Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tumikirani Mulungu Amene Amapereka Ufulu

Tumikirani Mulungu Amene Amapereka Ufulu

Tumikirani Mulungu Amene Amapereka Ufulu

“Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 YOH. 5:3.

KODI MUNGAYANKHE?

Kodi Satana amafuna kuti tiziona bwanji malamulo a Mulungu?

N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kwambiri ndi anthu amene timacheza nawo?

N’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu amene amapereka ufulu?

1. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji ufulu wake? Nanga anapatsa Adamu ndi Hava ufulu uti?

YEHOVA yekha ndi amene ali ndi ufulu wopanda malire. Koma sagwiritsa ntchito ufulu wake molakwika ndipo sapanikiza atumiki ake ndi malamulo ambirimbiri. M’malomwake, Mulungu wapatsa anthu ufulu woti azisankha okha zochita. Zimenezi zimawalola kugwiritsa ntchito nzeru zawo ndiponso kuchita zinthu zabwino zimene amalakalaka. Mwachitsanzo, Mulungu anangopatsa Adamu ndi Hava lamulo limodzi basi. Iye anawaletsa kudya “zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” (Gen. 2:17) Kunena zoona, anthuwa anali ndi ufulu wambiri pochita chifuniro cha Mlengi.

2. Kodi makolo athu oyamba anataya bwanji ufulu umene Mulungu anawapatsa?

2 N’chifukwa chiyani Mulungu anapatsa makolo athuwa ufulu wambiri chonchi? Iye anawalenga m’chifaniziro chake ndipo anawapatsa chikumbumtima. Ankayembekezera kuti iwo azichita zinthu zoyenera chifukwa chomukonda. (Gen. 1:27; Aroma 2:15) N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava sanayamikire ufulu umene Mlengi wawo anawapatsa. M’malomwake, anasankha ufulu umene Satana anapereka kuti azisankha okha zabwino ndi zoipa. Koma m’malo mopeza ufulu wambiri, makolo athuwo limodzi ndi ana awo amene anadzabadwa anakhala akapolo a uchimo. Zotsatira zake zinali zoopsa kwambiri.—Aroma 5:12.

3, 4. Kodi Satana amafuna kuti tiziona bwanji mfundo za Yehova?

3 Ngati Satana anakwanitsa kunyengerera anthu awiri angwiro komanso angelo ena kuti akane ulamuliro wa Mulungu, ifenso akhoza kutinyengerera. Satana sanasinthe. Iye amayesetsa kutipusitsa kuti tiziganiza zoti mfundo za Mulungu ndi zolemetsa ndipo zimatiletsa kusangalala. (1 Yoh. 5:3) Anthu ambiri amaganiza choncho ndipo ngati timacheza nawo kwambiri, nafenso tikhoza kutengera maganizo amenewa. Mlongo wina wa zaka 24, amene anachita chiwerewere, anati: “Ndinayamba kutengera maganizo oipa a anzanga chifukwa chakuti sindinkafuna kuoneka wosiyana nawo.” Mwina nanunso mumavutika kukhala osiyana ndi anzanu.

4 N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zina maganizo oipa amachokeranso kwa anthu a mu mpingo wachikhristu. M’bale wina wachinyamata anati: “Ndikudziwa achinyamata ena amene ankachita zibwenzi ndi anthu osakhulupirira. Kenako ndinadzazindikira kuti ndikamacheza nawo kwambiri, ndinkayamba kutengera maganizo awo. Ubwenzi wanga ndi Yehova unayamba kusokonezeka. Sindinkapindula ndi misonkhano ndipo ndinkangopita mu utumiki mwa apo ndi apo. Ndiyeno ndinaona kuti ndi bwino kusiya kucheza nawo.” Kodi inuyo mukudziwa kuti anzanu akhoza kukupotozani maganizo? Tiyeni tikambirane chitsanzo cha m’Baibulo chimene chingatithandize pa nkhaniyi.—Aroma 15:4.

