Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi mphamvu za Samisoni zinkachokera m’tsitsi lake?

Sikuti mphamvu zake zinkachokera m’tsitsi lenilenilo. Tsitsilo linkaimira ubwenzi wake wapadera ndi Mulungu monga Mnaziri. Delila atapeza njira yom’metera, ubwenziwu unasokonekera.—4/15, tsamba 9.

Mofanana ndi mtima weniweni, kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene zingathandize mtima wathu wophiphiritsa?

(1) Chakudya. Mtima wathu weniweni umafunika chakudya chopatsa thanzi. Nawonso mtima wathu wophiphiritsa umafunika chakudya chabwino chauzimu. (2) Masewera Olimbitsa Thupi. Kuchita khama mu utumiki kungathandize kuti mtima wathu wophiphiritsa ukhale wabwino. (3) Kumene Timakhala. Tikhoza kupewa nkhawa tikamacheza komanso kuchita zinthu zauzimu limodzi ndi Akhristu anzathu amene amatikonda.—4/15, tsamba 16.

Ngati wina m’banja wachita chigololo, kodi angatani kuti ayambirenso kukhulupirirana?

Iwo ayenera (1) kuuzana zoona; (2) kuchita zinthu mogwirizana; (3) kusintha zinthu zina zomwe ankachita ndiponso (4) kudziwa kuti zimatenga nthawi kuti ayambirenso kukhulupirirana.—5/1, tsamba 12-15.

N’chifukwa chiyani wokamba nkhani ya maliro sayenera kugwiritsa ntchito lemba la Salimo 116:15 pofotokoza za womwalirayo?

Lembali limati: “M’maso mwa Yehova imfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu.” Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu amaona kuti imfa ya anthu ake onse okhulupirika ndi nkhani yaikulu kwambiri moti sangalole kuti zichitike. Choncho iye sadzalola kuti gulu lonse la atumiki ake liwongongedwe padziko lapansi.—5/15, tsamba 22.

Kodi akopotala anali ndani?

Chaka cha 1931 chisanafike, anthu amene masiku ano timati apainiya ankatchedwa “akopotala.”—5/15, tsamba 31.

Kodi ndi zinthu ziti zimene zimasonyeza kuti Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena?

M’Baibulo muli maulosi ambiri amene anakwaniritsidwa. Limafotokoza molondola mbiri yakale ndipo nkhani zake si nthano chabe. Baibulo ndi lolondola pa nkhani zaukhondo. Nkhani zake n’zogwirizana ndipo malangizo ake ndi othandiza ngakhale masiku ano.—6/1, tsamba 4-8.

Kodi mawu oti “maufumu ena onsewo” pa Danieli 2:44 akunena za ndani?

Mawuwa akunena za maufumu, kapena kuti maboma, okhawo amene akuimiridwa ndi mbali zosiyanasiyana za chifaniziro chimene Danieli anafotokoza.—6/15, tsamba 17.

Kodi ndi liti pamene ulamuliro wa Britain ndi America unakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa 7 wotchulidwa mu ulosi wa m’Baibulo?

Zimenezi zinachitika pamene mayiko a Britain ndi United States anayamba kuchitira limodzi zinthu zikuluzikulu pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse.—6/15, tsamba 19.

Kodi Mulungu amakhululuka ndiponso kuiwala machimo a anthu amene alapa m’njira iti?

Ponena za anthu amene amawakonda, Yehova analonjeza kuti: “Machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yer. 31:34) Mulungu amatha kukhululukira machimo chifukwa cha dipo. Iye akakhululuka, amaiwala m’njira yoti sadzalanga munthuyo chifukwa cha machimowo.—7/1, tsamba 18.

Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti zozizwitsa zotchulidwa m’Baibulo zinachitikadi?

Nthawi zambiri zozizwitsa zinkachitika pali anthu ambirimbiri oonerera, osati mobisa. Ochita zozizwitsa sankachita zinthu mokokomeza. Iwo ankachita zozizwitsa n’cholinga choti Mulungu alemekezeke osati iwowo. Iwo ankachita zozizwitsa zosiyanasiyana ndipo anthu otsutsa sanakane kuti zinachitikadi. Choncho tikhoza kukhulupirira kuti zozizwitsa zimene zinatchulidwa m’Baibulo zinachitikadi.—8/1, tsamba 7-8.