Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musataye Mtima Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino

Musataye Mtima Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino

Musataye Mtima Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino

“Kwa okwatira ndikupereka malangizo awa, kwenikweni osati ineyo koma Ambuye.”​—1 AKOR. 7:10.

KODI MUNGAFOTOKOZE?

N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu amamanga pamodzi mwamuna ndi mkazi mu ukwati?

Kodi akulu angathandize bwanji Akhristu amene ali ndi mavuto a m’banja?

Kodi ukwati tiyenera kuuona bwanji?

1. Kodi Akhristu amaona bwanji ukwati, nanga n’chifukwa chiyani?

AKHRISTU amene akwatirana amakhala kuti alonjeza pa maso pa Mulungu ndipo lonjezo limeneli si lofunika kuliona mopepuka. (Mlal. 5:4-6) Popeza Yehova ndi amene anayambitsa ukwati ndiye kuti iye ‘amamanga pamodzi’ anthu amene akwatirana. (Maliko 10:9) Kaya malamulo a boma amanena chiyani pa nkhani ya ukwati, Mulungu amaona kuti anthu amene akwatirana amangidwa pamodzi. Ngakhale anthu amene sanali kutumikira Yehova pa nthawi imene ankakwatirana, ayenera kuonabe kuti ukwati wawo suyenera kutha.

2. Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhani ino?

2 Anthu amasangalala kwambiri ngati banja lawo likuyenda bwino. Koma kodi tingatani ngati banja silikuyenda bwino? Kodi banja lotereli likhoza kuyendanso bwino? Kodi anthu amene ali ndi mavuto m’banja mwawo angathandizidwe bwanji?

KODI LIDZAKHALA BANJA LOSANGALALA KAPENA LAMAVUTO?

3, 4. Kodi chingachitike n’chiyani ngati sitisankha mwanzeru wokwatirana naye?

3 Banja la Mkhristu likamayenda bwino, zimakhala zosangalatsa ndipo zimalemekeza Yehova. Koma ngati lasokonekera, zimamvetsa chisoni ndipo zikhoza kubweretsa mavuto aakulu. Mkhristu amene akufuna kulowa m’banja ndipo akufuna kuti zinthu zidzamuyendere bwino, ayenera kutsatira malangizo a Mulungu. Koma ngati munthu sasankha mwanzeru mwamuna kapena mkazi, akhoza kukhumudwa kwambiri ndiponso kumva chisoni. Mwachitsanzo, achinyamata ena amayamba chibwenzi asanakonzekere maudindo amene adzakhale nawo m’banja. Ena amafufuza munthu wokwatirana naye pa Intaneti n’kukwatirana mwamsangamsanga koma zotsatira zake zimakhala mavuto aakulu m’banja. Ena amachita machimo akuluakulu pa nthawi imene ali pa chibwenzi kenako n’kukwatirana. Izi zimachititsa kuti asamalemekezane akalowa m’banja.

4 Akhristu ena sakwatira kapena kukwatiwa “mwa ambuye” ndipo izi zimachititsa kuti akhale ndi mavuto m’banja chifukwa chosiyana zipembedzo. (1 Akor. 7:39) Ngati banja lanu lili lotere, pemphani Mulungu kuti akukhululukireni komanso akuthandizeni. Ngakhale kuti Iye saletsa zotsatira za machimo akale, amathandiza anthu olapa kuti apirire mavuto awo. (Sal. 130:1-4) Yesetsani kumusangalatsa ndi mtima wonse. Mukatero, ‘chimwemwe chimene Yehova amapereka chidzakhala malo anu achitetezo.’​—Neh. 8:10.

NGATI BANJA LILI PAFUPI KUTHA

5. Kodi tiyenera kupewa maganizo ati ngati sitikusangalala m’banja mwathu?

5 Anthu amene ali ndi mavuto m’banja akhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndiziyesetsadi kukhalabe m’banja lamavutoli? Kale likanati lizibwerera, ndikanasankha munthu wina ndipo bwenzi zinthu zikuyenda bwino.’ Akhoza kuganizanso kuti, ‘Bwanji ndingothetsa banjali kuti ndikhalenso ndi ufulu? Ngakhale kuti sindingathetse banja mogwirizana ndi Malemba, ndikhoza kungopatukana naye kuti ndipeze mtendere.’ Si bwino kuganizira zinthu zimenezi kapena za mmene zinthu zikanakhalira mukanapanda kulowa m’banja lanu. M’malomwake, muyenera kufunafuna malangizo a Mulungu ndiponso kuwatsatira n’cholinga choti muthane ndi mavuto m’banja lanu.

