Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khulupirirani Yehova, Mulungu wa “Nthawi ndi Nyengo”

Khulupirirani Yehova, Mulungu wa “Nthawi ndi Nyengo”

Khulupirirani Yehova, Mulungu wa “Nthawi ndi Nyengo”

“Iye amasintha nthawi ndi nyengo, amachotsa mafumu ndi kuika mafumu.”​—DAN. 2:21.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi chilengedwe ndiponso maulosi amene anakwaniritsidwa zimasonyeza bwanji kuti Yehova amachita zinthu pa nthawi yake?

Kodi kuzindikira kuti Yehova ndi Mulungu wa “nthawi ndi nyengo” kumatilimbikitsa kuchita chiyani?

N’chifukwa chiyani nthawi ya Yehova yochitira zinthu sisintha chifukwa cha zochitika za dzikoli ndiponso zofuna za anthu?

1, 2. N’chiyani chimasonyeza kuti Yehova amadziwa bwino za nthawi?

KALEKALE asanalenge anthu, Yehova Mulungu anakonzeratu zoti anthu azitha kuwerengera nthawi. Iye anachita zimenezi pa tsiku lachinayi la kulenga zinthu. Pa tsikulo anati: “Kukhale zounikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku ndipo zikhale zizindikiro, komanso kuti zisonyeze nyengo ndi masiku ndi zaka.” (Gen. 1:14, 19, 26) Zimenezi zinachitikadi mogwirizana ndi mawu akewo.

2 Kuyambira kalekale, asayansi samvetsa za mmene nthawi imayendera. Buku lina limati: “Nthawi ndi chimodzi mwa zinthu zodabwitsa kwambiri padziko lapansi. Palibe amene angakwanitse kuifotokoza.” Koma Yehova amadziwa bwinobwino za nthawi. Tikutero chifukwa iye ndi “Mlengi wa kumwamba, . . . amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga.” Iye ndi ‘amenenso amanena za mapeto kuyambira pa chiyambi. Kuyambira kalekale, amanena za zinthu zimene sizinachitike.’ (Yes. 45:18; 46:10) Tiyeni tione mmene chilengedwe ndiponso maulosi amene akwaniritsidwa zimasonyezera kuti Yehova amachita zinthu pa nthawi yake. Kuona zimenezi kutithandiza kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso Mawu ake, Baibulo.

CHILENGEDWE CHIMATITHANDIZA KUKHULUPIRIRA MULUNGU YEMWE AMACHITA ZINTHU PA NTHAWI YAKE

3. Tchulani zinthu zina zimene zimatsatira kwambiri nthawi.

3 M’chilengedwe muli zinthu zambiri zimene zimatsatira kwambiri nthawi. Mwachitsanzo, mapulaneti ndiponso nyenyezi zimayenda motsatira kwambiri nthawi moti munthu akhoza kudziwa malo amene zili pa nthawi ina iliyonse. M’pake kuti anthu amazigwiritsa ntchito kuti adziwe nyengo komanso kumene akulowera akamayenda pa ulendo. Yehova, yemwe analenga zinthu zimenezi zomwe zimayendera nthawi, alidi ndi “mphamvu zambiri zochitira zinthu” ndipo ndi woyenerera kutamandidwa.​—Werengani Yesaya 40:26.

