Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndiphunzitseni Kuchita Chifuniro Chanu”

“Ndiphunzitseni Kuchita Chifuniro Chanu”

“Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu, pakuti inu ndinu Mulungu wanga.”—SAL. 143:10.

1, 2. Kodi kuganizira zimene Mulungu amafuna kungatithandize bwanji? N’chifukwa chiyani tikambirana za Davide m’nkhani ino?

KODI munayamba mwakwera pamwamba pa phiri lalitali n’kumayang’ana malo amene mukufuna kupita? Munthu akakhala pamwamba amaona zinthu bwino ndipo zimakhala zosavuta kudziwa njira yoyenera kutenga kuti akafike pamalo enaake. Mfundo ngati imeneyi ikhozanso kuthandiza tikamasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Mlengi wathu amaona zinthu m’njira yapamwamba kwambiri. Kuona zinthu mmene iye amazionera kungatithandize ‘kuyenda m’njira’ imene imamusangalatsa.—Yes. 30:21.

2 Pa moyo wake wonse, Davide ankayesetsa kuganizira zimene Mulungu amafuna. Iye anali munthu amene ankatumikira Yehova Mulungu ndi mtima wathunthu. Kuti tiphunzire kwa iye, tiyeni tikambirane zochitika zina pa moyo wake.—1 Maf. 11:4.

DAVIDE ANKALEMEKEZA KWAMBIRI DZINA LA MULUNGU

3, 4. (a) N’chiyani chinalimbikitsa Davide kukamenyana ndi Goliati? (b) Kodi Davide ankaona bwanji dzina la Mulungu?

3 Taganizirani za nthawi imene Davide anapita kukakumana ndi Goliati, yemwe anali ngwazi ya Afilisti. N’chiyani chinalimbikitsa Davide, yemwe anali wachinyamata, kuti akamenyane ndi chiphona chachitali mamita 2.9 komanso chokhala ndi zida za nkhondo? (1 Sam. 17:4, mawu a m’munsi) Kodi kunali kulimba mtima kapena kukhulupirira Mulungu? Zinthu ziwiri zonsezi zinamuthandiza. Koma kulemekeza Yehova ndiponso dzina lake n’kumene kunamuthandiza kwambiri kukamenyana ndi chiphonacho. Chifukwa chopsa mtima, Davide anafunsa kuti: “Kodi Mfilisiti wosadulidwa ameneyu ndani kuti azinyoza asilikali a Mulungu wamoyo?”—1 Sam. 17:26.

4 Pokumana ndi Goliati, Davide ananena kuti: “Iwe ukubwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwera kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wam’tonza.” (1 Sam. 17:45) Chifukwa chodalira Mulungu woona, Davide anapha chiphonachi ndi mwala umodzi wokha. Si nthawi yokhayi pamene Davide anadalira Yehova ndiponso kulemekeza kwambiri dzina lake. Iye ankachita zimenezi pa moyo wake wonse. Davide ankalimbikitsanso Aisiraeli anzake ‘kunyadira dzina loyera la Yehova.’—Werengani 1 Mbiri 16:8-10.

5. Kodi mawu onyoza a Goliati angafanane ndi chiyani masiku ano?

5 Kodi mumanyadira kuti Yehova ndi Mulungu wanu? (Yer. 9:24) Kodi mumachita chiyani ngati aneba, anzanu akuntchito, anzanu akusukulu kapena achibale akunyoza Yehova kapena Mboni zake? Kodi mumalankhula chilichonse ngati dzina la Yehova likunyozedwa, n’kudalira kuti iye akuthandizani? N’zoona kuti pali “nthawi yokhala chete” koma sitiyenera kuchita manyazi kudziwika kuti ndife Mboni za Yehova ndiponso otsatira a Yesu. (Mlal. 3:1, 7; Maliko 8:38) Tiyenera kulankhula mosamala ndiponso mwaulemu kwa anthu onyoza choonadi. Koma tisakhale ngati Aisiraeli amene “anachita mantha kwambiri” ataopsezedwa ndi mawu onyoza a Goliati. (1 Sam. 17:11) M’malomwake, tizilankhula molimba mtima kuti tiyeretse dzina la Yehova Mulungu. Cholinga chathu chizikhala kuthandiza anthu kuti amudziwe bwino. Ndipo tizigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu powathandiza kudziwa kufunika komuyandikira.—Yak. 4:8.