6. Fotokozani zimene Yesu ananena pa Mateyu 19:9.

6 Malemba amasonyeza kuti ngati Mkhristu wathetsa banja, akhoza kukhala womasuka kapena wosamasuka kukwatirana ndi wina. Yesu anati: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.” (Mat. 19:9) Pamenepa, mawu akuti “dama” amanena za chigololo ndiponso machimo ena aakulu okhudza kugonana. Ngati Mkhristu akuganizira zothetsa banja pamene wina sanachite dama, m’pofunika kwambiri kupemphera ndiponso kuganizira mozama nkhani imeneyi.

7. Kodi anthu ena angaganize bwanji ngati banja la Akhristu latha?

7 Ngati banja la Mkhristu latha, zikhoza kusonyeza kuti Mkhristuyo sakuchita bwino mwauzimu. Mtumwi Paulo anafunsa funso lofunika kwambiri lakuti: “Ndithudi, ngati munthu sadziwa kuyang’anira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?” (1 Tim. 3:5) Ndipotu banja la anthu amene amati ndi Akhristu likatha anthu oona amangoti, ‘Aa anthu awa amangolalikira koma sachita zimene amanena.’​—Aroma 2:21-24.

8. Kodi vuto limakhala chiyani ngati m’bale ndi mlongo akuganiza zopatukana kapena kuthetsa banja lawo?

8 Ngati Akhristu obatizidwa akukonza zoti apatukane kapena athetse banja lawo popanda zifukwa za m’Malemba ndiye kuti zinthu sizili bwino mwauzimu. N’kutheka kuti mmodzi kapena onse awiri sakutsatira mfundo za m’Malemba. Ngati ‘amakhulupirira Yehova ndi mtima wawo wonse,’ akhoza kuthandiza kuti banja lawo liziyenda bwino.​Werengani Miyambo 3:5, 6.

9. Kodi Akhristu ena adalitsidwa bwanji chifukwa choyesetsa moleza mtima kuthetsa mavuto a m’banja lawo?

9 Mabanja ambiri amene poyamba anali ndi mavuto aakulu anayamba kuyenda bwino. Nthawi zambiri, Akhristu amene sasankha mwamsanga kusiya mwamuna kapena mkazi wawo amadalitsidwa. Taganizirani zimene zingachitike m’banja limene wina ndi wosakhulupirira. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.” (1 Pet. 3:1, 2) Munthu wosakhulupirira akhoza kuphunzira choonadi chifukwa cha khalidwe labwino la mkazi kapena mwamuna wake. Banja limene layamba kuyenda bwino limalemekeza Mulungu ndipo lingakhale dalitso lalikulu kwa mwamuna, mkazi ndiponso ana ngati alipo.

10, 11. Ndi mavuto otani amene banja likhoza kukumana nawo mosayembekezereka, koma kodi Mkhristu sayenera kukayikira za thandizo liti?

10 Akhristu ambiri amasankha mwamuna kapena mkazi amene ndi Mkhristu wobatizidwa chifukwa chofuna kusangalatsa Yehova. Koma ngakhale atachita zimenezi, akhoza kukumana ndi mavuto mosayembekezereka. Mwachitsanzo, wina m’banja akhoza kuyamba matenda a maganizo. Apo ayi, atakwatirana, wina patapita nthawi angadzasiye kulalikira. Zimenezi zinachitikira mlongo wina dzina lake Linda, * yemwe ndi Mkhristu wakhama ndiponso mayi wachikondi. Linda anamva chisoni pamene mwamuna wake, yemwe anali wobatizidwa, anayamba kuchita zinthu zosemphana ndi Malemba mosalapa mpaka kuchotsedwa. Kodi Mkhristu angatani ngati banja lake likusokonekera pa chifukwa ngati chimenechi?

11 Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndiyenera kuyesetsabe kuthetsa mavuto m’banja langa zivute zitani?’ Palibe munthu amene angakusankhireni zochita. Komabe pali zifukwa zomveka zopitirizira kukhala m’banja ngakhale kuti zinthu sizikuyenda bwino. Mkhristu amene amapirira mavuto a m’banja pofuna kuti akhale ndi chikumbumtima chabwino amakhala wamtengo wapatali pa maso pa Yehova. (Werengani 1 Petulo 2:19, 20.) Yehova adzagwiritsa ntchito Mawu ake ndiponso mzimu wake kuti athandize Mkhristu amene akuyesetsa kwambiri kuteteza banja lake limene silikuyenda bwino.

