Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbiri ya Moyo Wanga

“Chinsinsi” Chimene Taphunzira Potumikira Mulungu

“Chinsinsi” Chimene Taphunzira Potumikira Mulungu

Yosimbidwa ndi Olivier Randriamora

“Ndithudi, kukhala wosowa ndimakudziwa, kukhala ndi zochuluka ndimakudziwanso. M’zinthu zonse ndi m’zochitika zosiyanasiyana, ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhuta ndi chokhala wanjala. . . . Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—Afil. 4:12, 13.

KWA nthawi yaitali, ine ndi mkazi wanga Oly, takhala tikulimbikitsidwa ndi mawu a mtumwi Paulo amenewa. Mofanana ndi Paulo, kudalira Yehova kwatithandiza kuphunzira “chinsinsi” chimenechi pamene tikumutumikira kuno ku Madagascar.

Mayi a Oly anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova mu 1982. Pa nthawiyi n’kuti ine ndi Oly tikukonzekera kulowa m’banja. Ine ndinavomeranso kuphunzira Baibulo ndipo kenako Oly anayambanso kuphunzira. Tinakwatirana mu 1983 ndipo tinabatizidwa mu 1985. Titangobatizidwa, tinayamba upainiya wothandiza ndipo mu July 1986 tinayamba wokhazikika.

Mu September 1987, tinayamba kutumikira monga apainiya apadera. Poyamba, anatitumiza kukatauni kena kumpoto chakumadzulo kwa Madagascar. Kukatauni kameneka kunalibe mpingo. Ku Madagascar kuli mitundu pafupifupi 18 ya anthu ndiponso timafuko tambirimbiri. Miyambo ya anthu ndiponso zikhalidwe zimasiyanasiyana. Chinenero chachikulu ndi Chimalagase koma kuli zinenero zinanso. Choncho tinaphunzira chinenero chimene anthu akugawo lathu latsopano amalankhula. Zimenezi zinathandiza kuti anthu azitilandira bwino.

Tinkakhala anthu awiri okha pa misonkhano. Poyamba, ndinkakamba nkhani ya onse Lamlungu lililonse ndipo nkhaniyo ikatha Oly ankaombera m’manja. Tinkapanganso zonse za mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Oly ankakamba nkhani ndi mwininyumba woyerekezera. Koma woyang’anira dera atabwera anatiuza mokoma mtima kuti tisinthe zimene tinkachitazo ndipo tinasangalala kwambiri.

Makalata ankatipeza movutikira kwambiri moti miyezi ina sitinkalandira ndalama zoti tigwiritse ntchito. Izi zinathandiza kuti tizolowere kukhala opanda zinthu zina. Pa nthawi ina, tinalibe ndalama zokwanira zoti tikwerere basi popita ku msonkhano wadera umene unkachitika kumalo ena pa mtunda wa makilomita 130. Tinakumbukira malangizo amene m’bale wina anatiuza. Iye anati: “Muuzeni Yehova mavuto anu. Pajatu mukumutumikira iyeyo.” Choncho tinapemphera n’kuganiza zongouyamba wapansi. Koma titangotsala pang’ono kunyamuka, m’bale wina anafika mosayembekezereka n’kutipatsa mphatso ya ndalama. Ndipo zinangochitika kuti ndalamazo zinali zokwanira kukwerera basi.

NTCHITO YOYANG’ANIRA DERA

Mu February 1991, ndinaikidwa kukhala woyang’anira dera. Pa nthawi imeneyo, m’kagulu kathu munali ofalitsa 9. Pa ofalitsa amenewa, atatu anali obatizidwa ndipo tinkasonkhana anthu pafupifupi 50. Atatiphunzitsa ntchito yoyang’anira dera, anatitumiza kudera lina la kulikulu la dzikoli ku Antananarivo. Mu 1993, anatitumiza kudera lina la kum’mawa kwa dzikoli. Moyo wa kumeneku unali wosiyana kwambiri ndi wa mumzinda.

Kuti tikafike ku mipingo kapena ku timagulu takutali, tinkayenda wapansi. Nthawi zina unkakhala ulendo wamakilomita 145 wodutsa m’nkhalango zakumapiri. Tinkayesetsa kukhala ndi katundu wochepa kwambiri. Koma nthawi zina kalelo, nkhani ya woyang’anira dera inkafunika kuonetsa kanema. Zikatero, katundu wathu ankawonjezereka. Oly ankanyamula kanemayo pomwe ine ndinkanyamula batire la galimoto.

