Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Akusonkhanitsa Banja Lake

Yehova Akusonkhanitsa Banja Lake

Yehova Akusonkhanitsa Banja Lake

‘Ndikukuchondererani kuti muzisunga umodzi wathu mwa mzimu.’—AEF. 4:1, 3.

KODI MUNGAFOTOKOZE BWANJI?

Kodi cholinga cha dongosolo la Mulungu n’chiyani?

Kodi tingasunge bwanji ‘umodzi wathu mwa mzimu’?

N’chiyani chingatithandize ‘kukhala okomerana mtima’?

1, 2. Kodi cholinga cha Yehova chokhudza dziko lapansi ndiponso anthu n’chiyani?

KODI mumaganiza za chiyani mukamva mawu oti banja? Kodi mumaganiza za chikondi, chimwemwe kapena kuchitira zinthu limodzi? Kapena mumaganiza za malo abwino amene munthu angakuliremo ndiponso kuphunzira zinthu zosiyanasiyana? Mukhoza kuganizira zonsezi ngati m’banja lanu anthu amakondana. Yehova ndi amene anayambitsa banja. (Aef. 3:14, 15) Cholinga chake chinali chakuti onse m’banja lake kumwamba ndiponso padziko lapansi akhale otetezeka, azikhulupirirana ndiponso azigwirizana.

2 Adamu ndi Hava atachimwa, anthu sanakhalenso m’banja la Mulungu. Koma zimenezi sizinalepheretse cholinga cha Yehova. Iye adzaonetsetsa kuti dziko lapansi likhale Paradaiso ndipo lidzaze ndi ana a Adamu ndi Hava. (Gen. 1:28; Yes. 45:18) Mulungu wakonza kale njira yokwaniritsira cholinga chakechi. Zinthu zina zimene Mulungu wakonza kuti akwaniritse cholingachi zafotokozedwa m’buku la Aefeso. Bukuli kwenikweni limanena za mgwirizano. Tiyeni tikambirane mavesi ena a m’bukuli n’cholinga choti tione zimene tingachite kuti tigwirizane ndi cholinga cha Yehova chogwirizanitsa banja lake lonse.

CHOLINGA CHA DONGOSOLO LA MULUNGU

3. Kodi dongosolo la Mulungu lotchulidwa pa Aefeso 1:10 n’chiyani? Nanga mbali yake yoyamba inayamba liti?

3 Yehova amachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake. Choncho pa nthawi yake, Mulungu anakhazikitsa “dongosolo” loti agwirizanitse onse a m’banja lake. (Werengani Aefeso 1:8-10.) Dongosolo limeneli lili ndi mbali ziwiri. Mbali yoyamba ndi yokonzekeretsa Akhristu odzozedwa kuti akakhale kumwamba n’kumatsogoleredwa ndi Yesu Khristu. Mbali imeneyi inayamba pa Pentekosite m’chaka cha 33 C.E. Pa nthawiyi, Yehova anayamba kusonkhanitsa anthu oti adzalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba. (Mac. 2:1-4) Chifukwa cha nsembe ya dipo ya Khristu, Mulungu amaona kuti odzozedwa ndi olungama ndiponso oyenerera moyo. Odzozedwawa amadziwa kuti iwowo tsopano ndi “ana a Mulungu.”—Aroma 3:23, 24; 5:1; 8:15-17.

4, 5. Kodi mbali yachiwiri ya dongosolo la Mulungu ndi iti?

4 Mbali yachiwiri ndi yokonzekeretsa anthu amene adzakhale m’Paradaiso padziko lapansi motsogoleredwa ndi Ufumu wa Mesiya. Anthu a “khamu lalikulu” adzakhala oyamba kukhala m’Paradaiso. (Chiv. 7:9, 13-17; 21:1-5) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, anthu mabiliyoni ambiri adzaukitsidwa kuti adzakhale nawo m’Paradaiso. (Chiv. 20:12, 13) Anthuwa akadzaukitsidwa m’pamene zidzaonekere kwambiri kuti ndife ogwirizana. Ku mapeto kwa zaka 1,000 zimenezi, “zinthu zapadziko lapansi,” kapena kuti anthu okhala padziko, adzayesedwa komaliza. Anthu onse okhulupirika nawonso adzakhala “ana a Mulungu” padziko lapansi.—Aroma 8:21; Chiv. 20:7, 8.