AKULU NDI OKONZEKA KUKUTHANDIZANI

12. Kodi akulu angatione bwanji ngati titawapempha thandizo?

12 Ngati muli ndi mavuto m’banja lanu mungachite bwino kupempha thandizo kwa Akhristu okhwima mwauzimu. Akulu amatumikira monga abusa a nkhosa ndipo angasangalale kukuthandizani kugwiritsa ntchito malangizo a m’Malemba. (Mac. 20:28; Yak. 5:14, 15) Musaganize kuti munyozeka pa maso pa akulu ngati mutawapempha thandizo lauzimu pa mavuto a m’banja lanu. Iwo angakukondeni ndi kukulemekezani kwambiri ngati ataona kuti mumafunitsitsa kusangalatsa Mulungu.

13. Kodi pa 1 Akorinto 7:10-16 pali malangizo otani?

13 Akulu akapemphedwa kuti athandize Mkhristu amene ali pa banja ndi wosakhulupirira, amagwiritsa ntchito malangizo ngati amene Paulo anapereka. Iye anati: “Kwa okwatira ndikupereka malangizo awa, kwenikweni osati ineyo koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna wake, koma ngati angamusiye, akhale choncho wosakwatiwa. Apo ayi, abwererane ndi mwamuna wakeyo. Mwamunanso asasiye mkazi wake. . . . Pakuti mkaziwe, ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse mwamuna wako? Kapena mwamunawe, ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse mkazi wako?” (1 Akor. 7:10-16) Zimakhala zosangalatsa kwambiri ngati mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira wayamba kulambira Yehova.

14, 15. Kodi Mkhristu angasankhe kupatukana ndi mwamuna kapena mkazi wake pa zifukwa ziti, ndipo n’chifukwa chiyani kupemphera za nkhaniyi ndiponso kudzifufuza moona mtima zili zofunika?

14 Kodi mkazi wachikhristu angasankhe ‘kusiya’ kapena kuti kupatukana ndi mwamuna wake pa zifukwa ziti? Ena amasankha kuchita zimenezi ngati mwamuna sakusamalira banja lake mwadala. Ena amatero ngati mwamunayo akumuchitira nkhanza kwambiri kapena ngati akuika moyo wake wauzimu pa ngozi.

15 Munthu ayenera kusankha yekha kupatukana ndi mwamuna kapena mkazi wake. Koma munthu wobatizidwa amene akufuna kuchita zimenezi ayenera kupemphera kwa Yehova n’kudzifufuza moona mtima. Mwachitsanzo, kodi munthu wosakhulupirirayo akuikadi pa ngozi moyo wauzimu wa mnzake? Kapena kodi Mkhristuyo ndi amene wafooka pa nkhani ya kuphunzira Baibulo, kupezeka pa misonkhano ndiponso kulalikira?

16. N’chiyani chingathandize Akhristu kuti asasankhe mopupuluma zothetsa banja?

16 Popeza timafuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndiponso timayamikira mphatso ya ukwati imene iye wapereka, tiyenera kupewa kuthetsa banja mopupuluma. Atumiki a Yehovafe timaganizira kwambiri za kuyeretsa dzina la Mulungu. Choncho sitingapange mapulani othetsa banja n’cholinga choti tikwatire kapena kukwatiwa ndi munthu wina.​—Yer. 17:9; Mal. 2:13-16.

17. Kodi ndi pa nthawi iti pamene tinganene kuti Mulungu waitana Mkhristu kuti akhale mu mtendere?

17 Mkhristu amene ali pa banja ndi munthu wosakhulupirira ayenera kuyesetsa kuteteza ukwati wawo. Koma sayenera kudziimba mlandu ngati pambuyo poyesetsa kwambiri, wosakhulupirirayo wasankha kusiyana naye. Paulo analemba kuti: “Koma ngati wosakhulupirirayo wachoka, achoke. M’bale kapena mlongo sakhala womangika zinthu zikatero, koma Mulungu anakuitanani kuti mukhale mu mtendere.”​—1 Akor. 7:15. *

