Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Samalani ndi Chofufumitsa cha Afarisi”

“Samalani ndi Chofufumitsa cha Afarisi”

“Samalani ndi Chofufumitsa cha Afarisi”

Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Samalani ndi chofufumitsa cha Afarisi, chimene chili chinyengo.” (Luka 12:1) Mateyu analembanso nkhani yomweyi ndipo zimene ananena zimatithandiza kudziwa kuti Yesu anali kunena za zinthu zoipa zimene Afarisi ankaphunzitsa.​—Mat. 16:12.

Nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti “chofufumitsa” kutanthauza zinthu zimene zimaipitsa munthu. Maganizo a Afarisi ndiponso zimene ankaphunzitsa ziyenera kuti zinaipitsa anthu amene ankawamvetsera. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Afarisi ankaphunzitsa zinali zoipa?

1 Afarisi ankanyada ndipo ankadziona kuti ndi olungama kuposa anthu ena. Iwo ankanyozanso anthu wamba.

Tingaone khalidwe loipa limeneli m’fanizo lina la Yesu. Iye anati: “Mfarisi uja anaimirira ndi kuyamba kupemphera mumtima mwake. Iye anati, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi achigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu. Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu ndipo ndimapereka chakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’ Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’”​—Luka 18:11-13.

Yesu anayamikira kwambiri wokhometsa msonkhoyu chifukwa anali ndi mtima wodzichepetsa. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, Munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kukhala wolungama kwambiri kusiyana ndi [Mfarisi] uja, chifukwa aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzichepetsa adzamukweza.” (Luka 18:14) Ngakhale kuti okhometsa misonkho anali ndi mbiri yokhala achinyengo, Yesu anayesetsa kuthandiza omwe ankafuna kumumvetsera. Timadziwa za anthu awiri okhometsa misonkho omwe anakhala otsatira a Yesu. Iwo anali Mateyu ndiponso Zakeyu.

Kodi ifeyo timaganiza kuti ndife abwino kuposa anthu ena chifukwa cha maluso amene Mulungu watipatsa kapena maudindo amene tapatsidwa m’gulu lake? Kodi mwina timaganiza kuti ndife abwino chifukwa choona zofooka kapena zimene anthu ena amalephera? Tiyenera kuchotseratu maganizo amenewa mwamsanga chifukwa Malemba amati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi.”​—1 Akor. 13:4-6.

Tiyenera kukhala ndi maganizo ngati amene mtumwi Paulo anali nawo. Iye atanena kuti: “Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa,” anapitiriza kuti: “Mwa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.”​—1 Tim. 1:15.

Mafunso Oyenera Kuwasinkhasinkha:

Kodi ndimadziwa kuti ndine wochimwa ndipo ndidzangopulumuka chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova? Kapena kodi ndimadziona kuti ndine wapamwamba chifukwa choti ndatumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri, ndili ndi maudindo m’gulu la Mulungu kapena ndili ndi maluso achibadwa?

2 Afarisi ankachita zinthu zodzionetsera n’cholinga choti aoneke olungama pa maso pa anthu. Iwo ankafuna mayina aulemu ndiponso kuoneka apamwamba.

Koma Yesu anachenjeza kuti: “Zonse zimene amachita, amazichita kuti anthu awaone. Iwo amakulitsa timapukusi tokhala ndi malemba timene amavala monga zodzitetezera, ndipo amakulitsanso ulusi wopota wa m’mphepete mwa zovala zawo. Amakonda malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo ndi mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso kupatsidwa moni m’misika komanso kuti anthu aziwatchula kuti Rabi.” (Mat. 23:5-7) Maganizo a Yesu anali osiyana kwambiri ndi a Afarisi. Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu wangwiro, iye anali wodzichepetsa. Munthu wina atamutchula kuti “wabwino” Yesu ananena kuti: “N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.” (Maliko 10:18) Pa nthawi ina, Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake. Pochita zimenezi, anawapatsa chitsanzo cha kudzichepetsa.​—Yoh. 13:1-15.

Mkhristu weniweni amatumikira anzake. (Agal. 5:13) Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri kwa anthu amene amafuna kukhala oyang’anira mu mpingo. Ngati munthu “akuyesetsa kuti akhale woyang’anira” akuchita bwino koma cholinga chake chiyenera kukhala kuthandiza ena. Kukhala woyang’anira si udindo wapamwamba kapena wopatsa munthu mphamvu zolamulira ena. Munthu amene akutumikira monga woyang’anira ayenera kukhala “wodzichepetsa” ngati Yesu.​—1 Tim. 3:1, 6; Mat. 11:29.

Mafunso oyenera kuwasinkhasinkha:

Kodi ndimakondera anthu amene ali ndi udindo mu mpingo mwina n’cholinga choti ndizilemekezedwa kapena ndipatsidwe maudindo? Kodi ndimakonda kuchita utumiki woonekera kwambiri kwa anthu umene ungawachititse kundiyamikira? Kodi ndimafuna kuoneka wapamwamba?

3 Malamulo ndiponso miyambo ya Afarisi zinachititsa kuti anthu wamba azizunzika potsatira Chilamulo.

Yehova anapereka Chilamulo cha Mose kwa Aisiraeli kuti adziwe mmene angamulambirire. Koma sanawauze zonse zoti azichita kuti atsatire Chilamulochi. Mwachitsanzo, Chilamulo chinaletsa kugwira ntchito tsiku la Sabata, koma sichinafotokoze zonse zimene angachite kapena sangachite pa tsiku limeneli. (Eks. 20:10) Afarisi anawonjezera malamulo ndiponso miyambo chifukwa chakuti ankaganiza kuti Chilamulo cha Yehova sichinafotokoze mokwanira zoyenera kuchita. Koma Yesu ankatsatira Chilamulo cha Mose osati malamulo owonjezera a Afarisiwo. (Mat. 5:17, 18; 23:23) Iye ankazindikira mfundo zazikulu za Chilamulo ndipo ankadziwa kuti kumvera anthu chifundo n’kofunika kwambiri. Iye sankakwiya ngakhale pamene ophunzira ake amukhumudwitsa. Mwachitsanzo, iye atauza ophunzira ake atatu kuti akhale maso usiku umene Yesuyo anagwidwa, iwo ankangogona. Komabe, iye mokoma mtima anawauza kuti: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”​—Maliko 14:34-42.

Mafunso oyenera kuwasinkhasinkha:

Kodi ndimakonza malamulo okhwima kapena kufuna kuti anthu aziyendera maganizo anga? Kodi ndimayembekezera zambiri kwa ena?

Ganizirani kusiyana kwa zimene Yesu ankaphunzitsa ndi zimene Afarisi ankaphunzitsa. Kodi mukuona zinthu zimene mungasinthe kuti mufanane ndi Yesu? Ngati zili choncho, yesetsani kusintha.

[Chithunzi patsamba 28]

Afarisi ankavala timapukusi tokhala ndi malemba.​—Mat. 23:2, 5

[Zithunzi patsamba 29]

Mosiyana ndi Afarisi onyadawo, akulu achikhristu amakhala odzichepetsa ndipo amatumikira ena

[Chithunzi patsamba 30]

Kodi ndinu wokoma mtima ngati Yesu kapena mumayembekezera zambiri kwa ena?