Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kale Lathu

Oyang’anira Oyendayenda Akale

Oyang’anira Oyendayenda Akale

“AA! INE zolalikira khomo ndi khomozo ndiye ayi!” Anthu amene ayamba kuphunzira Baibulo amamva choncho akaganiza zoti azidzalalikira anthu osawadziwa. Koma munthu amene ananena mawuwa anali woyang’anira woyendayenda, wodziwa bwino kukamba nkhani ndiponso kuphunzitsa Baibulo.

Anthu ambiri amene ankawerenga Nsanja ya Olonda ndiponso amene anali atachoka m’chipembedzo chawo ankafuna kucheza ndi anthu ena ofunitsitsa kudziwa choonadi. Nsanja ya Olonda inkalimbikitsa anthu kufunafuna anthu ena achikhulupiriro n’kumasonkhana nawo kuti aphunzire Baibulo. Kuyambira cha m’ma 1894, Watch Tower Society inkatumiza abale kukayendera magulu amene apempha kuti ayenderedwe. Abalewa anali ngati oyang’anira oyendayenda ndipo ankasankhidwa chifukwa chakuti anali odzichepetsa, odziwa bwino Baibulo, aluso polankhula ndi kuphunzitsa komanso oti asonyeza kuti amakhulupirira dipo. Nthawi zambiri ankachezera gulu tsiku limodzi kapena masiku awiri okha ndipo ankatanganidwa kwambiri. Ophunzira Baibulo ambiri anayamba kulalikira popereka timapepala toitanira anthu ku nkhani ya woyang’anira woyendayenda. Tsiku lina M’bale Hugo Riemer, amene anadzakhala m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani kusukulu inayake. Atamaliza, anayamba kuyankha mafunso okhudza Baibulo mpaka pakati pa usiku. Iye anali atatopa koma wosangalala ndipo anati msonkhanowu unali “wabwino kwambiri.”

Nsanja ya Olonda inanena kuti cholinga cha oyang’anira oyendayenda chinali kulimbikitsa abale pochita misonkhano m’nyumba za abalewo. Ophunzira Baibulo ankafika kudzamvetsera nkhani ndiponso kukhala nawo pa nthawi ya mafunso ndi mayankho. Kenako ankadyera limodzi. Mlongo wina, dzina lake Maude Abbott, anafotokoza kuti tsiku lina ali mtsikana anamvetsera nkhani m’mawa ndipo kenako onse anakhala panja mozungulira tebulo lalikulu kuti adye. Iye anati: “Tinadya zakudya zabwino kwabasi ngati nyama yankhumba, nkhuku yokazinga, buledi wosiyanasiyana ndiponso makeke. Aliyense anadya mmene akanathera ndipo cha m’ma 2 koloko tinasonkhana kuti timvere nkhani ina.” Koma iye anati, “Pa nthawiyi aliyense anali kusinza.” M’bale Benjamin Barton, amene anakhala woyang’anira woyendayenda kwa nthawi yaitali, ananena kuti, ‘Ndikanakhala kuti ndinkamaliza zakudya zonse zonona zimene ankandipatsa, bwenzi nditafa kalekale.’ Patapita nthawi, likulu lathu ku Brooklyn linatumizira maguluwa kalata yowalangiza kuti zingakhale zothandiza kwa onse ngati alongo atamaphikira alendowo “zakudya wamba basi” ndiponso “kuwalola kuti azigona mokwanira.”

Oyang’anira oyendayenda ankaphunzitsa mwaluso ndiponso ankagwiritsa ntchito zinthu monga matchati kuti athandize anthu kumvetsa bwino nkhani zawo. Mwachitsanzo, nkhani za M’bale R. H. Barber “nthawi zonse zinkakhala zokoma kwabasi.” M’bale W. J. Thorn ankakamba nkhani ngati bambo akulankhula ndi ana ake. Ankalankhula “ngati makolo akale monga Abulahamu.” Tsiku lina, M’bale Shield Toutjian ali pa galimoto anangoti, “Taima kaye!” Kenako iye anadumpha m’galimotoyo n’kukathothola maluwa enaake n’kuwagwiritsa ntchito pophunzitsa anzakewo za chilengedwe cha Yehova.

