Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzichita Zinthu Monga Nzika za Ufumu

Muzichita Zinthu Monga Nzika za Ufumu

Muzichita Zinthu Monga Nzika za Ufumu

“Makhalidwe anu akhale oyenera uthenga wabwino.”—AFIL. 1:27.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi ndani angakhale nzika za Ufumu?

Kodi tiyenera kuchita chiyani pa nkhani ya chilankhulo, mbiri ndiponso malamulo a Ufumu?

Kodi nzika za Ufumu zimasonyeza bwanji kuti zimakonda malamulo a Mulungu?

1, 2. N’chifukwa chiyani malangizo a Paulo anali ndi tanthauzo lapadera kwa Akhristu mu mpingo wa ku Filipi?

MTUMWI PAULO analimbikitsa Akhristu a mu mpingo wa ku Filipi kuti ‘makhalidwe awo akhale oyenera uthenga wabwino.’ (Werengani Afilipi 1:27.) Mawu a Paulo amene anamasuliridwa kuti “makhalidwe” amachokera ku mawu achigiriki amene angatanthauze “kuchita zinthu monga nzika.” Mawu amenewa anali ndi tanthauzo lapadera kwa Akhristu a ku Filipi. Tikutero chifukwa chakuti mzinda wa Filipi unali umodzi mwa mizinda imene anthu ake anapatsidwa mwayi wokhala monga nzika za Roma. Anthu amene anali nzika za Roma ku Filipi komanso m’madera onse a mu ufumu wa Roma ankanyadira kwambiri mwayi umenewu. Iwo ankatetezedwa ndi malamulo a Aroma.

2 Koma Akhristu mu mpingo wa ku Filipi anali ndi mwayi winanso waukulu kwambiri. Paulo anakumbutsa Akhristuwo kuti iwo ndi “nzika zakumwamba” chifukwa chakuti anali odzozedwa. (Afil. 3:20) Choncho iwo anali nzika za Ufumu wa Mulungu osati wa anthu. Ufumu wa Mulungu unkawateteza ndiponso kuwathandiza kuposa ufumu uliwonse wa anthu.—Aef. 2:19-22.

3. (a) Kodi ndani ali ndi mwayi wokhala nzika za Ufumu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

3 Malangizo a Paulo, amene ali pa Afilipi 1:27, kwenikweni ankapita kwa Akhristu amene adzalamulire ndi Khristu kumwamba. (Afil. 3:20) Koma mfundo yake imagwiranso ntchito kwa anthu amene adzakhale padziko lapansi n’kumalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti Akhristu onse amatumikira Mfumu imodzi, yomwe ndi Yehova, komanso amatsatira malamulo ofanana. (Aef. 4:4-6) Masiku ano, anthu amayesetsa kwambiri kuti akhale nzika za dziko lotukuka. Ndiye kuli bwanji ifeyo? Tiyenera kunyadira kwambiri kuti ndife nzika za Ufumu chifukwa ndi mwayi waukulu kwambiri. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tione kufanana pakati pa zimene munthu amafunika kuchita kuti akhale nzika ya dziko linalake ndi zimene amafunika kuchita kuti akhale nzika ya Ufumu wa Mulungu. Kenako tikambirana zinthu zitatu zimene tiyenera kuchita kuti tikhalebe nzika za Ufumu wa Mulungu.

ZIMENE MUNTHU AYENERA KUCHITA KUTI AKHALE NZIKA

4. Kodi chilankhulo choyera n’chiyani ndipo timachilankhula bwanji?

4 Ayenera kuphunzira chilankhulo. Mayiko ena amafuna kuti munthu azilankhula chilankhulo cha dzikolo kuti akhale nzika. Koma munthu atakhala nzika, angayesetsebe kwa zaka zambiri kuti adziwe bwino chilankhulocho. Mwina angaphunzire msanga malamulo a chilankhulo koma zingatenge nthawi yaitali kuti azitha kutchula bwino mawu. Anthu ofuna kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu amafunikanso kuphunzira “chilankhulo choyera.” (Werengani Zefaniya 3:9.) Kodi chilankhulochi n’chiyani? Ndi choonadi cha m’Baibulo chonena za Mulungu ndi zolinga zake. Tikamachita zinthu mogwirizana ndi malamulo ndi mfundo za Mulungu, timakhala ngati tikulankhula chilankhulochi. Nzika za Ufumu wa Mulungu zikhoza kuphunzira msanga mfundo zoyambirira za m’Baibulo n’kubatizidwa. Koma ngakhale munthu atabatizidwa, ayenera kuyesetsabe kuti adziwe bwino chilankhulo choyerachi. Kodi angachite bwanji zimenezi? Aliyense ayenera kuyesetsabe kutsatira zimene amaphunzira m’Baibulo.

