Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Ecuador

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Ecuador

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Ecuador

M’BALE wina wachinyamata wa ku Italy, dzina lake Bruno, anafunika kusankha zochita. Anali atangomaliza kumene maphunziro a ku sekondale ndipo anakhoza bwino kuposa aliyense. Achibale ake ndiponso aphunzitsi anamulimbikitsa kuti apite ku yunivesite. Koma zaka zingapo izi zisanachitike, Bruno anadzipereka kwa Yehova. Iye analonjeza kuti aziika patsogolo chifuniro cha Mulungu. Kodi iye anasankha kuchita chiyani? Bruno anafotokoza kuti: “Ndinauza Yehova m’pemphero kuti ndiziika zofuna zake patsogolo. Koma ndinamuuzanso kuti ndikufuna kuchita zinthu zosiyanasiyana pomutumikira.”

Patapita zaka zochepa, Bruno anapita kudziko la Ecuador ku South America. Iye anati: “Yehova anayankha pemphero langa kuposa mmene ndinkayembekezera.” Atafika, anadabwa kuona kuti kunali achinyamata ambiri omwe anasamukira kumeneko kuti achite zambiri potumikira Yehova.

ACHINYAMATA AMENE AMADALIRA YEHOVA

Mofanana ndi achinyamata ambirimbiri padziko lonse, Bruno anachita zimene Yehova ananena zakuti: “Ndiyeseni chonde . . . kuti muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso.” (Mal. 3:10) Chifukwa chokonda Mulungu, achinyamatawo atsatira lembali. Iwo adzipereka kuti agwiritse ntchito nthawi, mphamvu ndiponso chuma chawo kukatumikira Mulungu kudziko lina kumene ofalitsa Ufumu ndi ochepa.

Achinyamata odziperekawa akafika kumene asamukira, amaona kuti “zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa.” (Mat. 9:37) Mwachitsanzo, Jaqueline wa ku Germany analembera kalata ofesi ya nthambi ya ku Ecuador. Iye anati: “Ndatumikira kuno zaka zoposa ziwiri koma panopa ndili ndi maphunziro 13 kale. Pa anthu amenewa, anayi amafika pa misonkhano nthawi zonse. Kodi kuyenda kwa zinthu kumaposa apa?” Mlongo wina wa ku Canada dzina lake Chantal anati: “Ndinabwera kuno mu 2008 kudzatumikira kudera la m’mphepete mwa nyanja kumene kunali mpingo umodzi wokha. Panopa kuli mipingo itatu ndiponso apainiya oposa 30. N’zosangalatsa kuona anthu ambiri akutsatira zimene aphunzira m’Baibulo.” Iye ananenanso kuti: “Posachedwapa ndinasamukira kumzinda wina umene uli pamwamba kwambiri mamita 2,743 m’mapiri a Andes. Mumzindawu muli anthu oposa 75,000 koma muli mpingo umodzi wokha. Anthu ambiri amafuna kuphunzira Baibulo. Ndikusangalala kwambiri kutumikira kuno.”

MAVUTO AMENE AMAKUMANA NAWO

Kutumikira kudziko lina kuli ndi mavuto ake. Achinyamata ena amakumana ndi mavuto ngakhale asananyamuke kwawo. Mlongo wina wa ku United States, dzina lake Kayla, anati: “Abale ena poona ngati akundithandiza ankanena zinthu zosalimbikitsa. Iwo sankamvetsa cholinga changa chopitira kudziko lina kukachita upainiya. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zina ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ndasankhadi mwanzeru?’” Koma Kayla anasamukabe. Iye anati: “Ndinkapemphera kwambiri kwa Yehova ndiponso kukambirana ndi abale ndi alongo odziwa zambiri. Izi zinandithandiza kudziwa kuti Yehova amadalitsa anthu odzipereka.”

Ambiri amavutika kuphunzira chinenero. Mlongo wina wa kudziko la Ireland, dzina lake Siobhan, anati: “Zinkandipweteka kwambiri kuona kuti ndinkakanika kufotokoza zinthu. Ndinkafunika kuleza mtima, kuchita khama kuphunzira chinenero ndiponso kungoseka ndikalakwitsa.” Mlongo wina wa kudziko la Estonia, dzina lake Anna, anati: “Kuphunzira Chisipanishi kunali kovuta kwambiri poyerekezera ndi kuzolowera nyengo yotentha kwambiri, fumbi ladzaoneni ndiponso kusamba madzi ozizira. Nthawi zina, ndinkaganiza zongosiya. Ndinkafunika kuganizira kwambiri zimene ndinali kukwanitsa osati zimene ndinkalakwitsa.”

Vuto lina limene amakumana nalo ndi kulakalaka kupita kwawo. M’bale wina wa ku United States, dzina lake Jonathan, anati: “Nditangofika, ndinayamba kuvutika chifukwa chosowana ndi anzanga ndiponso achibale. Koma kuchita khama kuphunzira Baibulo ndiponso kulowa mu utumiki kunandithandiza kwambiri. Pasanapite nthawi, pankachitika zinthu zosangalatsa mu utumiki komanso ndinapeza anzanga atsopano mu mpingo. Izi zinandithandiza kuti ndiyambenso kusangalala.”