6. Kodi cholinga cha Davide chinali chiyani pokamenyana ndi Goliati? Nanga ife tiyenera kukhala ndi cholinga chotani?

6 Kodi nkhani ya Davide ndi Goliati imatiphunzitsanso chiyani? Davide atafika kumalo omenyera nkhondo, anafunsa kuti: “Kodi munthu amene angakaphe Mfilisiti ameneyu ndi kuchotsa chitonzo pa Isiraeli amuchitira chiyani?” Poyankha, anthuwo anabwereza zimene ananena poyamba. Iwo anati: “Munthu amene angamukanthe [Goliati] ndi kumupha, mfumu idzam’patsa chuma chochuluka ndi kum’patsanso mwana wake wamkazi.” (1 Sam. 17:25-27) Koma cholinga cha Davide sichinali kupeza zinthu. Anali ndi cholinga chapamwamba kwambiri. Iye ankafunitsitsa kulemekeza Mulungu woona. (Werengani 1 Samueli 17:46, 47.) Nanga bwanji ifeyo? Kodi timafunitsitsa kutchuka m’dzikoli kapena kukhala ndi chuma chambiri? Tiyenera kukhala ngati Davide amene anaimba kuti: “Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine anthu inu, tiyeni tonse tikweze dzina lake.” (Sal. 34:3) Nthawi zonse tizikhulupirira Mulungu ndiponso kuchita zinthu zolemekeza dzina lake osati lathu.—Mat. 6:9.

7. Kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu kuti tithe kulalikirabe pokumana ndi anthu onyoza?

7 Kuti Davide alimbe mtima kukamenyana ndi Goliati, anafunika kudalira kwambiri Yehova. Mnyamatayu anali ndi chikhulupiriro champhamvu. Iye analimbitsa chikhulupiriro chake pa nthawi imene anali m’busa chifukwa ankadalira Mulungu. (1 Sam. 17:34-37) Ifenso timafunika kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu kuti tipitirize kulalikira ngakhale pamene tikukumana ndi anthu onyoza. Kudalira Mulungu tsiku ndi tsiku n’kumene kungalimbitse chikhulupiriro chathu. Mwachitsanzo, tikakhala pa ulendo, tingalankhule ndi anthu amene tayandikana nawo n’kukambirana nawo mfundo za m’Baibulo. Tizilankhulanso ndi anthu amene timakumana nawo m’njira tikamalalikira kunyumba ndi nyumba.—Mac. 20:20, 21.

DAVIDE ANKAYEMBEKEZA YEHOVA

8, 9. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti ankaganizira zofuna za Yehova pamene Sauli ankafuna kumupha?

8 Umboni wina wakuti Davide ankadalira kwambiri Yehova ndi mmene iye ankachitira zinthu ndi Sauli, yemwe anali mfumu yoyamba ya Isiraeli. Chifukwa cha nsanje, Sauli anayesa maulendo atatu kulasa Davide ndi mkondo koma Davide ankazemba ndipo sanafune kubwezera. Kenako anathawa. (1 Sam. 18:7-11; 19:10) Ndiyeno Sauli anatenga amuna osankhidwa 3,000 mu Isiraeli monse n’kumasakasaka Davide m’chipululu. (1 Sam. 24:2) Kenako mosazindikira, Sauli analowa m’phanga limene Davide ndi anthu ake anabisala. Uwu unali mwayi woti Davide athane ndi mfumu imene inkafuna kumupha. Ndipotu Mulungu anali atasankha Davide kuti akhale mfumu ya Isiraeli m’malo mwa Sauli. (1 Sam. 16:1, 13) Davide akanamvera malangizo a anthu ake akanaphadi Sauli. Koma Davide anati: “Sindinayenere m’pang’ono pomwe kuchitira mbuyanga zimenezi pamaso pa Yehova. Iye ndi wodzozedwa wa Yehova.” (Werengani 1 Samueli 24:4-7.) Pa nthawiyi, Sauli anali adakali mfumu yodzozedwa ndi Mulungu. Davide sanafune kulanda ufumu wa Sauli chifukwa Yehova anali asanamuchotse. M’malomwake, anangodula kansalu ka m’munsi mwa malaya a Sauli. Apa anasonyeza kuti analibe maganizo ofuna kumupha.—1 Sam. 24:11.