5 Mbali zonse ziwiri, zomwe ndi kusonkhanitsa anthu opita kumwamba ndi okhala padziko lapansi, zikukwaniritsidwa masiku ano. Koma kodi aliyense payekha angatani kuti achite zinthu mogwirizana ndi dongosololi?

‘TIZISUNGA UMODZI WATHU MWA MZIMU’

6. Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti Akhristu ayenera kusonkhana?

6 Malemba amasonyeza kuti Akhristu ayenera kusonkhana pamodzi. (1 Akor. 14:23; Aheb. 10:24, 25) Mawu oti kusonkhana satanthauza kungokhala pamalo amodzi ngati mmene anthu amachitira kumsika kapena kubwalo la masewera. Kungokhala pamalo amodzi sikuchititsa anthu kugwirizana. Timagwirizana tikamatsatira malangizo a Yehova ndiponso kutsogoleredwa ndi mzimu wake woyera.

7. Kodi tingatani kuti ‘tisunge umodzi wathu mwa mzimu’?

7 Popeza kuti timakhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu, Yehova amationa kuti ndife olungama. Iye amaona kuti odzozedwa ndi ana ake ndipo nkhosa zina ndi mabwenzi ake. Ngakhale zili choncho, m’dziko loipali nthawi zina timasemphana maganizo. (Aroma 5:9; Yak. 2:23) N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti tiyenera kupitiriza ‘kulolerana.’ Kodi tingatani kuti tizigwirizana ndi Akhristu anzathu? Tiyenera kuyesetsa kukhala ‘odzichepetsa nthawi zonse ndiponso ofatsa.’ Paulo anatilimbikitsa kuti ‘tiziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimu, ndi mwamtendere monga chomangira chotigwirizanitsa.’ (Werengani Aefeso 4:1-3.) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kulola mzimu wa Mulungu kutitsogolera ndiponso kutithandiza kukhala ndi makhalidwe amene mzimuwu umatulutsa. Makhalidwe amenewa amatigwirizanitsa koma ntchito za thupi zimasokoneza mgwirizano.

8. Kodi ntchito za thupi zimasokoneza bwanji mgwirizano?

8 Tiyeni tione mmene “ntchito za thupi” zimasokonezera mgwirizano. (Werengani Agalatiya 5:19-21.) Dama limasiyanitsa munthu ndi Yehova ndiponso ndi mpingo. Chigololo chikhoza kulekanitsa ana ndi makolo awo komanso munthu wosalakwa ndi mwamuna kapena mkazi wake. Zinthu zodetsa zimasokoneza mgwirizano umene munthu amakhala nawo ndi Mulungu ndiponso anzake. N’chimodzimodzi ndi mmene zimakhalira munthu akafuna kumata zinthu ziwiri pamodzi. Ngati chimodzi chili ndi fumbi, zinthuzo sizingamatike bwino. Khalidwe lopanda manyazi limasonyeza kuti munthu salemekeza ngakhale pang’ono malamulo olungama a Mulungu. Ntchito zonse za thupi zimasiyanitsa munthu ndi anzake komanso ndi Mulungu. Yehova amadana ndi ntchito zonsezi.

9. Kodi tingadzifunse mafunso ati kuti tione ngati tikuyesetsa ‘ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimu’?

9 Tonsefe tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayesetsa ndi mtima wonse “kusunga umodzi wathu mwa mzimu, ndi mwamtendere monga chomangira chotigwirizanitsa”? Kodi ndimatani pakakhala mavuto? Kodi ndimakonda kuuza anthu ambiri n’cholinga choti andiikire kumbuyo? Kodi ndimafuna kuti akulu andithetsere mavuto anga ndikasemphana maganizo ndi munthu wina m’malo moyesetsa pandekha kukhazikitsa mtendere? Kodi ndimapewa anthu amene amaona kuti ndawalakwira n’cholinga choti tisakambirane?’ Kodi kuchita zinthu zimenezi kungasonyeze kuti tikugwirizana ndi cholinga cha Yehova chosonkhanitsa anthu kuti akhale banja limodzi lolamuliridwa ndi Khristu?