Vuto linanso ndi lakuti moyo wa kumene munthu wasamukira umasiyana ndi wa kwawo. M’bale wina wa ku Canada, dzina lake Beau, anati: “Kwathu madzi ndi magetsi si nkhani, koma kuno zimavuta.” Kumayiko osauka, kumakhala mavuto chifukwa cha umphawi, kayendedwe ndiponso anthu ambiri sadziwa kuwerenga. Mlongo wina wa ku Austria, dzina lake Ines, amatha kupirira chifukwa choganizira kwambiri makhalidwe abwino a anthu a kumeneko. Iye anati: “Anthu ake ndi ochereza, ofatsa, okonda kuthandizana ndiponso odzichepetsa. Koma chosangalatsa kwambiri n’choti amakonda kuphunzira za Mulungu.”

‘MADALITSO OSOWA POWALANDIRIRA’

Achinyamatawa amene akutumikira ku Ecuador adzipereka kwambiri. Koma iwo amaona kuti Yehova wawapatsa “zazikulu kwambiri kuposa zonse” zimene ankayembekezera. (Aef. 3:20) Iwo akuona kuti alandira ‘madalitso osowa powalandirira.’ (Mal. 3:10) Tamvani zimene ananena.

Bruno: “Nditafika kuno ku Ecuador, ndinayamba kutumikira kudera la Amazon, lomwe ndi lochititsa chidwi. Kenako ndinapemphedwa kuti ndithandize pa ntchito yomanga nthambi ya kuno. Tsopano ndikutumikira pa Beteli. Pamene ndinali ku Italy, ndinasankha kuti ndiziika kutumikira Yehova pa malo oyamba. Panopa, Yehova akundithandiza kukhala ndi moyo wosangalala ndipo ndikuchita zinthu zosiyanasiyana pomutumikira.”

Beau: “Ku Ecuador kuno ndimagwiritsa ntchito nthawi yanga yonse potumikira Mulungu. Izi zandithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. M’mbuyo monsemu ndinkalakalaka kufika m’madera ochititsa chidwi. Zimenezi zathekanso nditabwera kuno.”

Anna: “Sindinkaganiza kuti mlongo wosakwatiwa ngati ineyo akhoza kumakhala ndi moyo wofanana ndi wa amishonale. Koma ndazindikira kuti n’zotheka. Panopa ndikusangalala kwambiri kuphunzitsa anthu Baibulo, kumanga Nyumba za Ufumu ndiponso kupeza anzanga atsopano. Yehova wandidalitsa kwabasi.”

Elke: “Ndili ku Austria ndinkapempha Yehova kuti andithandize kupeza phunziro la Baibulo limodzi. Koma kuno ndili ndi maphunziro 15. Ndimanyadira kwambiri kuona ophunzirawo akusangalala akamatsatira zimene akuphunzira.”

Joel: “N’zosangalatsa kwambiri kutumikira Yehova kudera lachilendo. Munthu umaphunzira kudalira kwambiri Yehova ndipo zimasangalatsa ukaona kuti iye akukudalitsa ukachita khama. Pamene ndinabwera kuno kuchokera ku United States, ndinafikira m’kagulu ka ofalitsa 6. Koma chisanathe chaka anawonjezeka kufika pa 21. Ndipo anthu 110 anafika pa Chikumbutso.”

KODI INUNSO MUNGAKATUMIKIRE KWINA?

Ngati ndinu wachinyamata, kodi mungasamukire kudziko limene kulibe ofalitsa Ufumu ambiri? Koma kuti izi zitheke m’pofunika kukonzekera bwino. Chofunika kwambiri ndi kukonda Yehova ndiponso anthu. Ngati mumakondadi Yehova ndi anthu ndipo mungakwanitse, ipempherereni nkhaniyi mochokera pansi pa mtima. Mungachite bwinonso kukambirana ndi makolo anu komanso akulu mu mpingo. Mwina mudzaona kuti nanunso mungathe kukhala ndi mwayi wosangalatsa wokatumikira Mulungu kudziko lina.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

“Ndinkapemphera kwambiri kwa Yehova ndiponso kukambirana ndi abale ndi alongo odziwa zambiri. Izi zinandithandiza kudziwa kuti Yehova amadalitsa anthu odzipereka.”​—Kayla wochokera ku United States

[Bokosi/Chithunzi Patsamba 6]

Zimene mungachite pokonzekera kukatumikira kudziko lina

• Muzikonda kwambiri kuphunzira Baibulo

• Onaninso Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2011, tsamba 4 mpaka 6

• Lankhulani ndi anthu amene atumikira kudziko lina

• Fufuzani za chikhalidwe ndiponso mbiri ya dzikolo

• Yambani kuphunzira chinenero cha kumeneko

[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]

Mmene ena amapezera ndalama zogwiritsa ntchito potumikira kudziko lina

• Ena amakagwira ntchito kwawo miyezi yochepa pa chaka

• Ena amachititsa lendi nyumba yawo kapena kusiya bizinezi m’manja mwa anthu ena

• Ena amagwirira ntchito pa Intaneti

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

1 Jaqueline wa ku Germany

2 Bruno wa ku Italy

3 Beau wa ku Canada

4 Siobhan wa ku Ireland

5 Joel wa ku United States

6 Jonathan wa ku United States

7 Anna wa ku Estonia

8 Elke wa ku Austria

9 Chantal wa ku Canada

10 Ines wa ku Austria