANKAKONDA KUULULA ZA ATATE AKE

14. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wofunitsitsa kuululira ena zokhudza Atate ake?

14 Olamulira ambiri a dzikoli amayesetsa kulamulira anthu awo mowabisira zinthu zimene anthuwo amafunika kuzidziwa. Amachita zimenezi kuti anthuwo aziwamvera m’chimbulimbuli. Koma Yesu sanali ngati olamulira amenewa. Iye anali wofunitsitsa kuululira ena za Atate ake kuti awadziwe bwino. (Werengani Mateyu 11:27.) Kuwonjezera pamenepo, Yesu anapatsa ophunzira ake ‘nzeru kuti amudziwe woonayo,’ yemwe ndi Yehova Mulungu. (1 Yoh. 5:20) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Yesu anatsegula maganizo a otsatira ake kuti amvetse zinthu zokhudza Atate zimene ankawaphunzitsa. Iye sanabise Atate ake. Sankaphunzitsa anthu zinthu zosamvetsetseka monga zoti mwa Mulungu mmodzi muli atatu.

15. N’chifukwa chiyani Yesu sananene zinthu zina zokhudza Atate ake?

15 Kodi Yesu anaulula zonse zimene ankadziwa zokhudza Atate? Ayi. Pali zinthu zina zimene ankadziwa zomwe sananene. (Werengani Yohane 16:12.) Iye anatero chifukwa chakuti pa nthawiyo, ophunzirawo ‘sakanatha kuzimvetsa.’ Koma Yesu ananena kuti zinthu zambiri zidzaululidwa kwa iwo akadzafika “mthandizi.” Apa anali kunena za mzimu woyera umene unali kudzawatsogolera “m’choonadi chonse.” (Yoh. 16:7, 13) Nthawi zina makolo anzeru sauza ana awo zinthu zina mpaka anawo atakula kuti azimvetse. Nayenso Yesu anadikira kuti ophunzirawo akule mwauzimu kuti amvetse mfundo zina zokhudza Atate. Yesu anali wokoma mtima ndipo ankadziwa zimene ophunzira ake sangakwanitse.

TSANZIRANI YESU POTHANDIZA ANTHU KUDZIWA YEHOVA

16, 17. N’chifukwa chiyani tili oyenera kuululira ena za Atate?

16 Inuyo mukadziwa bwino munthu wina n’kuona kuti ndi wachikondi, mumafuna kuuza ena. Yesu ali padziko lapansi, ankauza ena za Atate. (Yoh. 17:25, 26) Kodi ifeyo tingamutsanzire pa nkhani youza ena za Yehova?

17 Monga taonera, Yesu ankadziwa bwino kuposa aliyense za Atate ake. Iye ankafunitsitsa kuuza ena zimene ankadziwa ndipo anapatsa otsatira ake nzeru kuti amvetse mfundo zozama zokhudza makhalidwe a Mulungu. Kunena zoona, Yesu watithandiza kuwadziwa bwino Atate athu kuposa mmene anthu ambiri m’dzikoli amawadziwira. Ndife oyamikira kwambiri kuti Yesu anali wofunitsitsa kutiululira za Atate ake kudzera m’zimene anaphunzitsa komanso zochita zake. Ndipotu timanyadira kwabasi kuti timadziwa Atate. (Yer. 9:24; 1 Akor. 1:31) Chifukwa choyesetsa kuyandikira Yehova, iyenso watiyandikira. (Yak. 4:8) Choncho panopa ndife oyenera kuuza ena zimene tikudziwa. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

18, 19. Fotokozani njira zimene tingagwiritse ntchito kuululira ena za Atate.

18 Tiyenera kutsanzira Yesu poulula za Atate kudzera m’mawu athu komanso zochita zathu. Tizikumbukira kuti anthu ambiri amene timakumana nawo mu utumiki sadziwa Mulungu. Mwina iwo saona Mulungu moyenera chifukwa chosokonezedwa ndi ziphunzitso zonyenga. Tingachite bwino kuwauza zimene tikudziwa kuchokera m’Baibulo pa nkhani ya dzina la Mulungu, zolinga zake kwa anthu ndiponso makhalidwe ake. Tikazindikira mfundo zina zosonyeza makhalidwe a Mulungu m’nkhani za m’Baibulo, tingachite bwino kukambirana zimenezi ndi Akhristu anzathu. Tikatero, nawonso adzapindula.

19 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu poulula za Atate kudzera m’zochita zathu? Anthu akaona kuti zochita zathu zimasonyeza kuti tikutsanzira chikondi cha Khristu, amafuna kukhala pa ubwenzi ndi Atate komanso Yesu. (Aef. 5:1, 2) Mtumwi Paulo amatilimbikitsa kuti tiyenera ‘kutsanzira iye, monga mmene iyeyonso anatsanzirira Khristu.’ (1 Akor. 11:1) Ifeyo tili ndi mwayi waukulu wothandiza ena kudziwa Yehova kudzera m’zochita zathu. Choncho tiyeni tonse tizitsanzira Yesu poululira ena za Atate.

[Mafunso]