Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtendere Udzayamba mu Ulamuliro wa Zaka 1,000

Mtendere Udzayamba mu Ulamuliro wa Zaka 1,000

“Kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”—1 AKOR. 15:28.

1. Kodi a “khamu lalikulu” akuyembekezera zinthu ziti?

TANGOGANIZIRANI zinthu zosangalatsa zimene boma lamphamvu, lomwe wolamulira wake ndi wachilungamo ndiponso wachifundo, lingachitire anthu kwa zaka 1,000. Anthu osawerengeka, omwe ndi “khamu lalikulu,” adzaona zimenezi. “Khamu lalikulu” limeneli lidzapulumuka ‘chisautso chachikulu’ chimene chidzathetsa dziko loipali.—Chiv. 7:9, 14.

2. Kodi n’chiyani chachitika pa zaka 6,000 zapitazi?

2 Zaka 6,000 zimene anthu akhala akudzilamulira, akhala akukumana ndi mavuto adzaoneni. Kalekale Baibulo linanena kuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlal. 8:9) Kodi n’chiyani chikuchitika masiku ano? Pali nkhondo ndiponso anthu akuukira maboma. Palinso mavuto monga umphawi, matenda, kuwononga chilengedwe ndiponso kusokonekera kwa nyengo. Maboma amachenjeza anthu kuti ngati sasintha, zinthu zifika poipa kwambiri.

3. Kodi n’chiyani chidzachitike mu Ulamuliro wa Zaka 1,000?

3 Ufumu wa Mulungu, wolamulidwa ndi Yesu Khristu limodzi ndi a 144,000, udzathetsa mavuto onse amene anthu akhala akuvutika nawo padzikoli. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, lonjezo lolimbikitsa la Yehova Mulungu lidzakwaniritsidwa. Iye anati: “Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” (Yes. 65:17) Koma osanama, anthufe tidzasangalala kwambiri. Tiyeni tione maulosi a m’Baibulo amene angatithandize kudziwa zinthu zosangalatsa zimene tikuyembekezera.—2 Akor. 4:18.

‘ADZAMANGA NYUMBA NDI KUBZALA MINDA YA MPESA’

4. Kodi vuto la nyumba lafika pati masiku ano?

4 Aliyense amafuna kukhala ndi nyumba yakeyake kuti azikhala motetezeka ndi banja lake. Koma masiku ano, n’zovuta kukhala ndi nyumba yabwino. Anthu amangounjikana m’mizinda ndipo ambiri amangokhala m’tizisakasa. Zoti adzakhala ndi nyumba yawoyawo, anaiwala kalekale.

5, 6. (a) Kodi malemba a Yesaya 65:21 ndi Mika 4:4 adzakwaniritsidwa bwanji? (b) Kodi tingatani kuti tidzapeze madalitso amenewa?

5 Ufumu ukadzayamba kulamulira, aliyense adzakhala ndi nyumba. Yesaya analosera kuti: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.” (Yes. 65:21) Koma sitikuyembekezera nyumba zokha. Masiku ano, pali anthu ena amene ali ndi nyumba zawozawo ndipo ena amakhala m’nyumba zazikulu komanso zokongola. Koma akamakhala, amadera nkhawa kuti mavuto azachuma angawachititse kuti asamukire kwina. Amaderanso nkhawa kuti mbava kapena zigawenga zidzathyola. Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, palibe amene azidzada nkhawa. Mneneri Mika analemba kuti: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.”—Mika 4:4.

6 Kodi tingatani kuti tidzalandire madalitso amenewa? N’zoona kuti tonsefe timafunikira nyumba zabwino. Koma si bwino kudzipanikiza kapena kutenga ngongole kuti tipeze nyumba yabwino panopa. M’malomwake, tizisonyeza kuti timakhulupirira zimene Yehova walonjeza. Kumbukirani mawu a Yesu akuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.” (Luka 9:58) Yesu akanatha kumanga kapena kukhala ndi nyumba yapamwamba kwambiri. Koma n’chifukwa chiyani sanatero? Iye sankafuna kuti zinthu zina zimulepheretse kuika Ufumu pa malo oyamba. Tiyeni tiyesetse kumutsanzira. Tizikhala ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi ndipo tisalole kuti kufunafuna chuma ndiponso nkhawa za moyo zitisokoneze.—Mat. 6:33, 34.

