Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

“Mwana wanga, dziwa Mulungu wa bambo wako, um’tumikire ndi mtima wathunthu.”​—1 MBIRI 28:9.

FUFUZANI MAYANKHO A MAFUNSO AWA:

Kodi mtima wophiphiritsa n’chiyani?

Kodi ndi njira iti imene tingafufuzire mtima wathu?

Kodi tingatani kuti tipitirize kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu?

1, 2. (a) Kodi ndi chiwalo chiti chimene chimatchulidwa kwambiri mophiphiritsira m’Mawu a Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa tanthauzo la mtima wophiphiritsa?

NTHAWI zambiri Mawu a Mulungu amatchula ziwalo za thupi la munthu mophiphiritsira pofuna kufotokoza mfundo inayake. Mwachitsanzo, Yobu ananena kuti: “Manja anga sanachite zachiwawa.” Mfumu Solomo inanena kuti: “Uthenga wabwino umanenepetsa mafupa.” Yehova analimbikitsa Ezekieli pomuuza kuti: “Ndachititsa chipumi chako kukhala . . . cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi.” Nayenso mtumwi Paulo anauzidwa kuti: “Zimene ukufotokozazi ndi zinthu zachilendo m’makutu mwathu.”​—Yobu 16:17; Miy. 15:30; Ezek. 3:9; Mac. 17:20.

2 Mtima ndi chiwalo chimene chimatchulidwatchulidwa mophiphiritsa m’Baibulo. Mwachitsanzo, pamene munthu wokhulupirika Hana ankapemphera, anati: “Mtima wanga ukukondwera mwa Yehova.” (1 Sam. 2:1) Olemba Baibulo anatchula mtima pafupifupi nthawi 1,000 koma nthawi zambiri anagwiritsa ntchito mawuwa mophiphiritsira. Kudziwa zimene mawu oti “mtima” amaimira n’kofunika kwambiri chifukwa Baibulo limanena kuti tiyenera kuuteteza.​—Werengani Miyambo 4:23.

KODI MTIMA WOPHIPHIRITSA N’CHIYANI?

3. Kodi tingadziwe bwanji tanthauzo la mawu oti “mtima” m’Baibulo? Perekani chitsanzo.

3 Ngakhale kuti Mawu a Mulungu safotokoza mwachindunji tanthauzo la mawu oti “mtima,” amatithandiza kumvetsa mawuwo. Mwachitsanzo, taganizirani za phiri lalitali kwambiri. Munthu akakhala pafupi amangoona miyala ndi mitengo. Koma akatalikira m’pamene amaona phiri lonse. N’chimodzimodzi ndi mawu oti “mtima” m’Baibulo. Tikangoona malo ochepa amene mawuwa agwiritsidwa ntchito, sitingamvetse tanthauzo lake. Koma tikaona malo onse, tikhoza kumvetsa tanthauzo la mawuwa. Choncho tiyeni tikambirane tanthauzo lake.

4. (a) Kodi mawu oti “mtima” amatanthauza chiyani? (b) Kodi mawu a Yesu a pa Mateyu 22:37 amatanthauza chiyani?

4 Olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu oti “mtima” pofotokoza za munthu yense wamkati. Mawuwo amanena za zinthu monga zofuna zathu, maganizo athu, khalidwe lathu, maluso athu ndiponso zolinga zathu. (Werengani Deuteronomo 15:7; Miyambo 16:9; Machitidwe 2:26.) Koma pa malemba ena mawu oti “mtima” satanthauza zinthu zonsezi. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mat. 22:37) Pa lembali mawu akuti “mtima” akungonena za mmene munthu akumvera ndiponso zimene iye amafuna. Potchula mtima, moyo ndiponso maganizo, Yesu ankatsindika mfundo yoti tiyenera kukonda Mulungu mumtima mwathu komanso kusonyeza zimenezi ndi zochita zathu ndiponso zimene timaganiza. (Yoh. 17:3; Aef. 6:6) Koma mawu oti “mtima” akatchulidwa paokha amatanthauza munthu yense wamkati.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUTETEZA MTIMA WATHU?