4. Kodi tingaone bwanji nzeru za Mulungu pa zinthu za m’chilengedwe zimene zimatsatira kwambiri nthawi?

4 Zomera ndiponso zinyama zambiri zimachitanso zinthu motsatira kwambiri nthawi. Mwachitsanzo, mbalame zambiri mwachibadwa zimadziwa nthawi yoyenera kuchoka kudera lina kupita kudera lina. (Yer. 8:7) Anthunso mwachibadwa amachita zinthu motsatira nthawi. N’chifukwa chake munthu akayenda ulendo wautali pa ndege kupita kudera lina kumene nthawi ndi yosiyana kwambiri ndi kumene wachokera, pamatenga masiku angapo kuti thupi lake lizolowere nthawi ya kumaloko. Zitsanzo za m’chilengedwe zimene taonazi, zomwe zimachita zinthu motsatira nthawi, zikusonyeza kuti Mulungu wa “nthawi ndi nyengo” ali ndi mphamvu ndiponso nzeru. (Werengani Salimo 104:24.) Ndithudi, Mulungu ndi wanzeru zonse ndiponso wamphamvuyonse. Choncho tingakhulupirire kuti iye akhoza kukwaniritsa chifuniro chake.

MAULOSI OMWE ANAKWANIRITSIDWA PA NTHAWI YAKE AMALIMBITSA CHIKHULUPIRIRO

5. (a) Kodi ndi njira iti imene tingadziwire za tsogolo la anthu? (b) N’chifukwa chiyani Yehova amatha kulosera zam’tsogolo ndiponso nthawi imene zinthuzo zidzachitike?

5 Timaphunzira zambiri za “makhalidwe a Mulungu osaoneka” m’chilengedwe chake. Koma chilengedwe sichingatipatse mayankho a mafunso ena ofunika kwambiri monga funso lakuti, Kodi tsogolo la anthu ndi lotani? (Aroma 1:20) Kuti tipeze yankho la funso limeneli, tiyenera kuphunzira zimene Mulungu wanena m’Mawu ake, Baibulo. Tikamaphunzira Baibulo timapeza maulosi ambiri amene anakwaniritsidwa pa nthawi yake. Yehova akhoza kulosera zimene zidzachitike chifukwa amatha kudziwa zam’tsogolo. Komanso maulosi amakwaniritsidwa pa nthawi yake chifukwa chakuti Yehova Mulungu angachititse kuti zinthu zichitike pa nthawi imene iye akufuna ndiponso mogwirizana ndi chifuniro chake.

6. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti tizimvetsa maulosi a m’Baibulo?

6 Yehova amafuna kuti atumiki ake amvetse ndiponso kupindula ndi maulosi a m’Malemba. Koma Mulungu saona nthawi mofanana ndi mmene ife timaonera. Ngakhale zili choncho, iye akamanena nthawi imene zinthu zidzachitike amagwiritsa ntchito mawu amene tingathe kumva mosavuta. (Werengani Salimo 90:4.) Mwachitsanzo, buku la Chivumbulutso limanena za “angelo anayi” amene “anali okonzekera kuti pa ola, tsiku, mwezi, ndi chaka” achite zinazake. Apa anagwiritsa ntchito mawu ofotokoza nthawi omwe timatha kuwamvetsa. (Chiv. 9:14, 15) Kuona mmene maulosi anakwaniritsidwira pa nthawi yake, kumatithandiza kukhulupirira kwambiri Mulungu wa “nthawi ndi nyengo” ndiponso Mawu ake. Tiyeni tione zitsanzo zina za maulosi amene anakwaniritsidwa pa nthawi yake.

7. Kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yeremiya wonena za Yerusalemu ndi Yuda kukusonyeza bwanji kuti Yehova amachita zinthu pa nthawi yake?

7 Choyamba, tiyeni tione chitsanzo cha zimene zinachitika m’zaka za m’ma 600 B.C.E. “M’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda,” Yehova anauza Yeremiya mawu okhudza anthu a ku Yuda. (Yer. 25:1) Yehova analosera kuti Ababulo adzawononga Yerusalemu n’kutenga anthu a m’dziko la Yuda kupita nawo ku Babulo. Kumeneko iwo anayenera ‘kutumikira mfumu ya ku Babulo zaka 70.’ Asilikali a ku Babulo anawonongadi Yerusalemu mu 607 B.C.E., ndipo Ayuda ochokera ku dziko la Yuda anatengedwa kupita ku Babulo. Koma n’chiyani chinayenera kuchitika patapita zaka 70? Yeremiya analosera kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Zaka 70 zikadzakwanira muli ku Babulo ndidzakucheukirani anthu inu, ndipo ndidzakwaniritsa lonjezo langa lokubwezeretsani kumalo ano.’” (Yer. 25:11, 12; 29:10) Ulosi umenewu unakwaniritsidwadi pa nthawi yake mu 537 B.C.E., pamene Ayuda anabwerera kwawo. Izi zinachitika pambuyo poti Amedi ndi Aperisi amasula Ayudawo ku ukapolo ku Babulo.