“MMBULU NDI MWANA WA NKHOSA ZIDZADYERA PAMODZI”

7. Kodi Yehova analamula anthu kuchita chiyani?

7 Yehova atamaliza kulenga zinthu zina zonse padzikoli, analenga anthu. Yehova anagwiritsa ntchito Yesu monga mmisiri wake waluso ndipo anamuuza cholinga chake polenga anthu. Iye anati: “Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu, kuti akhale wofanana nafe. Ayang’anire nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso nyama zoweta. Ayang’anirenso dziko lonse lapansi ndi nyama zonse zokwawa padziko lapansi.” (Gen. 1:26) Choncho Adamu, Hava komanso anthu onse anayenera kuyang’anira zinyama.

8. Kodi ndi zinthu ziti zimene nyama zimachita masiku ano?

8 Kodi n’zothekadi kuti anthu aziyang’anira zinyama zonse n’kumakhala nazo mwamtendere? Anthu ambiri amakondana ndi ziweto zawo monga agalu ndi amphaka. Nanga bwanji nyama zakutchire? Kafukufuku wina amati: “Asayansi amene akhala pafupi kwambiri ndi nyama zakutchire apeza kuti nyama zonse zimene zimayamwitsa zimasonyeza kukhudzika ndi zinthu.” N’zoona kuti timaona nyama zikuchita mantha kapena kulusa zikaopsezedwa. Koma kodi zimathanso kusonyeza chikondi? Ochita kafukufukuwo anati: “Nyama zimasonyeza chikondi kwambiri zikamasamalira ana awo.”

9. Kodi nyama zidzasintha bwanji m’dziko latsopano?

9 Choncho sitiyenera kudabwa tikamawerenga m’Baibulo kuti anthu adzakhala pa mtendere ndi nyama. (Werengani Yesaya 11:6-9; 65:25.) N’chifukwa chiyani tikutero? Kumbukirani kuti Nowa ndi banja lake atatuluka m’chingalawa, Yehova anawauza kuti: ‘Cholengedwa chilichonse chamoyo cha padziko lapansi chizikuopani.’ Zimenezi zimathandiza kuti nyamazo zitetezeke. (Gen. 9:2, 3) Yehova akhoza kuchotsa mantha amenewo n’cholinga choti nyama zizigwirizananso ndi anthu ngati mmene analamulira poyamba. (Hos. 2:18) Anthu amene adzapulumuke adzasangalala kwabasi padzikoli.

“ADZAPUKUTA MISOZI YONSE”

10. N’chifukwa chiyani anthu amalira?

10 Solomo ataona “kuponderezana konse kumene kukuchitika padziko lapansi pano,” anadandaula kuti: “Ndinaona misozi ya anthu amene akuponderezedwa, koma panalibe wowatonthoza.” (Mlal. 4:1) Ndi mmenenso zilili masiku ano ndipo zawonjezeka. Palibe munthu amene sanalirepo. N’zoona kuti nthawi zina anthu amalira chifukwa chosangalala. Koma nthawi zambiri anthu amalira chifukwa chopwetekedwa mtima.