10, 11. (a) Kodi kukhala pa mtendere ndi abale athu n’kofunika bwanji? (b) Kodi tingachite chiyani kuti tilimbikitse mtendere ndiponso kuti Yehova atidalitse?

10 Yesu anati: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako. Thetsa nkhani mofulumira.” (Mat. 5:23-25) Yakobo analemba kuti: “Chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.” (Yak. 3:17, 18) Choncho sitingapitirize kuchita chilungamo ngati sitili pa mtendere ndi anthu ena.

11 Mwachitsanzo, m’madera amene kunkachitika nkhondo, malo ambiri salimidwa chifukwa choti anthu amaopa mabomba amene anakwiriridwa. Bomba likaphulika, anthu amasiya kulima dera lonselo. Izi zimachititsa kuti anthu a m’midzi asowe ntchito ndipo m’mizinda anthu amasowanso chakudya. Ifenso tikhoza kukhala ngati mabombawa ngati timavutika kukhala mwamtendere ndi anthu ena. Izi zingatilepheretse kukhala ndi makhalidwe abwino. Ngati zili choncho, tiyenera kusintha. Tikamafulumira kukhululuka ndiponso kuchitira ena zabwino, tingakhale pa mtendere ndiponso Yehova adzatidalitsa.

12. Kodi akulu angatithandize bwanji kuti tikhale ogwirizana?

12 Akulu, omwe ndi “mphatso za amuna,” amathandizanso kwambiri kuti ‘tifike pa umodzi m’chikhulupiriro.’ (Aef. 4:8, 13) Izi zikutanthauza kuti amathandiza mpingo kukhala wogwirizana. Iwo amatithandiza kuti tivale umunthu watsopano. Amachita zimenezi potumikira nafe limodzi komanso kutipatsa malangizo ochokera m’Baibulo. (Aef. 4:22-24) Kodi akulu akakupatsani malangizo, mumaona kuti Yehova akukukonzekeretsani kukhala m’dziko latsopano? Ngati ndinu mkulu, kodi mumalangiza anthu n’cholinga choti muwathandize kupulumuka?—Agal. 6:1.

“KHALANI OKOMERANA MTIMA”

13. Kodi chingachitike n’chiyani ngati sititsatira malangizo a pa Aefeso 4:25-32?

13 Pa Aefeso 4:25-29 pali makhalidwe amene tiyenera kuwapewa. Makhalidwe ake ndi monga chinyengo, mkwiyo, ulesi ndiponso kulankhula mawu owola m’malo molankhula mawu abwino olimbikitsa. Munthu amene satsatira malangizo amenewa amasokoneza mtendere. Choncho amamvetsa chisoni mzimu woyera umene umalimbikitsa mgwirizano. (Aef. 4:30) Kuti tilimbikitse mtendere, tiyeneranso kutsatira malangizo amene Paulo ananena m’mavesi otsatira. Iye anati: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse. Koma khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso Mulungu anakukhululukirani ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.”—Aef. 4:31, 32.

14. (a) N’chifukwa chiyani Paulo analemba malangizo oti “khalani okomerana mtima”? (b) N’chiyani chingatithandize kukhala okoma mtima?

14 Anthufe tikanakhala kuti timakomerana mtima nthawi zonse, Paulo sakanalemba mawu oti “khalani okomerana mtima.” Mawu akewa akusonyeza kuti tifunika kusintha. Tiziganizira zofuna za ena m’malo mongoganizira zofuna zathu. (Afil. 2:4) Nthawi zina timafuna kulankhula zinthu zoseketsa kapena zoti anthu aone kuti ndife ochenjera. Koma tiziyamba tadzifunsa ngati zimene tingalankhulezo zingasonyeze kuti ndife okoma mtima. Kuganizira zimenezi tisanalankhule kungatithandize kukhala okoma mtima.