8, 9. Kodi ulosi wa Danieli wonena za kubwera kwa Mesiya komanso kukhazikitsidwa kwa Ufumu wakumwamba, umasonyeza bwanji kuti Yehova ndi Mulungu wa “nthawi ndi nyengo”?

8 Tiyeni tione chitsanzo china cha ulosi umene umakhudza anthu a Mulungu a m’mbuyomu. Zitatsala zaka ziwiri kuti Ayuda achoke ku Babulo, Mulungu analosera kudzera mwa mneneri Danieli kuti Mesiya adzafika zaka 483 kuchokera nthawi imene lamulo lakuti Yerusalemu amangidwenso laperekedwa. Mfumu ya Mediya ndi Perisiya inapereka lamulo limeneli mu chaka cha 455 B.C.E. Ndipo ulosiwu unakwaniritsidwadi patapita zaka 483, mu 29 C.E. M’chaka chimenechi, Yesu wa ku Nazareti anadzozedwa ndi mzimu woyera pa ubatizo wake ndipo anakhala Mesiya. *​—Neh. 2:1, 5-8; Dan. 9:24, 25; Luka 3:1, 2, 21, 22.

9 Tsopano tiyeni tione maulosi a m’Malemba okhudza Ufumu. Maulosi ananeneratu kuti Ufumu wa Mesiya udzakhazikitsidwa kumwamba mu 1914. Mwachitsanzo, Baibulo linaneneratu za “chizindikiro” cha kukhalapo kwa Yesu. Linanena kuti pa nthawiyo padzakhala mavuto padziko chifukwa chakuti Satana adzakhala ataponyedwa pansi kuchokera kumwamba. (Mat. 24:3-14; Chiv. 12:9, 12) Komanso maulosi a m’Baibulo anasonyezeratu kuti m’chaka cha 1914, ‘nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina zidzakwana’ ndiponso kuti Ufumu wakumwamba udzayamba kulamulira.​—Luka 21:24; Dan. 4:10-17. *

10. Kodi ndi zinthu ziti zimene zidzachitikedi pa nthawi yake m’tsogolomu?

10 Yesu ananeneratu kuti “chisautso chachikulu” chidzachitika m’tsogolo. Kenako padzakhala ulamuliro wake wa zaka 1,000. Sitiyenera kukayikira kuti zinthuzi zidzachitikadi pa nthawi yake. Yesu ali padziko lapansi, Yehova anali ataikiratu ‘tsiku ndi ola’ limene zinthu zimenezi zidzachitike.​—Mat. 24:21, 36; Chiv. 20:6.

“MUZIGWIRITSA NTCHITO BWINO NTHAWI YANU”

11. Kodi kudziwa kuti tikukhala m’nthawi yamapeto kuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?

11 Kodi kudziwa kuti Ufumu wayamba kulamulira ndiponso kuti tikukhala “nthawi yamapeto” kuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani? (Dan. 12:4) Anthu ambiri amaona kuti m’dzikoli mavuto akuchulukirachulukira koma sazindikira kuti zimenezi zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo onena za masiku otsiriza. Ena amaganiza kuti dzikoli lidzangowonongeka koma ena amaganiza kuti anthu adzatha kukhazikitsa “bata ndi mtendere.” (1 Ates. 5:3) Nanga ifeyo tizitani? Ngati timazindikira kuti tikukhala pa mapeto a masiku otsiriza a dziko la Satanali, tiyenera kuyesetsa kugwiritsa ntchito nthawi imene yatsalayi kuti tizitumikira Mulungu wa “nthawi ndi nyengo.” Tiyeneranso kuthandiza anthu ena kuti adziwe Mulunguyo. (2 Tim. 3:1) Choncho m’pofunika kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu.​—Werengani Aefeso 5:15-17.

12. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu ananena zokhudza masiku a Nowa?

12 M’dzikoli muli zinthu zambiri zimene zingatisokoneze. Choncho n’kovuta ‘kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu.’ Yesu anachenjeza kuti: “Monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire.” Kodi zinthu zinali bwanji m’masiku a Nowa? Mulungu anauza Nowa kuti dziko la pa nthawiyo lidzatha. Ananenanso kuti anthu oipa adzawonongedwa ndi chigumula chimene chidzachitike padziko lonse. Nowa anali “mlaliki wa chilungamo” ndipo analalikira mokhulupirika uthenga wa Mulungu kwa anthu a m’nthawi yake. (Mat. 24:37; 2 Pet. 2:5) Koma anthuwo ‘anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa ndipo iwo ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo.’ Choncho Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.” (Mat. 24:38, 39, 44) Tiyenera kukhala ngati Nowa osati ngati anthu a m’nthawi yake. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala okonzeka?

13, 14. Kodi tizikumbukira chiyani zokhudza Yehova zomwe zingatithandize kumutumikira mokhulupirika pamene tikudikira kubwera kwa Mwana wa munthu?

13 Ngakhale kuti Mwana wa munthu adzabwera pa ola limene sitikuliganizira, tizikumbukira kuti Yehova amakwaniritsa chifuniro chake pa nthawi yake. Yehova sasintha nthawi yake chifukwa cha zimene zikuchitika m’dzikoli kapena zofuna za anthu. Iye amatha kusankha zimene zidzachitike ndiponso nthawi yoti zinthuzo zichitike kuti zikwaniritse chifuniro chake. (Werengani Danieli 2:21.) Lemba la Miyambo 21:1 limatiuza kuti: “Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova. Amautembenuzira kulikonse kumene iye akufuna.”

14 Yehova angachititse zinthu zina kuchitika n’cholinga choti chifuniro chake chichitike pa nthawi yake. Zinthu zikuluzikulu zambiri zimene zachitika m’dzikoli zakwaniritsa maulosi, makamaka maulosi okhudza kulalikira padziko lonse uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Taganizirani zimene zinachitika pamene ulamuliro wa Soviet Union unatha. Zinthu zandale zinasintha mosayembekezereka ndipo anthu ambiri sankayembekeza kuti zimenezi zingachitike mofulumira chonchi. Koma chifukwa cha kusintha kumeneko, uthenga wabwino ukulalikidwa m’madera ambiri amene m’mbuyomu ntchito yathu yolalikira inaletsedwa. Choncho tiyeni tiyesetse kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu kuti titumikire mokhulupirika Mulungu wa “nthawi ndi nyengo.”

SONYEZANI KUTI MUMAKHULUPIRIRA ZOTI YEHOVA AMACHITA ZINTHU PA NTHAWI YAKE

15. Gulu la Yehova likasintha zinthu, kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika?

15 Kuti tipitirize kulalikira uthenga wa Ufumu m’masiku otsiriza ano, tiyenera kukhulupirira kuti Yehova amachita zinthu pa nthawi yake. Popeza zinthu zikusintha m’dzikoli, nthawi zina timafunika kusintha njira zolalikirira. Gulu la Yehova likhoza kusintha zinthu n’cholinga choti litithandize kulalikira m’njira imene ingachititse anthu ambiri kumva uthengawo. Timasonyeza kuti timakhulupirira Mulungu wa “nthawi ndi nyengo” tikamatsatira mofunitsitsa zimene gulu lasintha. Timachita izi pamene tikutumikira Mulungu mokhulupirika ndiponso kumvera Mwana wake yemwe ndi “mutu wa mpingo.”​—Aef. 5:23.

16. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire kuti Yehova amatithandiza pa nthawi yake?

16 Yehova amafuna kuti tizipemphera kwa iye momasuka tili ndi chikhulupiriro chakuti adzatipatsa zimene tikufuna “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:16) Izi zikusonyeza kuti iye amaganizira aliyense payekha mwachikondi. (Mat. 6:8; 10:29-31) Timasonyeza kuti timakhulupirira Yehova Mulungu tikamapemphera kwa iye nthawi zonse kuti atithandize. Timasonyezanso zimenezi tikamachita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athuwo ndiponso malangizo ake. Tiyeneranso kukumbukira kupempherera Akhristu anzathu.

17, 18. (a) Kodi Yehova adzachita chiyani posachedwapa ndi adani ake? (b) Kodi tiyenera kupewa maganizo otani?

17 Ino si nthawi ‘yogwedezeka pa chikhulupiriro chathu.’ Koma ndi nthawi yokhala ndi chikhulupiriro champhamvu chimene chingatithandize kuchita chifuniro cha Mulungu. (Aroma 4:20) Satana ndi anzake, omwe ndi adani a Mulungu, akuyesetsa kuletsa ntchito imene Yesu anatipatsa. (Mat. 28:19, 20) Ngakhale zili choncho, timadziwa kuti Yehova ndi “Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu a mtundu uliwonse, koma makamaka okhulupirika.” Iye “amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.”​—1 Tim. 4:10; 2 Pet. 2:9.

18 Posachedwapa, Yehova awononga dziko loipali. Ngakhale kuti sitikudziwa zonse zimene zidzachitike ndiponso nthawi yeniyeni imene zidzachitikire, timadziwa kuti Khristu adzawononga adani a Mulungu pa nthawi yake. Pa nthawiyo onse adzadziwa kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. Choncho kusazindikira “nthawi ndi nyengo” imene tikukhalamoyi kungakhale ngozi yaikulu kwambiri. Tiyenera kukhala osamala kwambiri kuti tisayambe kuganiza zoti “zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.”​—1 Ates. 5:1; 2 Pet. 3:3, 4.

‘TIZIYEMBEKEZERA MOLEZA MTIMA’

19, 20. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera Yehova moleza mtima?

19 Yehova Mulungu atalenga anthu, anafuna kuti iwo akhale ndi moyo wosatha kuti azipitiriza mpaka kalekale kuphunzira za iye ndi zinthu zokongola zimene analenga. Lemba la Mlaliki 3:11 limati: “Chilichonse iye [Yehova] anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake. Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale kuti ntchito imene Mulungu woona wagwira, iwo asaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.”

20 Ndife osangalala kwambiri kuti Yehova sanasinthe cholinga chimenechi. (Mal. 3:6) Mulungu “sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” (Yak. 1:17) Dziko likamazungulira limachititsa mthunzi kusuntha, koma nthawi imene Yehova amayendera sikhudzidwa ndi zimenezi. Yehova ndi “Mfumu yamuyaya.” (1 Tim. 1:17) Choncho tiyeni ‘tiziyembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso chathu.’ (Mika 7:7) Tiyeni ‘tilimbe mtima ndipo tichite zinthu mwamphamvu, ife tonse amene tikuyembekezera Yehova.’​—Sal. 31:24.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! tsamba 186 mpaka 195.

^ ndime 9 Onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! tsamba 94 mpaka 97.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 19]

Danieli ankakhulupirira kuti maulosi ochokera kwa Mulungu adzakwaniritsidwa

[Chithunzi patsamba 21]

Kodi mumagwiritsa ntchito bwino nthawi yanu kutumikira Yehova?