11. Kodi ndi nkhani ya m’Baibulo iti imene imakumvetsani chisoni kwambiri?

11 Taganizirani zinthu zotchulidwa m’Baibulo zimene zinachititsa anthu kulira. Mwachitsanzo, pamene Sara anamwalira ali ndi zaka 127, “Abulahamu analowa muhema kukamulira.” (Gen. 23:1, 2) Pamene Naomi ankatsanzikana ndi apongozi ake, iwo “anayamba kulira mokweza mawu.” Atayesa kulankhula nawo, iwo “analiranso mokweza mawu.” (Rute 1:9, 14) Mfumu Hezekiya itadwala mwakayakaya, inapemphera kwa Mulungu. Popemphera, iye “anayamba kulira kwambiri” ndipo Yehova anamumvera chisoni. (2 Maf. 20:1-5) Nayonso nkhani yoti Petulo anakana Yesu ndi yomvetsa chisoni. Petulo atamva tambala akulira, “anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.”—Mat. 26:75.

12. Kodi anthu adzathandizidwa bwanji mu Ulamuliro wa Zaka 1,000?

12 Anthu amafunikira kutonthozedwa ndiponso kuthandizidwa chifukwa chokumana ndi mavuto ambiri. Zimenezi zidzachitika mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. Baibulo limati: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chiv. 21:4) N’zosangalatsa kuti kulira, kubuula ndiponso kupweteka zidzatha. Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti Mulungu walonjeza kuchotsanso mdani wathu wamkulu, amene ndi imfa. Kodi zimenezi zidzatheka bwanji?

‘ONSE ALI M’MANDA ACHIKUMBUTSO ADZATULUKA’

13. Kodi imfa yakhudza bwanji anthu kuyambira pamene Adamu anachimwa?

13 Imfa yakhala ngati mfumu yolamulira anthu kuyambira pamene Adamu anachimwa. Palibe munthu angagonjetse kapena kuzemba mdani ameneyu ndipo amatichititsa kulira kwambiri. (Aroma 5:12, 14) Panopa anthu ambiri amakhala “mu ukapolo moyo wawo wonse” chifukwa ‘choopa imfa.’—Aheb. 2:15.

14. Kodi ndi zinthu ziti zimene zidzachitike imfa ikamadzawonongedwa?

14 Baibulo limanena kuti idzafika nthawi pamene “imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” (1 Akor. 15:26) Pali magulu awiri a anthu amene adzapindule ndi zimenezi. Choyamba, a “khamu lalikulu” amene panopa ali moyo adzapulumuka n’kulowa m’dziko latsopano. Iwo adzakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Chachiwiri, anthu mabiliyoni ambiri amene panopa amwalira adzaukitsidwa. Kudzakhalatu chisangalalo chosaneneka khamu lalikulu likamadzalandira anthu oukitsidwa. Tiyeni tione nkhani za m’Baibulo zosonyeza mmene anthu anamvera pamene ena anaukitsidwa. Zimenezi zingatithandize kumvetsa mmene zidzakhalire m’tsogolo.—Werengani Maliko 5:38-42; Luka 7:11-17.

15. Kodi inuyo mukuganiza kuti mudzatani mukadzaona anzanu ataukitsidwa?

15 Pamene ena anaukitsidwa, anthu “anasangalala kwambiri” ndipo ena “anayamba kutamanda Mulungu.” Mwina inunso mukanakhalapo mukanachita chimodzimodzi. Kunena zoona, tidzasangalala kwabasi kuona anzathu amene anamwalira akuuka. Yesu anati: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Ifeyo sitinaonepo munthu ataukitsidwa, koma ndi chimodzi mwa zinthu zosangalatsa kwambiri zimene tikuyembekezera.

MULUNGU ADZAKHALA “ZINTHU ZONSE KWA ALIYENSE”

16. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kulankhula za madalitso amene tikuyembekezera? (b) Kodi Paulo ananena chiyani pofuna kulimbikitsa Akhristu a ku Korinto?