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu?

5 Ponena za mtima, Mfumu Davide inakumbutsa Solomo kuti: “Mwana wanga, dziwa Mulungu wa bambo wako, um’tumikire ndi mtima wathunthu ndi moyo wosangalala, chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.” (1 Mbiri 28:9) Yehova amasanthuladi mitima yonse kuphatikizapo mtima wathu. (Miy. 17:3; 21:2) Zimene amapeza mumtima mwathu zimakhudza kwambiri ubwenzi wathu ndi iye komanso tsogolo lathu. Choncho pali zifukwa zabwino zotichititsa kutsatira malangizo ouziridwa a Davide akuti tiziyesetsa kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu.

6. N’chiyani chingatilepheretse kutumikira Yehova ndi mtima wonse?

6 Atumiki a Yehovafe tikamachita khama pa ntchito yathu timasonyeza kuti tikufunitsitsa kutumikira Mulungu ndi mtima wathunthu. Koma timazindikira kuti dziko loipa la Satanali ndiponso zimene thupi lathu lopanda ungwiro limalakalaka ndi zamphamvu ndipo zingatilepheretse kutumikira Mulungu ndi mtima wonse. (Yer. 17:9; Aef. 2:2) Choncho tiyenera kufufuza mtima wathu nthawi zonse kuti zimenezi zisatichitikire. Kodi tingaufufuze bwanji?

7. N’chiyani chingasonyeze mmene mtima wathu ulili?

7 Mofanana ndi mtima wa mtengo, mtima wathu wophiphiritsa suoneka. Koma pa ulaliki wa paphiri, Yesu ananena kuti mtengo wabwino umadziwika ndi zipatso zake choncho zochita zathu n’zimene zingasonyeze ngati mtima wathu uli wabwino kapena ayi. (Mat. 7:17-20) Tiyeni tikambirane za chinthu china chimene chingasonyeze mmene mtima wathu ulili.

NJIRA IMODZI YOFUFUZIRA MTIMA WATHU

8. Kodi mawu a Yesu pa Mateyu 6:33 angatithandize bwanji kuzindikira zimene zili mumtima mwathu?

8 Pa ulaliki wa paphiri womwewo, Yesu anali atauza anthu chinthu chimene chingasonyeze ngati munthu amafuna kutumikira Yehova ndi mtima wonse kapena ayi. Iye anati: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mat. 6:33) Zinthu zimene timaika patsogolo pa moyo wathu zimasonyeza zimene tikulakalaka, kuganizira ndiponso zolinga zathu. Choncho kuona zimene tikuika patsogolo pa moyo wathu ndi njira imodzi yofufuzira ngati tikutumikiradi Mulungu ndi mtima wonse kapena ayi.

9. Kodi Yesu anauza anthu ena kuti achite chiyani, ndipo zimene anachita zinasonyeza chiyani?

9 Pasanapite nthawi kuchokera pamene Yesu anauza otsatira ake kuti “pitirizani kufunafuna ufumu choyamba,” panachitika nkhani ina. Nkhaniyi inatsimikizira kuti zimene munthu amaika patsogolo zimasonyeza mmene mtima wake ulili. Polemba nkhaniyi mu Uthenga Wabwino, Luka anayamba ndi mawu akuti Yesu “anatsimikiza mtima kupita ku Yerusalemu.” Yesu anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa bwino zimene zidzamuchitikira kumeneko. Iye ndi atumwi ake “ali pa ulendowo,” anakumana ndi anthu ena amene anawauza kuti ‘akhale otsatira ake.’ Anthuwo ankafuna kutsatira Yesu koma anali ndi vuto limodzi. Munthu wina anayankha kuti: “Ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.” Wina anati: “Ine ndikutsatirani Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsanzika a m’banja langa.” (Luka 9:51, 57-61) Yesu anasankha motsimikiza mtima kuti achite chifuniro cha Mulungu ndipo izi zinali zosiyana kwambiri ndi zimene anthuwa anachita. Poika zofuna zawo pa malo oyamba osati zinthu zokhudza Ufumu, iwo anasonyeza kuti sakufuna kutumikira Mulungu ndi mtima wathunthu.