ANAKOPA MITIMA YA ANTHU

5, 6. Kodi Abisalomu anapotoza bwanji maganizo a anthu? Nanga kodi chiwembu chake chinatheka?

5 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anapotoza maganizo a anzawo. Chitsanzo china ndi mwana wa Mfumu Davide, dzina lake Abisalomu. Iye anali mwamuna wooneka bwino kwambiri. Koma mofanana ndi Satana, anayamba kulakalaka udindo ndiponso mphamvu. Anayamba kusirira mpando wachifumu wa abambo ake ngakhale kuti sanali woyenera kukhala pa mpandowu. * Pofuna kulanda ufumu mochenjera, Abisalomu ankanamizira kuti amakonda kwambiri Aisiraeli anzake. Ankawachititsa kuganiza kuti mfumu ndi anthu ake sawaganizira. Mofanana ndi Mdyerekezi m’munda wa Edeni, Abisalomu ankadzionetsa ngati akufuna kuthandiza anthu koma pa nthawi imodzimodziyo akuipitsa mbiri ya atate wake.—2 Sam. 15:1-5.

6 Kodi chiwembu cha Abisalomu chinatheka? Tingati chinathekabe chifukwa Baibulo limati: “Abisalomu anapitiriza kukopa mitima ya anthu a mu Isiraeli.” (2 Sam. 15:6) Koma kenako, Abisalomu sizinamuyendere bwino chifukwa cha kudzikuza kwake. N’zomvetsa chisoni kuti pa mapeto pake Abisalomu anaphedwa limodzi ndi anthu ambirimbiri amene anawakopa.—2 Sam. 18:7, 14-17.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Abisalomu? (Onani chithunzi patsamba 14.)

7 N’chifukwa chiyani Aisiraeliwo anakopeka mosavuta? Mwina n’chifukwa chakuti ankalakalaka zinthu zimene Abisalomu anawalonjeza. Apo ayi, anakopeka ndi maonekedwe ake. Kaya maganizo awo anali otani, mfundo ndi yakuti: Iwo sanali okhulupirika kwa Yehova ndi mfumu yake. Masiku ano, Satana amagwiritsanso ntchito anthu amtima ngati wa Abisalomu kuti akope atumiki a Yehova. Iwo akhoza kutiuza kuti, ‘Mfundo za Yehova n’zopanikiza kwambiri. Wekhanso ukuona mmene anthu osatumikira Yehova akusangalalira.’ Kodi inuyo mudzaona kuti maganizo amenewa ndi bodza lamkunkhuniza n’kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu? Kodi mudzazindikira kuti ‘lamulo langwiro’ la Yehova, kapena kuti lamulo la Khristu, ndi limene lingakupatseni ufulu weniweni? (Yak. 1:25) Ngati ndi choncho, pitirizani kusonyeza kuti mumakonda kwambiri lamuloli ndipo musagwiritse ntchito molakwika ufulu wanu wachikhristu.—Werengani 1 Petulo 2:16.

8. Fotokozani zochitika zenizeni zosonyeza kuti munthu akanyalanyaza mfundo za Yehova sasangalala.

8 Satana amayesetsa kunyengerera makamaka achinyamata. M’bale wina, amene tsopano ali ndi zaka zoposa 30, anafotokoza za nthawi imene anali wachinyamata kuti: “Ndinkaona kuti mfundo za Yehova zokhudza makhalidwe n’zopanikiza osati zoteteza.” Chifukwa choganiza chonchi, iye anachita chiwerewere. Koma atachita zimenezi, sanasangalale. Iye anati, “Kwa zaka zambiri, ndinkadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zimene ndinachitazo.” Pokumbukira zimene anachita ali wachinyamata, mlongo wina analemba kuti: “Ukachita chiwerewere, umadziona kukhala wachabechabe. Panopa papita zaka 19 koma zimandipwetekabe ndikamakumbukira.” Mlongo wina anati: “Zinkandipweteka ndiponso kundisokoneza kwambiri ndikaganiza kuti zochita zanga zakhumudwitsa anthu amene ndimawakonda kwambiri. Ubwenzi ndi Yehova ukasokonekera, zinthu siziyenda.” Satana amafuna kuti tisamaganizire mavuto amene tingakumane nawo tikachimwa.

