Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziyamikira Mphatso ya Ukwati Yochokera kwa Mulungu

Muziyamikira Mphatso ya Ukwati Yochokera kwa Mulungu

Muziyamikira Mphatso ya Ukwati Yochokera kwa Mulungu

“Yehova akudalitseni. Aliyense apeze mpumulo m’nyumba ya mwamuna wake.”​—RUTE 1:9.

PEZANI MAYANKHO A MAFUNSO AWA:

N’chifukwa chiyani tinganene kuti atumiki a Mulungu akale ankayamikira mphatso ya ukwati?

Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafunitsitsa kuti tisankhe mwanzeru wokwatirana naye?

Kodi ndi malangizo ati a m’Baibulo okhudza ukwati amene mukufuna kutsatira?

1. Kodi Adamu anatani atapatsidwa mkazi?

ADAMU, yemwe anali mwamuna woyamba, anasangalala kwambiri atapatsidwa mkazi moti ananena mawu andakatulo akuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga ndi mnofu wa mnofu wanga. Ameneyutu adzatchedwa Mkazi, chifukwa iyeyu watengedwa kwa mwamuna.” (Gen. 2:23) Yehova atagoneka Adamu tulo tofa nato, anachotsa nthiti yake n’kupangira mkazi wokongola kwambiri ameneyu. Patapita nthawi, Adamu anamupatsa dzina loti Hava. Mulungu anamangitsa banja lawo ndipo iwo ankasangalala kwambiri. Popeza kuti Yehova analenga Hava pogwiritsa ntchito nthiti ya Adamu, ubwenzi wawo unali wolimba kwambiri kuposa mabanja a masiku ano.

2. N’chifukwa chiyani mwamuna ndi mkazi amakopeka ndi mnzake?

2 Chifukwa cha nzeru zake zosayerekezereka, Yehova analenga mwamuna ndi mkazi m’njira yoti wina azikopeka ndi mnzake n’kuyamba kukondana. Buku lina limati: “Mwamuna ndi mkazi amene akukwatirana amayembekeza kuti azigonana mosangalala ndiponso kukondana moyo wawo wonse.” (The World Book Encyclopedia) Izi n’zimene zikuchitika m’mabanja ambiri a anthu a Yehova.

ANTHU AMENE ANAYAMIKIRA MPHATSO YA UKWATI

3. Kodi Isaki anapeza bwanji mkazi?

3 Abulahamu, yemwe anali wokhulupirika, ankalemekeza kwambiri ukwati. Iye anatumiza mtumiki wake wamkulu ku Mesopotamiya kuti akapeze mkazi wa Isaki. Chifukwa chakuti mtumikiyu anapemphera kwa Yehova, anapeza mkazi wabwino. Rabeka, yemwe ankaopa Mulungu, anakhala mkazi wokondedwa wa Isaki ndipo Yehova anamugwiritsa ntchito pokwaniritsa cholinga chake chokhudza mbewu ya Abulahamu. (Gen. 22:18; 24:12-14, 67) Izi sizitanthauza kuti tizilumikiza anthu n’cholinga choti akwatirane asanatipemphe kuchita zimenezi. Masiku ano, anthu ambiri amasankha okha woti akwatirane naye. Mulungu sasankhira munthu mwamuna kapena mkazi. Komabe Mulungu amatha kutsogolera Mkhristu kuti asankhe bwino pa nkhani imeneyi kapena pa zinthu zina. Amatero ngati munthuyo amapemphera kwa iye kuti amutsogolere ndiponso ngati amalola kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu.​—Agal. 5:18, 25.

4, 5. N’chiyani chikusonyeza kuti Msulami ndi m’busa ankakondana kwambiri?

4 Mtsikana wina wa mu Isiraeli, yemwe anali Msulami wokongola kwambiri, sanalole kuti anzake amukakamize kuti akhale mmodzi mwa akazi a Mfumu Solomo. Iye anati: “Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu, kuti musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.” (Nyimbo 8:4) Msulami ankakondana kwambiri ndi m’busa wina. Iye ananena modzichepetsa kuti: “Ine ndine duwa lonyozeka la m’chigwa cha m’mphepete mwa nyanja. Inetu ndine duwa la m’chigwa.” Kodi m’busayo anayankha kuti bwanji? Anati: “Monga duwa pakati pa zitsamba zaminga, ndi mmene alili wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.” (Nyimbo 2:1, 2) Iwo ankakondanadi kwambiri.