10. (a) Kodi otsatira a Khristu achita bwanji ataitanidwa ndi Yesu? (b) Kodi Yesu anapereka fanizo liti?

10 Mosiyana ndi anthu amenewa, ifeyo tinasankha mwanzeru. Tikutero chifukwa Yesu atatiitana kuti tikhale otsatira ake, tinavomera ndipo tsopano tikutumikira Yehova tsiku ndi tsiku. Zimenezi zikusonyeza mmene timaonera Yehova mumtima mwathu. Koma ngakhale kuti tikuchita zambiri mu mpingo, tiyenera kusamala kuti mtima wathu usawonongeke. N’chiyani chingawononge mtima? Pokambirana ndi anthu aja, Yesu anafotokoza zimene zingawononge mtima. Iye anati: “Aliyense wogwira pulawo koma n’kumayang’ana zinthu za m’mbuyo sayenera ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:62) Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu amenewa?

KODI ‘TIMAGWIRITSITSA CHABWINO’?

11. Pa fanizo limene Yesu anapereka, kodi chinachitika n’chiyani pa ntchito yolima ndipo n’chifukwa chiyani?

11 Tiyeni tikambirane zinthu zina zokhudza fanizoli kuti tione bwinobwino zimene tikuphunzira. Tiyerekeze kuti munthu akulima m’munda ndi pulawo. Ndiyeno akuyamba kuganizira kwambiri zinthu za kunyumba monga banja lake, anzake, chakudya, nyimbo, zosangalatsa ndiponso mthunzi, mpaka akuyamba kuzilakalaka. Atalima ndithu, akufika polakalaka kwambiri zinthu zosangalatsazo moti akuima “n’kumayang’ana zinthu za m’mbuyo.” Ngakhale kuti pali ntchito yambiri yoti agwire nthawi yobzala isanafike, iye akusokonezeka ndipo ntchito sikuyenda. N’zosachita kufunsa kuti mwini mundawo adzakhumudwa chifukwa chakuti wantchitoyu sanapirire.

12. Kodi munthu wolima wa m’fanizo la Yesu akufanana bwanji ndi Akhristu ena masiku ano?

12 Tsopano tikambirane zochitika za masiku ano zimene zikufanana ndi nkhaniyi. Wolimayu angaimire Mkhristu amene akuoneka kuti akuchita bwino koma ali pa ngozi mwauzimu. Tiyerekeze kuti m’bale amachita zambiri mu utumiki. Koma ngakhale kuti amapezeka pa misonkhano ndiponso kulalikira, amaganizira kwambiri zinthu zina za m’dzikoli zimene amaona kuti n’zosangalatsa mpaka kufika pozilakalaka. Iye atachita utumiki wake kwa zaka zambiri, akulakalaka kwambiri zinthu za m’dzikoli moti akuima “n’kumayang’ana zinthu za m’mbuyo.” Ngakhale kuti pali ntchito yambiri yoti agwire mu utumiki, iye wasiya “kugwira mwamphamvu mawu amoyo” ndipo ntchito yake yauzimu sikuyenda. (Afil. 2:16) Yehova, yemwe ndi “Mwini zokololazo,” akhoza kukhumudwa kwambiri ngati munthu wasiya kupirira.​—Luka 10:2.