Nthawi zambiri, tinkayenda pafupifupi makilomita 40 pa tsiku popita ku mpingo wina. Tinkadutsa m’tinjira tam’mapiri, kuwoloka mitsinje ndiponso kuyenda m’matope. Nthawi zina, tinkagona panjira koma nthawi zambiri tinkafufuza nyumba n’kupempha malo ogona. Pena tinkapempha malo kwa anthu oti sitikuwadziwa ngakhale pang’ono. Tikapeza malo ogona, tinkayamba kuphika chakudya. Oly ankabwereka poto n’kupita kukatunga madzi kumtsinje wapafupi kapena kunyanja. Ine ndikatsala, ndinkabwereka nkhwangwa n’kuyamba kuwaza nkhuni. Chilichonse chinkatenga nthawi yaitali. Nthawi zina, tinkagula nkhuku yamoyo n’kuizinga kenako kuikonzakonza.

Tikatha kudya, tinkatunga madzi osamba. Nthawi zina tinkagona m’khitchini. Kukamagwa mvula tili m’nyumba yodontha, tinkagona kukhoma kwenikweni kuti tisanyowe.

Tinkayesetsa kulalikira kwa anthu amene ankatisunga. Tikafika pa mpingo, abale ndi alongo ankatilandira bwino kwabasi ndipo anali okoma mtima. Iwo ankayamikira kwambiri kufika kwathu moti zimenezi zinkatiiwalitsa mavuto onse amene tinkakumana nawo m’njira.

Tikamakhala kunyumba ya abale ndi alongo, tinkawathandiza ntchito zapakhomo. Izi zinkathandiza kuti azipeza nthawi yolowa nafe mu utumiki. Sitinkayembekezera kuti anthu atipatse chakudya chapadera kapena zinthu zapamwamba zimene sakanakwanitsa.

TINKAYENDERA TIMAGULU TAKUTALI

Tinkasangalala kuyendera timagulu takutali. Ku timagulu timeneti, abale ankatipatsa ntchito yambirimbiri moti nthawi zambiri sitinkapeza mpata woti ‘tipumule pang’ono.’ (Maliko 6:31) Titafika kwina, banja lina linaitana ophunzira Baibulo awo onse okwana 40 kuti tikhale nawo pa phunziro lililonse. Oly anali ndi mlongoyo pa maphunziro 20 pomwe ine ndinali ndi m’baleyo pa maphunziro 20 enawo. Wophunzira wina akachoka, wina ankabwera nthawi yomweyo kuti tiyambe phunziro lake. Ndiyeno nthawi ina tinasiya kaye maphunzirowo n’cholinga choti tichite misonkhano ya mpingo. Misonkhano itatha, tinapitiriza maphunzirowo mpaka cha m’ma 8 koloko usiku.

Titafika ku kagulu kena, tonse m’kaguluko tinanyamuka cha m’ma 8 koloko m’mawa kupita kukalalikira m’mudzi wina. Tonse tinavala zovala zakale. Titayenda nthawi yaitali m’nkhalango, tinafika kumudziwo cha m’ma 12 koloko masana. Ndiyeno tinavala zovala zabwino n’kuyamba kulalikira kunyumba ndi nyumba. Ofalitsa anali ambiri koma nyumba zake zinali zochepa. Choncho tinamaliza gawolo patangopita mphindi 30. Kenako tinapita kumudzi wotsatira. Titalalikira kumeneko, tinanyamuka n’kuyamba chiulendo chobwerera. Poyamba, zimenezi sizinkatisangalatsa. Tinayenda chiulendo chachitali komanso chotopetsa koma kungolalikira ola limodzi lokha. Koma abale ndi alongo akumeneko sankadandaula. Iwo ankachitabe khama.

Kagulu kena ka ku Taviranambo kanali cha pamwamba pa phiri. Kumeneko, tinapeza banja lina la Mboni lomwe linkakhala m’nyumba yopanda chipinda. Chapafupi ndi nyumbayo panali nyumba ina imene ankaigwiritsa ntchito pochita misonkhano. Kenako m’baleyo anayamba kuitana mofuula kwambiri kuti, “Abaaalee!” Ndiyeno tinangomva kuchokera pamwamba pa phiri lina munthu akuyankha kuti, “Ee!” Ndiyeno m’baleyo anati, “Woyang’anira dera uja wafika!” Ndiye enawo anayankha kuti, “Oo! Chabwino.” Zikuoneka kuti uthengawu unafikanso kwa anthu ena amene ankakhala kutali. Pasanapite nthawi yaitali, anthu anayamba kubwera moti pamene tinkayamba misonkhano panali anthu oposa 100.