9. (a) Kodi ndi mafunso ati amene tingachite bwino kudzifunsa ponena za Yehova, malamulo ake ndiponso mfundo zake? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kumudziwa bwino kwambiri Mulungu?

9 Nthawi zambiri munthu amavutika koopsa akachita zosangalatsa zauchimo. N’zomvetsa chisoni kuti achinyamata ambiri m’gulu la Yehova komanso achikulire ena azindikira mfundo imeneyi pambuyo pokumana ndi mavuto. (Agal. 6:7, 8) Choncho dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimazindikira ziwembu za Satana akamayesa kundikopa? Kodi ndimaona kuti Yehova ndi mnzanga wapamtima amene amandiuza zoona zokhazokha ndiponso amandifunira zabwino? Kodi ndimakhulupiriradi kuti iye sangandimane chinthu chabwino chimene chingandithandize kukhala wosangalala?’ (Werengani Yesaya 48:17, 18.) Mungathe kuyankha kuti inde mochokera pansi pa mtima ngati mumadziwa bwino kwambiri Yehova. Muyenera kuzindikira kuti anapereka malamulo ndi mfundo zake m’Baibulo chifukwa chokukondani osati kufuna kukupanikizani.—Sal. 25:14.

MUZIPEMPHA MULUNGU KUTI AKUPATSENI MTIMA WANZERU NDI WOMVERA

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kutsanzira zimene Mfumu Solomo inachita ili mnyamata?

10 Solomo ali wachinyamata anapemphera kuti: “Komatu ndine mwana ndipo sindikudziwa zinthu zambiri.” Kenako anapempha Mulungu kuti amupatse mtima wanzeru ndi womvera. (1 Maf. 3:7-9, 12) Yehova anayankha pemphero lake lochokera pansi pa mtimali. Akhozanso kuyankha mapemphero anu, kaya ndinu wamng’ono kapena wamkulu. N’zoona kuti Yehova sangakupatseni nzeru m’njira yozizwitsa, koma akhoza kukuthandizani kukhala anzeru. Angatero ngati mumaphunzira mwakhama Mawu ake, kupempha mzimu wake woyera ndiponso kutsatira malangizo amene amapereka kudzera mu mpingo. (Yak. 1:5) Yehova amathandiza atumiki ake, ngakhale ang’onoang’ono, kukhala anzeru. Iwo amaposa anthu onse amene amanyalanyaza malangizo a Yehova, kuphatikizapo amene amaonedwa m’dzikoli kuti ndi “anzeru ndi ozama m’maphunziro.”—Luka 10:21; werengani Salimo 119:98-100.

11-13. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa Salimo 26:4, Miyambo 13:20 ndi 1 Akorinto 15:33? (b) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo za m’malemba amenewa?

11 Tiyeni tikambirane malemba ena kuti timvetse ubwino wophunzira Baibulo ndiponso kusinkhasinkha n’cholinga choti tidziwe bwino Yehova. Lemba lililonse likufotokoza mfundo yofunika kwambiri yotithandiza kusankha bwino anthu ocheza nawo. Loyamba limati: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu achinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.” (Sal. 26:4) Lachiwiri limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miy. 13:20) Lomaliza limati: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akor. 15:33.