13. Kodi kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu kumatanthauza chiyani?

13 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Zimakhala zosangalatsa tikamapezeka pa misonkhano ndiponso mu utumiki wakumunda nthawi zonse. Koma kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu sikumangotanthauza zinthu zokhazo. (2 Mbiri 25:1, 2, 27) Ngati Mkhristu mumtima mwake amakondabe “zinthu za m’mbuyo,” kapena kuti zinthu zina za m’dzikoli, ubwenzi wake ndi Mulungu umakhala pa ngozi. (Luka 17:32) Tikhoza kukhala ‘oyenera ufumu wa Mulungu’ pokhapokha ngati ‘timanyansidwa ndi choipa, n’kugwiritsitsa chabwino.’ (Aroma 12:9; Luka 9:62) Ngakhale kuti zinthu zina m’dziko la Satanali zingaoneke zothandiza kapena zosangalatsa, tiyenera kusamala kuti chinthu china chilichonse chisatilepheretse kutumikira Yehova ndi mtima wonse.​—2 Akor. 11:14; werengani Afilipi 3:13, 14.

KHALANIBE MASO

14, 15. (a) Kodi Satana akuchita zotani pofuna kuwononga mtima wathu? (b) Perekani fanizo losonyeza kuti njira imene Satana akugwiritsa ntchito ndi yoopsa kwambiri.

14 Tinasankha kudzipereka kwa Yehova chifukwa chomukonda. Kuyambira nthawi imeneyo, ambirife tasonyeza kwa zaka zambiri kuti tikufunitsitsa kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu. Koma Satana sanagwe mphwayi. Iye akufunabe kuwononga mtima wathu. (Aef. 6:12) Komabe iye akhoza kuzindikira kuti sitingasiye kutumikira Yehova kamodzi n’kamodzi. Choncho iye angagwiritse ntchito mochenjera zinthu za m’dzikoli kuti atichititse kusiya pang’onopang’ono khama lathu potumikira Mulungu. (Werengani Maliko 4:18, 19.) N’chifukwa chiyani njira ya Satana imeneyi ili yoopsa kwambiri?

15 Kuti tiyankhe funsoli, tiyerekeze kuti mukufuna kumwa thobwa koma m’malo motenga kapu ya thobwa mwatenga kapu ya madzi. Popeza thobwa ndi madzi zimasiyana kwambiri maonekedwe ndiponso kukoma kwake, mungazindikire nthawi yomweyo. Ndiye tiyerekeze kuti mwasiya thobwalo kuti mukachite zinthu zinazake ndipo munthu wina wabwera n’kupungula pang’ono thobwalo kenako n’kuthiramo madzi pang’ono. Kodi mukabweranso, mungazindikire kuti lasakanizidwa ndi madzi? Mosakayikira, simungazindikire. Nanga ngati mutachokanso munthuyu wapungulanso thobwalo pang’ono n’kuthira madzi m’kapumo, mungazindikire? Mwinanso ayi. Tikutero chifukwa chakuti akusungunula thobwalo pang’onopang’ono moti sizingaoneke msanga. N’chimodzimodzi ndi zinthu za m’dziko la Satanali. Zikhoza kutichititsa kusiya khama lathu pang’onopang’ono. Zimenezi zikachitika, zili ngati Satana wasungunula khama lathu lotumikira Yehova. Ngati Mkhristu sali maso, mwina sangazindikire kuti khama lake likucheperachepera.​—Mat. 24:42; 1 Pet. 5:8.

KUPEMPHERA N’KOFUNIKA KWAMBIRI

16. Kodi tingadziteteze bwanji ku misampha ya Satana?

16 Kodi tingadziteteze bwanji ku misampha ya Satana imeneyi n’cholinga choti tizitumikira Yehova ndi mtima wathunthu? (2 Akor. 2:11) Kupemphera n’kofunika kwambiri. Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘asasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.’ Kenako anawauza kuti: “Muzipemphera pa chochitika chilichonse . . . , mwa mtundu uliwonse wa pemphero ndi pembedzero.”​—Aef. 6:11, 18; 1 Pet. 4:7.