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira zambiri zokhudza mbiri ya anthu a Yehova?

5 Ayenera kuphunzira mbiri ya dzikolo. Munthu amene akufuna kukhala nzika ya dziko linalake angafunike kudziwa zinthu zina zokhudza mbiri ya dzikolo. Nawonso anthu ofuna kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu ayenera kuphunzira zambiri zokhudza mbiri yake. Ana a Kora, amene ankatumikira mu Isiraeli, anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iwo ankakonda kwambiri mzinda wa Yerusalemu ndi malo ake olambirira ndipo ankakonda kuuza ena mbiri ya mzindawu. Chimene chinkawachititsa chidwi si kukongola kwa mzindawu koma zimene mzindawo komanso malo ake olambirira zinkaimira. Yerusalemu anali “mudzi wa Mfumu Yaikulu” chifukwa chakuti anthu ankalambira Yehova ndiponso kuphunzira Chilamulo chake kumeneko. Komanso Yehova ankakomera mtima anthu olamulidwa ndi Mfumu ya ku Yerusalemu. (Werengani Salimo 48:1, 2, 9, 12, 13.) Kodi nanunso mumakonda kuphunzira ndiponso kuuza ena mbiri ya anthu a Yehova? Mudzayamba kuyamikira kwambiri Ufumu wa Mulungu mukamaphunzira zambiri zokhudza anthu a Mulungu ndiponso mmene Yehova amawathandizira. Izi zidzakuthandizani kukhala ndi mtima wofuna kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—Yer. 9:24; Luka 4:43.

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova salakwitsa pofuna kuti tiphunzire ndiponso kutsatira malamulo ndi mfundo za Ufumu wake?

6 Ayenera kudziwa malamulo a dzikolo. Mayiko amafuna kuti nzika zake zizidziwa ndiponso kutsatira malamulo ake. Choncho n’zomveka kuti Yehova amafunanso kuti tiphunzire komanso kutsatira malamulo ndiponso mfundo zokhudza Ufumu wake. (Yes. 2:3; Yoh. 15:10; 1 Yoh. 5:3) Nthawi zambiri malamulo a anthu amakhala ndi mavuto ake ndipo amapondereza anthu ena. Koma “chilamulo cha Yehova ndi changwiro.” (Sal. 19:7) Kodi timakonda chilamulo cha Mulungu n’kumawerenga Mawu ake tsiku ndi tsiku? (Sal. 1:1, 2) Tonsefe tiyenera kuchita khama kuti tiphunzire malamulo a Mulungu chifukwa munthu wina sangatiphunzirire.

NZIKA ZA UFUMU ZIMAKONDA MALAMULO A MULUNGU

7. Kodi nzika za Ufumu zimamvera malamulo a Mulungu chifukwa chiyani?

7 Kuti tikhalebe nzika za Ufumu, tiyenera kudziwa malamulo a Mulungu komanso kuwakonda. Nzika zambiri zimanena kuti zimavomereza malamulo a dziko limene zikukhala. Koma anthuwo satsatira malamulo akaona kuti sakuwakomera ndipo palibe amene akuwaona. Iwo amangofuna “kukondweretsa anthu.” (Akol. 3:22) Koma nzika za Ufumu zimatsatira malamulo a Mulungu chifukwa chokonda amene anapereka malamulowo. Choncho zimatsatira malamulowo ngakhale pamene anthu ena sakuwaona.—Yes. 33:22; werengani Luka 10:27.

8, 9. Kodi mungadziwe bwanji ngati mumakondadi malamulo a Mulungu?

8 Kodi mungadziwe bwanji ngati mumakondadi malamulo a Mulungu? Muyenera kudzifunsa kuti, Kodi ndimatani ndikapatsidwa malangizo pa nkhani imene ndikuona kuti ndili ndi ufulu wosankha? Tiyerekeze nkhani ya kavalidwe. Mwina musanakhale nzika ya Ufumu munkavala motayirira. Koma mutayamba kukonda kwambiri Yehova, munasintha kuti kavalidwe kanu kakhale kolemekeza Mulungu. (1 Tim. 2:9, 10; 1 Pet. 3:3, 4) Muyenera kuti panopa mumaona kuti mumavala bwino. Koma nanga bwanji mkulu atakuuzani kuti anthu angapo mu mpingo amakhumudwa ndi kavalidwe kanu? Kodi mungatani? Kodi mudzayamba kudziikira kumbuyo, kukwiya kapena kuchita makani? Limodzi mwa malamulo akuluakulu a nzika za Ufumu wa Mulungu ndi lakuti aliyense azitsanzira Khristu. (1 Pet. 2:21) Ponena za chitsanzo cha Yesu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa. Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha.” (Aroma 15:2, 3) Mkhristu amene amakonda mtendere savutika kulolera zinthu zina chifukwa choganizira chikumbumtima cha anzake.—Aroma 14:19-21.