12 Kodi tikuphunzira chiyani pa malemba amenewa? (1) Yehova amafuna kuti tizisamala posankha anthu ocheza nawo. Amafuna kutiteteza kuti tisakhale ndi makhalidwe oipa komanso tisawononge ubwenzi wathu ndi iye. (2) Anthu amene timacheza nawo angatilimbikitse kuchita zabwino kapena zoipa. Mfundo imeneyi ndi yosatsutsika. Mavesiwa analembedwa m’njira yosonyeza kuti Yehova akufuna kutifika pamtima kuti tizindikire tokha zoyenera kuchita. N’chifukwa chiyani tikutero? Onani kuti malemba onsewa sanalembedwe ngati malamulo. Sanena kuti, “Musachite zakutizakuti.” M’malomwake, anangowalemba monga mfundo zoona. Zili ngati Yehova akunena kuti, ‘Mfundo zoona ndi izi. Kodi ukumva bwanji mumtima mwako? Uzitsatira kapena suzitsatira?’

13 Popeza kuti malembawa analembedwa monga mfundo zoona, amagwirabe ntchito masiku ano ndipo amathandiza anthu pa zochitika zosiyanasiyana. Mungachite bwino kudzifunsa kuti: Kodi ndingapewe bwanji kucheza ndi “anthu obisa umunthu wawo”? Kodi anthu oterewa ndingakumane nawo kuti? (Miy. 3:32; 6:12) Kodi “anthu anzeru” amene Yehova akufuna kuti ndizicheza nawo ndi ati? Nanga “anthu opusa” amene iye akufuna kuti ndiziwapewa ndi ati? (Sal. 111:10; 112:1; Miy. 1:7) Kodi ndi “makhalidwe abwino” ati amene ndingawawononge chifukwa chogwirizana ndi anthu oipa? Kodi anthu osayenera kucheza nawo amangopezeka kudziko kokha? (2 Pet. 2:1-3) Kodi inuyo mungayankhe bwanji mafunso amenewa?

14. Kodi mungatani kuti Kulambira kwa Pabanja kukhale kothandiza kwambiri?

14 Mungachite bwino kuwerenga malemba ena n’kuwaganizira ngati mmene tachitira ndi malemba atatuwa. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zofunika kwa inuyo ndi banja lanu. * Ngati ndinu makolo mungachite bwino kukambirana nkhani zoterezi pa Kulambira kwa Pabanja. Mukamachita zimenezi, cholinga chanu chizikhala kuthandiza aliyense m’banjamo kuzindikira kuti Mulungu anapereka malamulo ndi mfundo chifukwa chakuti amatikonda kwambiri. (Sal. 119:72) Kuphunzira m’njira imeneyi kudzathandiza kuti m’banjamo muzikondana komanso muzikonda Yehova.

15. Kodi mungadziwe bwanji ngati muli ndi mtima wanzeru ndiponso womvera?

15 Kodi mungadziwe bwanji ngati muli ndi mtima wanzeru ndiponso womvera? Njira ina ndi kuona ngati maganizo anu akufanana ndi a anthu okhulupirika akale. Mwachitsanzo, Mfumu Davide inalemba kuti: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.” (Sal. 40:8) Nayenso wolemba Salimo 119 anati: “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.” (Sal. 119:97) Muyenera kuchita khama kuti nanunso muzikonda kwambiri malamulo a Mulungu. Mungachite zimenezi pophunzira Baibulo mozama, kupemphera ndiponso kusinkhasinkha. Mungakondenso malamulowo mukamaganizira madalitso amene mwapeza chifukwa chotsatira mfundo za Mulungu.—Sal. 34:8.