5 Msulami ndi m’busayo ankayembekezera kukhala ndi ukwati wolimba kwambiri chifukwa onse ankakonda Mulungu ndi mtima wonse. Msulami anauza m’busa yemwe ankamukonda kwambiriyo kuti: “Undiike pamtima pako ngati chidindo, ndiponso undiike ngati chidindo padzanja lako, chifukwa chikondi n’champhamvu ngati imfa. Mofanana ndi Manda, chikondi sichigonja ndipo chimafuna kudzipereka ndi mtima wonse. Kuyaka kwake kuli ngati kuyaka kwa moto. Chikondicho ndi lawi la Ya [popeza n’chochokera kwa iye]. Madzi ambiri sangathe kuzimitsa chikondi, ndipo mitsinje singachikokolole. Munthu atapereka zinthu zonse zamtengo wapatali za m’nyumba mwake posinthanitsa ndi chikondi, anthu anganyoze zinthuzo.” (Nyimbo 8:6, 7) Mtumiki wa Yehova akamaganizira zolowa m’banja angachite bwino kupeza munthu yemwe angakhale nayedi pa ubwenzi woterewu.

MULUNGU AKUFUNITSITSA KUTI TISANKHE MWANZERU

6, 7. Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu amafuna kuti tisankhe bwino munthu wokwatirana naye?

6 Yehova amafuna kuti musankhe bwino munthu wodzakwatirana naye. Iye anachenjeza Aisiraeli za anthu a ku Kanani kuti: “Usadzachite nawo mgwirizano wa ukwati. Usadzapereke ana ako aakazi kwa ana awo aamuna ndipo usadzatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana ako aamuna. Pakuti adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatire ndipo adzatumikira ndithu milungu ina. Pamenepo mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani ndithu mofulumira.” (Deut. 7:3, 4) Patapita zaka zambirimbiri, Ezara, yemwe anali wansembe, ananena kuti: “Inuyo mwachita zosakhulupirika chifukwa mwatenga akazi achilendo n’kuwonjezera pa machimo a Isiraeli.” (Ezara 10:10) Nayenso mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Mkazi ndi womangika pa nthawi yonse imene mwamuna wake ali moyo. Komano mwamuna wake akamwalira, mkaziyo ndi womasuka kukwatiwa ndi aliyense amene akufuna, koma akwatiwe mwa Ambuye.”​1 Akor. 7:39.

7 Ngati Mkhristu wodzipereka kwa Yehova atakwatirana ndi munthu wosakhulupirira ndiye kuti sakumvera Mulungu. M’masiku a Ezara, Aisiraeli anali osakhulupirika chifukwa ‘anatenga akazi achilendo.’ Kungakhale kulakwa kupeputsa mfundo zosapita m’mbali za m’Malemba. (Ezara 10:10; 2 Akor. 6:14, 15) Mkhristu amene amakwatirana ndi munthu wosakhulupirira sapereka chitsanzo chabwino ndipo amasonyeza kuti sayamikira mphatso ya ukwati imene Mulungu wapereka. Ngati munthu wobatizidwa atachita zimenezi, sangaloledwe kuti achite zinthu zina m’gulu la Mulungu. Sizingakhale zomveka kuti munthu wotere ayembekezere Mulungu kumudalitsa popempha kuti: ‘Yehova, ndasankha kusakumverani koma chonde mundidalitsebe.’

ATATE WATHU WAKUMWAMBA AMADZIWA BWINO ZA UKWATI

8. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo a Mulungu pa nkhani ya ukwati?

8 Munthu wopanga makina ndi amene amadziwa bwino mmene makinawo amagwirira ntchito. Ngati anthu akufuna kulumikiza makinawo, iyeyo ndi amene angapereke malangizo abwino. Kodi chingachitike n’chiyani ngati wina atanyalanyaza malangizo n’kulumikiza mmene akufunira? Makinawo akhoza kusokonezeka, apo ayi sangagwire ntchito n’komwe. Choncho ngati tikufuna kukhala m’banja lachimwemwe, tiyenera kutsatira malangizo a Yehova chifukwa ndi amene anayambitsa ukwati.

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amadziwa zoti munthu akakhala yekha amasungulumwa komanso zoti anthu angasangalale m’banja?

9 Yehova amadziwa zonse zokhudza anthu ndiponso ukwati. Iye ndi amene anapatsa anthu chilakolako chofuna kugonana kuti iwo ‘aberekane ndi kuchuluka.’ (Gen. 1:28) Mulungu amadziwa kuti anthufe tikakhala tokha timasungulumwa. Tikutero chifukwa asanalenge mkazi woyamba, iye anati: “Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.” (Gen. 2:18) Yehova amadziwanso bwino mmene anthu angasangalalire akakhala m’banja.​—Werengani Miyambo 5:15-18.