17. Kodi tikuphunzira chiyani pa mapemphero a Yesu?

17 Yesu ankakonda kupemphera ndipo izi zikusonyeza kuti iye ankafunitsitsa kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Kuti tilimbane ndi Satana, nafenso tiyenera kutsanzira Yesu pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo, onani zimene Luka analemba pofotokoza mmene Yesu anapempherera usiku woti aphedwa mawa lake. Iye anati: “Atazunzika koopsa mumtima mwake, anapitiriza kupemphera ndi mtima wonse.” (Luka 22:44) Aka sikanali koyamba kuti Yesu apemphere ndi mtima wonse. Koma pa nthawiyi, ankayembekezera mayesero ovuta kwambiri pa moyo wake choncho anapemphera ndi mtima wonse mochonderera kwambiri ndipo pemphero lake linayankhidwa. Chitsanzo cha Yesu chikusonyeza kuti nthawi zina tikamapemphera timafunika kuchonderera mwamphamvu kuposa nthawi zina. Choncho pamene mayesero athu ndi ovuta kwambiri ndiponso pamene Satana akutiyesa kwambiri m’pamene tiyenera kuchonderera mwamphamvu kuti Yehova atiteteze.

18. (a) Kodi ndi funso liti limene tiyenera kudzifunsa pa nkhani ya pemphero ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize kuti tikhale ndi mtima wabwino? (Onani  Bokosi patsamba  16.)

18 Kodi mapemphero oterewa angatithandize bwanji? Paulo ananena kuti: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.” (Afil. 4:6, 7) Kupemphera ndi mtima wonse ndiponso nthawi zonse n’kofunika kuti titumikire Yehova ndi mtima wathunthu. (Luka 6:12) Choncho muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimapemphera ndi mtima wonse ndiponso nthawi zonse?’ (Mat. 7:7; Aroma 12:12) Yankho lanu pa funso limeneli lingasonyeze ngati mukufunadi kutumikira Mulungu ndi mtima wathunthu.

19. Kodi mungatani kuti mupitirize kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu?

19 Monga taonera, zimene timaika patsogolo pa moyo wathu zimasonyeza ngati tili ndi mtima wabwino kapena ayi. Tiyenera kusamala kuti zinthu za m’mbuyo kapena misampha ya Satana zisatilepheretse kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu. (Werengani Luka 21:19, 34-36.) Choncho mofanana ndi Davide, tiyenera kupempha Yehova mochonderera kuti: “Ndipatseni mtima wosagawanika.”​—Sal. 86:11.

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 16]

 ZINTHU ZITATU ZOTHANDIZA KUTI MTIMA UKHALE WABWINO

Pali zinthu zimene tingachite kuti mtima wathu weniweni ukhale wabwino. N’chimodzimodzi ndi mtima wathu wophiphiritsa. Tiyeni tione zinthu zitatu zimene zingathandize kuti ukhale wabwino:

1 Chakudya: Mtima wathu weniweni umafunika chakudya chokwanira ndiponso chopatsa thanzi. Nawonso mtima wathu wophiphiritsa umafunika chakudya chabwino chauzimu. Choncho tiyenera kuphunzira Baibulo nthawi zonse, kusinkhasinkha ndiponso kufika pa misonkhano.​—Sal. 1:1, 2; Miy. 15:28; Aheb. 10:24, 25.

2 Masewera Olimbitsa Thupi: Kuti tikhale ndi thanzi labwino, nthawi zina timafunikira kuchita masewera olimbitsa thupi n’cholinga choti mtima wathu weniweni uzipopa magazi mwamphamvu. Kuchita khama mu utumiki, kapena kuti kuwonjezera zimene timachita mu utumikiwu, kungathandizenso kuti mtima wathu wophiphiritsa ukhale wabwino.​—Luka 13:24; Afil. 3:12.

3 Kumene Timakhala: Popeza kuti timakhala ndiponso kugwira ntchito m’dziko loipali, mtima wathu weniweni komanso wophiphiritsa umakhala pa ngozi. Koma tikhoza kuuteteza tikamacheza komanso kuchita zinthu zauzimu limodzi ndi Akhristu anzathu amene amatikonda ndiponso amatumikira Mulungu ndi mtima wathunthu.​—Sal. 119:63; Miy. 13:20.