MUZIKONDANA NDIPONSO KULEMEKEZANA M’BANJA

15. Kodi lemba la Aefeso 5:28 limathandiza bwanji amuna kudziwa mmene angatsatirire Khristu?

15 Baibulo limasonyeza kuti mpingo uli ngati mkazi wa Khristu. Chitsanzo cha Khristu chimathandiza amuna kudziwa kuti ayenera kukonda, kusamalira ndiponso kutsogolera bwino akazi awo. Chitsanzochi chimathandizanso akazi kudziwa kuti ayenera kugonjera amuna awo. (Aef. 5:22-33) Paulo analemba kuti: “Mwa njira imeneyi amuna akonde akazi awo monga matupi awo.” (Aef. 5:28) Kodi ankanena za njira iti? Paulo asananene mawu amenewa, anafotokoza mmene “Khristu anakondera mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo, ndipo anauyeretsa pousambitsa m’madzi a mawu a Mulungu.” Choncho mwamuna ali ndi udindo wophunzitsa banja lake Mawu a Mulungu. Akatero ndiye kuti akuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Yehova chosonkhanitsa anthu m’banja limodzi lolamulidwa ndi Khristu.

16. Kodi chimachitika n’chiyani ngati makolo akukwaniritsa udindo wawo wochokera kwa Yehova?

16 Makolo ayenera kukumbukira kuti Yehova anawapatsa udindo wosamalira ana. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri masiku ano sakonda ana awo. (2 Tim. 3:1, 3) Azibambo ambiri amanyalanyaza udindo wawo ndipo zimenezi zimasokoneza kwambiri moyo wa ana awo. Paulo analangiza azibambo achikhristu kuti: “Musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Ana amayambira m’banja kudziwa za chikondi, ulemu ndiponso kumvera. Makolo amene amaphunzitsa ana awo zimenezi amachita mogwirizana ndi cholinga cha Yehova chogwirizanitsa anthu. Tiyenera kusonyeza chikondi m’banja ndiponso kupewa kupsa mtima, mkwiyo ndiponso mawu achipongwe. Imeneyi ndi njira yabwino yophunzitsa ana athu chikondi, ulemu ndiponso kumvera. Zimenezi zimawathandiza kukonzekera moyo wa m’dziko latsopano.

17. Kodi tiyenera kutani kuti tilimbane ndi Mdyerekezi?

17 Tiyenera kudziwa kuti Mdyerekezi aziyesetsa kwambiri kutisokoneza pamene tikuchita chifuniro cha Mulungu. Pajatu iye ndi amene anasokoneza mtendere poyambirira. Anthu ambiri masiku ano akuchita zofuna za Satana. Mabanja akutha, anthu angotengana m’malo mokwatirana mwalamulo ndipo ambiri amavomereza ukwati wa amuna kapena akazi okhaokha. Koma ife sitiyenera kutengera makhalidwe a anthu a m’dzikoli. M’malomwake timatsanzira Khristu. (Aef. 4:17-21) Kuti tipambane pa nkhondo yolimbana ndi Mdyerekezi ndiponso ziwanda zake, tiyenera kutsatira malangizo akuti tivale “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.”—Werengani Aefeso 6:10-13.

“YENDANIBE M’CHIKONDI”

18. N’chiyani chingatithandize kwambiri kukhala ogwirizana?

18 Chikondi n’chimene chingatithandize kwambiri kukhala ogwirizana. Popeza timakondana ndi mtima wonse komanso kukonda kwambiri Ambuye wathu Yesu Khristu ndiponso Mulungu wathu Yehova, tiziyesetsa kukhala mwamtendere ndiponso mogwirizana. (Aef. 4:3-6) Yesu anatchula za chikondi chimenechi m’pemphero lake. Iye anati: “Sindikupemphera awa okha, komanso amene amakhulupirira ine kudzera m’mawu awo, kuti onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana, kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife . . . Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”—Yoh. 17:20, 21, 26.

19. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

19 Ngati zikutivuta kusintha khalidwe linalake, chikondi chiyenera kutilimbikitsa kupemphera kwa Yehova ngati mmene anachitira wamasalimo. Iye anati: “Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” (Sal. 86:11) Tiyeni tisalole kuti Mdyerekezi atisiyanitse ndi Yehova komanso abale ndi alongo athu. Tiziyesetsa ‘kutsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa ndiponso kuyendabe m’chikondi.’ Tizichita zimenezi m’banja, mu utumiki ndiponso mu mpingo.—Aef. 5:1, 2.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 29]

Uyu wasiya mphatso yake paguwa kuti akayanjane ndi m’bale wake

[Chithunzi patsamba 31]

Makolo aziphunzitsa ana awo kukhala aulemu