10. Kodi Akhristu okwatirana ayenera kuganizira mfundo ziti pa nkhani ya kugonana?

10 Chifukwa cha uchimo ndiponso kupanda ungwiro kumene tinatengera kwa Adamu, mabanja a masiku ano sangapeweretu mavuto. Koma atumiki a Yehova akamatsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu amakhala ndi mabanja osangalala. Mwachitsanzo, taganizirani malangizo a Paulo pa nkhani ya kugonana mu ukwati. (Werengani 1 Akorinto 7:1-5.) Sikuti Malemba amati anthu azigonana pongofuna kubereka basi. Anthu okwatirana akhoza kumagonana n’cholinga choti asonyezane chikondi komanso asangalale. Koma Mulungu sasangalala ngati anthu okwatirana akugonana m’njira zosayenera. Amuna ndi akazi achikhristu ayenera kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya kugonana ndiponso kukhala ndi cholinga chosangalatsa mnzake. Akatero, zimakhala zosavuta kusonyezana chikondi. Koma iwo ayenera kupewa kuchita chilichonse chimene chingakhumudwitse Yehova.

11. Kodi Rute anadalitsidwa bwanji chifukwa chotsatira malangizo a Yehova?

11 Munthu ayenera kusangalala m’banja osati kumangokhalira kuti nanga n’tani. M’banja lachikhristu muyenera kukhala ngati malo ampumulo komanso amtendere. Taganizirani zimene zinachitika zaka 3,000 zapitazo. Naomi, yemwe anali wokalamba, anali kuchokera ku Mowabu kupita ku Yuda limodzi ndi Olipa ndi Rute, omwe anali apongozi ake. Akazi onsewa anali amasiye. Naomi anauza apongozi akewo kuti abwerere kwa anthu akwawo. Koma Rute, yemwe anali wa ku Mowabu, sanasiye Naomi. Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu woona ndipo anauzidwa kuti: “Yehova, Mulungu wa Isiraeli akufupe mokwanira. Iye amene m’mapiko mwake wathawiramo ndi kupezamo chitetezo.” (Rute 1:9; 2:12) Rute ankayamikira kwambiri mphatso ya Mulungu ya ukwati. Iye anakwatiwa ndi munthu wachikulire dzina lake Boazi, yemwe anali mtumiki wa Yehova wokhulupirika. Iye akadzaukitsidwa padziko lapansi m’dziko latsopano adzasangalala kwambiri kudziwa kuti anadzakhala kholo la Yesu Khristu. (Mat. 1:1, 5, 6; Luka 3:23, 32) Rute anadalitsidwa kwambiri chifukwa chotsatira malangizo a Yehova.

MALANGIZO OTHANDIZA KUTI BANJA LIZIYENDA BWINO

12. Kodi tingapeze kuti malangizo othandiza pa nkhani ya ukwati?

12 Woyambitsa ukwati amatiuza zinthu zimene zingathandize kuti banja liziyenda bwino. Palibe munthu aliyense amene amadziwa bwino zimenezi koma Baibulo ndi lothandiza nthawi zonse. Choncho munthu akafuna kupereka malangizo abwino pa nkhani ya ukwati, malangizowo ayenera kugwirizana ndi zimene zili m’Baibulo. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.” (Aef. 5:33) M’lembali palibe mawu amene Mkhristu wokhwima mwauzimu anganene kuti sakuwamvetsa. Nkhani yagona pa kutsatira malangizowo. Munthu amene amayamikiradi mphatso ya ukwati amawatsatira. *

13. Kodi chingachitike n’chiyani ngati mwamuna satsatira malangizo opezeka pa 1 Petulo 3:7?

13 Mwamuna wachikhristu ayenera kuchita zinthu ndi mkazi wake mwachikondi. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Inunso amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino, ndi kuwapatsa ulemu monga chiwiya chosalimba, kuti mapemphero anu asatsekerezedwe, pakuti mudzalandira nawo limodzi moyo umene Mulungu adzakupatseni chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.” (1 Pet. 3:7) Mapemphero a mwamuna angatsekerezedwe ngati satsatira malangizo a Yehova. Izi zingachititse kuti moyo wauzimu wa onse m’banja usokonezeke ndipo zingayambitse kuvutika maganizo, mikangano ndiponso kuchitirana nkhanza.