9 Tiyeni tikambirane mmene timaonera nkhani ya kugonana komanso ukwati. Anthu amene si nzika za Ufumu wa Mulungu amaona kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha kulibe vuto. Amaganiza kuti kuonera zolaula kulibenso vuto ndipo amaona kuti kuchita chigololo ndiponso kuthetsa banja ndi chosankha cha munthu. Koma nzika za Ufumu zimaganizira zotsatira za zochita zawo ndiponso mmene zingakhudzire anthu ena. Akhristu ambiri, omwe anali achiwerewere asanadziwe choonadi, anasintha ndipo panopa amaona kuti kugonana ndiponso ukwati ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. Iwo amakonda malamulo a Yehova ndipo amadziwa kuti anthu onse osamvera malamulo a Mulungu pa nkhani ya kugonana ndiponso ukwati sangakhale nzika za Ufumu. (1 Akor. 6:9-11) Koma amadziwanso kuti mtima ndi wonyenga. (Yer. 17:9) Choncho amayamikira akapatsidwa machenjezo owathandiza kutsatira malamulo a Mulungu.

NZIKA ZA UFUMU ZIMAMVERA MACHENJEZO

10, 11. Kodi Ufumu wa Mulungu wapereka machenjezo ati? Nanga mumawaona bwanji machenjezo amenewa?

10 Nthawi zina maboma amapereka malangizo okhudza chakudya ndiponso mankhwala. Si mankhwala onse kapena zakudya zonse zimene ndi zoipa. Koma ngati mankhwala ena kapena zakudya zina zili zoopsa, boma lingachenjeze anthu ake pofuna kuwateteza. Ngati boma silipereka chenjezo, limakhala ndi mlandu wosasamalira anthu ake. Ufumu wa Mulungu umaperekanso machenjezo okhudza zinthu zimene zingatichititse kuphwanya malamulo a Mulungu kapena kusokoneza ubwenzi wathu ndi iye. Mwachitsanzo, anthu ambiri amagwiritsa ntchito Intaneti kuti alankhulane ndi anzawo, aphunzire zinthu ndiponso kuti achite masewera enaake. Gulu la Mulungu limagwiritsanso ntchito Intaneti kuti lichite zinthu zambiri zabwino. Koma mawebusaiti ambiri a pa Intaneti si abwino kwa anthu otumikira Mulungu. Ena ndi oipa kwambiri chifukwa amasonyeza zolaula. Kwa zaka zambiri, gulu la kapolo wokhulupirika lakhala likutichenjeza za zimenezi. Tiyenera kuyamikira kwambiri machenjezo amenewa.

11 Masiku ano, pa Intaneti palinso mawebusaiti ochezera. Anthu ambiri amawagwiritsa ntchito ndipo ndi othandiza. Koma ngati munthu sasamala, akhoza kuyamba kucheza ndi anthu oipa omwe angawononge makhalidwe ake abwino. (1 Akor. 15:33) N’chifukwa chake gulu la Mulungu limapereka machenjezo okhudza nkhani imeneyi. Kodi mwawerenga nkhani zonse zimene kapolo wokhulupirika walemba zokhudza mawebusaitiwa? Si bwino kutsegula mawebusaiti ngati amenewa musanawerenge nkhanizi. * Kuchita zimenezi kuli ngati kumwa mankhwala amphamvu musanawerenge malangizo ake.

12. N’chifukwa chiyani si nzeru kunyalanyaza machenjezo?

12 Anthu amene satsatira machenjezo ochokera kwa kapolo wokhulupirika amakumana ndi mavuto omwe amavutitsanso anzawo. Ena ayamba chizolowezi choonera zolaula kapena achita chiwerewere n’kumaganiza kuti Yehova sakuona zimene akuchita. Kuganiza kuti Yehova sakuona zochita zathu n’kupusa. (Miy. 15:3; werengani Aheberi 4:13.) Mulungu amafuna kuthandiza anthu oterewa ndipo amagwiritsa ntchito akulu kuti awathandize. (Agal. 6:1) Mayiko amatha kuthamangitsa anthu amene apalamula milandu inayake. Nayenso Yehova amachotsa m’gulu lake anthu amene amachimwa mosalapa. * (1 Akor. 5:11-13) Komabe Yehova ndi wachifundo. Anthu amene amalapa n’kusintha angakhalenso pa ubwenzi ndi Yehova komanso kupitiriza kukhala nzika za Ufumu. (2 Akor. 2:5-8) Ndi mwayi waukulu kwambiri kutumikira Mfumu yachikondi imeneyi.