16 Anthu amene ndi okhulupirika kwa Yehova m’masiku ovuta ano ali ndi tsogolo losangalatsa kwambiri. Kuganizira madalitso amene tikuyembekezera kungatithandize kuti tiziika patsogolo zinthu zofunika kwambiri. Kungatithandizenso kuti tisasokonezedwe ndi zinthu za m’dzikoli. (Luka 21:34; 1 Tim. 6:17-19) Tiyeni tizilankhula za madalitso amenewa tikamaphunzira Baibulo ndi banja lathu, tikamacheza ndi Akhristu anzathu komanso tikamakambirana ndi ophunzira Baibulo kapena anthu ena mu utumiki. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tizikhulupirira ndi mtima wonse malonjezowa. Izi n’zimene mtumwi Paulo anachita polimbikitsa Akhristu anzake. Iye anawathandiza kuganizira mmene zidzakhalire pa mapeto a Ulamuliro wa Zaka 1,000. Taganizirani zimene Paulo ananena pa 1 Akorinto 15:24, 25, 28.Werengani.

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu atangolengedwa kumene, Yehova anali “zinthu zonse kwa aliyense”? (b) Kodi Yesu adzachita chiyani kuti abwezeretse mtendere ndi mgwirizano?

17 Mawu osangalatsa kwambiri ndi akuti ‘Mulungu adzakhala zinthu zonse kwa aliyense.’ Zimenezi zidzachitika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000. Koma kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? Taganizirani mmene zinalili Adamu ndi Hava ali angwiro mu Edeni. Iwo anali m’banja la Yehova lamtendere ndiponso logwirizana. Yehova monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse ankalamulira mwachindunji angelo ndiponso anthu. Iwo ankalankhula naye komanso kumulambira. Mulungu ankawadalitsa ndipo iye anali “zinthu zonse kwa aliyense.”

18 Ubwenzi umenewu unasokonekera pamene Satana anachititsa anthu kupandukira ulamuliro wa Yehova. Koma kuyambira mu 1914, Ufumu wa Mesiya wakhala ukubwezeretsa mtendere ndi mgwirizano. (Aef. 1:9, 10) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, zinthu zosangalatsa zimene tikuyembekezera zidzachitika. Ndiyeno n’chiyani chidzachitika “pa mapeto pake,” kapena kuti pa mapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000? Ngakhale kuti Yesu anapatsidwa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi,” iye alibe mtima wofuna kulanda udindo wa Yehova. Yesu ndi wodzichepetsa ndipo “adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake.” Iye adzagwiritsa ntchito udindo wake kuti ‘alemekeze Mulungu.’—Mat. 28:18; Afil. 2:9-11.

19, 20. (a) Kodi anthu olamulidwa ndi Ufumu adzasonyeza bwanji kuti ali ku mbali ya ulamuliro wa Yehova? (b) Kodi tikuyembekezera zinthu zosangalatsa ziti?

19 Pa nthawi imeneyo, anthu olamulidwa ndi Ufumu padziko lapansi adzakhala angwiro. Iwo adzatsatira chitsanzo cha Yesu. Adzagonjera ulamuliro wa Yehova modzichepetsa ndiponso mofunitsitsa. Iwo akadzapambana mayesero omaliza adzasonyeza kuti alidi ndi mtima wofuna kugonjera Yehova. (Chiv. 20:7-10) Pambuyo pake, adani onse a Mulungu, kungoyambira anthu, ziwanda komanso Satana weniweniyo, adzawonongedwa. Nthawi imeneyi idzakhala yosangalatsa kwambiri. Onse a m’banja la Yehova adzamutamanda mosangalala ndipo iye adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”—Werengani Salimo 99:1-3.

20 Kuganizira madalitso amene Ufumu udzabweretse kuyenera kutilimbikitsa kuika patsogolo chifuniro cha Mulungu. Kodi mudzapewa kusokonezedwa ndi zinthu za m’dziko la Satanali zimene zingaoneke zothandiza? Kodi mudzakhala ku mbali ya ulamuliro wa Yehova zivute zitani? Moyo wanu uzisonyeza kuti mukufunitsitsa kuchita zimenezi kwamuyaya. Mukatero, mudzakhala ndi mwayi wokhala mwamtendere kuyambira mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 mpaka muyaya.