14. Kodi mkazi wachikondi amathandiza bwanji banja lake?

14 Mkazi amene amalola kutsogoleredwa ndi Mawu a Yehova komanso mzimu wake woyera akhoza kuchita zambiri pothandiza kuti m’banja mukhale mtendere ndiponso chimwemwe. Mwachibadwa, mwamuna woopa Mulungu amakonda mkazi wake ndiponso kumuteteza mwakuthupi ndi mwauzimu. Mkazi amafunitsitsa kukondedwa choncho ayenera kuchita zinthu zimene zingachititse mwamunayo kum’konda. Lemba la Miyambo 14:1 limati: “Mkazi amene alidi wanzeru amamanga nyumba yake, koma wopusa amaigwetsa ndi manja ake.” Mkazi wanzeru komanso wachikondi amathandiza kwambiri kuti m’banja mukhale chimwemwe. Amasonyezanso kuti amayamikira kwambiri mphatso ya ukwati imene Mulungu wapereka.

15. Kodi pa Aefeso 5:22-25 pali malangizo otani?

15 Amuna ndi akazi amene amachita zinthu m’banja motsanzira zimene Yesu amachitira mpingo wake, amasonyeza kuti amayamikira mphatso ya ukwati imene Mulungu wapereka. (Werengani Aefeso 5:22-25.) Mwamuna ndi mkazi amadalitsidwa ngati amakondana kwambiri, sadzikuza ndiponso amakambirana monga akuluakulu pakakhala vuto. Amadalitsidwanso ngati amapewa makhalidwe oipa alionse amene angasokoneze ukwati wawo.

MUNTHU ASAWALEKANITSE

16. N’chifukwa chiyani Akhristu ena sakwatira kapena kukwatiwa?

16 Ngakhale kuti anthu ambiri amaganiza zokwatira pa nthawi inayake, atumiki a Yehova ena amakhalabe osakwatira kapena osakwatiwa chifukwa choti sakupeza munthu wowayenerera amenenso ndi wokonda Yehova. Ena ali ndi mphatso ya Mulungu yokhala osakwatira kapena osakwatiwa ndipo amatumikira Yehova ndi mtima wonse popanda zowasokoneza. Anthu amene sali pa banja angatumikire Yehova mosangalala ngati nawonso akutsatira malangizo a Yehova.​—Mat. 19:10-12; 1 Akor. 7:1, 6, 7, 17.

17. (a) Kodi tizikumbukira mawu ati a Yesu pa nkhani ya ukwati? (b) Kodi ngati Mkhristu wayamba kulakalaka mkazi kapena mwamuna wa wina ayenera kuchita chiyani mwamsanga?

17 Kaya tili pa banja kapena ayi, tiyenera kukumbukira mawu a Yesu akuti: “Kodi simunawerenge kuti [Mulungu] amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:4-6) Kulakalaka mkazi kapena mwamuna wa munthu wina ndi tchimo. (Deut. 5:21) Mkhristu yemwe wayamba kuchita zimenezi ayenera kusiya mwamsanga. Popeza kuti iye walola chilakolako chimenechi kukula mumtima mwake, kuchichotsa kungakhale kopweteka kwambiri komabe ayenera kutero. (Mat. 5:27-30) N’kofunika kwambiri kuti tisinthe maganizo oterewa ndi kuchotsa chilakolako choipachi mumtima wathu wonyenga.​—Yer. 17:9.

18. Kodi tiyenera kuona bwanji mphatso ya ukwati imene Mulungu wapereka?

18 Ngakhale anthu amene sakudziwa bwino za Yehova Mulungu ndiponso mphatso yake ya ukwati, amatha kusonyeza kuti amayamikira ukwati. Ngati zili choncho, kuli bwanji ifeyo amene tadzipereka kwa Yehova yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Tiyenera kusangalala ndi zonse zimene iye watipatsa komanso kusonyeza kuti timayamikiradi mphatso yake ya ukwati.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Kuti mumve zambiri pa nkhani ya ukwati, onani mutu 10 ndi 11 m’buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu.”

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Banja likamayenda bwino, limalemekeza Yehova ndipo aliyense m’banjamo amasangalala

[Chithunzi patsamba 5]

Rute anasonyeza kuti ankayamikira mphatso ya ukwati imene Mulungu wapereka

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi mumasonyeza kuti mumayamikiradi mphatso ya ukwati imene Yehova wapereka?