NZIKA ZA UFUMU ZIMAONA KUTI MAPHUNZIRO NDI OFUNIKA

13. Kodi nzika za Ufumu zimasonyeza bwanji kuti zimayamikira maphunziro?

13 Maboma ambiri amalimbikitsa maphunziro. Amatsegula sukulu zosiyanasiyana kuti nzika zake ziphunzire kuwerenga, kulemba komanso ntchito zosiyanasiyana. Anthu amene ndi nzika za Ufumu amayamikira zimenezi ndipo amayesetsa kuphunzira n’cholinga choti azitha kuwerenga, kulemba ndiponso kuti azitha kupeza kangachepe. Koma amaona kuti maphunziro amene Ufumu wa Mulungu umawapatsa ndi apamwamba kwambiri. Mu mpingo, Yehova amalimbikitsa Akhristu kuti aziphunzira kuwerenga ndi kulemba. Makolo amalimbikitsidwa kuti aziwerengera ana awo aang’ono. Mwezi uliwonse kapolo wokhulupirika amapereka makope awiri a Nsanja ya Olonda ndi kope limodzi la Galamukani! Ngati mutamawerenga masamba angapo tsiku lililonse, mukhoza kumaliza magazini onsewa pa mwezi. Mukamatero, ndiye kuti muzipindula ndi maphunziro amene Yehova akutipatsa.

14. (a) Kodi timaphunzitsidwa m’njira ziti? (b) Kodi ndi njira ziti zochitira Kulambira kwa Pabanja zimene zimakusangalatsani?

14 Mlungu uliwonse, nzika za Ufumu zimaphunzitsidwa ku misonkhano ya mpingo. Mwachitsanzo, kwa zaka zoposa 60, Sukulu ya Utumiki wa Mulungu yakhala ikuthandiza Akhristu kukhala aphunzitsi aluso a Mawu a Mulungu. Kodi inuyo munalembetsa sukuluyi? Masiku ano, kapolo wokhulupirika akutilimbikitsa kwambiri kuti tizichita Kulambira kwa Pabanja. Kuchita zimenezi kumalimbitsa banja. Kodi mumagwiritsa ntchito njira zochitira kulambiraku zofotokozedwa m’mabuku athu? *

15. Kodi tili ndi mwayi waukulu kwambiri uti?

15 Nzika za mayiko zimachita kampeni ya chipani chawo. Nthawi zina zimachita kuyenda khomo ndi khomo. Padziko lonse, nzika za Ufumu zimachita khama kwambiri polalikira za Ufumu wa Mulungu m’misewu ndiponso khomo ndi khomo. Monga tanenera m’nkhani yophunzira yapita ija, magazini ya Nsanja ya Olonda, yomwe imalengeza Ufumu wa Yehova, imafalitsidwa kuposa magazini ena onse padzikoli. Kuuza anthu za Ufumu wa Mulungu ndi mwayi waukulu kwambiri. Kodi inuyo mumachita khama kulalikira za Ufumuwu?—Mat. 28:19, 20.

16. Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu nzika yabwino ya Ufumu wa Mulungu?

16 Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene uzidzalamulira dzikoli. Anthu azidzayendera malamulo a Ufumu wokhawu basi. Kodi pa nthawiyo, mudzakhala nzika yabwino ya Ufumu wa Mulungu? Inoyi ndi nthawi yosonyeza kuti mudzatero. Muziyesetsa kuti zochita zanu tsiku lililonse zizilemekeza Yehova. Mukatero, mudzasonyeza kuti mukuchita zinthu monga nzika yabwino ya Ufumu wa Mulungu.—1 Akor. 10:31.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 2011, tsamba 6 ndi 7 ndiponso Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2011, tsamba 3 mpaka 6.

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Kodi mumatsatira machenjezo ochokera kwa kapolo wokhulupirika okhudza Intaneti?

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi mumakonda kwambiri kulambira koona ndiponso mbiri yake ngati ana a Kora?

[Chithunzi patsamba 15]

Kulambira kwa Pabanja kungakuthandizeni kwambiri kukhala nzika zabwino za Ufumu