9 Pa nthawi yomaliza imene Davide anaona Sauli, anasonyezanso kuti ankalemekeza wodzozedwa wa Mulungu. Davide ndi Abisai anafika pamsasa umene Sauli ndi asilikali ake ankagona. Apa Abisai anaona kuti Mulungu wapereka Sauli m’manja mwa Davide ndipo anapempha kuti amubaye ndi kumukhomerera pansi ndi mkondo. Koma Davide sanalole zimenezi. (1 Sam. 26:8-11) Davide ankafunitsitsa kutsatira malangizo a Mulungu choncho sanamvere zimene Abisai anamuuza podziwa kuti n’zosemphana ndi zimene Yehova ankafuna.

10. Kodi nafenso tingakumane ndi zotani? Nanga n’chiyani chingatithandize kuti titsatire maganizo a Yehova?

10 Nafenso anzathu akhoza kutikakamiza kuti titsatire maganizo awo m’malo motilimbikitsa kuchita zimene Yehova amafuna. Mofanana ndi Abisai, anthuwo angatilimbikitse kuchita zinthu mosaganizira zimene Mulungu amafuna. Kuti asatipusitse, tiyenera kudziwa bwino maganizo a Yehova pa nkhaniyo n’kutsimikiza mumtima mwathu kuwatsatira.

11. Kodi inuyo mwaphunzira chiyani kwa Davide pa nkhani yoganizira kwambiri zimene Mulungu amafuna?

11 Davide anapemphera kwa Yehova kuti: “Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu.” (Werengani Salimo 143:5, 8, 10.) M’malo modalira maganizo ake kapena kumvera zonena za anthu ena, Davide ankafunitsitsa kuphunzitsidwa ndi Mulungu. Iye ‘ankasinkhasinkha zochita za Yehova ndiponso kuganizira ntchito ya manja ake ndi mtima wonse.’ Nafenso tikhoza kudziwa zimene Yehova Mulungu amafuna ngati timaphunzira Baibulo mwakhama n’kumasinkhasinkha mmene iye ankachitira zinthu ndi anthu.

DAVIDE ANKATSATIRA MFUNDO ZA M’CHILAMULO

12, 13. N’chifukwa chiyani Davide anathira pansi madzi amene amuna atatuwo anamubweretsera?

12 Davide anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yofunitsitsa kutsatira mfundo za m’Chilamulo. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika Davide atanena kuti ankafunitsitsa kumwa “madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu.” Asilikali atatu a Davide anakalowa mwamphamvu mumzindawo, womwe pa nthawiyo unali utalandidwa ndi Afilisiti. Iwo anakatunga madzi m’chitsimecho n’kubwera nawo. Koma “Davide anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.” N’chifukwa chiyani sanamwe? Iye anafotokoza kuti: “Sindingachite zimenezo chifukwa ndimalemekeza Mulungu wanga. Kodi ndimwe magazi a anthuwa omwe anaika moyo wawo pachiswe? Iwowa akanataya moyo wawo pokatunga madziwa.”—1 Mbiri 11:15-19.

13 Davide anadziwa kuti Chilamulo chimanena kuti magazi sayenera kudyedwa koma kuperekedwa kwa Yehova. Iye ankadziwa kuti “moyo wa nyama [kapena munthu] uli m’magazi.” Komatu Davide anakana madzi osati magazi. Ndiye anakaniranji? Iye anakana chifukwa ankadziwa mfundo ya m’lamulolo. Davide ankaona kuti madziwo anali amtengo wapatali ngati magazi a amuna atatuwa. Choncho ankaona kuti n’kulakwa kwambiri kumwa madziwo. Chotero sanamwe koma anawathira pansi.—Lev. 17:11; Deut. 12:23, 24.

