Zochuluka Zimene Anali Nazo Zinathandiza Anthu Osowa
MU 49 C.E., Petulo, Yakobo ndi Yohane, “amene anali ngati mizati” ya mpingo wachikhristu, anatuma Paulo ndi Baranaba kukalalikira kwa anthu a mitundu ina. Koma anawauza kuti polalikira azikumbukira Akhristu aumphawi. (Agal. 2:9, 10) Kodi iwo anachita bwanji zimenezi?
Makalata a Paulo amasonyeza kuti iye ankaganiziradi aumphawi. Mwachitsanzo, iye analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Ponena za chopereka chopita kwa oyerawo, inunso tsatirani malangizo amene ndinapereka ku mipingo ya ku Galatiya. Tsiku lililonse loyamba la mlungu, aliyense wa inu aziika kenakake pambali kunyumba kwake malinga ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wake, kuti ndikadzafika, zopereka zisadzaperekedwe pa nthawi imeneyo. Koma ndikadzafika kumeneko, amuna alionse amene mungawavomereze m’makalata, ndidzawatuma kuti adzapititse mphatso yanu yachifundoyo ku Yerusalemu.”—1 Akor. 16:1-3.
M’kalata yake yachiwiri yopita kwa Akorinto, Paulo anatchulanso cholinga cha zopereka zimene anatchula m’kalata yoyamba. Iye anati: “Ndikufuna kuti zochuluka zimene muli nazo zithandizire pa zimene iwowo akusowa.”—2 Akor. 8:12-15.
Pamene Paulo ankalembera kalata Akhristu a ku Roma cha m’ma 56 C.E., zoperekazi zinali zitatsala pang’ono kusonkhanitsidwa pamodzi. Iye anawauza kuti: “Ndatsala pang’ono kupita ku Yerusalemu kukatumikira oyera. Abale amene ali ku Makedoniya ndi ku Akaya akhala ali ofunitsitsa kupereka mphatso kwa oyera osauka a ku Yerusalemu.” (Aroma 15:25, 26) Zikuoneka kuti Paulo anapereka mphatsozi pasanapite nthawi yaitali. Tikutero chifukwa chakuti atafika ku Yerusalemu n’kumangidwa, iye anauza bwanamkubwa wachiroma dzina lake Felike kuti: “Ndinabwera kudzapatsa mtundu wanga mphatso zachifundo, ndiponso kudzapereka nsembe.”—Mac. 24:17.
Zimene Paulo ananena zokhudza abale a ku Makedoniya zimatithandiza kudziwa mtima umene Akhristu oyambirira anali nawo. Ponena za iwo, iye anati: “Anapitiriza kutipempha mochokera pansi pa mtima ndiponso mochonderera kwambiri, kuti tiwapatse mwayi wopereka nawo mphatso zachifundo.” Ndiyeno mtumwiyu analimbikitsa Akorinto kutengera chitsanzo chimenechi. Iye anawauza kuti: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” N’chiyani chinalimbikitsa Akhristu m’mipingoyi kuti akhale ndi mtima wopereka? Sikuti ankangofuna ‘kupatsa oyerawo zinthu zochuluka zimene ankafunikira, koma ankachititsanso anthu ambiri kupereka mapemphero ochuluka oyamika Mulungu.’ (2 Akor. 8:4; 9:7, 12) Nafenso tingakhale ndi cholinga chimenechi popereka zopereka. Yehova Mulungu adzatidalitsa kwambiri tikamasonyeza mtima wopatsa umenewu ndipo tizikumbukira kuti madalitso ake ndi amene amalemeretsa.—Miy. 10:22.
MMENE ENA AMAPEREKERA ZOPEREKA ZA NTCHITO YAPADZIKO LONSE
Mofanana ndi nthawi ya Paulo, Akhristu ambiri masiku ano amapanga bajeti kapena kuika kandalama “kenakake pambali” kuti akaponye m’mabokosi a zopereka za “Ntchito Yapadziko Lonse.” (1 Akor. 16:2) Mwezi uliwonse mipingo imatumiza zopereka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha zopereka zanu ku maofesi ngati amenewa. Mungafunse ku ofesi ya nthambi m’dziko lanu kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi. Adiresi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.pr418.com/ny. Mungapereke zopereka zanu m’njira izi:
ZOPEREKA MWACHINDUNJI
Mukhoza kupereka ndalama, zinthu ngati ndolo, mphete, zibangiri ndiponso zinthu zina zamtengo wapatali.
Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti zinthuzo ndi chopereka.
ZONGOBWEREKA
Mungapereke ndalama n’kufotokoza kuti ngati nthawi ina mungazifune mudzaitanitsa.
Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti ndalamazo ndi zongobwereka.
MPHATSO ZINA
Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali, pali njira zinanso zoperekera zinthu popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu padziko lonse. Njira zimenezi zili m’munsimu. Musanasankhe njira iliyonse, muyenera kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziwe njira zimene ndi zotheka m’dziko lanu ndiponso mmene mungachitire. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenera kufunsanso anthu odziwa bwino za malamulo ndiponso misonkho.
Inshulansi: Mungakonze zoti gulu la Yehova lidzalandire ndalama za inshulansi kapena za penshoni.
Maakaunti Akubanki: Mukhoza kuikiza m’manja mwa gulu la Yehova maakaunti anu akubanki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, gululi lidzatenge zinthuzi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.
Masheya: Mungapereke ku gulu la Yehova masheya amene muli nawo m’kampani kapena kukonza zoti lidzalandire mukadzamwalira.
Malo ndi Nyumba: Mungapereke ku gulu la Yehova malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe. Ngati ili nyumba yoti mukukhalamo, mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo.
Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ndi boma kuti gulu la Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.
Ngati mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatso zimenezi, lankhulani ndi a ku Accounting Office pa telefoni kapena alembereni kalata pa adiresi imene ili pansipa. Apo ayi, mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.