MAVUTO A KAYENDEDWE

Mu 1996 anatitumizanso kudera lina la pafupi ndi mzinda wa Antananarivo kumapiri a pakatikati pa dzikoli. M’derali munalinso mavuto ake. Panalibe mabasi kapena magalimoto otenga anthu nthawi zonse kupita kumadera akutali kwambiri. Tinayenera kukafika ku kagulu ka kutauni ya Beankàna (Besakay), yomwe inali pa mtunda wa makilomita 240 kuchokera ku Antananarivo. Titakambirana ndi dalaivala wa galimoto ina, anatitenga. M’galimotoyo munali anthu ena pafupifupi 30. Ena anakwera mkati, ena pamwamba ndipo ena anangozendewera kumbuyo.

Tisanapite patali, galimoto inawonongeka panjira ndipo izi sizinali zachilendo. Ife tinangopitiriza wapansi. Titayenda ndithu kwa maola angapo, chigalimoto china chinatipeza. Munali anthu ndi katundu tho koma dalaivala anaimabe. Tinakwera koma tinayenera kungoimirira. Kenako tinafika pamtsinje wina n’kupeza kuti mlatho wake wawonongeka. Tinatsikanso n’kuyamba wapansi mpaka kukafika pakamudzi kena kumene kunkakhala apainiya ena apadera. Ngakhale kuti sunali mpingo woti tichezere pa nthawiyi, tinakhala n’kumalalikira. Tinatero podikira kuti mlathowu ukonzedwe ndiponso kuti galimoto ina idzatitenge.

Galimoto ina inafika patadutsa mlungu umodzi ndipo tinapitiriza ulendo wathu. Msewu wake unali wokumbikakumbika. Nthawi zambiri, tinkatsika n’kukankha galimotoyo kuti iwoloke madzi ofika m’maondo. Pochita zimenezi tinkapunthwa n’kugwa. Tinafika kukamudzi kena m’mawa kusanache ndipo tinatsika. Tinasiya msewu waukulu n’kumadutsa m’tinjira ta m’minda yampunga ndipo tinkayenda m’madzi akuda ofika m’chiuno.

Aka kanali koyamba kufika kuderali, choncho tinaganiza zolalikira kwa anthu amene ankagwira ntchito m’minda yampunga. Tinkafunanso kuwafunsa kumene tingapeze a Mboni za Yehova. Tinasangalala kwambiri kudziwa kuti iwowo anali abale athu auzimu.

TINKALIMBIKITSA ENA KUCHITA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE

Kwa zaka zambiri, tasangalala kuona ubwino wolimbikitsa anthu kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Titafika ku mpingo wina umene unali ndi apainiya okhazikika 9, tinalimbikitsa mpainiya aliyense kuti alimbikitse wofalitsa mmodzi kuyambanso upainiya. Titabwerera ku mpingowu pambuyo pa miyezi 6, tinapeza kuti chiwerengero cha apainiya chafika pa 22. Alongo awiri achitsikana, omwe anali apainiya, anali atalimbikitsa abambo awo kuti ayambe upainiya. Ndipo abale awiriwa, omwe anali akulu, analimbikitsa mkulu wina kuti nayenso ayambe upainiya. Pasanapite nthawi, mkulu wachitatuyu anaikidwa kukhala mpainiya wapadera. Kenako, anadzakhala woyang’anira dera n’kumayenda limodzi ndi mkazi wake. Nanga bwanji akulu awiriwo? Wina ndi woyang’anira dera pomwe wina amagwira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu.

Tsiku lililonse timathokoza Yehova chifukwa chotithandiza. Timadziwa kuti sitingachite chilichonse mwa mphamvu zathu zokha. N’zoona kuti nthawi zina timatopa ndiponso kudwala koma timasangalala tikaganizira zotsatira za utumiki wathu. Yehova amachititsa kuti ntchito yake ipite patsogolo. Panopa tikutumikira monga apainiya apadera ndipo tikusangalala kuthandiza nawo pang’ono pa ntchito yakeyo. Taphunziradi “chinsinsi” chifukwa chodalira Yehova ‘amene amatipatsa mphamvu.’

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Taphunzira “chinsinsi” chifukwa chodalira Yehova

[Mapu/​Zithunzi patsamba 4]

Madagascar ndi chilumba. Dzina lake lina ndi Chilumba Chachikulu Chofiira ndipo ndi chachinayi pa zilumba zikuluzikulu padzikoli. Dothi lake n’lofiira. Zomera ndi zinyama zake zambiri sizipezeka kwina

[Chithunzi patsamba 5]

Kayendedwe kanali kovuta koopsa

[Zithunzi patsamba 5]

Timasangala kwambiri kuchititsa maphunziro a Baibulo