MUZIMENYERA NKHONDO UFULU WANU WACHIKHRISTU

16. Kodi tiyenera kuzindikira chiyani kuti tipambane pa nkhondo yomenyera ufulu weniweni?

16 Kwa zaka zambiri, mayiko akhala akumenyana koopsa kuti apeze ufulu. Ndiye kuli bwanji inuyo? Muyenera kumenya kwambiri nkhondo yauzimu kuti mukhalebe ndi ufulu wachikhristu. N’zoona kuti Satana, dzikoli ndiponso mzimu wake woipa ndi adani anu. Koma zindikirani kuti mdani wanu wina ndi thupi lanu lopanda ungwiro, lomwe likuphatikizapo mtima wanu wonyenga. (Yer. 17:9; Aef. 2:3) Koma Yehova akhoza kukuthandizani kupambana pa nkhondoyi. Nthawi iliyonse imene mwapambana pamachitika zinthu ziwiri zabwino. Choyamba, mumakondweretsa mtima wa Yehova. (Miy. 27:11) Chachiwiri, mukaona kuti mwapezadi ufulu chifukwa chotsatira ‘lamulo langwiro,’ mumakhala wofunitsitsa kuyendabe pa ‘msewu wopanikiza’ wopita ku moyo wosatha. M’tsogolomu, mudzapeza ufulu wosaneneka umene Yehova adzapatsa anthu ake okhulupirika.—Yak. 1:25; Mat. 7:13, 14.

17. N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwa ulesi tikalakwitsa zinazake? Kodi Yehova adzatithandiza bwanji?

17 N’zoona kuti nthawi zina timalakwitsa zinthu. (Mlal. 7:20) Izi zikachitika simuyenera kukhumudwa kwambiri kapena kudziona kuti ndinu wopanda pake. Ngati mwapunthwa, ingonyamukaninso n’kumapita patsogolo ngakhale kupempha akulu kuti akuthandizeni. Yakobo analemba kuti: “Pemphero [lawo] lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.” (Yak. 5:15) Musaiwale kuti Mulungu ndi wachifundo ndipo ndi amene anakukokerani mu mpingo wake. Anachita zimenezi chifukwa anaona kuti mungathe kuchita zabwino. (Werengani Salimo 103:8, 9.) Choncho ngati mupitirizabe kutumikira Yehova ndi mtima wonse, iye sadzasiya kukuthandizani.—1 Mbiri 28:9.

18. Kodi tingatani kuti Yehova azitiyang’anira mogwirizana ndi lemba la Yohane 17:15?

18 Usiku woti aphedwa mawa lake Yesu anapemphera ndi atumwi ake 11 okhulupirika. Powapempherera, ananena mawu olimbikitsa akuti: “Muwayang’anire kuopera woipayo.” (Yoh. 17:15) Apa sikuti Yesu ankangoganizira za atumwi ake okha koma za anthu onse omutsatira. Choncho tisakayikire zoti Yehova ayankha pemphero la Yesu potiyang’anira m’masiku ovuta ano. “Kwa anthu oyenda ndi mtima wosagawanika, [Yehova] amakhala chishango . . . ndipo adzateteza njira ya anthu ake okhulupirika.” (Miy. 2:7, 8) N’zoona kuti tizikumana ndi mavuto osiyanasiyana poyesetsa kutumikira Yehova ndi mtima wosagawanika. Koma ndi njira yokhayi imene ingatithandize kupeza moyo wosatha komanso ufulu weniweni. (Aroma 8:21) Musalole kuti aliyense akupatutseni panjirayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Lonjezo la Mulungu lonena za “mbewu” ya Davide yodzabadwa m’tsogolo, imene idzatenge mpando wachifumu, linaperekedwa Abisalomu atabadwa kale. Choncho Abisalomu anayenera kudziwa kuti sanasankhidwe ndi Yehova kuti alowe ufumu wa Davide.—2 Sam. 3:3; 7:12.

^ ndime 14 Mungakambirane 1 Akorinto 13:4-8, pamene Paulo akufotokoza za chikondi. Mungakambiranenso Salimo 19:7-11, pamene akufotokoza madalitso amene anthu omvera malamulo a Yehova amapeza.

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 14]

Kodi tingadziwe bwanji anthu amtima ngati wa Abisalomu ndipo tingadziteteze bwanji kuti asatikope?