Ntchito yoyendayenda inali yovuta makamaka kwa achikulire. Koma anthu ena anavutika kwambiri pamene cholinga cha ntchitoyi chinasintha. Anayenera kutsogolera polalikira kunyumba ndi nyumba. Nsanja ya Olonda ya March 15, 1924, inati “cholinga china chachikulu” cha Akhristu oona “ndi kuchitira umboni za ufumu. Ndipo oyang’anira oyendayenda amatumizidwa kuti akatsogolere ntchito imeneyi.”

Oyang’anira oyendayenda ena sanasangalale ndi kusinthaku moti anasiya utumiki mpaka ena anayambitsa magulu awo achipembedzo. M’bale Robie D. Adkins ananena kuti woyang’anira woyendayenda wina, amene ankakamba nkhani mwaluso, anadandaula kwambiri kuti: “Aa! Ine zolalikira khomo ndi khomozo ndiye ayi! Chomwe ndimadziwa ndi kukamba nkhani papulatifomu basi.” M’bale Adkins anati: “Ndinamuonanso m’baleyu mu 1924 pa msonkhano wachigawo wa ku Columbus, Ohio. Ngakhale kuti kunali abale masauzande ambiri osangalala, iye ankaoneka wokhumudwa kwambiri ndipo anangoima yekhayekha pansi pa mtengo. Kuchokera pa nthawiyi, sindinamuonenso. Kenako anachoka m’gulu la Yehova.” Komabe pa msonkhanowu, “abale ambiri anali kukakwera magalimoto awo atanyamula mabuku.” Iwo ankaoneka kuti akufunitsitsa kukalalikira kunyumba ndi nyumba.—Mac. 20:20, 21.

Oyang’anira oyendayenda ambiri ankagwira ntchitoyi ndi mtima wonse ngakhale kuti iwowo limodzi ndi anthu amene ankawaphunzitsa ankachita mantha. M’bale Maxwell G. Friend, yemwe ankalankhula Chijeremani ndipo anali woyang’anira woyendayenda, analemba kuti, “Ntchito yolalikira imachititsa kuti kuyendera magulu kukhale kosangalatsa.” M’bale John A. Bohnet ananena kuti abale ambiri ankaona kuti kulalikira za Ufumu n’kofunika kwambiri. Iye ananena kuti ambiri “ankafunitsitsa kutsogolera pa ntchito imeneyi.”

Kwa zaka zambiri, oyang’anira oyendayenda okhulupirika akhala akuthandiza kwambiri. M’bale Norman Larson, yemwe wakhala m’choonadi nthawi yaitali, anati: “Kuyambira ndili mwana, ndimaona kuti oyang’anira oyendayenda ndi ofunika kwambiri. Iwo anandithandiza kwambiri kuti ndizikonda utumiki.” Mpaka pano, oyang’anira oyendayenda okhulupirika komanso odzipereka amathandiza Akhristu anzawo kuti azikonda kulalikira khomo ndi khomo.

[Mawu Otsindika patsamba 32]

Tinkasangalala kwambiri oyang’anira oyendayenda akafika

[Chithunzi patsamba 31]

M’bale Benjamin Barton anaima malo okwanira 170 poyendera magulu m’chaka cha 1905

[Chithunzi patsamba 32]

Walter J. Thorn anali woyang’anira woyendayenda yemwe anthu ankangomutcha Adadi chifukwa ankachita zinthu ngati bambo komanso Khristu

[Chithunzi patsamba 32]

J. A. Browne anatumizidwa ku Jamaica cha m’ma 1902 kuti azikayendera ndi kulimbikitsa timagulu 14

[Chithunzi patsamba 32]

Oyang’anira oyendayenda ankathandiza Akhristu kukhala olimba ndiponso ogwirizana. Ankawathandizanso kudalira kwambiri gulu la Yehova