Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
N’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti “imfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu”?
▪ Wamasalimo anaimba mouziridwa kuti: “M’maso mwa Yehova imfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu.” (Sal. 116:15) Yehova amaona kuti moyo wa munthu aliyense amene amamulambira ndi wamtengo wapatali kwambiri. Koma mawu a pa Salimo 116 sakungonena za imfa ya munthu mmodzi.
Pokamba nkhani ya maliro a Mkhristu, si bwino kugwiritsa ntchito lemba la Salimo 116:15 pofotokoza za munthu womwalirayo ngakhale kuti iye wamwalira ali wokhulupirika kwa Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti mawu a wamasalimoyu sakunena za munthu mmodzi womwalira. Mawuwa akutanthauza kuti Mulungu amaona kuti imfa ya gulu lonse la anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu kwambiri moti sangalole kuti zichitike.—Onani Salimo 72:14; 116:8.
Lemba la Salimo 116:15 limatitsimikizira kuti Yehova sadzalola kuti gulu lonse la atumiki ake liwonongedwe padziko lapansi. Mbiri yathu imasonyeza kuti tapirira mobwerezabwereza kuyesedwa komanso kuzunzidwa koopsa. Izi zikusonyezeratu kuti Mulungu sadzaloladi kuti anthu ake onse awonongeke.
Popeza Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire komanso cholinga chake sichingalephereke, iye sadzalola kuti gulu lonse la anthu akefe liwonongedwe. Ngati Mulungu atalola zimenezi kuti zichitike, zingatanthauze kuti adani ake ndi amphamvu kwambiri kuposa iyeyo, zomwe n’zosatheka m’pang’ono pomwe. Cholinga cha Yehova n’chakuti padziko lonse pakhale anthu okhulupirika ndipo sichingalephereke. (Yes. 45:18; 55:10, 11) Ngati angaloledi kuti anthu ake onse awonongedwe ndiye kuti sipangakhale anthu ochita utumiki wopatulika kwa Yehova pabwalo la padziko m’kachisi wake wamkulu wauzimu. Ndiye kutinso sipangakhale maziko a “dziko lapansi latsopano,” lomwe ndi anthu olungama amene adzakhale padzikoli molamulidwa ndi “kumwamba kwatsopano.” (Chiv. 21:1) Izinso zingatanthauze kuti Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu sungachitike chifukwa sipadzakhala anthu oti udzawalamulire padzikoli.—Chiv. 20:4, 5.
Ngati Mulungu atalola kuti adani ake awononge gulu lonse la anthu ake ndiye kuti ulamuliro wake ndiponso mbiri yake zikhoza kukayikiridwa. Izi zikhoza kuipitsa mbiri ya Yehova monga Wolamulira Chilengedwe Chonse. Komanso popeza kuti Yehova amadzilemekeza ndiponso kulemekeza dzina lake loyera, iye sadzalola kuti gulu lonse la anthu ake okhulupirika liwonongedwe. Tiyeneranso kukumbukira kuti Mulungu “sachita chosalungama.” Choncho iye sadzalephera kuteteza gulu la anthu amene akhala akumutumikira mokhulupirika. (Deut. 32:4; Gen. 18:25) Komanso ngati atalola kuti atumiki ake onse awonongedwe ndiye kuti zingasemphane ndi Mawu ake amene amati: “Chifukwa cha dzina lake lalikulu, Yehova sadzasiya anthu ake.” (1 Sam. 12:22) Ndithudi, “Yehova sadzataya anthu ake, kapena kusiya cholowa chake.”—Sal. 94:14.
N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti anthu a Yehova sadzatheratu pa dziko lapansi. Choncho tiyeni tonse tipitirize kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndipo tisamakayikire lonjezo lake lakuti: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana, ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane nawe pamlandu udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndipo chilungamo chawo n’chochokera kwa ine.”—Yes. 54:17.
[Mawu Otsindika patsamba 22]
Mulungu sadzalola kuti anthu ake onse awonongedwe