Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Zimene Ndinkafuna Zatheka”

“Zimene Ndinkafuna Zatheka”

“Zimene Ndinkafuna Zatheka”

Mlongo wina dzina lake Emilia anali mpainiya zaka 15 zapitazo koma anasiya. Posachedwapa anayamba kuganizira mmene ankasangalalira ndi upainiya ndipo ankafuna kuyambiranso.

Koma Emilia ankapanikizika kwambiri ndi ntchito ndipo izi sizinkamusangalatsa. Tsiku lina ali kuntchito, ankauza anzake kuti: “Ndingasangalale nditamagwira ntchito maola ochepa.” Abwana ake atamva, anamufunsa ngati akunena zoona. Iye anayankha kuti akunenadi zoona. Koma kuti izi zitheke iye anafunika kukambirana ndi bwana wamkulu chifukwa chakuti pakampaniyo ankafuna kuti aliyense azigwira ntchito maola onse. Mlongoyu anakonzekera zokakambirana ndi bwana wamkuluyo ndipo anapempha Mulungu kuti amuthandize kuti asaope.

Pokambiranapo, Emilia anapempha molimba mtima koma mwaulemu kuti azigwira ntchito maola ochepa. Ananena kuti amakonda kuthandiza anthu pa nthawi imene sakugwira ntchito. Iye anati: “Ndine wa Mboni za Yehova ndipo ndimaphunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Masiku ano, anthu ambiri alibe makhalidwe abwino. Baibulo likhoza kuwathandiza kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Choncho, ndikufuna kukhala ndi nthawi yambiri yothandiza anthu koma sikuti zimenezi zindilepheretsa kugwira ntchito mwakhama kunoko.”

Bwanayo anamvetsera mwachidwi ndipo ananena kuti nayenso nthawi inayake ankafuna kugwira ntchito yothandiza anthu. Kenako anati: “Ndikuona kuti zifukwa zakozi ndi zomveka. Koma ukudziwa kuti uzilandira ndalama zochepa?” Emilia ananena kuti akudziwa ndipo ndi wokonzeka kuyamba moyo wosalira zambiri. Ananenanso kuti: “Cholinga changa chachikulu ndi kuthandiza kwambiri anthu.” Poyankha bwanayo anati: “Ndimalemekeza kwambiri anthu amene amadzipereka kuti athandize ena.”

Pa kampaniyi, Emilia anali woyamba kupatsidwa mwayi wogwira ntchito masiku ochepa. Panopa amagwira ntchito masiku anayi okha pa mlungu. Chochititsa chidwi n’chakuti malipiro ake anawonjezeredwa moti ndalama zimene akulandira n’zofanana ndi zimene ankalandira akugwira masiku onse. Emilia anati: “Zimene ndinkafuna zatheka. Panopa nditha kuchitanso upainiya.”

Kodi inuyo munaganizapo zosintha zinthu zina n’cholinga choti muchite upainiya, kapena ngati munasiya muyambenso?

[Mawu Otsindika patsamba 32]

Bwanayo anamuuza kuti: “Ndimalemekeza kwambiri anthu amene amadzipereka kuti athandize ena”