14. N’chiyani chinathandiza Davide kudziwa maganizo a Yehova?

14 Nthawi zonse Davide ankayesetsa kuganizira chilamulo cha Mulungu. Iye anaimba kuti: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.” (Sal. 40:8) Davide ankaphunzira ndiponso kusinkhasinkha kwambiri chilamulo cha Mulungu. Iye ankakhulupirira kuti malamulo a Yehova ndi anzeru. Choncho Davide ankafunitsitsa kumvera Chilamulo cha Mose komanso mfundo zake. Tikamaphunzira Baibulo, tiyenera kusinkhasinkha zimene tikuwerenga n’kumazisunga mumtima mwathu. Kuchita zimenezi kungatithandize kudziwa zimene zimakondweretsa Yehova pa nkhani zosiyanasiyana.

15. Kodi Solomo analephera bwanji kutsatira Chilamulo cha Mulungu?

15 Yehova Mulungu ankakonda kwambiri Solomo, yemwe anali mwana wa Davide. Koma patapita nthawi, Solomo anasiya kulemekeza Chilamulo cha Mulungu. Iye sanamvere lamulo la Yehova lakuti mfumu ya Isiraeli ‘isachulukitse akazi.’ (Deut. 17:17) Solomo anakwatira akazi ambirimbiri a mitundu ina. Atakalamba, “akazi ake anali atapotoza mtima wake moti iye anali kutsatira milungu ina.” Kaya iye anachita izi pa zifukwa zotani, mfundo ndi yakuti: “Solomo anayamba kuchita zinthu zimene zinali zoipa m’maso mwa Yehova, ndipo sanatsatire Yehova ndi mtima wonse ngati Davide bambo ake.” (1 Maf. 11:1-6) Apa zikusonyezeratu kuti ndi nzeru kutsatira malamulo ndiponso mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri tikamaganiza zolowa m’banja.

16. Kodi kumvetsa mfundo ya lamulo lakuti tizikwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye” kungathandize bwanji omwe akufuna kulowa m’banja?

16 Kodi timatani munthu wosakhulupirira akayamba kutikopa? Kodi timatsanzira Davide kapena Solomo? Akhristu oona amauzidwa kuti ayenera kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Izi zikutanthauza kuti Mkhristu akafuna kulowa m’banja ayenera kukwatirana ndi Mkhristu mnzake. Koma kumvetsa mfundo ya m’lamulo limeneli kungatithandize kuti tisayambe n’komwe kukopana ndi anthu osakhulupirira.

17. N’chiyani chingatithandize kupewa zolaula?

17 Chitsanzo cha Davide pa nkhani yofunitsitsa kutsatira malangizo a Mulungu chingatithandizenso kupewa zolaula. Tawerengani malemba awa n’kuganizira mfundo zake. Ndiyeno yesani kuona maganizo a Yehova pa nkhani imeneyi. (Werengani Salimo 119:37; Mateyu 5:28, 29; Akolose 3:5.) Kuganizira mfundo zake zapamwamba kungatithandize kuti tipeweretu zolaula zilizonse.

NTHAWI ZONSE MUZIONA ZINTHU MMENE MULUNGU AMAZIONERA

18, 19. (a) N’chiyani chinathandiza Davide kukhalabe pa ubwenzi ndi Mulungu ngakhale kuti anali wopanda ungwiro? (b) Nanga inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?

18 Ngakhale kuti Davide ankachita bwino zinthu zambiri, iye anachita machimo akuluakulu. (2 Sam. 11:2-4, 14, 15, 22-27; 1 Mbiri 21:1, 7) Koma akachimwa, ankalapa. Iye anatumikira Mulungu “ndi mtima wosagawanika.” (1 Maf. 9:4) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti Davide ankayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna.

19 Ifenso tingakhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ngakhale kuti ndife opanda ungwiro. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndiponso kusinkhasinkha zimene timaphunzira kuti zikhazikike mumtima mwathu. Ndiyeno tizichita zinthu mogwirizana ndi zimene taphunzirazo. Tikamatero, tidzafanana ndi wamasalimo amene anapempha Yehova modzichepetsa kuti: “Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu.”