YEMBEKEZERANI YEHOVA

18. Ngati munthu wayesetsa kuti ateteze banja lake koma n’kutha, kodi pamakhala ubwino uliwonse?

18 Polimbana ndi mavuto a m’banja, muyenera kudalira Yehova kuti akulimbitseni mtima ndipo muyenera kumuyembekezera. (Werengani Salimo 27:14.) Taganizirani za Linda amene tamutchula uja. Iye anayesetsa kwa zaka zambiri kuti ateteze banja lake koma linatha. Kodi iye amaona kuti anangotaya nthawi yake? Iye anati: “Sindinataye nthawi. Zimene ndinachita pofuna kuteteza banja lathu zinathandiza kuti anthu alemekeze Yehova. Panopa chikumbumtima changa n’choyera. Chosangalatsa kwambiri n’chakuti zaka zimenezi zinathandiza kuti mwana wanga wamkazi alimbe m’choonadi. Iye anadzipereka kwa Yehova ndipo ndi mtumiki wakhama kwambiri.”

19. Kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu atayesetsa kuti ateteze banja lake?

19 Mlongo wina dzina lake Marilyn amasangalala kuti ankakhulupirira Mulungu ndipo anayesetsa kuti ateteze banja lake. Iye anati: “Ndinangotsala pang’ono kupatukana ndi mwamuna wanga chifukwa chakuti sankasamalira banja ndipo ankaika moyo wanga wauzimu pa ngozi. Mwamuna wanga anali mkulu, koma anayamba kuchita zinthu zokayikitsa pa bizinezi. Iye anayamba kujomba ku misonkhano ndipo tinasiya kukambirana zinthu. Uchigawenga utavuta mumzinda wathu, ndinkachita mantha kwambiri moti ndinasiya kucheza ndi anthu. Ndiyeno ndinazindikira kuti nanenso ndinkachititsa mavuto ena m’banja. Kenako tinayambanso kukambirana, kuphunzira Baibulo monga banja ndiponso kupezeka pa misonkhano nthawi zonse. Akulu ankatikomera mtima ndiponso kutithandiza kwambiri. Zinthu zinayambanso kuyenda bwino m’banja lathu. Patapita nthawi, mwamuna wanga anayenereranso maudindo mu mpingo. Ndinaphunzira zinthu m’njira yopweteka kwambiri, koma kenako banja lathu linadzakhalanso losangalala.”

20, 21. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani m’banja lathu?

20 Kaya tili pa banja kapena ayi, tiyeni tikhale olimba mtima ndipo tiziyembekezera Yehova. Ngati tili ndi mavuto m’banja tiyeni tiyesetse kuwathetsa podziwa kuti ngati tili m’banja ndiye kuti ‘sitilinso awiri, koma thupi limodzi.’ (Mat. 19:6) Tiyenera kukumbukira kuti ngati titapirira mavuto m’banja limene wina ndi wosakhulupirira, winayo akhoza kuyamba kulambira Yehova. Zimenezi zingakhale zosangalatsa kwambiri.

21 Kaya panopa tikukumana ndi zotani, tiyeni tiyesetse kuchita zinthu mwanzeru n’cholinga choti khalidwe lathu lizichitira umboni kwa anthu amene sali mu mpingo. Ngati banja lathu lili pafupi kutha, tiyeni tizipemphera mwakhama, kudzifufuza moona mtima, kuganizira kwambiri Malemba komanso kupempha thandizo lauzimu kwa akulu. Koposa zonse, tiyeni tikhale ndi mtima wofuna kusangalatsa Yehova Mulungu pa zochita zathu zonse komanso kusonyeza kuti timayamikira kwambiri mphatso ya ukwati imene iye wapereka.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mayina asinthidwa.

^ ndime 17 Onani buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” tsamba 219 mpaka 222; Nsanja ya Olonda ya November 1, 1988, tsamba 26 mpaka 27; September 15, 1975, tsamba 575 (mu Chingelezi).

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Akhristu amene sasankha mwamsanga kusiya mwamuna kapena mkazi wawo amadalitsidwa

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Nthawi zonse tiyenera kuyembekezera Yehova ndiponso kumudalira kuti atilimbitse mtima

[Chithunzi patsamba 9]

Yehova amadalitsa Akhristu amene amayesetsa kuteteza banja lawo limene lili ndi mavuto

[Chithunzi patsamba 11]

Munthu angalimbikitsidwe ndiponso kuthandizidwa mwauzimu mu mpingo wachikhristu